< Mika 5 >

1 Iwe mzinda wa anthu ankhondo, sonkhanitsa anthu ako ankhondo, pakuti anthu atizungulira kuti alimbane nafe. Adzakantha ndi ndodo pa chibwano cha wolamulira wa Israeli.
עַתָּה֙ תִּתְגֹּדְדִ֣י בַת־גְּד֔וּד מָצֹ֖ור שָׂ֣ם עָלֵ֑ינוּ בַּשֵּׁ֙בֶט֙ יַכּ֣וּ עַֽל־הַלְּחִ֔י אֵ֖ת שֹׁפֵ֥ט יִשְׂרָאֵֽל׃ ס
2 “Koma iwe Betelehemu Efurata, ngakhale uli wonyozeka pakati pa mafuko a Yuda, mwa iwe mudzatuluka munthu amene adzalamulira Israeli, amene chiyambi chake nʼchakalekale, nʼchamasiku amakedzana.”
וְאַתָּ֞ה בֵּֽית־לֶ֣חֶם אֶפְרָ֗תָה צָעִיר֙ לִֽהְיֹות֙ בְּאַלְפֵ֣י יְהוּדָ֔ה מִמְּךָ֙ לִ֣י יֵצֵ֔א לִֽהְיֹ֥ות מֹושֵׁ֖ל בְּיִשְׂרָאֵ֑ל וּמֹוצָאֹתָ֥יו מִקֶּ֖דֶם מִימֵ֥י עֹולָֽם׃
3 Nʼchifukwa chake Israeli adzasiyidwa mpaka pa nthawi imene mayi amene ali woyembekezera adzachire. Ndipo abale ake onse otsalira adzabwerera kudzakhala pamodzi ndi Aisraeli.
לָכֵ֣ן יִתְּנֵ֔ם עַד־עֵ֥ת יֹולֵדָ֖ה יָלָ֑דָה וְיֶ֣תֶר אֶחָ֔יו יְשׁוּב֖וּן עַל־בְּנֵ֥י יִשְׂרָאֵֽל׃
4 Iye adzalimbika, ndipo adzaweta nkhosa zake mwa mphamvu ya Yehova, mu ulemerero wa dzina la Yehova Mulungu wake. Ndipo iwo adzakhala mu mtendere, pakuti ukulu wake udzakhala ponseponse pa dziko lapansi.
וְעָמַ֗ד וְרָעָה֙ בְּעֹ֣ז יְהוָ֔ה בִּגְאֹ֕ון שֵׁ֖ם יְהוָ֣ה אֱלֹהָ֑יו וְיָשָׁ֕בוּ כִּֽי־עַתָּ֥ה יִגְדַּ֖ל עַד־אַפְסֵי־אָֽרֶץ׃
5 Ndipo Iye adzakhala mtendere wawo. Asiriya akadzalowa mʼdziko lathu ndi kuyamba kuthira nkhondo malo athu otetezedwa, tidzawadzutsira abusa asanu ndi awiri, ngakhalenso atsogoleri asanu ndi atatu.
וְהָיָ֥ה זֶ֖ה שָׁלֹ֑ום אַשּׁ֣וּר ׀ כִּֽי־יָבֹ֣וא בְאַרְצֵ֗נוּ וְכִ֤י יִדְרֹךְ֙ בְּאַרְמְנֹתֵ֔ינוּ וַהֲקֵמֹ֤נוּ עָלָיו֙ שִׁבְעָ֣ה רֹעִ֔ים וּשְׁמֹנָ֖ה נְסִיכֵ֥י אָדָֽם׃
6 Iwo adzagonjetsa dziko la Asiriya ndi lupanga, dziko la Nimurodi adzalilamulira mwankhondo. Adzatipulumutsa kwa Asiriya akadzafika mʼmalire a mʼdziko lathu kudzatithira nkhondo.
וְרָע֞וּ אֶת־אֶ֤רֶץ אַשּׁוּר֙ בַּחֶ֔רֶב וְאֶת־אֶ֥רֶץ נִמְרֹ֖ד בִּפְתָחֶ֑יהָ וְהִצִּיל֙ מֵֽאַשּׁ֔וּר כִּֽי־יָבֹ֣וא בְאַרְצֵ֔נוּ וְכִ֥י יִדְרֹ֖ךְ בִּגְבוּלֵֽנוּ׃ ס
7 Otsalira a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu ngati mame ochokera kwa Yehova, ngati mvumbi pa udzu, omwe sulamulidwa ndi munthu kapena kudikira lamulo la anthu.
