< Mika 6 >

1 Tamverani zimene Yehova akunena: “Nyamukani, fotokozani mlandu wanu pamaso pa mapiri; zitunda zimve zimene inu muti muyankhule.
Listen now to what the LORD says: "Arise, plead your case before the mountains, and let the hills hear what you have to say.
2 Imvani mlandu wa Yehova, inu mapiri; tamverani, maziko amuyaya a dziko lapansi. Pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi anthu ake; Iye akutsutsa Aisraeli.
Hear, you mountains, the LORD's controversy, and you enduring foundations of the earth; for the LORD has a controversy with his people, and he will contend with Israel.
3 “Anthu anga, kodi ndakuchitirani chiyani? Kodi ndakutopetsani bwanji? Ndiyankheni.
My people, what have I done to you? How have I burdened you? Answer me.
4 Ine ndinakutulutsani ku dziko la Igupto ndi kukuwombolani ku nyumba ya ukapolo. Ndinatuma Mose kuti akutsogolereni, pamodzi ndi Aaroni ndi Miriamu.
For I brought you up out of the land of Egypt, and redeemed you out of the house of bondage. I sent before you Moses, Aaron, and Miriam.
5 Anthu anga, kumbukirani zimene Balaki mfumu ya ku Mowabu inafuna kukuchitirani ndiponso zimene Balaamu mwana wa Beori anayankha. Kumbukirani zomwe zinachitika pa ulendo wochoka ku Sitimu kupita ku Giligala, kuti mudziwe machitidwe olungama a Yehova.”
My people, remember now what Balak king of Moab devised, and what Balaam the son of Beor answered him from Shittim to Gilgal, that you may know the righteous acts of the LORD."
6 Kodi ndidzatenga chiyani kupita nacho pamaso pa Yehova ndi kukagwada pamaso pa Mulungu wakumwamba? Kodi ndidzabwera pamaso pake ndi nsembe yopsereza, ndi ana angʼombe a chaka chimodzi?
How shall I come before the LORD, and bow myself before the exalted God? Shall I come before him with burnt offerings, with calves a year old?
7 Kodi Yehova adzakondwera ndi nkhosa zazimuna 1,000, kapena ndi mitsinje yosalekeza ya mafuta? Kodi ndipereke nsembe mwana wanga woyamba kubadwa chifukwa cha zolakwa zanga? Chipatso cha thupi langa chifukwa cha tchimo la moyo wanga?
Will the LORD be pleased with thousands of rams? With tens of thousands of rivers of oil? Shall I give my firstborn for my disobedience? The fruit of my body for the sin of my soul?
8 Munthu iwe, Yehova wakuonetsa kale chimene chili chabwino. Tsono kodi Yehova akuyembekezera chiyani kwa iwe? Uzichita zolungama ndi kukonda chifundo ndiponso kuyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.
He has shown you, O man, what is good. What does the LORD require of you, but to act justly, to love mercy, and to walk humbly with your God?
9 Tamverani! Yehova akuyitana anthu okhala mu mzinda ndi nzeru kuopa dzina lanu. “Mverani mfumu ndi Iye amene anayikhazikitsa.
The LORD's voice calls to the city, and wisdom sees your name: "Listen to the rod, and he who appointed it.
10 Inu anthu oyipa, kodi Ine nʼkuyiwala chuma chanu chimene munachipeza mwachinyengo, ndiponso muyeso wanu woperewera umene ndi wotembereredwa?
Are there yet treasures of wickedness in the house of the wicked, and a short ephah that is accursed?
11 Kodi ndimutenge ngati wosalakwa munthu amene ali ndi sikelo yachinyengo, ndiponso miyeso yabodza mʼthumba lake?
Shall I be pure with dishonest scales, and with a bag of deceitful weights?
12 Anthu ake olemera amachita zachiwawa; anthu ake ndi abodza ndipo pakamwa pawo pamayankhula zachinyengo.
Her rich men are full of violence, her inhabitants speak lies, and their tongue is deceitful in their speech.
13 Choncho, ndayamba kukuwonongani, kukusakazani chifukwa cha machimo anu.
Therefore I also have struck you with a grievous wound. I have made you desolate because of your sins.
14 Mudzadya, koma simudzakhuta; mudzakhalabe ndi njala. Mudzasunga zinthu, koma sizidzasungika, chifukwa zimene mudzasunga zidzawonongedwa ndi lupanga.
You shall eat, but not be satisfied. Your humiliation will be in your midst. You will store up, but not save; and that which you save I will give up to the sword.
15 Mudzadzala, koma simudzakolola. Mudzayenga mafuta a olivi, koma simudzawagwiritsa ntchito. Mudzaponda mphesa, koma simudzamwa vinyo wake.
You will sow, but won't reap. You will tread the olives, but won't anoint yourself with oil; and crush grapes, but won't drink the wine.
16 Inu mwatsatira malangizo a Omuri ndiponso machitidwe onse a banja la Ahabu, ndi khalidwe lawo lonse. Choncho Ine ndidzakuperekani kuti muwonongedwe ndiponso anthu anu kuti azunguzike mitu; mudzanyozedwa ndi anthu a mitundu ina.”
For the statutes of Omri are kept, and all the works of the house of Ahab; and you walk in their counsels. Therefore I will make you a desolation, and her inhabitants an object of contempt; and you will bear the scorn of the nations."

< Mika 6 >