< Mateyu 5 >

1 Iye ataona anthu ambiri, anakwera pa phiri nakhala pansi. Ndipo ophunzira ake anabwera kwa Iye,
예수께서 무리를 보시고 산에 올라가 앉으시니 제자들이 나아온지라
2 ndipo anayamba kuwaphunzitsa kuti,
입을 열어 가르쳐 가라사대
3 “Odala ndi amene ali osauka mu mzimu, chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.
심령이 가난한 자는 복이 있나니 천국이 저희 것임이요
4 Odala ndi amene ali achisoni, chifukwa adzatonthozedwa.
애통하는 자는 복이 있나니 저희가 위로를 받을 것임이요
5 Odala ndi amene ali ofatsa, chifukwa adzalandira dziko lapansi.
온유한 자는 복이 있나니 저희가 땅을 기업으로 받을 것임이요
6 Odala ndi amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo, chifukwa adzakhutitsidwa.
의에 주리고 목마른 자는 복이 있나니 저희가 배부를 것임이요
7 Odala ndi amene ali ndi chifundo, chifukwa adzawachitira chifundo.
긍휼히 여기는 자는 복이 있나니 저희가 긍휼히 여김을 받을 것임이요
8 Odala ndi amene ali oyera mtima, chifukwa adzaona Mulungu.
마음이 청결한 자는 복이 있나니 저희가 하나님을 볼 것임이요
9 Ndi odala amene amabweretsa mtendere, chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.
화평케 하는 자는 복이 있나니 저희가 하나님의 아들이라 일컬음을 받을 것임이요
10 Odala ndi amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo, pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo.”
의를 위하여 핍박을 받은 자는 복이 있나니 천국이 저희 것임이라
11 “Inu ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani, kukunenerani zoyipa zilizonse ndi kukunamizirani chifukwa cha Ine.
나를 인하여 너희를 욕하고 핍박하고 거짓으로 너희를 거스려 모든 악한 말을 할 때에는 너희에게 복이 있나니
12 Sangalalani, kondwerani chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu kumwamba, chifukwa moterenso ndi mmene anazunzira aneneri inu musanabadwe.
기뻐하고 즐거워하라 하늘에서 너희의 상이 큼이라 너희 전에 있던 선지자들을 이같이 핍박하였느니라
13 “Inu ndinu mchere wa dziko lapansi. Koma ngati mcherewo usukuluka, adzawukometsanso ndi chiyani? Ulibenso ntchito koma kungowutaya kunja, anthu nawuponda.
너희는 세상의 소금이니 소금이 만일 그 맛을 잃으면 무엇으로 짜게 하리요 후에는 아무 쓸데 없어 다만 밖에 버리워 사람에게 밟힐 뿐이니라
14 “Inu ndinu kuwunika kwa dziko lapansi. Mzinda wa pa phiri sungathe kubisika.
너희는 세상의 빛이라 산 위에 있는 동네가 숨기우지 못할 것이요
15 Anthu sayatsa nyale ndikuyivundikira ndi mbiya, mʼmalo mwake amayika poonekera ndipo imawunikira onse mʼnyumbamo.
사람이 등불을 켜서 말 아래 두지 아니하고 등경 위에 두나니 이러므로 집안 모든 사람에게 비취느니라
16 Momwemonso kuwunika kwanu kuwale pamaso pa anthu kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kulemekeza Atate anu akumwamba.
이같이 너희 빛을 사람 앞에 비취게 하여 저희로 너희 착한 행실을 보고 하늘에 계신 너희 아버지께 영광을 돌리게 하라
17 “Musaganize kuti ndinadza kudzathetsa malamulo kapena zonena za aneneri; sindinabwere kudzathetsa koma kukwaniritsa.
내가 율법이나 선지자나 폐하러 온 줄로 생각지 말라 폐하러 온 것이 아니요 완전케 하려 함이로다
18 Ine ndikukuwuzani zoonadi kuti, kufikira kutha kwa thambo ndi dziko lapansi, chilichonse chimene chinalembedwa mʼmalamulo, ngakhale kalemba kakangʼonongʼono, chidzakwaniritsidwa.
진실로 너희에게 이르노니 천지가 없어지기 전에는 율법의 일점 일획이라도 반드시 없어지지 아니하고 다 이루리라
19 Chifukwa chake aliyense amene aphwanya limodzi la malamulowa ngakhale lalingʼonongʼono ndi kuphunzitsa ena kuti achite chimodzimodzi, adzakhala wotsirizira mu ufumu wakumwamba, koma aliyense amene achita ndi kuphunzitsa malamulo awa adzakhala wamkulu mu ufumu wakumwamba.
