< Mateyu 6 >
1 “Samalani kuti musachite ntchito zanu zolungama pamaso pa anthu kuti akuoneni. Popeza ngati mutero simudzalandira mphotho yochokera kwa Atate anu akumwamba.
"Be careful that you do not do your righteousness before people, to be seen by them, or else you have no reward from your Father who is in heaven.
2 “Pamene mupereka zachifundo, musachite modzionetsera monga amachita achiphamaso mʼmasunagoge ndi pa misewu kuti atamidwe ndi anthu. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwowo alandiriratu mphotho yawo yonse.
Therefore when you practice charitable giving, do not sound a trumpet before yourself, as the hypocrites do in the synagogues and in the streets, that they may get glory from people. Truly I tell you, they have received their reward.
3 Koma pamene mupereka zachifundo, dzanja lanu lamanzere lisadziwe chimene dzanja lanu lamanja likuchita,
But when you practice charitable giving, do not let your left hand know what your right hand does,
4 kotero kuti kupereka kwanu kukhale mwachinsinsi. Ndipo Atate anu amene amaona zochitika mwachinsinsi, adzakupatsani mphotho.
so that your charitable giving may be in secret, then your Father who sees in secret will reward you.
5 “Pamene mupemphera, musakhale ngati achiphamaso, chifukwa iwo amakonda kupemphera choyimirira mʼmasunagoge ndi pa mphambano za mʼmisewu kuti anthu awaone. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwo alandiriratu mphotho yawo yonse.
"And when you pray, you are not to be as the hypocrites, for they love to stand and pray in the synagogues and in the corners of the streets, that they may be seen by others. Truly, I tell you, they have received their reward.
6 Koma pamene mupemphera, lowani mʼchipinda chanu chamʼkati, ndi kutseka chitseko ndipo mupemphere kwa Atate anu amene saoneka. Ndipo Atate anu, amene amaona zochitika mseri, adzakupatsani mphotho.
But you, when you pray, enter into your inner chamber, and having shut your door, pray to your Father who is in secret, and your Father who sees in secret will reward you.
7 Ndipo pamene mukupemphera, musamabwerezabwereza monga akunja, pakuti iwo amaganiza kuti adzamveka chifukwa chochulutsa mawu.
And in praying, do not use vain repetitions, as the unbelievers do; for they think that they will be heard for their much speaking.
8 Musakhale ngati iwo chifukwa Atate anu amadziwa zimene musowa musanapemphe.
Therefore do not be like them, for your Father knows what things you need, before you ask him.
9 “Chifukwa chake pempherani motere: “‘Atate athu akumwamba, dzina lanu lilemekezedwe,
Therefore, you should pray this way: 'Our Father in heaven, holy be your name.
10 Ufumu wanu ubwere, chifuniro chanu chichitike pansi pano monga kumwamba.
Let your Kingdom come. Let your will be done, on earth as it is in heaven.
11 Mutipatse chakudya chathu chalero.
Give us today our daily bread.
12 Mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso tawakhululukira amangawa athu.
And forgive us our debts, as we also forgive our debtors.
13 Ndipo musatitengere kokatiyesa; koma mutipulumutse kwa woyipayo.’
And lead us not into temptation, but deliver us from evil.'
14 Ngati inu mukhululukira anthu pamene akuchimwirani, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani.
"For if you forgive people their wrongdoing, your heavenly Father will also forgive you.
15 Koma ngati inu simukhululukira anthu zolakwa zawo, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu.
But if you do not forgive people, neither will your Father forgive your wrongdoing.
16 “Pamene mukusala kudya, musaonetse nkhope yachisoni monga achita achiphamaso, pakuti iwo amasintha nkhope zawo kuonetsa anthu kuti akusala kudya. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwo alandiriratu mphotho yawo yonse.
"Moreover when you fast, do not be like the hypocrites, with sad faces. For they disfigure their faces, that they may be seen by people to be fasting. Truly I tell you, they have received their reward.
17 Koma pamene ukusala kudya, samba mʼmaso nudzole mafuta kumutu,
But you, when you fast, anoint your head, and wash your face;
18 kuti usaonekere kwa anthu kuti ukusala kudya koma kwa Atate ako ali mseri; ndipo Atate ako amene amaona za mseri adzakupatsa mphotho.
so that you are not seen by people to be fasting, but by your Father who is in secret, and your Father, who sees in secret, will reward you.
