< Nehemiya 12 >

1 Ansembe ndi Alevi amene anabwerera pamodzi ndi Zerubabeli mwana wa Sealatieli ndi Yesuwa anali awa: Seraya, Yeremiya, Ezara,
Nämät ovat papit ja Leviläiset, jotka menivät ylös Serubbabelin Sealtielin pojan ja Jesuan kanssa: Seraja, Jeremia, Esra,
2 Amariya, Maluki, Hatusi,
Amaria, Malluk, Hattus,
3 Sekaniya, Rehumu, Meremoti,
Sekania, Rehum, Meremot,
4 Ido, Ginetoyi, Abiya
Iddo, Ginetoi, Abia,
5 Miyamini, Maadiya, Biliga,
Mijamin, Maadia, Bilga,
6 Semaya, Yowaribu, Yedaya,
Semaja, Jojarib, Jedaja,
7 Salu, Amoki, Hilikiya ndi Yedaya. Awa ndiye anali atsogoleri a ansembe ndi abale awo pa nthawi ya Yesuwa.
Sallu, Amok, Hilkia ja Jedaja: nämät olivat pappein ja heidän veljeinsä päämiehet Jesuan aikana.
8 Alevi anali Yesuwa, Binuyi, Kadimieli, Serebiya, Yuda, ndiponso Mataniya, amene pamodzi ndi abale ake ankatsogolera nyimbo za mayamiko.
Ja Leviläiset: Jesua, Binnui, Kadmiel, Serebia, Juuda ja Mattania kiitosvirtten päällä, hän ja hänen veljensä;
9 Abale awo, Bakibukiya ndi Uri, ankayimba nyimbo molandizana.
Bakbukia ja Unni veljinensä olivat vartiana heidän tykönänsä.
10 Yesuwa anabereka Yowakimu, Yowakimu anabereka Eliyasibu, Eliyasibu anabereka Yoyada.
Jesua siitti Jojakimin, Jojakim siitti Eljasibin, Eljasib siitti Jojadan,
11 Yoyada anabereka Yonatani, ndipo Yonatani anabereka Yaduwa.
Jojada siitti Jonatanin, Jonatan siitti Jadduan.
12 Pa nthawi ya Yowakimu, awa ndiwo anali atsogoleri a mabanja a ansembe: Mtsogoleri wa fuko la Seraya anali Meraya; wa fuko la Yeremiya anali Hananiya;
Ja Jojakimin aikana olivat nämät ylimmäiset isät pappein seassa: Serajasta Meraja, Jeremiasta Hanania,
13 wa fuko la Ezara anali Mesulamu; wa fuko la Amariya anali Yehohanani;
Esrasta oli Mesullam, Amariasta Johanan,
14 wa fuko la Maluki anali Yonatani; wa fuko la Sebaniya anali Yosefe;
Mallukista Jonatan, Sebaniasta Joseph,
15 wa fuko la Harimu anali Adina; wa fuko la Merayoti anali Helikayi;
Harimista Adna, Merajotista Helkai,
16 wa fuko la Ido anali Zekariya; wa fuko la Ginetoni anali Mesulamu;
Iddosta Sakaria, Ginthonista Mesullam,
17 wa fuko la Abiya anali Zikiri; wa fuko la Miniyamini ndi banja la Maadiya anali Pilitayi;
Abiasta Sikri, Minjaminista ja Moadiasta Piltai,
18 wa fuko la Biliga anali Samuwa; wa fuko la Semaya anali Yonatani;
Bilgasta Sammua, Semajasta Jonatan,
19 wa fuko la Yowaribu anali Matenayi; wa fuko la Yedaya anali Uzi;
Jojaribista Matnai, Jedajasta Ussi,
20 wa fuko la Salai anali Kalai; wa fuko la Amoki anali Eberi;
Sallaista Kallai, Amakista Eber,
21 wa fuko la Hilikiya anali Hasabiya; wa fuko la Yedaya anali Netaneli.
Hilkiasta Hasabia, Jedajasta Natanael.
22 Pa nthawi ya Eliyasibu, Yoyada, Yohanani ndi Yaduwa panalembedwa atsogolera a mabanja a Alevi ndi a ansembe mpaka pa nthawi ya ulamuliro wa Dariyo Mperisi.
Leviläiset Eljasibin, Jojadan, Johanan ja Jadduan aikana, kirjoitetut isäin päämiehet; niin myös papit, Dariuksen Persialaisen valtakuntaan asti.
23 Zidzukulu za Levi, makamaka atsogoleri a mabanja awo analembedwa mʼbuku la mbiri mpaka pa nthawi ya Yohanani mwana wa Eliyasibu.
Levin lapset, ylimmäiset isät, ovat kirjoitetut Aikakirjaan, Johananin Eljasibin pojan aikaan asti.
24 Ndipo atsogoleri a Alevi awa, Hasabiya, Serebiya, Yesuwa mwana wa Kadimieli ndi abale awo, ankayimba nyimbo zotamanda ndi zothokoza molandizana. Gulu limodzi linkavomerezana ndi linzake monga mmene Davide munthu wa Mulungu analamulira.
