< Numeri 15 >

1 Yehova anawuza Mose kuti,
Und der HERR redete mit Mose und sprach:
2 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukupatsanilo,
Rede mit den Kindern Israel und sprich zu ihnen: Wenn ihr in das Land eurer Wohnung kommt, das ich euch geben werde,
3 ndipo mukamadzapereka kwa Yehova, nsembe yotentha pa moto ya ngʼombe kapena nkhosa monga fungo lokoma kwa Yehova, kaya ndi nsembe yopsereza kapena nsembe zina, nsembe yapadera chifukwa cha lumbiro kapena nsembe yoperekedwa mwaufulu kapenanso yoperekedwa pa chikondwerero,
und wollt dem HERRN Opfer tun, es sei ein Brandopfer oder ein Opfer zum besonderen Gelübde oder ein freiwilliges Opfer oder euer Festopfer, auf daß ihr dem HERRN einen süßen Geruch machet von Rindern oder von Schafen:
4 munthu amene akubweretsa zopereka zake, azikapereka kwa Yehova chopereka chachakudya cholemera kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta wokwana lita imodzi.
wer nun seine Gabe dem HERRN opfern will, der soll das Speisopfer tun, ein Zehntel Semmelmehl, mit einem viertel Hin Öl;
5 Pamodzi ndi mwana wankhosa aliyense wa nsembe yopsereza kapena nsembe ina, muzikakonzanso lita imodzi la vinyo ngati chopereka cha chakumwa.’”
und Wein zum Trankopfer, auch ein viertel Hin, zu dem Brandopfer oder sonst zu dem Opfer, da ein Lamm geopfert wird.
6 “Pamodzi ndi nkhosa yayimuna, muzikakonzanso chopereka cha chakudya cholemera makilogalamu awiri a ufa wosalala, wosakaniza ndi mafuta okwanira lita imodzi ndi theka,
Wenn aber ein Widder geopfert wird, sollst du das Speisopfer machen aus zwei Zehntel Semmelmehl, mit einem drittel Hin Öl gemengt,
7 ndi vinyo wokwanira lita imodzi ndi theka ngati chopereka cha chakumwa. Muzikapereka monga nsembe yopereka fungo lokoma kwa Yehova.
und Wein zum Trankopfer, auch ein drittel Hin; das sollst du dem HERRN zum süßen Geruch opfern.
8 “‘Pamene mukukonza mwana wangʼombe wamwamuna kuti akhale nsembe yopsereza kapena nsembe ina iliyonse: ya lumbiro lapadera kapena nsembe yachiyanjano kwa Yehova,
Willst du aber ein Rind zum Brandopfer oder zum besonderen Gelübdeopfer oder zum Dankopfer dem HERRN machen,
9 pamodzi ndi mwana wangʼombe wamwamunayo muzibweretsa nsembe yachakudya yolemera makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta okwana malita awiri.
so sollst du zu dem Rind ein Speisopfer tun, drei Zehntel Semmelmehl, mit einem halben Hin Öl gemengt,
10 Komanso muzibweretsa vinyo wokwanira malita awiri monga chopereka chachakumwa. Imeneyi idzakhala chopereka chotentha pa moto kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova.
und Wein zum Trankopfer, auch ein halbes Hin; das ist ein Opfer dem HERRN zum süßen Geruch.
11 Ngʼombe yayimuna iliyonse kapena nkhosa yayimuna iliyonse, mwana wankhosa aliyense kapena mbuzi yayingʼono, zizikonzedwa motere.
Also sollst du tun mit einem Ochsen, mit einem Widder, mit einem Schaf oder mit einer Ziege.
12 Ngakhale zingachuluke chotani, chitani izi kwa iliyonse ya nyamazo.
Darnach die Zahl dieser Opfer ist, darnach soll auch die Zahl der Speisopfer und Trankopfer sein.
13 “‘Mbadwa iliyonse ya mu Israeli izichita zimenezi pamene ibweretsa nsembe yotentha pa moto kuti ikhale fungo lokoma kwa Yehova.
Wer ein Einheimischer ist, der soll solches tun, daß er dem HERRN opfere ein Opfer zum süßen Geruch.
14 Ku mibado yanu yonse ya mʼtsogolo, pamene mlendo kapena wina aliyense wokhala pakati panu apereka chopereka chotentha pa moto kuti chikhale fungo lokoma kwa Yehova, azichita mofanana ndi momwe inu mumachitira.
