< Nehemiya 7 >
1 Khoma linamangidwa ndipo zitseko zinayikidwa. Pambuyo pake alonda a Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo ndiponso Alevi anasankhidwa.
성이 건축되매 문짝을 달고 문지기와 노래하는 자들과 레위 사람들을 세운 후에
2 Kenaka ine ndinasankha mʼbale wanga Hanani pamodzi ndi Hananiya woyangʼanira nsanja yankhondo kukhala olamulira Yerusalemu chifukwa iyeyu anali munthu odalirika ndi woopa Mulungu kuposa anthu ena.
내 아우 하나니와 영문의 관원 하나냐로 함께 예루살렘을 다스리게 하였는데 하나냐는 위인이 충성되어 하나님을 경외함이 무리에서 뛰어난자라
3 Ine ndinawawuza kuti, “Musalole kuti zipata za Yerusalemu zitsekulidwe mpaka dzuwa litatentha, ndipo alonda asanaweruke aonetsetse kuti atseka zitseko ndi kuzipiringidza. Musankhe alonda pakati pa anthu okhala mu Yerusalemu, ena akhale pa malo pawo ndi ena akhale moyangʼanana ndi nyumba zawo.”
내가 저희에게 이르기를 해가 높이 뜨기 전에는 예루살렘 성문을 열지 말고 아직 파수할 때에 곧 문을 닫고 빗장을 지르며 또 예루살렘 거민으로 각각 반차를 따라 파수하되 자기 집 맞은편을 지키게 하라 하였노니
4 Tsono mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu koma munali anthu ochepa ndipo nyumba zinali zisanamangidwe.
그 성은 광대하고 거민은 희소하여 가옥을 오히려 건축하지 못하였음이니라
5 Ndipo Mulungu wanga anayika mu mtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, akuluakulu ndi anthu onse kuti alembetse mayina mwa mabanja awo. Ndinapeza buku limene munalembedwa mayina a mabanja a iwo amene anayamba kubwera kuchokera ku ukapolo. Izi ndi zimene ndinazipeza zitalembedwa mʼmenemo:
내 하나님이 내 마음을 감동하사 귀인들과 민장과 백성을 모아 보계대로 계수하게 하신고로 내가 처음으로 돌아온 자의 보계를 얻었는데 거기 기록한 것을 보면
6 Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerera kuchokera ku ukapolo amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawatenga ukapolo. Iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake.
옛적에 바벨론 왕 느부갓네살에게 사로잡혀 갔던 자 중에서 놓임을 받고 예루살렘과 유다로 돌아와 각기 본성에 이른 자 곧
7 Anabwera pamodzi ndi atsogoleri awa: Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu ndi Baana. Tsono chiwerengero cha anthu a ku Israeli chinali chotere:
스룹바벨과, 예수아와, 느헤미야와, 아사랴와, 라아마와, 나하마니와, 모르드개와, 빌산과, 미스베렛과, 비그왜와, 느훔과, 바아나 등과 함께 나온 이스라엘 백성의 명수가 이러하니라
