< Numeri 13 >

1 Yehova anawuza Mose kuti,
ibi locutus est Dominus ad Mosen dicens
2 “Tuma anthu kuti akazonde dziko la Kanaani limene ndikupereka kwa Aisraeli. Kuchokera pa fuko lililonse utume munthu mmodzi amene ndi mtsogoleri wawo.”
mitte viros qui considerent terram Chanaan quam daturus sum filiis Israhel singulos de singulis tribubus ex principibus
3 Monga mwa mawu a Yehova, Mose anawatuma kuchokera ku chipululu cha Parani. Onsewo anali atsogoleri a Aisraeli.
fecit Moses quod Dominus imperarat de deserto Pharan mittens principes viros quorum ista sunt nomina
4 Mayina awo ndi awa: kuchokera ku fuko la Rubeni, Samuwa mwana wa Zakuri;
de tribu Ruben Semmua filium Zecchur
5 kuchokera ku fuko la Simeoni, Safati mwana wa Hori;
de tribu Symeon Saphat filium Huri
6 kuchokera ku fuko la Yuda, Kalebe mwana wa Yefune;
de tribu Iuda Chaleb filium Iepphonne
7 kuchokera ku fuko la Isakara, Igala mwana wa Yosefe;
de tribu Isachar Igal filium Ioseph
8 kuchokera ku fuko la Efereimu, Hoseya mwana wa Nuni;
de tribu Ephraim Osee filium Nun
9 kuchokera ku fuko la Benjamini, Paliti mwana wa Rafu;
de tribu Beniamin Phalti filium Raphu
10 kuchokera ku fuko la Zebuloni, Gadieli mwana wa Sodi;
de tribu Zabulon Geddihel filium Sodi
11 kuchokera ku fuko la Manase (fuko la Yosefe), Gadi mwana wa Susi;
de tribu Ioseph sceptri Manasse Gaddi filium Susi
12 kuchokera ku fuko la Dani, Amieli mwana wa Gemali;
de tribu Dan Ammihel filium Gemalli
13 kuchokera ku fuko la Aseri, Seturi mwana wa Mikayeli;
de tribu Aser Sthur filium Michahel
14 kuchokera ku fuko la Nafutali, Naabi mwana wa Vofisi;
de tribu Nepthali Naabbi filium Vaphsi
15 kuchokera ku fuko la Gadi, Geuweli mwana wa Maki.
de tribu Gad Guhel filium Machi
16 Amenewa ndiwo mayina a anthu amene Mose anawatuma kukazonda dzikolo. (Hoseya mwana wa Nuni, Mose anamupatsa dzina loti Yoswa).
haec sunt nomina virorum quos misit Moses ad considerandam terram vocavitque Osee filium Nun Iosue
17 Mose atawatuma kuti akazonde Kanaani anati, “Mupite kudzera ku Negevi, mukapitirire mpaka ku dziko la mapiri.
misit ergo eos Moses ad considerandam terram Chanaan et dixit ad eos ascendite per meridianam plagam cumque veneritis ad montes
18 Mukaone dzikolo kuti ndi lotani ndi anthu okhala mʼmenemo ngati ndi amphamvu kapena ofowoka, ochepa kapena ambiri.
considerate terram qualis sit et populum qui habitator est eius utrum fortis sit an infirmus pauci numero an plures
19 Nanga dziko limene akukhalako ndi lotani? Ndi labwino kapena loyipa? Mizinda imene akukhalamo ndi yotani? Kodi ilibe malinga kapena ndi ya malinga?
ipsa terra bona an mala urbes quales muratae an absque muris
20 Nthaka yake ndi yotani? Yachonde kapena yopanda chonde? Kodi dzikolo lili ndi mitengo kapena lilibe mitengo? Mukayesetse kubweretsako zipatso za mʼdzikomo.” (Inali nthawi yamphesa zoyamba kupsa).
humus pinguis an sterilis nemorosa an absque arboribus confortamini et adferte nobis de fructibus terrae erat autem tempus quando iam praecoquae uvae vesci possunt
21 Choncho anapita kukazonda dzikolo kuchokera ku chipululu cha Zini mpaka ku Rehobu, mopenyana ndi Lebo Hamati.
cumque ascendissent exploraverunt terram a deserto Sin usque Roob intrantibus Emath
22 Anapita kudzera ku Negevi ndi kukafika ku Hebroni, kumene Ahimani, Sesai ndi Talimai, ana a Anaki ankakhala. (Anamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri asanamange Zowani ku Igupto).
