< Numeri 14 >

1 Usiku umenewo gulu lonse la Aisraeli linalira mofuwula kwambiri.
ותשא כל העדה ויתנו את קולם ויבכו העם בלילה ההוא
2 Ndipo Aisraeli onse anayankhula motsutsana ndi Mose ndi Aaroni. Gulu lonse linanena kwa iwo kuti, “Kunali bwino tikanafera ku Igupto kapena mʼchipululu muno!
וילנו על משה ועל אהרן כל בני ישראל ויאמרו אלהם כל העדה לו מתנו בארץ מצרים או במדבר הזה לו מתנו
3 Nʼchifukwa chiyani Yehova akutilowetsa mʼdziko limenelo? Kodi kuti tikaphedwe ndi lupanga? Kuti akazi ndi ana athu akatengedwe ngati katundu wolanda ku nkhondo? Kodi sikungakhale bwino kuti tibwerere ku Igupto?”
ולמה יהוה מביא אתנו אל הארץ הזאת לנפל בחרב--נשינו וטפנו יהיו לבז הלוא טוב לנו שוב מצרימה
4 Ndipo anawuzana wina ndi mnzake kuti, “Tiyeni tisankhe mtsogoleri ndipo tibwerere ku Igupto.”
ויאמרו איש אל אחיו נתנה ראש ונשובה מצרימה
5 Koma Mose ndi Aaroni anadzigwetsa pansi chafufumimba pamaso pa Aisraeli onse omwe anasonkhana pamenepo.
ויפל משה ואהרן על פניהם לפני כל קהל עדת בני ישראל
6 Yoswa mwana wa Nuni ndi Kalebe mwana wa Yefune, omwe anali amodzi mwa amene anakazonda nawo dziko, anangʼamba zovala zawo
ויהושע בן נון וכלב בן יפנה מן התרים את הארץ--קרעו בגדיהם
7 ndipo anati kwa gulu lonse la Aisraeli, “Dziko limene tinakayendamo ndi kuliona ndi labwino kwambiri zedi.
ויאמרו אל כל עדת בני ישראל לאמר הארץ אשר עברנו בה לתור אתה--טובה הארץ מאד מאד
8 Ngati Yehova akukondwera nafe, adzatitsogolera kulowa mʼdziko limenelo. Dziko loyenda mkaka ndi uchi adzalipereka kwa ife,
אם חפץ בנו יהוה--והביא אתנו אל הארץ הזאת ונתנה לנו ארץ אשר הוא זבת חלב ודבש
9 koma musawukire Yehova. Komanso musaope anthu a mʼdzikomo, pakuti tidzawagonjetsa. Chitetezo chawachokera, koma ife Yehova ali nafe. Musawaope.”
אך ביהוה אל תמרדו ואתם אל תיראו את עם הארץ כי לחמנו הם סר צלם מעליהם ויהוה אתנו אל תיראם
10 Koma gulu lonse linayankhula zofuna kuwagenda miyala. Pamenepo ulemerero wa Yehova unaonekera kwa Aisraeli onse ku tenti ya msonkhano.
ויאמרו כל העדה לרגום אתם באבנים וכבוד יהוה נראה באהל מועד אל כל בני ישראל
11 Yehova anawuza Mose kuti, “Anthu awa adzandinyoza mpaka liti? Sadzandikhulupirira mpaka liti, ngakhale ndachita zizindikiro zozizwitsa zonsezi pakati pawo?
ויאמר יהוה אל משה עד אנה ינאצני העם הזה ועד אנה לא יאמינו בי בכל האתות אשר עשיתי בקרבו
12 Ndidzawakantha ndi mliri ndi kuwawononga. Koma ndidzakusandutsa iwe mtundu waukulu ndi wamphamvu kuposa iwo.”
אכנו בדבר ואורשנו ואעשה אתך לגוי גדול ועצום ממנו
13 Mose anati kwa Yehova, “Aigupto adzamva zimenezi! Mwa mphamvu yanu munawatulutsa anthu amenewa pakati pawo.
ויאמר משה אל יהוה ושמעו מצרים כי העלית בכחך את העם הזה מקרבו
14 Ndipo iwowo adzawuza anthu okhala mʼdziko lino zimenezi. Anthuwa amva kale kuti Inu Yehova mumakhala pakati pa anthu amenewa ndi kuti Inuyo Yehova mwawaonekera maso ndi maso. Mtambo wanu umakhala pamwamba pawo ndiponso mumayenda nawo mu mtambo woyima, masana ndi moto woyima, usiku.