8 Zidzukulu za Parosi 2,172
바로스 자손이 이천 일백 칠십 이명이요
9 Zidzukulu za Sefatiya 372
스바댜 자손이 삼백 칠십 이명이요
11 Zidzukulu za Pahati-Mowabu (kudzera mu mʼbado wa Yesuwa ndi Yowabu) 2,818
바핫모압 자손 곧 예수아와 요압 자손이 이천 팔백 십 팔명이요
12 Zidzukulu za Elamu 1,254
엘람 자손이 일천 이백 오십 사명이요
14 Zidzukulu za Zakai 760
삭개 자손이 칠백 육십명이요
15 Zidzukulu za Binuyi 648
빈누이 자손이 육백 사십 팔명이요
16 Zidzukulu za Bebai 628
브배 자손이 육백 이십 팔명이요
17 Zidzukulu za Azigadi 2,322
아스갓 자손이 이천 삼백 이십 이명이요
18 Zidzukulu za Adonikamu 667
아도니감 자손이 육백 육십 칠명이요
19 Zidzukulu za Abigivai 2,067
비그왜 자손이 이천 육십 칠명이요
20 Zidzukulu za Adini 655
아딘 자손이 육백 오십 오명이요
21 Zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya) 98
아델 자손 곧 히스기야 자손이 구십 팔명이요
22 Zidzukulu za Hasumu 328
하숨 자손이 삼백 이십 팔명이요
23 Zidzukulu za Bezayi 324
베새 자손이 삼백 이십 사명이요
24 Zidzukulu za Harifu 112
하립 자손이 일백 십 이명이요
25 Zidzukulu za Gibiyoni 95.
기브온 사람이 구십 오명이요
26 Anthu a ku Betelehemu ndi Netofa 188
베들레헴과 느도바 사람이 일백 팔십 팔명이요
27 Anthu a ku Anatoti 128
아나돗 사람이 일백 이십 팔명이요
28 Anthu a ku Beti-Azimaveti 42
벧아스마웹 사람이 사십 이명이요
29 Anthu a ku Kiriati Yeyarimu Kefira ndi Beeroti 743
기럇여아림과 그비라와 브에롯 사람이 칠백 사십 삼명이요
30 Anthu a ku Rama ndi Geba 621
라마와 게바 사람이 육백 이십 일명이요
31 Anthu a ku Mikimasi 122
믹마스 사람이 일백 이십 이명이요
32 Anthu a ku Beteli ndi Ai 123
벧엘과 아이 사람이 일백 이십 삼명이요
33 Anthu a ku Nebo winayo 52
기타 느보 사람이 오십 이명이요
34 Ana a Elamu wina 1,254
기타 엘람 자손이 일천 이백 오십 사명이요
35 Zidzukulu za Harimu 320
하림 자손이 삼백 이십명이요
36 Zidzukulu za Yeriko 345
여리고 자손이 삼백 사십 오명이요
37 Zidzukulu za Lodi, Hadidi ndi Ono 721
로드와 하딧과 오노 자손이 칠백 이십 일명이요
38 Zidzukulu za Senaya 3,930.
스나아 자손이 삼천 구백 삼십명이었느니라
39 Ansembe anali awa: A banja la Yedaya (ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa) 973
제사장들은 예수아의 집 여다야 자손이 구백 칠십 삼명이요
40 Zidzukulu za Imeri 1,052
임멜 자손이 일천 오십 이명이요
41 Zidzukulu za Pasi-Huri 1,247
바수훌 자손이 일천 이백 사십 칠명이요
42 Zidzukulu za Harimu 1,017.
하림 자손이 일천 십 칠명이였느니라
43 Alevi anali awa: A banja la Yesuwa ndi Kadimieli, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya 74.
레위 사람들은 호드야 자손 곧 예수아와 갓미엘 자손이 칠십 사명이요
44 Anthu oyimba: Zidzukulu za Asafu 148.
노래하는 자들은 아삽 자손이 일백 사십 팔명이요
45 Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu za Salumu, Ateri, Talimoni, Hatita ndi Sobai 138.
문지기들은 살룸 자손과, 아델 자손과, 달문 자손과, 악굽 자손과, 하디다 자손과, 소배 자손이 모두 일백 삼십 팔명이었느니라
46 Anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu za Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti,
느디님 사람들은 시하 자손과, 하수바 자손과, 답바옷 자손과
47 Zidzukulu Kerosi, zidzukulu za Siya, zidzukulu za Padoni
게로스 자손과, 시아 자손과, 바돈 자손과, 르바나 자손과
48 Zidzukulu za Lebana za Hagaba, ndi za Salimayi,
하가바 자손과, 살매 자손과
49 Zidzukulu za Hanani, zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari,
하난 자손과, 깃델 자손과, 가할 자손과
50 Zidzukulu za Reyaya, zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nehoda,
르아야 자손과, 르신 자손과, 느고다 자손과
51 Zidzukulu za Gazamu, zidzukulu za Uza, zidzukulu za Paseya,
갓삼 자손과, 웃사 자손과, 바세아 자손과
52 Zidzukulu za Besai, zidzukulu za Meunimu, zidzukulu za Nefusimu,
베새 자손과, 므우님 자손과, 느비스심 자손과
53 Zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri,
박북 자손과, 하그바 자손과, 할훌 자손과
54 Zidzukulu za Baziliti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa,
바슬릿 자손과, 므히다 자손과, 하르사 자손과
55 Zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema
바르고스 자손과, 시스라 자손과, 데마 자손과
56 Zidzukulu za Neziya, ndi zidzukulu za Hatifa.
느시야 자손과, 하디바 자손이었느니라
57 Zidzukulu za antchito a Solomoni: Zidzukulu za Sotai, zidzukulu za Sofereti, zidzukulu za Perida
솔로몬의 신복의 자손은 소대 자손과, 소베렛 자손과, 브리다 자손과
58 zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli,
야알라 자손과, 다르곤 자손과, 깃델 자손과
59 zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu zidzukulu za Pokereti-Hazebaimu ndi zidzukulu Amoni.