그러므로 누구든지 이 계명 중에 지극히 작은 것 하나라도 버리고 또 그같이 사람을 가르치는 자는 천국에서 지극히 작다 일컬음을 받을 것이요 누구든지 이를 행하며 가르치는 자는 천국에서 크다 일컬음을 받으리라
20 Chifukwa chake ndikuwuzani kuti ngati chilungamo chanu sichiposa cha Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo, zoonadi, simudzalowa mu ufumu wakumwamba.
내가 너희에게 이르노니 너희 의가 서기관과 바리새인보다 더 낫지 못하면 결단코 천국에 들어가지 못하리라
21 “Munamva kuti kunanenedwa kwa anthu kale kuti, ‘Usaphe ndipo kuti aliyense amene apha munthu adzaweruzidwa.’
옛 사람에게 말한 바 살인치 말라 누구든지 살인하면 심판을 받게 되리라 하였다는 것을 너희가 들었으나
22 Koma Ine ndikukuwuzani kuti aliyense wokwiyira mʼbale wake adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene wonena mʼbale wake kuti, ‘Ndiwe wopanda phindu,’ adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu lalikulu. Ndipo aliyense amene anganene mnzake ‘wopandapake’ adzatengeredwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene angamunene mnzake kuti, ‘Chitsiru iwe,’ adzaponyedwa ku gehena. (Geenna g1067)
나는 너희에게 이르노니 형제에게 노하는 자마다 심판을 받게 되고 형제를 대하여 라가라 하는 자는 공회에 잡히게 되고 미련한 놈이라 하는 자는 지옥 불에 들어가게 되리라 (Geenna g1067)
23 “Nʼchifukwa chake, pamene ukupereka chopereka chako pa guwa lansembe ndipo nthawi yomweyo ukumbukira kuti mʼbale wako ali nawe chifukwa,
그러므로 예물을 제단에 드리다가 거기서 네 형제에게 원망들을 만한 일이 있는 줄 생각나거든
24 usiye choperekacho pa guwa lansembepo, choyamba pita kayanjane ndi mʼbale wako; ukatero bwera kudzapereka chopereka chakocho.
예물을 제단 앞에 두고 먼저 가서 형제와 화목하고 그 후에 와서 예물을 드리라
25 “Fulumira kuyanjana ndi mnzako amene unamulakwira nthawi ya milandu isanafike chifukwa angakupereke kwa oweruza amene angakupereke kwa mlonda ndipo mlondayo angakutsekere mʼndende.
너를 송사하는 자와 함께 길에 있을 때에 급히 사화하라 그 송사하는 자가 너를 재판관에게 내어주고 재판관이 관예에게 내어주어 옥에 가둘까 염려하라
26 Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti sudzatuluka mʼndende mpaka utalipira zonse.
진실로 네게 이르노니 네가 호리라도 남김이 없이 다 갚기 전에는 결단코 거기서 나오지 못하리라
27 “Munamva kuti kunanenedwa kuti, ‘Usachite chigololo.’
또 간음치 말라 하였다는 것을 너희가 들었으나
28 Koma Ine ndikuwuzani kuti aliyense woyangʼana mkazi momusirira wachita naye kale chigololo mu mtima mwake.
나는 너희에게 이르노니 여자를 보고 음욕을 품는 자마다 마음에 이미 간음하였느니라
29 Ngati diso lako lakumanja likuchimwitsa, ulichotse ndi kulitaya. Pakuti nʼkwabwino kwa iwe kutaya chiwalo chimodzi cha thupi lako, kusiyana ndi kuti thupi lonse liponyedwe mʼgehena. (Geenna g1067)
만일 네 오른 눈이 너로 실족케 하거든 빼어 내버리라 네 백체 중 하나가 없어지고 온 몸이 지옥에 던지우지 않는 것이 유익하며 (Geenna g1067)
30 Ndipo ngati dzanja lako lamanja likuchimwitsa, ulidule ndi kulitaya. Pakuti nʼkwabwino kwa iwe kutaya chiwalo chimodzi cha thupi lako, kusiyana ndi kuti thupi lonse liponyedwe mʼgehena. (Geenna g1067)
또한 만일 네 오른손이 너로 실족케 하거든 찍어 내버리라 네 백체 중 하나가 없어지고 온 몸이 지옥에 던지우지 않는 것이 유익하니라 (Geenna g1067)
31 “Ananena kuti, ‘Aliyense wosudzula mkazi wake ayenera amupatse kalata ya chisudzulo.’
또 일렀으되 누구든지 아내를 버리거든 이혼 증서를 줄 것이라 하였으나
32 Koma Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake pa chifukwa china chilichonse osati chifukwa cha chiwerewere, akumuchititsa mkaziyo chigololo ndipo aliyense wokwatira mkaziyo, akuchitanso chigololo.