ואמרו אל יושב הארץ הזאת שמעו כי אתה יהוה בקרב העם הזה אשר עין בעין נראה אתה יהוה ועננך עמד עלהם ובעמד ענן אתה הלך לפניהם יומם ובעמוד אש לילה
15 Tsono mukawapha anthu onsewa nthawi imodzi, mayiko amene anamva za Inu adzati,
והמתה את העם הזה כאיש אחד ואמרו הגוים אשר שמעו את שמעך לאמר
16 ‘Yehova walephera kuwalowetsa anthuwo mʼdziko lomwe anawalonjeza molumbira, ndipo wawapha mʼchipululu.’
מבלתי יכלת יהוה להביא את העם הזה אל הארץ אשר נשבע להם וישחטם במדבר
17 “Chonde Ambuye wonetsani mphamvu yanu monga munalonjezera kuti,
ועתה יגדל נא כח אדני כאשר דברת לאמר
18 ‘Yehova sakwiya msanga, ndipo ndi wodzaza ndi chikondi chosasinthika, wokhululukira tchimo ndi kuwukira. Koma Iye sadzaleka kulanga ochimwa. Iyeyo amalanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo kufikira mʼbado wachitatu ndi wachinayi.’
יהוה ארך אפים ורב חסד נשא עון ופשע ונקה לא ינקה--פקד עון אבות על בנים על שלשים ועל רבעים
19 Chifukwa cha kukula kwa chikondi chanu chosasinthika, akhululukireni anthuwa tchimo lawo monga mwakhala mukuwakhululukira kuchokera pa nthawi imene anachoka ku Igupto mpaka tsopano.”
סלח נא לעון העם הזה--כגדל חסדך וכאשר נשאתה לעם הזה ממצרים ועד הנה
20 Yehova anayankha kuti, “Ndawakhululukira monga wapemphera.
ויאמר יהוה סלחתי כדברך
21 Komabe, ndikunenetsa kuti pali Ine, ndiponso pamene dziko lapansi ladzaza ndi ulemerero wa Yehova,
ואולם חי אני וימלא כבוד יהוה את כל הארץ
22 palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu amene anaona ulemerero wanga ndi zizindikiro zozizwitsa zimene ndinazichita ku Igupto ndi mʼchipululu muno, koma osandimvera ndi kundiyesa kokwanira kakhumi,
כי כל האנשים הראים את כבדי ואת אתתי אשר עשיתי במצרים ובמדבר וינסו אתי זה עשר פעמים ולא שמעו בקולי
23 palibe ndi mmodzi yemwe wa anthu amenewa amene adzaone dziko limene ndinalonjeza ndi lumbiro kwa makolo awo. Aliyense amene anandinyoza sadzaliona dzikolo.
אם יראו את הארץ אשר נשבעתי לאבתם וכל מנאצי לא יראוה
24 Koma mtumiki wanga Kalebe, pakuti ali ndi mtima wosiyana ndi ena ndiponso amanditsatira ndi mtima wonse, ndidzamulowetsa mʼdziko limene anapitamolo ndipo zidzukulu zake zidzalandira dzikolo ngati cholowa chawo.
ועבדי כלב עקב היתה רוח אחרת עמו וימלא אחרי--והביאתיו אל הארץ אשר בא שמה וזרעו יורשנה
25 Ndipo popeza kuti Aamaleki ndi Akanaani akukhala ku chigwa, mawa mubwerere ndipo mupite ku chipululu podzera ku Nyanja Yofiira.”
והעמלקי והכנעני יושב בעמק מחר פנו וסעו לכם המדבר--דרך ים סוף
26 Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti,
וידבר יהוה אל משה ואל אהרן לאמר
27 “Kodi anthu oyipawa adzangʼungʼudza ndi kutsutsana nane mpaka liti? Ndamva madandawulo a Aisraeli ongʼungʼudzawa.
עד מתי לעדה הרעה הזאת אשר המה מלינים עלי את תלנות בני ישראל אשר המה מלינים עלי--שמעתי
28 Tsono awuze kuti, ‘Ndikulumbira pali Ine,’ akutero Yehova, ‘Ndidzakuchitirani zinthu zonse zimene ndamva inu mukunena:
אמר אלהם חי אני נאם יהוה אם לא כאשר דברתם באזני כן אעשה לכם
29 Mitembo yanu idzakhala ili ngundangunda mʼchipululu muno; mtembo wa munthu aliyense pakati panu amene ali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, amene anawerengedwa pa chiwerengero chija ndipo anangʼungʼudza motsutsana nane.
במדבר הזה יפלו פגריכם וכל פקדיכם לכל מספרכם מבן עשרים שנה ומעלה אשר הלינתם עלי
30 Palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene adzalowe mʼdziko lomwe ndinalumbira mokweza manja kuti likhale lanu, kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.
