< Numeri 11 >

1 Anthu atadandaula kwa Yehova chifukwa cha mavuto awo, Yehovayo anamva ndipo anakwiya kwambiri. Kenaka moto wa Yehova unayaka pakati pawo ndi kutentha zigawo zina za kunja kwa msasa.
ויהי העם כמתאננים רע באזני יהוה וישמע יהוה ויחר אפו ותבער בם אש יהוה ותאכל בקצה המחנה
2 Anthuwo analira kwa Mose ndipo Moseyo atapemphera kwa Yehova, motowo unazima.
ויצעק העם אל משה ויתפלל משה אל יהוה ותשקע האש
3 Motero malowo anawatcha Tabera, chifukwa moto wa Yehova unayaka pakati pawo.
ויקרא שם המקום ההוא תבערה כי בערה בם אש יהוה
4 Anthu ena osokoneza amene anali pakati pa Aisraeli anayamba kukhumba chakudya cha ku Igupto ndipo Aisraeli nawonso anayamba kufuwula kwambiri nʼkumati, “Tikanangopeza nyama yoti nʼkudya!
והאספסף אשר בקרבו התאוו תאוה וישבו ויבכו גם בני ישראל ויאמרו מי יאכלנו בשר
5 Tikukumbukira nsomba zaulere zimene tinkadya ku Igupto komanso nkhaka, mavwende, anyezi wamitundumitundu ndi adyo.
זכרנו את הדגה אשר נאכל במצרים חנם את הקשאים ואת האבטחים ואת החציר ואת הבצלים ואת השומים
6 Koma tsopano chilakolako chathu chatha. Sitikuona kanthu kena kakudya koma mana basi!”
ועתה נפשנו יבשה אין כל--בלתי אל המן עינינו
7 Mana ankafanana ndi mbewu zamapira ndipo maonekedwe ake anali ngati ulimbo wowuma.
והמן כזרע גד הוא ועינו כעין הבדלח
8 Anthu ankapita kukatola manawo, nʼkumasinja mu mtondo kapena kupera. Ankawaphika mu mʼphika kapena kupanga makeke. Ndipo ankakoma ngati makeke ophikira mafuta a olivi.
שטו העם ולקטו וטחנו ברחים או דכו במדכה ובשלו בפרור ועשו אתו עגות והיה טעמו כטעם לשד השמן
9 Mame akamagwa pa msasawo usiku ankagwera kumodzi ndi manawo.
וברדת הטל על המחנה לילה ירד המן עליו
10 Mose anamva anthu a banja lililonse akufuwula, banja lililonse pa khomo la tenti yake. Yehova anakwiya kwambiri ndipo Mose anavutikanso mu mtima.
וישמע משה את העם בכה למשפחתיו--איש לפתח אהלו ויחר אף יהוה מאד ובעיני משה רע
11 Mose anafunsa Yehova kuti, “Chifukwa chiyani mwabweretsa mavuto otere pa mtumiki wanune? Nʼchiyani chimene ndachita choti sichinakusangalatseni mpaka kundisenzetsa katundu wa anthu onsewa?
ויאמר משה אל יהוה למה הרעת לעבדך ולמה לא מצתי חן בעיניך לשום את משא כל העם הזה--עלי
12 Kodi Ndine amene ndinatenga pathupi pa anthu onsewa? Kodi ndinawabala ndine? Bwanji mukundiwuza kuti ndiwanyamule mʼmanja mwanga, monga momwe mlezi amanyamulira kamwana, kupita nawo ku malo omwe munalonjeza ndi lumbiro kwa makolo awo?