나는 너희에게 이르노니 누구든지 음행한 연고 없이 아내를 버리면 이는 저로 간음하게 함이요 또 누구든지 버린 여자에게 장가드는 자도 간음함이니라
33 “Munamvanso kuti kunanenedwa kwa anthu akale kuti, ‘Musaphwanye lonjezo; koma sungani malonjezo anu amene mwachita kwa Yehova.’
또 옛 사람에게 말한 바 헛 맹세를 하지 말고 네 맹세한 것을 주께 지키라 하였다는 것을 너희가 들었으나
34 Koma ndikuwuzani kuti musalumbire ndi pangʼono pomwe kutchula kumwamba chifukwa kuli mpando waufumu wa Mulungu.
나는 너희에게 이르노니 도무지 맹세하지 말찌니 하늘로도 말라 이는 하나님의 보좌임이요
35 Kapena kutchula dziko lapansi, chifukwa ndi chopondapo mapazi ake; kapena kutchula Yerusalemu, chifukwa ndi mzinda wa mfumu yayikulu.
땅으로도 말라 이는 하나님의 발등상임이요 예루살렘으로도 말라 이는 큰 임금의 성임이요
36 Ndipo musalumbire ndi mutu wanu chifukwa simungathe kuyeretsa ngakhale kudetsa tsitsi limodzi.
네 머리로도 말라 이는 네가 한 터럭도 희고 검게 할 수 없음이라
37 Koma ‘Inde’ wanu akhaledi ‘Inde’ kapena ‘Ayi’ wanu akhaledi ‘Ayi,’ chilichonse choposera apa, chichokera kwa woyipayo.
오직 너희 말은 옳다 옳다, 아니라 아니라 하라 이에서 지나는 것은 악으로 좇아 나느니라
38 “Munamva kuti, ‘Diso kulipira diso ndi dzino kulipira dzino.’
또 눈은 눈으로, 이는 이로 갚으라 하였다는 것을 너희가 들었으나
39 Koma ndikuwuzani kuti musamukanize munthu woyipa, akakumenya patsaya mupatseni tsaya linalo.
나는 너희에게 이르노니 악한 자를 대적지 말라 누구든지 네 오른편 뺨을 치거든 왼편도 돌려 대며
40 Ndipo ngati wina afuna kukuzenga mlandu kuti akulande malaya ako, umupatsenso mkanjo wako.
또 너를 송사하여 속옷을 가지고자 하는 자에게 겉옷까지도 가지게 하며
41 Ngati wina akukakamiza kuti uyende naye mtunda umodzi, iwe uyende naye mitunda iwiri.
또 누구든지 너로 억지로 오 리를 가게 하거든 그 사람과 십 리를 동행하고
42 Wina akakupempha kanthu umupatse, ndipo wofuna kubwereka usamukanize.
네게 구하는 자에게 주며 네게 꾸고자 하는 자에게 거절하지 말라
43 “Munamva kuti, ‘Konda mnansi wako ndi kudana ndi mdani wako.’
또 네 이웃을 사랑하고 네 원수를 미워하라 하였다는 것을 너희가 들었으나
44 Koma Ine ndikuwuzani kuti, ‘Kondani adani anu ndi kuwapempherera okuzunzani
나는 너희에게 이르노니 너희 원수를 사랑하며 너희를 핍박하는 자를 위하여 기도하라
45 kuti mukhale ana a Atate anu akumwamba, amene awalitsa dzuwa lake pa oyipa ndi pa abwino, nagwetsa mvula pa olungama ndi pa osalungama.’
이같이 한즉 하늘에 계신 너희 아버지의 아들이 되리니 이는 하나님이 그 해를 악인과 선인에게 비취게 하시며 비를 의로운 자와 불의한 자에게 내리우심이니라
46 Ngati mukonda amene akukondani inu, mudzapeza mphotho yanji? Kodi ngakhale amisonkho sachita chimodzimodzi?
너희가 너희를 사랑하는 자를 사랑하면 무슨 상이 있으리요 세리도 이같이 아니하느냐
47 Ndipo ngati inu mupatsa moni abale anu okhaokha mukuchita chiyani choposa ena? Kodi ngakhale akunja sachita chimodzimodzi?
또 너희가 너희 형제에게만 문안하면 남보다 더 하는 것이 무엇이냐 이방인들도 이같이 아니하느냐
48 Nʼchifukwa chake, inu khalani angwiro monga Atate anu akumwamba ali wangwiro.”
그러므로 하늘에 계신 너희 아버지의 온전하심과 같이 너희도 온전하라

< Mateyu 5 >