< Numeri 1 >

1 Yehova anayankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai, mu tenti ya msonkhano, pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, mʼchaka chachiwiri atatuluka mu Igupto, kuti,
וידבר יהוה אל משה במדבר סיני באהל מועד באחד לחדש השני בשנה השנית לצאתם מארץ מצרים--לאמר
2 “Werengani Aisraeli onse mʼmafuko awo ndi mʼmabanja awo, lemba dzina la munthu wamwamuna aliyense, mmodzimmodzi.
שאו את ראש כל עדת בני ישראל למשפחתם לבית אבתם--במספר שמות כל זכר לגלגלתם
3 Iwe ndi Aaroni mwawerenge mwa magulu awo mu Israeli, amuna onse a zaka makumi awiri zakubadwa ndi opitirirapo omwe angathe kugwira ntchito ya usilikali.
מבן עשרים שנה ומעלה כל יצא צבא בישראל--תפקדו אתם לצבאתם אתה ואהרן
4 Munthu mmodzi wochokera ku fuko lililonse yemwe ndi mtsogoleri wa banja lake, ndiye akuthandizeni pa ntchitoyi.
ואתכם יהיו איש איש למטה--איש ראש לבית אבתיו הוא
5 Mayina a anthu amene akuthandizeniwo ndi awa: Elizuri mwana wa Sedeuri, kuchokera ku fuko la Rubeni,
ואלה שמות האנשים אשר יעמדו אתכם לראובן אליצור בן שדיאור
6 Selumieli mwana wa Zurisadai, kuchokera ku fuko la Simeoni,
לשמעון שלמיאל בן צורישדי
7 Naasoni mwana wa Aminadabu, kuchokera ku fuko la Yuda,
ליהודה נחשון בן עמינדב
8 Netanieli mwana wa Zuwara, kuchokera ku fuko la Isakara,
ליששכר נתנאל בן צוער
9 Eliabu mwana wa Heloni, kuchokera ku fuko la Zebuloni,
לזבולן אליאב בן חלן
10 Mwa ana a Yosefe: kuchokera ku fuko la Efereimu, Elisama mwana wa Amihudi; kuchokera ku fuko la Manase, Gamalieli mwana wa Pedazuri;
לבני יוסף--לאפרים אלישמע בן עמיהוד למנשה גמליאל בן פדהצור
11 Abidani mwana wa Gideoni, kuchokera ku fuko la Benjamini,
לבנימן אבידן בן גדעני
12 Ahiyezeri mwana wa Amisadai, kuchokera ku fuko la Dani,
לדן אחיעזר בן עמישדי
13 Pagieli mwana wa Okirani, kuchokera ku fuko la Aseri,
לאשר פגעיאל בן עכרן
14 Eliyasafu mwana wa Deuweli, kuchokera ku fuko la Gadi,
לגד אליסף בן דעואל
15 Ahira mwana wa Enani, kuchokera ku fuko la Nafutali.”
לנפתלי אחירע בן עינן
16 Amenewa ndi anthu amene anasankhidwa kuchokera mʼmagulu mwawo, eni mbumba a mafuko a makolo awo. Iwowa anali atsogoleri a mafuko a Israeli.
אלה קריאי (קרואי) העדה נשיאי מטות אבותם ראשי אלפי ישראל הם
17 Mose ndi Aaroni anatenga anthu amene mayina awo anaperekedwa,
ויקח משה ואהרן את האנשים האלה אשר נקבו בשמת
18 ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, anasonkhanitsa anthu onse pamodzi. Anthuwo anafotokoza za makolo awo mwa mafuko awo ndi mabanja awo. Ndipo mayina a amuna onse amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo analembedwa, mmodzimmodzi
ואת כל העדה הקהילו באחד לחדש השני ויתילדו על משפחתם לבית אבתם במספר שמות מבן עשרים שנה ומעלה--לגלגלתם
19 monga momwe Yehova analamulira Mose. Motero iyeyo anawawerenga mʼchipululu cha Sinai:
כאשר צוה יהוה את משה ויפקדם במדבר סיני
20 Kuchokera mwa ana a Rubeni, mwana wamwamuna woyamba wa Israeli: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali, anawalemba mayina awo, mmodzimmodzi monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
ויהיו בני ראובן בכר ישראל תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמות לגלגלתם--כל זכר מבן עשרים שנה ומעלה כל יצא צבא
21 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Rubeni chinali 46,500.
פקדיהם למטה ראובן--ששה וארבעים אלף וחמש מאות
22 Kuchokera mwa zidzukulu za Simeoni: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo, mmodzimmodzi monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
לבני שמעון תולדתם למשפחתם לבית אבתם פקדיו במספר שמות לגלגלתם--כל זכר מבן עשרים שנה ומעלה כל יצא צבא
23 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Simeoni chinali 59,300.
פקדיהם למטה שמעון--תשעה וחמשים אלף ושלש מאות
24 Kuchokera mwa zidzukulu za Gadi: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
לבני גד תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמות מבן עשרים שנה ומעלה--כל יצא צבא
25 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Gadi chinali 45, 650.
פקדיהם למטה גד--חמשה וארבעים אלף ושש מאות וחמשים
26 Kuchokera mwa zidzukulu za Yuda: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
לבני יהודה תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמת מבן עשרים שנה ומעלה--כל יצא צבא
27 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Yuda chinali 74, 600.
