< Nehemiya 1 >
1 Awa ndi mawu a Nehemiya mwana wa Hakaliya: Pa mwezi wa Kisilevi, chaka cha makumi awiri, pamene ndinali mu mzinda wa Susa,
Nehemias', Hakaljas sønns historie. I måneden kislev, i det tyvende år, da jeg var i borgen Susan,
2 Hanani mmodzi mwa abale anga, anabwera ndi anthu ena kuchokera ku Yuda, ndipo ine ndinawafunsa za Ayuda otsala amene sanatengedwe ukapolo, ndiponso za mzinda wa Yerusalemu.
kom Hanani, en av mine brødre, og nogen andre menn fra Juda. Jeg spurte dem da om jødene - den rest som var blitt frelst fra fangenskapet - og om Jerusalem.
3 Anandiyankha kuti, “Amene sanatengedwe ukapolo aja ali pa mavuto aakulu ndipo ali ndi manyazi. Khoma la Yerusalemu ndilogamukagamuka ndipo zipata zake zinatenthedwa ndi moto.”
De svarte mig: De som er blitt igjen fra fangenskapet og nu bor der i landskapet, er i stor ulykke og vanære; Jerusalems mur er nedrevet og portene opbrent.
4 Nditamva zimenezi, ndinakhala pansi ndi kuyamba kulira. Ndinalira kwa masiku angapo. Ndinkasala zakudya ndi kumapemphera pamaso pa Mulungu Wakumwamba.
Da jeg hørte denne tidende, satte jeg mig ned og gråt og sørget dag efter dag, og jeg fastet og bad for himmelens Guds åsyn.
5 Ndinkati: “Inu Yehova, Mulungu wakumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa. Mumasunga pangano ndi kuonetsa chikondi chosasinthika kwa onse amene amakukondani ndi kumvera malamulo anu.
Og jeg sa: Akk, Herre, himmelens Gud, du store og forferdelige Gud, som holder din pakt og bevarer din miskunnhet mot dem som elsker dig og holder dine bud!
6 Tcherani khutu lanu ndi kutsekula maso anu kuti mumve pemphero la mtumiki wanune limene ndikupemphera usana ndi usiku pamaso panu kupempherera Aisraeli, atumiki anu. Ndikuvomereza machimo a Aisraeli amene tinakuchimwirani. Ndithu, ine ndi banja la makolo anga tinakuchimwirani.
La ditt øre være åpent og dine øine oplatt, så du hører på din tjeners bønn, den som jeg nu beder for ditt åsyn, både dag og natt, for dine tjenere Israels barn, idet jeg bekjenner Israels barns synder, som vi har gjort mot dig! Både jeg og min fars hus har syndet;
7 Ife tinakuchitirani zoyipa zambiri. Sitinamvere mawu anu, malamulo ndi malangizo anu amene munapereka kwa mtumiki wanu Mose.
vi har båret oss ille at mot dig og ikke holdt de bud og lover og forskrifter som du gav din tjener Moses.
8 “Kumbukirani mawu amene munawuza mtumiki wanu Mose akuti, ‘Ngati mukhala osakhulupirika, ndidzakubalalitsani pakati pa mitundu ina.
Kom i hu det ord som du talte til din tjener Moses da du sa: Bærer I eder troløst at, så vil jeg sprede eder blandt folkene;
9 Koma mukabwerera kwa Ine, mukamvera malamulo anga ndi kuwatsatadi, ndiye kuti ngakhale anthu anu atabalalika kutali chotani, Ine ndidzawasonkhanitsa kuchokera kumeneko ndi kubwera nawo ku malo amene ndinasankha kuti azidzayitanira dzina langa.’
men vender I om til mig og holder mine bud og gjør efter dem, da vil jeg, om enn de bortdrevne blandt eder er ved himmelens ende, samle dem derfra og føre dem til det sted jeg har utvalgt til å la mitt navn bo der.
10 “Iwo ndi atumiki anu ndi anthu anu, amene munawawombola ndi mphamvu yanu yayikulu ndi dzanja lanu lamphamvu.
De er dog dine tjenere og ditt folk, som du har utfridd med din store kraft og din sterke hånd.
11 Inu Ambuye tcherani khutu lanu kuti mumve pemphero la mtumiki wanune ndiponso pemphero la atumiki anu amene amakondwera kuchitira ulemu dzina lanu. Lolani kuti mtumiki wanune zinthu zindiyendere bwino lero ndi kuti mfumu indichitire chifundo.” Nthawi imeneyi nʼkuti ndili woperekera zakumwa kwa mfumu.
Akk, Herre! La ditt øre merke på din tjeners og dine tjeneres bønn, de som gjerne vil frykte ditt navn, og la det idag lykkes for din tjener, og la ham finne barmhjertighet hos denne mann! - Jeg var dengang munnskjenk hos kongen.