האנכי הריתי את כל העם הזה--אם אנכי ילדתיהו כי תאמר אלי שאהו בחיקך כאשר ישא האמן את הינק על האדמה אשר נשבעת לאבתיו
13 Ndingayipeze kuti nyama yoti anthu onsewa adye? Iwowa akulirira ine kuti, ‘Tipatse nyama tidye!’
מאין לי בשר לתת לכל העם הזה כי יבכו עלי לאמר תנה לנו בשר ונאכלה
14 Sindingathe kusamala anthu onsewa ndekha. Katundu ameneyu ndi wolemera kwambiri kwa ine.
לא אוכל אנכי לבדי לשאת את כל העם הזה כי כבד ממני
15 Ngati umu ndi mmene muzichitira nane, chonde ingondiphani pompano. Koma ngati mwandikomera mtima ndiye ndisaonenso mavutowa.”
ואם ככה את עשה לי הרגני נא הרג--אם מצאתי חן בעיניך ואל אראה ברעתי
16 Yehova anawuza Mose kuti, “Undibweretsere anthu 70 ochokera pakati pa akuluakulu a Aisraeli, amene umawadziwa kuti ndiwo atsogoleri komanso akuluakulu a mabanja. Abwere ku tenti ya msonkhano kuti ayime kumeneko pamodzi ndi iwe.
ויאמר יהוה אל משה אספה לי שבעים איש מזקני ישראל אשר ידעת כי הם זקני העם ושטריו ולקחת אתם אל אהל מועד והתיצבו שם עמך
17 Ndidzatsika ndi kuyankhula nawe kumeneko, ndipo ndidzatenga mzimu umene uli pa iwe ndi kuyika pa iwowo. Adzakuthandiza kusenza nkhawa za anthuwa ndipo sudzasenzanso wekha.”
וירדתי ודברתי עמך שם ואצלתי מן הרוח אשר עליך ושמתי עליהם ונשאו אתך במשא העם ולא תשא אתה לבדך
18 “Uwawuze anthuwo kuti, ‘Mudziyeretse, kukonzekera mawa, pamene mudzadya nyama.’ Yehova anakumvani pamene munkalira kuti, ‘Zikanakhala bwino tikanapeza nyama yoti tidye! Tinkakhala bwino ku Igupto!’ Tsopano Yehova adzakupatsani nyama ndipo mudzayidyadi.
ואל העם תאמר התקדשו למחר ואכלתם בשר--כי בכיתם באזני יהוה לאמר מי יאכלנו בשר כי טוב לנו במצרים ונתן יהוה לכם בשר ואכלתם
19 Simudzadya tsiku limodzi lokha, kapena masiku awiri, kapena asanu, khumi kapena masiku makumi awiri,
לא יום אחד תאכלון ולא יומים ולא חמשה ימים ולא עשרה ימים ולא עשרים יום
20 koma mwezi wonse, mpaka itakukolani ndi kutopa nayo chifukwa mwakana Yehova yemwe ali pakati panu ndipo mwalira pamaso pake kuti, ‘Bwanji tinachoka ku Igupto?’”
עד חדש ימים עד אשר יצא מאפכם והיה לכם לזרא יען כי מאסתם את יהוה אשר בקרבכם ותבכו לפניו לאמר למה זה יצאנו ממצרים
21 Koma Mose anati, “Taonani pano ndili pakati pa anthu 600,000 amene ndi kuyenda nawo ndipo Inuyo mukuti, ‘Ndidzawapatsa nyama kuti adye mwezi wathunthu!’
ויאמר משה שש מאות אלף רגלי העם אשר אנכי בקרבו ואתה אמרת בשר אתן להם ואכלו חדש ימים
22 Kodi ngakhale titapha nkhosa ndi ngʼombe, zingawakwanire? Ngakhale titagwira nsomba zonse za mʼnyanja, kodi zingawakwanire iwowa?”
הצאן ובקר ישחט להם ומצא להם אם את כל דגי הים יאסף להם ומצא להם
23 Yehova anayankha Mose kuti, “Kodi dzanja langa ndi lalifupi? Uwona tsopano ngati zimene ndanenazo zichitike kapena ayi.”
ויאמר יהוה אל משה היד יהוה תקצר עתה תראה היקרך דברי אם לא
24 Choncho Mose anatuluka nakawuza anthu zomwe Yehova ananena. Anasonkhanitsa pamodzi akuluakulu makumi asanu ndi awiri aja ndi kuwayimiritsa mozungulira Chihema.
