< Mateyu 1 >

1 Buku lofotokoza za mʼbado wa Yesu Khristu mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu:
Ježíšův rodokmen sahá přes Davida až k Abrahamovi.
2 Abrahamu anabereka Isake, Isake anabereka Yakobo, Yakobo anabereka Yuda ndi abale ake.
Abraham – Izák Izák – Jákob
3 Yuda anabereka Perezi ndi Zara, amene amayi awo anali Tamara. Perezi anabereka Hezironi, Hezironi anabereka Aramu.
Jákob – Juda (a bratři) Juda – Peres a Zerach (matka Támar) Peres – Chesrón Chesrón – Rám
4 Aramu anabereka Aminadabu, Aminadabu anabereka Naasoni, Naasoni anabereka Salimoni.
Rám – Amínadab Amínadab – Nachšón Nachšón – Salmón
5 Salimoni anabereka Bowazi amene amayi ake anali Rahabe, Bowazi anabereka Obedi amene amayi ake anali Rute, Obedi anabereka Yese.
Salmón – Bóaz (matka: Rachab) Bóaz – Obéd (matka: Rút) Obéd – Jišaj
6 Yese anabereka Mfumu Davide. Ndipo Davide anabereka Solomoni, amene amayi ake anali mkazi wa Uriya.
Jišaj – David (král) David – Šalomoun (matka: Batšeba).
7 Solomoni anabereka Rehabiamu, Rehabiamu anabereka Abiya, Abiya anabereka Asa,
Šalomoun – Rechabeám Rechabeám – Abijám Abijám – Ása
8 Asa anabereka Yehosafati, Yehosafati anabereka Yoramu, Yoramu anabereka Uziya.
Ása – Jóšafat Jóšafat – Jóram Jóram – Uzijáš
9 Uziya anabereka Yotamu, Yotamu anabereka Ahazi, Ahazi anabereka Hezekiya.
Uzijáš – Jótam Jótam – Achaz Achaz – Chizkijáš
10 Hezekiya anabereka Manase, Manase anabereka Amoni, Amoni anabereka Yosiya.
Chizkijáš – Menaše Menaše – Ámon Ámon – Jóšijáš
11 Yosiya anali atabala Yekoniya ndi abale ake pamene Ayuda anatengedwa ukapolo kupita ku Babuloni.
Jóšijáš – Jechoniáš
12 Ali ku ukapolo ku Babuloni, Yekoniya anabereka Salatieli, Salatieli anabereka Zerubabeli.
Jekonjáš a jeho bratři. Babylónské zajetí – Jekonjáš – Šealtíel Šealtíel – Zerubábel
13 Zerubabeli anabereka Abiudi, Abiudi anabereka Eliakimu, Eliakimu anabereka Azoro.
Zerubábel – Abiud Abiud – Eljakim Eljakim – Azór
14 Azoro anabereka Zadoki, Zadoki anabereka Akimu, Akimu anabereka Eliudi.
Azór – Sádok Sádok – Achim Achim – Eliud
15 Eliudi anabereka Eliezara, Eliezara anabereka Matani, Matani anabereka Yakobo.
Eliud – Eleazar Eleazar – Mattan Mattan – Jákob
16 Yakobo anabereka Yosefe, mwamuna wa Mariya. Mariyayu ndiye anabereka Yesu wotchedwa Khristu.
Jákob – Josef Josef (muž Marie) JEŽÍŠ KRISTUS (narozen z Marie). Rodokmen uzavírá Josef, manžel Marie, které se narodil Ježíš – Boží Syn.
17 Kuyambira pa Abrahamu mpaka pa Davide, pali mibado khumi ndi inayi. Ndipo kuyambira pa Davide mpaka pamene Ayuda anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babuloni, pali mibado khumi ndi inayi. Ndiponso kuyambira nthawi ya ukapolo ku Babuloni mpaka pamene Khristu anabadwa, palinso mibado khumi ndi inayi.
Od praotce Abrahama k Davidovi je to čtrnáct generací, dále čtrnáct generací od Davida po babylónské zajetí a od zajetí v Babylóně až ke Kristu také čtrnáct.
18 Kubadwa kwa Yesu Khristu kunali motere: Amayi ake, Mariya, anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanagone malo amodzi, anapezeka ali woyembekezera mwana mwa mphamvu ya Mzimu Woyera.
S narozením Ježíše Krista to bylo takto: Ježíšova matka Marie byla zasnoubena s Josefem. Dříve, než se vzali, se však ukázalo, že bude matkou.
19 Popeza Yosefe mwamuna wake anali munthu wolungama, sanafune kumuchititsa manyazi pomuleka poyera. Choncho anaganiza zomuleka mosaonetsera.
Josef byl ohleduplný muž a nechtěl Marii vystavit veřejné hanbě, proto se rozhodl, že se s ní rozejde.
20 Koma akuganiza zimenezi, taonani, mngelo wa Ambuye anamuonekera mʼmaloto nati, “Yosefe mwana wa Davide, usaope kumutenga Mariya kukhala mkazi wako, chifukwa mwana akuyembekezerayo ndi wochokera kwa Mzimu Woyera.
Když o tom uvažoval, ukázal se mu ve snu Boží posel a řekl: „Josefe, Davidův synu, neboj se vzít si Marii. Co v ní bylo počato, je z Ducha svatého.
21 Ndipo adzabala mwana wamwamuna, udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.”
Porodí syna a dáš mu jméno Ježíš. On vysvobodí svůj lid z moci zla.
22 Zonsezi zinachitika kukwaniritsa zimene Ambuye ananena mwa mneneri kuti,
Těmito událostmi se splní předpověď proroka Izajáše:
23 “Onani namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli,” kutanthauza kuti, “Mulungu ali nafe.”
‚Slyšte! Panna bude těhotná a porodí syna. Budete mu říkat Immanuel, to znamená: Bůh je s námi.‘“
24 Yosefe atadzuka, anachita zomwe mngelo wa Ambuye uja anamulamulira. Iye anamutenga Mariya kukhala mkazi wake.
Když se Josef probudil, udělal vše tak, jak mu přikázal Boží posel, a oženil se s Marií.
25 Koma sanagone malo amodzi mpaka mwanayo atabadwa ndipo anamutcha dzina lake Yesu.
Ale nežil s ní manželsky až do doby, kdy se jí narodil syn, kterému dal jméno Ježíš.

< Mateyu 1 >