< Nehemiya 10 >
1 Amene anasindikiza chidindo anali awa: Nehemiya, bwanamkubwa uja, mwana wa Hakaliya. Zedekiya,
그 인친 자는 하가랴의 아들 방백 느헤미야와 시드기야,
2 Seraya, Azariya, Yeremiya
스라야, 아사랴, 예레미야,
3 Pasuri, Amariya, Malikiya,
바스훌, 아마랴, 말기야,
4 Hatusi, Sebaniya, Maluki,
핫두스, 스바냐, 말룩,
5 Harimu, Meremoti, Obadiya,
하림, 므레못, 오바댜,
6 Danieli, Ginetoni, Baruki,
다니엘, 긴느돈, 바룩,
7 Mesulamu, Abiya, Miyamini
므술람, 아비야, 미야민,
8 Maziya, Biligai ndi Semaya Awa anali ansembe.
마아시야, 빌개, 스마야니 이는 다 제사장이요
9 Alevi anali awa: Yesuwa mwana wa Azaniya, Binuyi wa fuko la Henadadi, Kadimieli,
또 레위 사람 곧 아사냐의 아들 예수아, 헤나닷의 자손 중 빈누이, 갓미엘과
10 ndi abale awo awa: Sebaniya, Hodiya, Kelita, Pelaya, Hanani,
그 형제 스바냐, 호디야, 그리다, 블라야, 하난,
11 Mika, Rehobu, Hasabiya,
미가, 르홉, 하사뱌,
12 Zakuri, Serebiya, Sebaniya,
삭굴, 세레뱌, 스바냐,
13 Hodiya, Bani ndi Beninu.
호디야, 바니, 브니누요
14 Atsogoleri a anthu anali awa: Parosi, Pahati-Mowabu, Elamu, Zatu, Bani,
또 백성의 두목들 곧 바로스, 바핫모압, 엘람, 삿두, 바니,
16 Adoniya, Bigivai, Adini,
아도니야, 비그왜, 아딘,
17 Ateri, Hezekiya, Azuri,
아델, 히스기야, 앗술,
18 Hodiya, Hasumu, Bezayi
호디야, 하숨, 베새,
19 Harifu, Anatoti, Nebayi,
하립, 아나돗, 노배,
20 Magipiyasi, Mesulamu, Heziri
막비아스, 므술람, 헤실,
21 Mesezabeli, Zadoki, Yaduwa
므세사벨, 사독, 얏두아,
22 Pelatiya, Hanani, Ananiya,
블라댜, 하난, 아나야,
23 Hoseya, Hananiya, Hasubu
호세아, 하나냐, 핫숩,
24 Halohesi, Piliha, Sobeki,
할르헤스, 빌하, 소벡,
25 Rehumu, Hasabiya, Maaseya,
르훔, 하삼나, 마아세야,
27 Maluki, Harimu ndi Baana.
말룩, 하림, 바아나이었느니라
28 Ife otsalafe, ndiye kuti ansembe, Alevi, alonda a ku Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu, onse amene anadzipatula pakati pa anthu a mitundu ina kuti atsate malamulo a Yehova, pamodzi ndi akazi athu, ana athu ndi onse amene ali ndi nzeru,
그 남은 백성과 제사장들과 레위 사람들과 문지기들과 노래하는 자들과 느디님 사람들과 및 이방 사람과 절교하고 하나님의 율법을 준행하는 모든 자와 그 아내와 그 자녀들 무릇 지식과 총명이 있는 자가
29 tikuphatikana ndi abale athu wolemekezeka, ndipo tikulonjeza molumbira kuti tidzayenda motsata malamulo a Mulungu amene anapereka kudzera mwa Mose mtumiki wa Mulungu. Tilonjeza kumvera ndi kutsata bwino mawu onse, miyambo yonse ndi malangizo onse a Yehova. Yehova atilange ngati sitidzachita zimenezi.
다 그 형제 귀인들을 좇아 저주로 맹세하기를 우리가 하나님의 종 모세로 주신 하나님의 율법을 좇아 우리 주 여호와의 모든 계명과 규례와 율례를 지켜
30 “Ife tikulonjeza kuti sitidzapereka ana athu aakazi kuti akwatiwe ndi amuna a mayiko ena kapena kutenga ana awo aakazi kuti akwatiwe ndi ana athu aamuna.
우리 딸은 이 땅 백성에게 주지 아니하고 우리 아들을 위하여 저희 딸을 데려오지 아니하며
31 “Ngati anthu a mitundu ina abwera ndi zinthu za malonda, monga tirigu, kudzagulitsa pa tsiku la Sabata, sitidzawagula pa tsiku la Sabata kapena pa tsiku lina lililonse loyera. Pa chaka chilichonse cha chisanu ndi chiwiri tidzagoneka munda wosawulima ndipo tidzafafaniza ngongole zonse.