Ja Leviläisten päämiehet: Hasabia, Serebia ja Jesua Kadmielin poika, ja heidän veljensä heidän vieressänsä, ylistämässä ja kiittämässä, niinkuin David Jumalan mies oli käskenyt, yksi vartia toisen kohdalla.
25 Mataniya, Bakibukiya, Obadiya, Mesulamu, Talimoni ndi Akubu anali olonda nyumba zosungiramo chuma pa zipata za ku Nyumba ya Mulungu.
Mattania, Bakbukia, Obadia, Mesullam, Talmon ja Akkub olivat ovenvartiat, tavaraporttein vartioitsemisessa.
26 Iwo ndiwo ankatumikira pa nthawi ya Yowakimu mwana wa Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndiponso pa nthawi ya bwanamkubwa Nehemiya ndi wansembe Ezara amene analinso mlembi.
Nämät olivat Jojakimin Jesuan pojan Jotsadakin pojan aikana, ja Nehemian maanvanhimman, ja Esran papin, kirjanoppineen, aikana.
27 Pa mwambo wopereka khoma la Yerusalemu anayitana Alevi kulikonse kumene ankakhala kuti abwere ku Yerusalemu ku mwambo wopereka khoma kwa Mulungu, mwachimwemwe ndi mothokoza poyimba nyimbo pamodzi ndi ziwiya za malipenga, azeze ndi apangwe.
Ja Jerusalemin muurin vihkimiselle etsivät he Leviläisiä kaikista heidän paikoistansa, tuodaksensa heitä Jerusalemiin pitämään vihkimistä ilolla, kiitoksella, virsillä, symbaleilla, psalmeilla ja harpuilla.
28 Tsono anthu a mabanja a Alevi oyimba nyimbo aja anasonkhana pamodzi kuchokera ku madera onse ozungulira Yerusalemu ndiponso ku midzi ya Anetofati,
Ja veisaajain lapset tulivat kokoon Jerusalemin ympäristöltä ja Netophatin kylistä,
29 Beti-Giligala ndi ku madera a ku Geba ndi Azimaveti, pakuti oyimbawo anali atamanga midzi yawo mozungulira Yerusalemu.
Ja Gilgalin huoneesta, ja Gibean ja Asmavetin pelloilta; sillä veisaajat olivat rakentaneet itsellensä taloja Jerusalemin ympärillä.
30 Tsono ansembe ndi Alevi anachita mwambo wodziyeretsa. Pambuyo pake anachita mwambo woyeretsa anthu onse ndi khoma la Yerusalemu.
Ja papit ja Leviläiset puhdistivat itsensä: he puhdistivat myös kansan ja portit ja muurit.
31 Ine ndinabwera nawo atsogoleri a dziko la Yuda ndi kukwera nawo pa khoma. Ndipo ndinasankha magulu awiri akuluakulu oyimba nyimbo za matamando. Gulu limodzi linadzera mbali ya ku dzanja lamanja pa khoma mpaka ku Chipata cha Kudzala.
Ja minä annoin Juudan päämiehet mennä ylös muurille, ja asetin kaksi suurta laulukuntaa ja juhlasaattoa muurin päälle: (yhden) oikialle puolelle Sontaporttia.
32 Pambuyo pawo panali Hosayia, theka la atsogoleri a Yuda aja
Ja Hosaja ja toinen puoli Juudan päämiehistä kävivät heidän perässänsä,
33 pamodzi ndi Azariya, Ezara, Mesulamu,
Ja Asaria, Esra, Mesullam,
34 Yuda, Benjamini, Semaya ndi Yeremiya.
Juuda, Benjamin, Semaja ja Jeremia,
35 Ena mwa ana a ansembe amene ankayimba malipenga awo anali awa: Zekariya mwana wa Yonatani mwana wa Semaya mwana wa Mataniya, mwana wa Mikaya, mwana wa Zakuri, mwana wa Asafu,
Ja muutamat pappein lapsista vaskitorvein kanssa: Sakaria Jonatanin poika, Semajan pojan, Mattanian pojan, Mikajan pojan, Sakkurin pojan, Asaphin pojan;
36 pamodzi ndi abale awo awa: Semaya, Azareli, Milalai, Gilalayi, Maayi, Netaneli, Yuda ndi Hanani. Onse ankagwiritsa ntchito zida zoyimbira za Davide, munthu wa Mulungu. Tsono Ezara mlembi uja ankawatsogolera.
Ja hänen veljensä Semaja, Asareel, Milalai, Gilalai, Maai, Netaneel, Juuda, Hanani, Davidin Jumalan miehen kanteleiden kanssa, ja Esra kirjanoppinut heidän edellänsä.
37 Kuchokera ku Chipata cha Kasupe anayenda nakakwera makwerero opita ku mzinda wa Davide pa njira yotsatira khoma, chakumtundu kwa nyumba ya Davide mpaka ku Chipata cha Madzi, mbali ya kummawa.
Ja Lähdeporttia päin menivät he ylös heidän kohdallansa astuimia myöten Davidin kaupunkiin, (ja siitä) astuimilla muurein päälle, Davidin huoneesta Vesiporttiin asti itään päin.