스바댜 자손과, 핫딜 자손과, 보게렛하스바임 자손과, 아몬 자손이니
60 Anthu onse ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za antchito a Solomoni analipo 392.
모든 느디님 사람과 솔로몬의 신복의 자손이 삼백 구십 이명이었느니라
61 Ali munsiwa anachokera ku Teli-Mela, Teri-Harisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, koma sanathe kunena mwa tchutchutchu kuti makolo awo kapena mafuko awo analidi Aisraeli kapena ayi.
델멜라와, 델하르사와, 그룹과, 앗돈과, 임멜로부터 올라온 자가 있으나 그 종족과 보계가 이스라엘에 속하였는지는 증거할 수 없으니
62 Zidzukulu za Delaya, zidzukulu za Tobiya ndi zidzukulu za Nekoda 642.
저희는 들라야 자손과, 도비야 자손과, 느고다 자손이라 도합이 육백 사십 이명이요
63 Ndiponso ena pakati pa ansembe anali awa: zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai (munthu amene anakwatira mwana wamkazi wa Barizilai wa ku Giliyadi ndipo amatchedwa dzina limenelo).
제사장 중에는 호바야 자손과 학고스 자손과 바르실래 자손이니 바르실래는 길르앗 사람 바르실래의 딸 중에 하나로 아내를 삼고 바르실래의 이름으로 이름한 자라
64 Iwowa anafufuzafufuza mayina awo mʼbuku la mibado ya mabanja awo ndipo sanapeze mayina awo kotero anachotsedwa pa unsembe nawerengedwa ngati odetsedwa pa chipembedzo.
이 사람들이 보계중에서 자기 이름을 찾아도 얻지 못한고로 저희를 부정하게 여겨 제사장의 직분을 행치 못하게 하고
65 Choncho bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya china chilichonse choperekedwa kwa Mulungu mpaka patapezeka wansembe wodziwa kugwiritsa bwino ntchito ya Urimu ndi Tumimu.
방백이 저희에게 명하여 `우림과 둠밈을 가진 제사장이 일어나기 전에는 지성물을 먹지 말라' 하였느니라
66 Chiwerengero chonse cha anthuwa chinali 42,360.
온 회중의 합계가 사만 이천 삼백 육십명이요
67 Kuwonjezera pamenepa panali antchito awo aamuna ndi aakazi 7,337 ndiponso anthu aamuna ndi aakazi oyimba nyimbo okwanira 245.
그 외에 노비가 칠천 삼백 삼십 칠명이요, 노래하는 남녀가 이백 사십 오명이요
68 Panali akavalo 736, abulu angʼonoangʼono 245.
말이 칠백 삼십 육이요, 노새가 이백 사십 오요
69 Ngamira zawo zinalipo 435 ndipo abulu analipo 6,720.
약대가 사백 삼십 오요, 나귀가 육천 칠백 이십이었느니라
70 Atsogoleri ena a mabanja anapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa anapereka ku thumba losungira chuma, ndalama zagolide za makilogalamu asanu ndi atatu, mabeseni makumi asanu ndi zovala za ansembe 530.
어떤 족장들은 역사를 위하여 보조하였고 방백은 금 일천 다릭과, 대접 오십과, 제사장의 의복 오백 삼십 벌을 보물 곳간에 드렸고
71 Atsogoleri ena amabanja anapereka ku thumba losungira chuma ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndiponso ndalama za siliva zokwana makilogalamu 1,250.
또 어떤 족장들은 금 이만 다릭과 은 이천 이백 마네를 역사 곳간에 드렸고
72 Anthu ena onse otsala anapereka ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndalama za siliva zokwana makilogalamu 140, ndiponso zovala za ansembe 67.
그 나머지 백성은 금 이만 다릭과 은 이천 마네와 제사장의 의복 육십 칠 벌을 드렸느니라
73 Choncho ansembe, Alevi, alonda a Nyumba ya Mulungu, anthu oyimba nyimbo, ena mwa anthu wamba, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmizinda yawo. Pofika mwezi wachisanu ndi chiwiri Aisraeli onse anali atakhazikika mʼmizinda yawo.
이와 같이 제사장들과 레위 사람들과 문지기들과 노래하는 자들과 백성 몇명과 느디님 사람들과 온 이스라엘이 다 그 본성에 거하였느니라