< Mika 1 >
1 Yehova anayankhula ndi Mika wa ku Moreseti pa nthawi ya ulamuliro wa Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda. Awa ndi masomphenya amene iye anaona onena za Samariya ndi Yerusalemu.
當猶大王約坦、亞哈斯、希西家在位的時候,摩利沙人彌迦得耶和華的默示,論撒馬利亞和耶路撒冷。
2 Tamverani, inu anthu a mitundu yonse, mvetsera iwe dziko lapansi ndi okhala mʼmenemo, pakuti Ambuye Yehova achitira umboni wokutsutsani, Ambuye akuyankhula ali mʼnyumba yake yopatulika.
萬民哪,你們都要聽! 地和其上所有的,也都要側耳而聽! 主耶和華從他的聖殿 要見證你們的不是。
3 Taonani! Yehova akubwera kuchokera ku malo ake; Iye akutsika ndipo akuponda pa malo okwera a dziko lapansi.
看哪,耶和華出了他的居所, 降臨步行地的高處。
4 Mapiri akusungunuka pansi pake, ndipo zigwa zikugawikana ngati phula pa moto, ngati madzi ochokera mʼphiri.
眾山在他以下必消化, 諸谷必崩裂, 如蠟化在火中, 如水沖下山坡。
5 Zonsezi ndi chifukwa cha cholakwa cha Yakobo, chifukwa cha machimo a nyumba ya Israeli. Kodi cholakwa cha Yakobo nʼchiyani? Kodi si Samariya? Kodi malo achipembedzo a Yuda ndi ati? Kodi si Yerusalemu?
這都因雅各的罪過, 以色列家的罪惡。 雅各的罪過在哪裏呢? 豈不是在撒馬利亞嗎? 猶大的邱壇在哪裏呢? 豈不是在耶路撒冷嗎?
6 “Choncho Ine ndidzasandutsa Samariya kukhala bwinja, malo odzalamo mphesa. Miyala yake ndidzayitaya ku chigwa ndipo ndidzafukula maziko ake.
所以我必使撒馬利亞變為田野的亂堆, 又作為種葡萄之處; 也必將她的石頭倒在谷中, 露出根基來。
7 Mafano ake onse ndidzawaphwanyaphwanya; mphatso zake zonse ndidzazitentha ndi moto; ndidzawononga zifanizo zonse za milungu yake. Popeza analandira mphatso zake kuchokera ku malipiro a akazi achiwerewere, mphatsozonso zidzagwiritsidwa ntchito ndi ena ngati malipiro a akazi achiwerewere.”
她一切雕刻的偶像必被打碎; 她所得的財物必被火燒; 所有的偶像我必毀滅; 因為是從妓女雇價所聚來的, 後必歸為妓女的雇價。
8 Chifukwa cha zimenezi ine ndidzalira momvetsa chisoni; ndidzayenda wopanda nsapato ndi wamaliseche. Ndidzafuwula ngati nkhandwe ndi kulira ngati kadzidzi.
先知說:因此我必大聲哀號, 赤腳露體而行; 又要呼號如野狗, 哀鳴如鴕鳥。
9 Pakuti chilonda cha Samariya nʼchosachizika; chafika ku Yuda. Chafika pa chipata chenicheni cha anthu anga, mpaka mu Yerusalemu mwenimwenimo.
因為撒馬利亞的傷痕無法醫治, 延及猶大和耶路撒冷我民的城門。
10 Musanene zimenezi ku Gati; musalire nʼkomwe. Mugubuduzike mu fumbi ku Beti-Leafura.
不要在迦特報告這事, 總不要哭泣; 我在伯‧亞弗拉滾於灰塵之中。
11 Inu anthu okhala ku Safiro, muzipita ku ukapolo muli amaliseche ndi amanyazi. Iwo amene akukhala ku Zanaani sadzatuluka. Beti-Ezeli akulira mwachisoni; chitetezo chake chakuchokerani.
沙斐的居民哪,你們要赤身蒙羞過去。 撒南的居民不敢出來。 伯‧以薛人的哀哭使你們無處可站。
12 Anthu amene amakhala ku Maroti akubuwula ndi ululu, akuyembekezera thandizo, chifukwa Yehova wabweretsa tsoka, lafika mpaka pa chipata cha Yerusalemu.
瑪律的居民心甚憂急,切望得好處, 因為災禍從耶和華那裏臨到耶路撒冷的城門。
13 Inu anthu okhala ku Lakisi mangani akavalo ku magaleta. Inu amene munayamba kuchimwitsa mwana wamkazi wa Ziyoni, pakuti zolakwa za Israeli zinapezeka pakati panu.
拉吉的居民哪,要用快馬套車; 錫安民的罪由你而起; 以色列人的罪過在你那裏顯出。
14 Chifukwa chake perekani mphatso zolawirana ndi a ku Moreseti Gati. Mzinda wa Akizibu udzaonetsa kunama kwa mafumu a Israeli.
猶大啊,你要將禮物送給摩利設‧迦特。 亞革悉的眾族必用詭詐待以色列諸王。
15 Ndidzabweretsa mgonjetsi kudzalimbana ndi inu okhala mu Maresa. Ulemerero wa Israeli udzafika ku Adulamu.
瑪利沙的居民哪, 我必使那奪取你的來到你這裏; 以色列的尊貴人必到亞杜蘭。
16 Metani mipala mitu yanu kuonetsa kuti mukulirira ana anu amene mumawakonda; mudzichititse dazi ngati dembo, pakuti anawo adzatengedwa pakati panu kupita ku ukapolo.
猶大啊,要為你所喜愛的兒女剪除你的頭髮, 使頭光禿,要大大地光禿,如同禿鷹, 因為他們都被擄去離開你。