38 Gulu loyimba lachiwiri linadzera mbali ya kumanzere kwa khomalo. Tsono ine ndi theka lina la atsogoleri aja tinkalitsata pambuyo tikuyenda pamwamba pa khomalo. Tinapitirira Nsanja ya Ngʼanjo mpaka ku Khoma Lotambasuka.
Ja toinen laulukunta kävi vastaan, ja minä sen perässä, ja toinen puoli kansaa muurin päällä, Pätsitornista leviään muuriin saakka,
39 Tinadutsanso Chipata cha Efereimu, Chipata cha Yesana, Chipata cha Nsomba, Nsanja ya Hananeli, Nsanja ya Zana mpaka kukafika ku Chipata cha Nkhosa. Ndipo mdipiti uwu unakayima pa Chipata cha Mlonda.
Ja Ephraimin portista, Vanhan portin ja Kalaportin ja Hananeelin tornin ja Mean tornin ohitse Lammasporttiin asti; ja seisahtivat Vankiportissa.
40 Choncho magulu onse awiri oyimba nyimbo zothokoza aja anakayima pafupi ndi Nyumba ya Mulungu. Pamodzi ndi ine ndi theka la atsogoleri aja,
Ja ne kaksi kiitoskuoria seisoivat Jumalan huoneessa, ja minä ja toinen puoli ylimmäisiä minun kanssani,
41 panalinso ansembe awa akuyimba malipenga: Eliyakimu, Maaseya, Miniyamini, Mikaya, Eliyoenai, Zekariya ndi Hananiya.
Ja papit Eliakim, Maeseja, Minjamin, Mikaja, Eljoenai, Sakaria, Hanania olivat vaskitorvein kanssa,
42 Panalinso ansembe awa: Maaseya, Semaya, Eliezara, Uzi, Yehohanani, Milikiya, Elamu ndi Ezeri. Gulu loyimba linkatsogozedwa ndi Yezirahayiya.
Ja Maeseja, Semaja, Eleatsar, Ussi, Johanan, Malkia, Elam ja Asar. Ja veisaajat veisasivat korkiasti, ja Jisrahia oli esimiehenä.
43 Pa tsiku limenelo anthu anapereka nsembe zambiri ndipo anakondwera chifukwa Mulungu anawapatsa chimwemwe chachikulu. Nawonso akazi ndi ana anakondwera ndipo kukondwa kwa anthu a mu mzinda wa Yerusalemu kunamveka kutali.
Ja he uhrasivat sinä päivänä suuret uhrit, ja olivat iloiset; sillä Jumala oli heitä iloittanut suurella ilolla, että myös vaimot ja lapsetkin iloitsivat, ja Jerusalemin ilo kuului kauvas.
44 Tsiku limenelo panasankhidwa anthu oyangʼanira zipinda zosungiramo zopereka zaufulu, zipatso zoyamba kucha, zopereka za chakhumi. Anthuwo ankasonkhanitsa zopereka kuchokera ku minda ya midzi yonse kuti azipereke kwa ansembe ndi Alevi malingana ndi malamulo. Izi zinali chomwechi chifukwa Ayuda ankakondwera ndi utumiki wa ansembe ndi Alevi.
Siihen aikaan asetettiin miehet tavarakammioin päälle, joissa ylennykset, ensimäiset hedelmät ja kymmenykset olivat, joita heidän piti kokooman kaupunkein pelloista, papeille ja Leviläisille jaettaa lain jälkeen; sillä Juudalaisilla oli ilo papeista ja Leviläisistä, jotka seisoivat.
45 Iwowa ankagwira ntchito ya Mulungu wawo, makamaka mwambo woyeretsa zinthu. Nawonso oyimba nyimbo ndi olonda ku Nyumba ya Mulungu anagwira ntchito zawo monga Davide ndi mwana wake Solomoni analamula.
Ja he pitivät vaarin Jumalan vartiosta ja puhdistuksen vartiosta, niin myös veisaajista ja ovenvartioista, Davidin ja Salomon hänen poikansa käskyn jälkeen,
46 Pakuti kalekale, pa nthawi ya Davide ndi Asafu, panali atsogoleri a anthu oyimba nyimbo za matamando ndi nyimbo zoyamika Mulungu.
Sillä Davidin ja Asaphin aikana olivat muinen asetetut ylimmäiset veisaajat, ja kiitosvirret ja kiitokset Jumalalle.
47 Choncho mu nthawi ya Zerubabeli ndi Nehemiya, Aisraeli onse anakapereka mphatso tsiku ndi tsiku kwa anthu oyimba nyimbo ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu. Ankayikanso padera chigawo cha zopereka cha Alevi. Nawonso Alevi ankayika padera chigawo cha zopereka cha ansembe, zidzukulu za Aaroni.
Mutta koko Israel antoi veisaajille ja ovenvartioille osan, Serubbabelin ja Nehemian aikana, joka päivä heidän osansa; ja pyhittivät sen Leviläisille, ja Leviläiset pyhittivät Aaronin lapsille.

< Nehemiya 12 >