ascenderuntque ad meridiem et venerunt in Hebron ubi erant Ahiman et Sisai et Tholmai filii Enach nam Hebron septem annis ante Tanim urbem Aegypti condita est
23 Atafika ku chigwa cha Esikolo, anadulako nthambi ya mpesa ya phava limodzi la mphesa ndipo anthu awiri ananyamulizana, natenganso makangadza ndi nkhuyu.
pergentesque usque ad torrentem Botri absciderunt palmitem cum uva sua quem portaverunt in vecte duo viri de malis quoque granatis et de ficis loci illius tulerunt
24 Malo amenewo anawatcha chigwa cha Esikolo chifukwa cha phava la mphesa limene Aisraeli anadula kumeneko.
qui appellatus est Neelescol id est torrens Botri eo quod botrum inde portassent filii Israhel
25 Patapita masiku makumi anayi, anthu aja anabwerako kokazonda dziko lija.
reversique exploratores terrae post quadraginta dies omni regione circuita
26 Ndipo atabwerako anapita kwa Mose ndi Aaroni ndi kwa Aisraeli onse ku Kadesi mʼchipululu cha Parani. Kumeneko anafotokozera anthu onse nawaonetsanso zipatso za mʼdzikolo.
venerunt ad Mosen et Aaron et ad omnem coetum filiorum Israhel in desertum Pharan quod est in Cades locutique eis et omni multitudini ostenderunt fructus terrae
27 Anthuwo anafotokozera Mose kuti, “Tinapita ku dziko komwe munatituma. Dzikolo ndi loyenda mkaka ndi uchi ndipo zipatso zake ndi izi.
et narraverunt dicentes venimus in terram ad quam misisti nos quae re vera fluit lacte et melle ut ex his fructibus cognosci potest
28 Koma anthu amene amakhala mʼdzikomo ndi amphamvu, mizinda yawo ndi ya malinga aakulu kwambiri. Tinaonanso Aanaki kumeneko.
sed cultores fortissimos habet et urbes grandes atque muratas stirpem Enach vidimus ibi
29 Aamaleki amakhala ku Negevi, Ahiti, Ayebusi ndi Aamori amakhala mʼdziko la mapiri ndipo Akanaani amakhala pafupi ndi nyanja, mʼmbali mwa Yorodani.”
Amalech habitat in meridie Hettheus et Iebuseus et Amorreus in montanis Chananeus vero moratur iuxta mare et circa fluenta Iordanis
30 Koma Kalebe anawakhalitsa chete anthuwo pamaso pa Mose, ndipo anati, “Tiyeni tipite ndithu ndi kutenga dzikolo, pakuti tingathe kulitenga.”
inter haec Chaleb conpescens murmur populi qui oriebatur contra Mosen ait ascendamus et possideamus terram quoniam poterimus obtinere eam
31 Koma anthu aja amene anapita naye anati, “Sitingathe kulimbana ndi anthuwo popeza ndi amphamvu kuposa ifeyo.”
alii vero qui fuerant cum eo dicebant nequaquam ad hunc populum valemus ascendere quia fortior nobis est
32 Choncho anthuwo anafalitsa pakati pa Aisraeli mbiri yoyipa ya dziko lomwe anakalionalo. Iwo anati, “Dziko limene tinapita kukalizonda limawononga anthu okhala mʼmenemo. Ndipo anthu onse amene tinakawaona kumeneko ndi ataliatali.
detraxeruntque terrae quam inspexerant apud filios Israhel dicentes terram quam lustravimus devorat habitatores suos populum quem aspeximus procerae staturae est
33 Kumeneko tinaona Anefili (ana a Aanaki ochokera kwa Nefili). Ifeyo timangodziona ngati ziwala mʼmaso mwawo, ndipo kwa iwo timaonekadi motero ndithu.”
ibi vidimus monstra quaedam filiorum Enach de genere giganteo quibus conparati quasi lucustae videbamur

< Numeri 13 >