< Mika 3 >

1 Ndipo ine ndinati, “Tamverani, inu atsogoleri a Yakobo, inu olamulira nyumba ya Israeli. Kodi sindinu oyenera kudziwa kuweruza molungama,
Y DIJE: Oid ahora, príncipes de Jacob, y cabezas de la casa de Israel: ¿No [pertenecía] á vosotros saber el derecho?
2 inu amene mumadana ndi zabwino ndi kukonda zoyipa; inu amene mumasenda khungu la anthu anga, ndipo mumakungunula mnofu pa mafupa awo;
Que aborrecen lo bueno y aman lo malo, que les quitan su piel y su carne de sobre los huesos;
3 inu amene mumadya anthu anga, mumasenda khungu lawo ndi kuphwanya mafupa awo; inu amene mumawadula nthulinthuli ngati nyama yokaphika?”
Que comen asimismo la carne de mi pueblo, y les desuellan su piel de sobre ellos, y les quebrantan sus huesos y los rompen, como para el caldero, y como carnes en olla.
4 Pamenepo adzalira kwa Yehova, koma Iye sadzawayankha. Nthawi imeneyo Iye adzawabisira nkhope yake chifukwa cha zoyipa zimene anazichita.
Entonces clamarán á Jehová y no les responderá; antes esconderá de ellos su rostro en aquel tiempo, por cuanto hicieron malvadas obras.
5 Yehova akuti, “Aneneri amene amasocheretsa anthu anga, ngati munthu wina awapatsa chakudya amamufunira ‘mtendere;’ ngati munthu wina sawapatsa zakudya amamulosera zoyipa.
Así ha dicho Jehová acerca de los profetas que hacen errar á mi pueblo, que muerden con sus dientes, y claman, Paz, y al que no les diere que coman, aplazan contra él batalla:
6 Nʼchifukwa chake kudzakuderani, simudzaonanso masomphenya, mdima udzakugwerani ndipo simudzawombezanso. Dzuwa lidzawalowera aneneriwo, ndipo mdima udzawagwera.
Por tanto, de la profecía se os hará noche, y oscuridad del adivinar; y sobre los profetas se pondrá el sol, y el día se entenebrecerá sobre ellos.
7 Alosi adzachita manyazi ndipo owombeza mawula adzanyazitsidwa. Onse adzaphimba nkhope zawo chifukwa Mulungu sakuwayankha.”
Y serán avergonzados los profetas, y confundiránse los adivinos; y ellos todos cubrirán su labio, porque no hay respuesta de Dios.
8 Koma kunena za ine, ndadzazidwa ndi mphamvu, ndi Mzimu wa Yehova, ndi kulungama, ndi kulimba mtima, kuti ndilalikire za kugalukira kwa Yakobo, kwa Israeli za tchimo lake.
Yo empero estoy lleno de fuerza del espíritu de Jehová, y de juicio, y de fortaleza, para denunciar á Jacob su rebelión, y á Israel su pecado.
9 Imvani izi, inu atsogoleri a nyumba ya Yakobo, inu olamulira nyumba ya Israeli, inu amene mumadana ndi kuweruza kolungama; ndipo mumakhotetsa zinthu zonse zolondola;
Oid ahora esto, cabezas de la casa de Jacob, y capitanes de la casa de Israel, que abomináis el juicio, y pervertís todo el derecho;
10 inu amene mukumanga Ziyoni pokhetsa magazi, ndi Yerusalemu ndi kuyipa kwanu.
Que edificáis á Sión con sangre, y á Jerusalem con injusticia;
11 Atsogoleri ake amalandira chiphuphu kuti aweruze, ansembe ake amalandira malipiro kuti alalikire, ndipo aneneri ake amanenera kuti alandire ndalama. Komatu amatsamira pa Yehova nʼkumanena kuti, “Kodi Yehova sali pakati pathu? Palibe tsoka limene lidzatigwere.”
Sus cabezas juzgan por cohecho, y sus sacerdotes enseñan por precio, y sus profetas adivinan por dinero; y apóyanse en Jehová diciendo: ¿No está Jehová entre nosotros? No vendrá mal sobre nosotros.
12 Choncho chifukwa cha inu, Ziyoni adzatipulidwa ngati munda, Yerusalemu adzasanduka bwinja, ndipo phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango yowirira.
Por tanto, á causa de vosotros será Sión arada como campo, y Jerusalem será majanos, y el monte de la casa como cumbres de breñal.

< Mika 3 >