< Mika 7 >
1 Tsoka ine! Ndili ngati munthu wokunkha zipatso nthawi yachilimwe, pa nthawi yokolola mphesa; palibe phava lamphesa loti nʼkudya, palibe nkhuyu zoyambirira zimene ndimazilakalaka kwambiri.
哀哉!我好像夏天的果子已被收盡, 又像摘了葡萄所剩下的, 沒有一掛可吃的; 我心羨慕初熟的無花果。
2 Anthu opembedza atha mʼdziko; palibe wolungama ndi mmodzi yemwe amene watsala. Anthu onse akubisalirana kuti aphane; aliyense akusaka mʼbale wake ndi khoka.
地上虔誠人滅盡; 世間沒有正直人; 各人埋伏,要殺人流血, 都用網羅獵取弟兄。
3 Manja awo onse ndi aluso pochita zoyipa; wolamulira amafuna mphatso, woweruza amalandira ziphuphu, anthu amphamvu amalamula kuti zichitike zimene akuzifuna, onse amagwirizana zochita.
他們雙手作惡; 君王徇情面,審判官要賄賂; 位分大的吐出惡意, 都彼此結聯行惡。
4 Munthu wabwino kwambiri pakati pawo ali ngati mtengo waminga, munthu wolungama kwambiri pakati pawo ndi woyipa kuposa mpanda waminga. Tsiku limene alonda ako ananena lafika, tsiku limene Mulungu akukuchezera. Tsopano ndi nthawi ya chisokonezo chawo.
他們最好的,不過是蒺藜; 最正直的,不過是荊棘籬笆。 你守望者說,降罰的日子已經來到。 他們必擾亂不安。
5 Usadalire mnansi; usakhulupirire bwenzi. Usamale zoyankhula zako ngakhale kwa mkazi amene wamukumbatira.
不要倚賴鄰舍; 不要信靠密友。 要守住你的口; 不要向你懷中的妻提說。
6 Pakuti mwana wamwamuna akunyoza abambo ake, mwana wamkazi akuwukira amayi ake, mtengwa akukangana ndi apongozi ake, adani a munthu ndi amene amakhala nawo mʼbanja mwake momwe.
因為,兒子藐視父親; 女兒抗拒母親; 媳婦抗拒婆婆; 人的仇敵就是自己家裏的人。
7 Koma ine ndikudikira Yehova mwachiyembekezo, ndikudikira Mulungu Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga adzamvetsera.
至於我,我要仰望耶和華, 要等候那救我的上帝; 我的上帝必應允我。
8 Iwe mdani wanga, usandiseke! Ngakhale ndagwa, ndidzauka. Ngakhale ndikukhala mu mdima, Yehova ndiye kuwunika kwanga.
我的仇敵啊,不要向我誇耀。 我雖跌倒,卻要起來; 我雖坐在黑暗裏, 耶和華卻作我的光。
9 Ndidzapirira mkwiyo wa Yehova, chifukwa ndinamuchimwira, mpaka ataweruza mlandu wanga ndi kukhazikitsa chilungamo changa. Iye adzanditulutsa ndi kundilowetsa mʼkuwunika; ndidzaona chilungamo chake.
我要忍受耶和華的惱怒; 因我得罪了他, 直等他為我辨屈,為我伸冤。 他必領我到光明中; 我必得見他的公義。
10 Ndipo mdani wanga adzaona zimenezi nadzagwidwa ndi manyazi, iye amene anandifunsa kuti, “Ali kuti Yehova Mulungu wako?” Ndidzaona kugonjetsedwa kwake ndi maso anga; ngakhale tsopano adzaponderezedwa ngati matope mʼmisewu.
那時我的仇敵, 就是曾對我說「耶和華-你上帝在哪裏」的, 他一看見這事就被羞愧遮蓋。 我必親眼見他遭報; 他必被踐踏,如同街上的泥土。
11 Idzafika nthawi yomanganso makoma anu, nthawi yokulitsanso malire anu.
以色列啊,日子必到, 你的牆垣必重修; 到那日,你的境界必開展。
12 Nthawi imeneyo anthu adzabwera kwa inu kuchokera ku Asiriya ndi mizinda ya ku Igupto, ngakhale kuchokera ku Igupto mpaka ku Yufurate ndiponso kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja inanso kuchokera ku phiri lina mpaka ku phiri linanso.
當那日,人必從亞述, 從埃及的城邑, 從埃及到大河, 從這海到那海, 從這山到那山, 都歸到你這裏。
13 Dziko lapansi lidzasanduka chipululu chifukwa cha anthu okhala mʼdzikomo, potsatira zochita za anthuwo.
然而,這地因居民的緣故, 又因他們行事的結果,必然荒涼。
14 Wetani anthu anu ndi ndodo yanu yowateteza, nkhosa zimene ndi cholowa chanu, zimene zili zokha mʼnkhalango, mʼdziko la chonde. Muzilole kuti zidye mu Basani ndi mu Giliyadi monga masiku akale.
求耶和華在迦密山的樹林中, 用你的杖牧放你獨居的民, 就是你產業的羊群。 求你容他們在巴珊和基列得食物,像古時一樣。
15 “Ndidzawaonetsa zodabwitsa zanga, ngati masiku amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto.”
耶和華說: 我要把奇事顯給他們看, 好像出埃及地的時候一樣。
16 Mitundu ya anthu idzaona zimenezi ndipo idzachita manyazi, ngakhale ali ndi mphamvu zotani. Adzagwira pakamwa pawo ndipo makutu awo adzagontha.
列國看見這事就必為自己的勢力慚愧; 他們必用手摀口,掩耳不聽。
17 Adzabwira fumbi ngati njoka, ngati zolengedwa zomwe zimakwawa pansi. Adzabwera akunjenjemera kuchokera mʼmaenje awo; mwamantha adzatembenukira kwa Yehova Mulungu wathu ndipo adzachita nanu mantha.
他們必舔土如蛇, 又如土中腹行的物, 戰戰兢兢地出他們的營寨。 他們必戰懼投降耶和華, 也必因我們的上帝而懼怕。
18 Kodi alipo Mulungu wofanana nanu, amene amakhululukira tchimo ndi kuyiwala zolakwa za anthu otsala amene ndi cholowa chake? Inu simusunga mkwiyo mpaka muyaya koma kwanu nʼkuonetsa chikondi chosasinthika.
上帝啊,有何神像你,赦免罪孽, 饒恕你產業之餘民的罪過, 不永遠懷怒,喜愛施恩?
19 Inu mudzatichitiranso chifundo; mudzapondereza pansi machimo athu ndi kuponyera zolakwa zathu zonse pansi pa nyanja.
必再憐憫我們, 將我們的罪孽踏在腳下, 又將我們的一切罪投於深海。
20 Mudzakhala wokhulupirika kwa Yakobo, ndi kuonetsa chifundo chanu kwa Abrahamu, monga munalonjeza molumbira kwa makolo athu masiku amakedzana.
你必按古時起誓應許我們列祖的話, 向雅各發誠實, 向亞伯拉罕施慈愛。