19 “Musadziwunjikire chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimawononga ndi pamene mbala zimathyola ndi kuba.
"Do not store up treasures for yourselves on the earth, where moth and decay destroy, and where thieves break through and steal;
20 Koma mudziwunjikire chuma kumwamba kumene njenjete ndi dzimbiri siziwononga ndipo mbala sizithyola ndi kuba.
but store up for yourselves treasures in heaven, where neither moth nor decay destroy, and where thieves do not break through and steal;
21 Pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wako udzakhala komweko.
for where your treasure is, there your heart will be also.
22 “Diso ndi nyale ya thupi. Ngati maso ako ali bwino, thupi lako lonse lidzakhala mʼkuwala.
"The lamp of the body is the eye. If therefore your eye is sound, your whole body will be full of light.
23 Koma ngati maso ako sali bwino, thupi lako lonse lidzakhala mu mdima. Koma ngati kuwala kuli mwa iwe ndi mdima, ndiye kuti mdimawo ndi waukulu bwanji!
But if your eye is bad, your whole body will be full of darkness. If therefore the light that is in you is darkness, how great is the darkness.
24 “Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri. Pakuti pena adzamuda mmodzi ndi kukonda winayo kapena adzagwira ntchito mokhulupirika kwa mmodzi, nadzanyoza winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa chuma pa nthawi imodzi.
"No one can serve two masters, for either he will hate the one and love the other; or else he will be devoted to one and despise the other. You cannot serve both God and Mammon.
25 “Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu kuti mudzadya chiyani kapena mudzamwa chiyani; kapenanso za thupi lanu kuti mudzavala chiyani. Kodi moyo suposa chakudya? Kodi thupi siliposa zovala?
Therefore I tell you, do not be anxious about your life, what you will eat or what you will drink; or about your body, what you will wear. Is not life more than food, and the body more than clothing?
26 Onani mbalame zamlengalenga sizifesa kapena kukolola kapena kusunga mʼnkhokwe komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Kodi inu simuziposa kwambiri?
See the birds of the sky, that they do not sow, neither do they reap, nor gather into barns, and your heavenly Father feeds them. Are you not of much more value than they?
27 Kodi ndani wa inu podandaula angathe kuwonjeza ora limodzi pa moyo wake?
"And which of you, by being anxious, can add one cubit to his height?
28 “Ndipo bwanji inu mudera nkhawa za zovala? Onani makulidwe a maluwa akutchire. Sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu.
And why are you anxious about clothing? Consider the lilies of the field, how they grow. They do not toil, neither do they spin,
29 Ndikukuwuzani kuti angakhale Solomoni mu ulemerero wake sanavale mofanana ndi limodzi la maluwa amenewa.
yet I tell you that even Solomon in all his glory was not dressed like one of these.
30 Ngati umu ndi mmene Mulungu avekera udzu wa kutchire umene ulipo lero ndipo mawa uponyedwa ku moto, kodi sadzakuvekani koposa? Aa! Inu a chikhulupiriro chochepa!
But if God so clothes the grass of the field, which today exists, and tomorrow is thrown into the oven, won't he much more clothe you, you of little faith?
31 Chifukwa chake musadere nkhawa ndi kuti, ‘Tidzadya chiyani?’ kapena ‘Tidzamwa chiyani?’ kapena ‘Tidzavala chiyani?’
"Therefore do not be anxious, saying, 'What will we eat?', 'What will we drink?' or, 'With what will we be clothed?'
32 Pakuti anthu akunja amazifuna zinthu zonsezi ndipo Atate anu akumwamba adziwa kuti musowa zimenezi.
For the unbelievers seek after all these things, for your heavenly Father knows that you need all these things.
33 Koma muyambe mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake ndipo zinthu zonsezi zidzapatsidwa kwa inu.
But seek first the Kingdom and his righteousness, and all these things will be given to you as well.
34 Chifukwa chake musadere nkhawa ndi za mawa, popeza tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira.
Therefore do not be anxious for tomorrow, for tomorrow will be anxious for itself. Each day has enough trouble of its own.