וְהָיָ֣ה ׀ שְׁאֵרִ֣ית יַעֲקֹ֗ב בְּקֶ֙רֶב֙ עַמִּ֣ים רַבִּ֔ים כְּטַל֙ מֵאֵ֣ת יְהוָ֔ה כִּרְבִיבִ֖ים עֲלֵי־עֵ֑שֶׂב אֲשֶׁ֤ר לֹֽא־יְקַוֶּה֙ לְאִ֔ישׁ וְלֹ֥א יְיַחֵ֖ל לִבְנֵ֥י אָדָֽם׃
8 Otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu ya anthu, mʼgulu la anthu a mitundu yambiri, ngati mkango pakati pa nyama za mʼnkhalango. Ngati mwana wa mkango pakati pa gulu la nkhosa, amene pozidutsa amazidya ndi kuzikhadzula, ndipo palibe angathe kuzilanditsa.
וְהָיָה֩ שְׁאֵרִ֨ית יַעֲקֹ֜ב בַּגֹּויִ֗ם בְּקֶ֙רֶב֙ עַמִּ֣ים רַבִּ֔ים כְּאַרְיֵה֙ בְּבַהֲמֹ֣ות יַ֔עַר כִּכְפִ֖יר בְּעֶדְרֵי־צֹ֑אן אֲשֶׁ֧ר אִם עָבַ֛ר וְרָמַ֥ס וְטָרַ֖ף וְאֵ֥ין מַצִּֽיל׃
9 Mudzagonjetsa adani anu, ndipo adani anu onse adzawonongeka.
תָּרֹ֥ם יָדְךָ֖ עַל־צָרֶ֑יךָ וְכָל־אֹיְבֶ֖יךָ יִכָּרֵֽתוּ׃ פ
10 Yehova akuti, “Tsiku limenelo ndidzawononga akavalo anu onse ndi kuphwasula magaleta anu.
וְהָיָ֤ה בַיֹּום־הַהוּא֙ נְאֻם־יְהוָ֔ה וְהִכְרַתִּ֥י סוּסֶ֖יךָ מִקִּרְבֶּ֑ךָ וְהַאֲבַדְתִּ֖י מַרְכְּבֹתֶֽיךָ׃
11 Ndidzawononga mizinda ya mʼdziko mwanu ndi kugwetsa malinga anu onse.
וְהִכְרַתִּ֖י עָרֵ֣י אַרְצֶ֑ךָ וְהָרַסְתִּ֖י כָּל־מִבְצָרֶֽיךָ׃
12 Ndidzawononga ufiti wanu ndipo sikudzakhalanso anthu owombeza mawula.
וְהִכְרַתִּ֥י כְשָׁפִ֖ים מִיָּדֶ֑ךָ וּֽמְעֹונְנִ֖ים לֹ֥א יִֽהְיוּ־לָֽךְ׃
13 Ndidzawononga mafano anu osema pamodzi ndi miyala yanu yopatulika imene ili pakati panu; simudzagwadiranso zinthu zopanga ndi manja anu.
וְהִכְרַתִּ֧י פְסִילֶ֛יךָ וּמַצֵּבֹותֶ֖יךָ מִקִּרְבֶּ֑ךָ וְלֹֽא־תִשְׁתַּחֲוֶ֥ה עֹ֖וד לְמַעֲשֵׂ֥ה יָדֶֽיךָ׃
14 Ndidzazula mitengo ya mafano a Asera imene ili pakati panu, ndipo ndidzawononga mizinda yanu.
וְנָתַשְׁתִּ֥י אֲשֵׁירֶ֖יךָ מִקִּרְבֶּ֑ךָ וְהִשְׁמַדְתִּ֖י עָרֶֽיךָ׃
15 Ndidzayilanga mwaukali ndi mokwiya mitundu imene sinandimvere Ine.”
וְעָשִׂ֜יתִי בְּאַ֧ף וּבְחֵמָ֛ה נָקָ֖ם אֶת־הַגֹּויִ֑ם אֲשֶׁ֖ר לֹ֥א שָׁמֵֽעוּ׃ ס

< Mika 5 >