Und wenn ein Fremdling bei euch wohnt oder unter euch bei euren Nachkommen ist, und will dem HERRN ein Opfer zum süßen Geruch tun, der soll tun, wie ihr tut.
15 Gulu lonse likhale ndi malamulo ofanana a inu kapena mlendo wokhala pakati panu. Limeneli ndi lamulo lamuyaya kwa mibado imene ikubwera. Inuyo ndi mlendo mudzakhala wofanana pamaso pa Yehova.
Der ganzen Gemeinde sei eine Satzung, euch sowohl als den Fremdlingen; eine ewige Satzung soll das sein euren Nachkommen, daß vor dem HERRN der Fremdling sei wie ihr.
16 Mudzakhale ndi malamulo ndi miyambo yofanana, inuyo ndi mlendo wokhala pakati panu.’”
Ein Gesetz, ein Recht soll euch und dem Fremdling sein, der bei euch wohnt.
17 Yehova anawuza Mose kuti,
Und der HERR redete mit Mose und sprach:
18 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo unene kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukutengeraniko
Rede mit den Kindern Israel und sprich zu ihnen: Wenn ihr in das Land kommt, darein ich euch bringen werde,
19 ndipo mukakadya chakudya cha mʼdzikolo, mukapereke gawo lina kwa Yehova monga chopereka.
daß ihr esset von dem Brot im Lande, sollt ihr dem HERRN eine Hebe geben:
20 Pa buledi wanu woyamba, mukapereke mmodzi monga nsembe, ngati chopereka chochokera ku malo wopunthira tirigu.
als eures Teiges Erstling sollt ihr einen Kuchen zur Hebe geben; wie die Hebe von der Scheune,
21 Pa mibado yanu yonse muzidzapereka chopereka ichi kwa Yehova kuchokera ku zakudya zanu zoyamba za mʼnthaka.
also sollt ihr auch dem HERRN eures Teiges Erstling zur Hebe geben bei euren Nachkommen.
22 “‘Ndipo ngati muchimwa mosadziwa posasunga ena mwa malamulo awa amene Yehova wapereka kwa Mose,
Und wenn ihr aus Versehen dieser Gebote irgend eins nicht tut, die der HERR zu Mose geredet hat,
23 lina lililonse mwa malamulo a Yehova amene wapereka kwa inu kudzera mwa Mose, kuyambira tsiku limene Yehova anawapereka mpaka mibado ya mʼtsogolo,
alles, was der HERR euch durch Mose geboten hat, von dem Tage an, da er anfing zu gebieten auf eure Nachkommen;
24 ndipo ngati zimenezi zachitika osati mwadala ndipo gulu lonse silinadziwe, zikatero gulu lonselo lipereke mwana wangʼombe wamwamuna monga nsembe yopsereza kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova pamodzinso ndi chopereka chachakudya ndi chopereka cha chakumwa ndi mbuzi yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo potsata zimene zinalamulidwa.
wenn nun ohne Wissen der Gemeinde etwas versehen würde, so soll die ganze Gemeinde einen jungen Farren aus den Rindern zum Brandopfer machen, zum süßen Geruch dem HERRN, samt seinem Speisopfer, wie es recht ist, und einen Ziegenbock zum Sündopfer.
25 Wansembe apereke nsembe yopepesera machimo a gulu lonse la Aisraeli, ndipo adzakhululukidwa, pakuti linali tchimo lochita mosadziwa. Ndipo chifukwa cha tchimo lawolo, abweretse kwa Yehova nsembe yotentha pa moto ndi nsembe yopepesera machimo.
Und der Priester soll also die ganze Gemeinde der Kinder Israel versöhnen, so wird's ihnen vergeben sein; denn es ist ein Versehen. Und sie sollen bringen solch ihre Gabe zum Opfer dem HERRN und ihr Sündopfer vor dem HERRN über ihr Versehen,
26 Gulu lonse la Aisraeli ndi alendo okhala pakati pawo adzakhululukidwa chifukwa anthu onsewo anachimwa mosadziwa.
so wird's vergeben der ganzen Gemeinde der Kinder Israel, dazu auch dem Fremdling, der unter euch wohnt, weil das ganze Volk an solchem versehen teilhat.
27 “‘Koma ngati munthu mmodzi achimwa mosadziwa, ayenera kubweretsa mbuzi yayikazi ya chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo.