ויצא משה--וידבר אל העם את דברי יהוה ויאסף שבעים איש מזקני העם ויעמד אתם סביבת האהל
25 Ndipo Yehova anatsika mʼmitambo ndi kuyankhula naye ndipo anatengako mzimu womwe unali pa Mose ndi kuwuyika pa akuluakulu makumi asanu ndi awiri aja. Pamene mzimuwo unakhazikika pa akuluakuluwo, anayamba kunenera koma sanapitirize.
וירד יהוה בענן וידבר אליו ויאצל מן הרוח אשר עליו ויתן על שבעים איש הזקנים ויהי כנוח עליהם הרוח ויתנבאו ולא יספו
26 Koma anthu ena awiri omwe mayina awo anali Elidadi ndi Medadi, anatsalira mu msasa. Anali nawo mʼgulu la olembedwa aja, koma sanapite nawo ku Chihema. Komabe mzimu unakhala pa iwo ndipo ananenera ali mu msasa.
וישארו שני אנשים במחנה שם האחד אלדד ושם השני מידד ותנח עלהם הרוח והמה בכתבים ולא יצאו האהלה ויתנבאו במחנה
27 Mnyamata wina anathamanga kudzawuza Mose kuti, “Elidadi ndi Medadi akunenera mu msasa.”
וירץ הנער ויגד למשה ויאמר אלדד ומידד מתנבאים במחנה
28 Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose kuyambira ubwana wake, anayankha kuti, “Mbuye wanga Mose, aletseni!”
ויען יהושע בן נון משרת משה מבחריו--ויאמר אדני משה כלאם
29 Koma Mose anati, “Kodi ukuchita nsanje chifukwa cha ine? Ndikanakonda kuti anthu onse a Yehova akhale aneneri ndi kuti Yehova ayike mzimu wake pa iwo!”
ויאמר לו משה המקנא אתה לי ומי יתן כל עם יהוה נביאים--כי יתן יהוה את רוחו עליהם
30 Mose ndi akuluakulu a Israeli aja anabwerera ku msasa.
ויאסף משה אל המחנה--הוא וזקני ישראל
31 Pamenepo Yehova anawutsa mphepo yochokera ku nyanja imene inabweretsa zinziri. Zinzirizo zinagwera pansi kuzungulira msasa, mtunda wa kilomita imodzi mbali zonse ndipo msinkhu wake unali mita imodzi.
ורוח נסע מאת יהוה ויגז שלוים מן הים ויטש על המחנה כדרך יום כה וכדרך יום כה סביבות המחנה--וכאמתים על פני הארץ
32 Tsiku limenelo masana onse mpaka usiku ndiponso tsiku lotsatiralo, anthu anatuluka kunja kukatola zinziri. Palibe amene anasonkhanitsa zochepera makilogalamu 1,000 ndipo anaziyanika kuzungulira msasa wonse.
ויקם העם כל היום ההוא וכל הלילה וכל יום המחרת ויאספו את השלו--הממעיט אסף עשרה חמרים וישטחו להם שטוח סביבות המחנה
33 Koma pamene anthuwo ankadya nyamayo, asanayimeze nʼkomwe, ukali wa Yehova unafika pa iwo ndipo Iye anawakantha ndi mliri woopsa.
הבשר עודנו בין שניהם--טרם יכרת ואף יהוה חרה בעם ויך יהוה בעם מכה רבה מאד
34 Nʼchifukwa chake malowo anawatcha Kibiroti Hatava chifukwa pamenepo anakwirirapo anthu osusuka aja.
ויקרא את שם המקום ההוא קברות התאוה כי שם קברו את העם המתאוים
35 Kuchoka pa Kibiroti Hatava anthuwo anayenda kupita ku Heziroti ndipo anakhala kumeneko kwa kanthawi.
מקברות התאוה נסעו העם חצרות ויהיו בחצרות

< Numeri 11 >