אם אתם תבאו אל הארץ אשר נשאתי את ידי לשכן אתכם בה--כי אם כלב בן יפנה ויהושע בן נון
31 Koma ana anu amene mukunena kuti adzatengedwa ngati katundu wolanda ku nkhondo, Ine ndidzawalowetsa kuti akasangalale mʼdziko limene munalikana.
וטפכם--אשר אמרתם לבז יהיה והביאתי אתם--וידעו את הארץ אשר מאסתם בה
32 Koma inu mitembo yanu idzakhala ngundangunda mʼchipululu muno.
ופגריכם אתם--יפלו במדבר הזה
33 Ana anu adzakhala abusa mʼchipululu muno zaka makumi anayi, kuvutika chifukwa cha kusakhulupirika kwanu, mpaka munthu womaliza mwa inu atafa mʼchipululu muno.
ובניכם יהיו רעים במדבר ארבעים שנה ונשאו את זנותיכם--עד תם פגריכם במדבר
34 Mudzavutika chifukwa cha machimo anu kwa zaka makumi anayi Chaka chimodzi chikuyimira tsiku limodzi la masiku makumi anayi amene munakazonda dziko lija ndipo mudzadziwa kuyipa kwake kwa kukangana ndi Ine.’
במספר הימים אשר תרתם את הארץ ארבעים יום--יום לשנה יום לשנה תשאו את עונתיכם ארבעים שנה וידעתם את תנואתי
35 Ine Yehova, ndanena, ndidzachitadi zimenezi kwa anthu onse oyipawa, amene agwirizana kunditsutsa. Adzathera mʼchipululu momwe muno, adzafera muno basi.”
אני יהוה דברתי אם לא זאת אעשה לכל העדה הרעה הזאת הנועדים עלי במדבר הזה יתמו ושם ימתו
36 Ndipo anthu amene Mose anawatuma kukazonda dziko aja anachoka pamaso pake nachititsa gulu lonse la anthu kuwukira Moseyo chifukwa chofalitsa mbiri yoyipa ya dzikolo.
והאנשים אשר שלח משה לתור את הארץ וישבו וילונו (וילינו) עליו את כל העדה להוציא דבה על הארץ
37 Anthu amene ankafalitsa mbiri yoyipa ya dzikolo anakanthidwa ndi mliri ndipo anafa pamaso pa Yehova.
וימתו האנשים מוצאי דבת הארץ רעה--במגפה לפני יהוה
38 Mwa anthu amene anakaona dzikolo, Yoswa mwana wa Nuni ndi Kalebe mwana wa Yefune ndi okhawo amene anapulumuka.
ויהושע בן נון וכלב בן יפנה חיו מן האנשים ההם ההלכים לתור את הארץ
39 Mose atafotokoza izi kwa Aisraeli onse, anthuwo analira kwambiri.
וידבר משה את הדברים האלה אל כל בני ישראל ויתאבלו העם מאד
40 Mmamawa tsiku linalo anapita mbali ya ku dziko la mapiri. Iwo anati, “Tachimwa, tipita ku dziko limene Yehova anatilonjeza.”
וישכמו בבקר ויעלו אל ראש ההר לאמר הננו ועלינו אל המקום אשר אמר יהוה--כי חטאנו
41 Koma Mose anati, “Chifukwa chiyani simukumvera lamulo la Yehova? Zimenezi sizitheka!
ויאמר משה למה זה אתם עברים את פי יהוה והוא לא תצלח
42 Musapite chifukwa Yehova sali pakati panu. Mudzagonjetsedwa ndi adani anu
אל תעלו כי אין יהוה בקרבכם ולא תנגפו לפני איביכם
43 chifukwa kumeneko mukakumana ndi Aamaleki ndi Akanaani. Popeza mwaleka kutsata Yehova, Iyeyo sadzakhala nanu ndipo mudzaphedwa ndi lupanga.”
כי העמלקי והכנעני שם לפניכם ונפלתם בחרב כי על כן שבתם מאחרי יהוה ולא יהיה יהוה עמכם
44 Komabe mwa maganizo awo anapita molunjika dziko la mapiri ngakhale kuti Mose sanachoke ndi Bokosi la Chipangano la Yehova pa msasa.
ויעפלו לעלות אל ראש ההר וארון ברית יהוה ומשה לא משו מקרב המחנה
45 Koma Aamaleki ndi Akanaani amene ankakhala ku dziko lamapirilo anatsika ndi kumenyana nawo ndipo anawakantha mʼnjira yonse mpaka ku Horima.
וירד העמלקי והכנעני הישב בהר ההוא ויכום ויכתום עד החרמה

< Numeri 14 >