Wenn aber eine Seele aus Versehen sündigen wird, die soll eine jährige Ziege zum Sündopfer bringen.
28 Wansembe apereke nsembe yopepesera machimowo pamaso pa Yehova chifukwa cha munthu yemwe anachimwa mosadziwayo. Nsembe yopepesera tchimo lakelo ikaperekedwa, munthuyo adzakhululukidwa.
Und der Priester soll versöhnen solche Seele, die aus Versehen gesündigt hat, vor dem HERRN, daß er sie versöhne und ihr vergeben werde.
29 Lamulo lomweli ligwiritsidwe ntchito kwa aliyense wochimwa mosadziwa, kaya ndi mbadwa ya mu Israeli kapena mlendo.
Und es soll ein Gesetz sein für die, so ein Versehen begehen, für den Einheimischen unter den Kindern Israel und für den Fremdling, der unter ihnen wohnt.
30 “‘Koma aliyense amene achimwa mwadala, kaya ndi mbadwa kapena mlendo, nachitira chipongwe Yehova, ameneyo achotsedwe ndithu pakati pa anthu ake.
Wenn aber eine Seele aus Frevel etwas tut, es sei ein Einheimischer oder Fremdling, der hat den HERRN geschmäht. Solche Seele soll ausgerottet werden aus ihrem Volk;
31 Popeza wanyoza mawu a Yehova ndi kuphwanya malamulo ake. Munthu ameneyo achotsedwe ndithu, kuchimwa kwake kudzakhala pa iyeyo.’”
denn sie hat des HERRN Wort verachtet und sein Gebot lassen fahren. Ja, sie soll ausgerottet werden; die Schuld sei ihr.
32 Aisraeli ali mʼchipululu, munthu wina anapezeka akutola nkhuni tsiku la Sabata.
Als nun die Kinder Israel in der Wüste waren, fanden sie einen Mann Holz lesen am Sabbattage.
33 Amene anamupeza akutola nkhunizo anabwera naye kwa Mose ndi Aaroni ndi kwa gulu lonse
Und die ihn darob gefunden hatten, da er das Holz las, brachten sie ihn zu Mose und Aaron und vor die ganze Gemeinde.
34 ndipo anamutsekera mʼndende chifukwa sankadziwa choti achite naye.
Und sie legten ihn gefangen; denn es war nicht klar ausgedrückt, was man mit ihm tun sollte.
35 Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, “Munthu ameneyu ayenera kuphedwa. Gulu lonse liyenera kumugenda ndi miyala kunja kwa msasa.”
Der HERR aber sprach zu Mose: Der Mann soll des Todes sterben; die ganze Gemeinde soll ihn steinigen draußen vor dem Lager.
36 Choncho gululo linamutengera kunja kwa msasa ndi kumupha pomugenda ndi miyala, monga momwe Yehova analamulira Mose.
Da führte die ganze Gemeinde ihn hinaus vor das Lager und steinigten ihn, daß er starb, wie der HERR dem Mose geboten hatte.
37 Yehova anawuza Mose kuti,
Und der HERR sprach zu Mose:
38 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Pa mibado yanu yonse muzisokerera mphonje pa ngodya za zovala zanu ndipo pa ngodya ya mphonje iliyonse azisokererapo chingwe chobiriwira.
Rede mit den Kindern Israel und sprich zu ihnen, daß sie sich Quasten machen an den Zipfeln ihrer Kleider samt allen ihren Nachkommen, und blaue Schnüre auf die Quasten an die Zipfel tun;
39 Mudzakhala ndi mphonje zimenezi kuti mukaziona muzikakumbukira malamulo onse a Yehova ndi kuwamvera kuti musamatsatenso zilakolako za mʼmitima mwanu ndi za maso anu.
und sollen euch die Quasten dazu dienen, daß ihr sie ansehet und gedenket aller Gebote des HERRN und tut sie, daß ihr nicht von eures Herzens Dünken noch von euren Augen euch umtreiben lasset und abgöttisch werdet.
40 Motero mudzakumbukira kumvera malamulo anga ndipo mudzakhala opatulikira a Mulungu wanu.
Darum sollt ihr gedenken und tun alle meine Gebote und heilig sein eurem Gott.
41 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti ndikhale Mulungu wanu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”
Ich bin der HERR, euer Gott, der euch aus Ägyptenland geführt hat, daß ich euer Gott wäre, ich, der HERR, euer Gott.

< Numeri 15 >