< Numeri 17 >

1 Yehova anawuza Mose kuti,
וידבר יהוה אל משה לאמר
2 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo akupatse ndodo khumi ndi ziwiri, imodzi kuchokera kwa mtsogoleri wa fuko lililonse. Ulembe dzina la munthu aliyense pa ndodo yake.
דבר אל בני ישראל וקח מאתם מטה מטה לבית אב מאת כל נשיאהם לבית אבתם--שנים עשר מטות איש את שמו תכתב על מטהו
3 Pa ndodo ya Levi ulembepo dzina la Aaroni, chifukwa pafunika ndodo imodzi ya mtsogoleri pa fuko lililonse.
ואת שם אהרן תכתב על מטה לוי כי מטה אחד לראש בית אבותם
4 Uyike ndodozo mu tenti ya msonkhano, kutsogolo kwa Bokosi la Umboni, kumene ndimakumana nawe.
והנחתם באהל מועד--לפני העדות אשר אועד לכם שמה
5 Ndodo ya munthu amene ndamusankha idzachita maluwa potero ndidzaletsa madandawulo osatha a Aisraeli otsutsana nawe.”
והיה האיש אשר אבחר בו--מטהו יפרח והשכתי מעלי את תלנות בני ישראל אשר הם מלינם עליכם
6 Choncho Mose anayankhula ndi Aisraeli, ndipo atsogoleri awo anapereka ndodo khumi ndi ziwiri, imodzi kuchokera kwa mtsogoleri wa fuko lililonse ndipo ndodo ya Aaroni inali pakati pa ndodo zawozo.
וידבר משה אל בני ישראל ויתנו אליו כל נשיאיהם מטה לנשיא אחד מטה לנשיא אחד לבית אבתם--שנים עשר מטות ומטה אהרן בתוך מטותם
7 Mose anayika ndodozo pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano.
וינח משה את המטת לפני יהוה באהל העדת
8 Pa tsiku lotsatira Mose analowa mu tenti ya msonkhanoyo ndipo anaona kuti ndodo ya Aaroni, yomwe inkayimira fuko la Levi, sinangophuka masamba chabe, komanso inachita maluwa nʼkubala zipatso za alimondi.
ויהי ממחרת ויבא משה אל אהל העדות והנה פרח מטה אהרן לבית לוי ויצא פרח ויצץ ציץ ויגמל שקדים
9 Choncho Mose anatulutsa ndodo zonse pamaso pa Yehova napita nazo kwa Aisraeli onse. Iwowo anaziona ndipo munthu aliyense anatenga ndodo yake.
ויצא משה את כל המטת מלפני יהוה אל כל בני ישראל ויראו ויקחו איש מטהו
10 Yehova anawuza Mose kuti, “Bwezera ndodo ya Aaroni patsogolo pa Bokosi la Umboni, kuti chikhale chizindikiro cha kuwukira kwawo. Zimenezi zidzathetsa kudandaula kwawo kotsutsana nane, kuopa kuti angafe.”
ויאמר יהוה אל משה השב את מטה אהרן לפני העדות למשמרת לאות לבני מרי ותכל תלונתם מעלי ולא ימתו
11 Mose anachita monga Yehova anamulamulira.
ויעש משה כאשר צוה יהוה אתו כן עשה
12 Aisraeli anati kwa Mose, “Tikufa! Tatayika, tonse tatayika!
ויאמרו בני ישראל אל משה לאמר הן גוענו אבדנו כלנו אבדנו
13 Aliyense woyandikira chihema adzafa. Kodi ndiye kuti tonse tikufa?”
כל הקרב הקרב אל משכן יהוה ימות האם תמנו לגוע

< Numeri 17 >