혹시 이 땅 백성이 안식일에 물화나 식물을 가져다가 팔려 할지라도 우리가 안식일이나 성일에는 사지 않겠고 제칠년마다 땅을 쉬게 하고 모든 빚을 탕감하리라 하였고
32 “Tikulonjezanso molumbira kuti chaka ndi chaka tizipereka magalamu anayi a siliva kuti zithandize ntchito ya ku Nyumba ya Mulungu wathu.
우리가 또 스스로 규례를 정하기를 해마다 각기 세겔의 삼분 일을 수납하여 하나님의 전을 위하여 쓰게 하되
33 Ndalamayi izithandiza kulipirira buledi wa pa tebulo, chopereka cha chakudya cha nthawi zonse, zopereka zopsereza za nthawi zonse, zopereka za pa tsiku la Sabata, za pachikondwerero cha Mwezi Watsopano, za pa masiku a chikondwerero osankhika, zopereka za zinthu zopatulika, zopereka za nsembe yopepesera machimo a Aisraeli ndi ntchito ina iliyonse ya ku Nyumba ya Mulungu.
곧 진설병과 항상 드리는 소제와 항상 드리는 번제와 안식일과 초하루와 정한 절기에 쓸 것과 성물과 이스라엘을 위하는 속죄제와 우리 하나님의 전의 모든 일을 위하여 쓰게 하였고
34 “Ife ansembe, Alevi ndi anthu onse, tachita maere kuti tidziwe pamene banja lathu lililonse lidzabweretsa ku nyumba ya Mulungu wathu pa nthawi yoyikika ya chaka zopereka za nkhuni zoyaka pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wathu, monga momwe zinalembedwera mʼMalamulo.”
또 우리 제사장들과 레위 사람들과 백성들이 제비 뽑아 각기 종족대로 해마다 정한 기한에 나무를 우리 하나님의 전에 드려서 율법에 기록한 대로 우리 하나님 여호와의 단에 사르게 하였고
35 “Tilonjezanso kuti tidzabwera ndi zipatso zoyamba kucha za mʼminda yathu ndi zipatso zoyamba kucha za mtengo uliwonse wa zipatso chaka ndi chaka kuti tidzapereke ku Nyumba ya Mulungu wathu.”
해마다 우리 토지 소산의 맏물과 각종 과목의 첫 열매를 여호와의 전에 드리기로 하였고
36 “Tidzabweranso nawo ku Nyumba ya Mulungu, kwa ansembe amene amatumikira ku Nyumba ya Mulungu ana athu aamuna oyamba kubadwa ndi ana angʼombe oyamba kubadwa monga zalembedwera mu Malamulo. Tidzaperekanso ana oyamba kubadwa a ziweto zathu ndi ana ankhosa oyamba kubadwa.”
또 우리의 맏아들들과 생축의 처음 난 것과 우양의 처음 난 것을 율법에 기록된 대로 우리 하나님의 전으로 가져다가 우리 하나님의 전에서 섬기는 제사장들에게 주고
37 “Ndiponso ku zipinda za Nyumba ya Mulungu wathu, kwa ansembe tidzaperekanso mtanda wathu wa buledi wa ufa ndi mphatso zina monga zipatso za mtengo uliwonse, vinyo ndi mafuta. Tidzaperekanso kwa alevi chakhumi cha mbewu zathu pakuti alevi ndiwo amasonkhanitsa chakhumi mʼmidzi yathu yonse.
또 처음 익은 밀의 가루와 거제물과 각종 과목의 열매와 새 포도주와 기름을 제사장들에게로 가져다가 우리 하나님의 전 골방에 두고 또 우리 물산의 십일조를 레위 사람들에게 주리라 하였나니 이 레위 사람들은 우리의 모든 성읍에서 물산의 십일조를 받는 자임이며
38 Wansembe, mdzukulu wa Aaroni azikhala pamodzi ndi Alevi pamene akulandira chakhumi. Ndipo Alevi azibwera ndi chakhumicho ku nyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda zosungiramo chuma.”
레위 사람들이 십일조를 받을 때에는 아론의 자손 제사장 하나가 함께 있을 것이요 레위 사람들은 그 십일조의 십분 일을 가져다가 우리 하나님의 전 골방 곧 곳간에 두되
39 Choncho Israeli, kuphatikiza zidzukulu za Alevi, azipititsa zopereka za tirigu, vinyo ndi mafuta ku zipinda zosungiramo katundu wopatulika, komanso kokhala ansembe amene akutumikira pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu ndi anthu oyimba nyimbo. “Kwambiri ife sitidzaleka kusamala Nyumba ya Mulungu.”
곧 이스라엘 자손과 레위 자손이 거제로 드린바 곡식과 새 포도주와 기름을 가져다가 성소의 기명을 두는 골방 곧 섬기는 제사장들과 및 문지기들과 노래하는 자들이 있는 골방에 둘 것이라 그리하여 우리가 우리 하나님의 전을 버리지 아니하리라