< Mika 4 >
1 Mʼmasiku otsiriza, phiri la Nyumba ya Yehova adzalikhazikitsa kukhala lalitali kuposa mapiri ena onse. Lidzaonekera pamwamba pa mapiri ena onse, ndipo anthu amitundu yonse adzathamangira kumeneko.
2 Mayiko ambiri adzabwera ndikunena kuti, “Tiyeni, tikwere ku phiri la Yehova, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo. Iye adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tidzayenda mʼnjira zakezo.” Malangizo adzachokera ku Ziyoni, mawu a Yehova adzachokera ku Yerusalemu.
3 Iye adzaweruza pakati pa anthu amitundu yambiri ndipo adzathetsa kusamvana pakati pa anthu amphamvu akutali ndi apafupi omwe. Anthuwo adzasandutsa malupanga awo kukhala makasu ndiponso mikondo yawo kukhala zomwetera. Mtundu wina sudzatenganso lupanga kumenyana ndi mtundu wina, kapena kuphunziranso za nkhondo.
4 Munthu aliyense adzakhala pansi pa tsinde pa mtengo wake wa mpesa ndi pa tsinde pa mtengo wake wamkuyu, ndipo palibe amene adzawachititse mantha, pakuti Yehova Wamphamvuzonse wayankhula.
5 Mitundu yonse ya anthu itha kutsatira milungu yawo; ife tidzayenda mʼnjira za Yehova Mulungu wathu mpaka muyaya.
6 “Tsiku limenelo, Yehova akuti, “ndidzasonkhanitsa olumala; ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu ochotsedwa ndiponso amene ndinawalanga.
7 Anthu olumalawo ndidzawasandutsa anthu anga otsala. Anthu amene ndinawachotsa ndidzawasandutsa mtundu wamphamvu. Yehova adzawalamulira mʼPhiri la Yehova kuyambira tsiku limenelo mpaka muyaya.
8 Kunena za iwe, nsanja ya ziweto zanga, iwe linga la mwana wamkazi wa Ziyoni, ulamuliro wako wakale udzabwezeretsedwa kwa iwe; ufumu udzabwera pa mwana wamkazi wa Yerusalemu.”
9 Chifukwa chiyani tsopano ukulira mofuwula, kodi ulibe mfumu? Kodi phungu wako wawonongedwa, kotero kuti ululu wako uli ngati wa mayi amene akubereka?
10 Gubuduka ndi ululu, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, ngati mayi pa nthawi yake yobereka, pakuti tsopano muyenera kuchoka mu mzinda ndi kugona kunja kwa mzindawo. Udzapita ku Babuloni; kumeneko udzapulumutsidwa, kumeneko Yehova adzakuwombola mʼmanja mwa adani ako.
11 Koma tsopano mitundu yambiri ya anthu yasonkhana kulimbana nawe. Iwo akuti, “Tiyeni timudetse, maso athu aone chiwonongeko cha Ziyoni!”
12 Koma iwo sakudziwa maganizo a Yehova; iwo sakuzindikira cholinga chake, Iye amene amawatuta ngati mitolo ya tirigu ku malo opunthira tirigu.
13 “Imirira, puntha, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, pakuti ndidzakupatsa nyanga zachitsulo; ndidzakupatsa ziboda zamkuwa ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu.” Phindu lawo lolipeza molakwikalo udzalipereka kwa Yehova, chuma chawo kwa Yehova wa dziko lonse lapansi.