פקדיהם למטה יהודה--ארבעה ושבעים אלף ושש מאות
28 Kuchokera mwa zidzukulu za Isakara: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
לבני יששכר תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמת מבן עשרים שנה ומעלה--כל יצא צבא
29 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Isakara chinali 54,400.
פקדיהם למטה יששכר--ארבעה וחמשים אלף וארבע מאות
30 Kuchokera mwa zidzukulu za Zebuloni: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
לבני זבולן תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמת מבן עשרים שנה ומעלה--כל יצא צבא
31 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Zebuloni chinali 57,400.
פקדיהם למטה זבולן--שבעה וחמשים אלף וארבע מאות
32 Kuchokera mwa ana aamuna a Yosefe: Kuchokera mwa zidzukulu za Efereimu: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
לבני יוסף לבני אפרים תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמת מבן עשרים שנה ומעלה--כל יצא צבא
33 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Efereimu chinali 40,500.
פקדיהם למטה אפרים--ארבעים אלף וחמש מאות
34 Kuchokera mwa zidzukulu za Manase: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
לבני מנשה תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמות מבן עשרים שנה ומעלה--כל יצא צבא
35 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Manase chinali 32,200.
פקדיהם למטה מנשה--שנים ושלשים אלף ומאתים
36 Kuchokera mwa zidzukulu za Benjamini: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
לבני בנימן תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמת מבן עשרים שנה ומעלה--כל יצא צבא
37 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Benjamini chinali 35,400.
פקדיהם למטה בנימן--חמשה ושלשים אלף וארבע מאות
38 Kuchokera mwa zidzukulu za Dani: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
לבני דן תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמת מבן עשרים שנה ומעלה--כל יצא צבא
39 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Dani chinali 62,700.
פקדיהם למטה דן--שנים וששים אלף ושבע מאות
40 Kuchokera mwa zidzukulu za Aseri: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
לבני אשר תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמת מבן עשרים שנה ומעלה--כל יצא צבא
41 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Aseri chinali 41,500.
פקדיהם למטה אשר--אחד וארבעים אלף וחמש מאות
42 Kuchokera mwa zidzukulu za Nafutali: Aamuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
בני נפתלי תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמת מבן עשרים שנה ומעלה--כל יצא צבא
43 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Nafutali chinali 53,400.
פקדיהם למטה נפתלי--שלשה וחמשים אלף וארבע מאות
44 Amenewa ndiwo anthu amene Mose ndi Aaroni anawawerenga mothandizidwa ndi atsogoleri khumi ndi awiri a Israeli, aliyense kuyimira fuko lake.
אלה הפקדים אשר פקד משה ואהרן ונשיאי ישראל--שנים עשר איש איש אחד לבית אבתיו היו
45 Aisraeli onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali mʼgulu lankhondo la Israeli anawawerenga monga mwa mabanja awo.
ויהיו כל פקודי בני ישראל לבית אבתם מבן עשרים שנה ומעלה כל יצא צבא בישראל
46 Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 603,550.
ויהיו כל הפקדים--שש מאות אלף ושלשת אלפים וחמש מאות וחמשים
47 Koma mabanja a fuko la Levi okha sanawawerenge pamodzi ndi ena.
והלוים למטה אבתם--לא התפקדו בתוכם
48 Pakuti Yehova anawuza Mose kuti,
וידבר יהוה אל משה לאמר
49 “Usawerenge fuko la Levi kapena kuliphatikiza mʼkawundula wa Aisraeli.
אך את מטה לוי לא תפקד ואת ראשם לא תשא בתוך בני ישראל
50 Koma uyike Aleviwo kuti aziyangʼanira tenti yanga yopatulika, zipangizo zake ndi zonse zili mʼmenemo. Azinyamula tentiyo pamodzi ndi zipangizo zake zonse; azisamalira ndi kumanga misasa mozungulira tentiyo.
ואתה הפקד את הלוים על משכן העדת ועל כל כליו ועל כל אשר לו--המה ישאו את המשכן ואת כל כליו והם ישרתהו וסביב למשכן יחנו
51 Pamene akusamutsa tentiyo, Alevi ndiwo aziyitsitsa, akafuna kuyimanganso, Alevi ndiwo aziyimiritsa. Wina aliyense amene adzayandikire tentiyo adzaphedwa.
ובנסע המשכן יורידו אתו הלוים ובחנת המשכן יקימו אתו הלוים והזר הקרב יומת
52 Aisraeli azimanga matenti awo mʼmagulumagulu, munthu aliyense ku gulu lake pansi pa mbendera yake.
וחנו בני ישראל איש על מחנהו ואיש על דגלו לצבאתם
53 Alevi nawonso, azimanga matenti awo mozungulira tenti yopatulika kuti chilango chisagwere Aisraeli onse. Ndipo Alevi aziyangʼanira ndi kusamalira tenti yopatulikayo.”
והלוים יחנו סביב למשכן העדת ולא יהיה קצף על עדת בני ישראל ושמרו הלוים את משמרת משכן העדות
54 Choncho Aisraeli anachita monga Yehova analamulira Mose.
ויעשו בני ישראל ככל אשר צוה יהוה את משה--כן עשו

< Numeri 1 >