< Mateyu 27 >

1 Mmamawa, akulu a ansembe onse ndi akuluakulu anavomerezana kuti aphe Yesu.
לפנות בוקר שוב התכנסו ראשי הכוהנים וזקני העם, כדי להתייעץ כיצד לשכנע את המושל הרומאי להוציא את ישוע להורג.
2 Anamumanga, napita naye kukamupereka kwa bwanamkubwa Pilato.
הם כבלו אותו ושלחו אותו לפילטוס, המושל הרומאי.
3 Yudasi, amene anamupereka Iye, ataona kuti Yesu waweruzidwa kuti akaphedwe, anatsutsika mu mtima mwake nakabweza ndalama zamasiliva makumi atatu zija kwa akulu a ansembe ndi kwa akuluakulu.
כאשר ראה יהודה הבוגד שישוע נידון למוות, התחרט על המעשה שעשה והחזיר את הכסף לראשי הכוהנים והזקנים.
4 Iye anati, “Ndachimwa pakuti ndapereka munthu wosalakwa.” Iwo anayankha nati, “Ife tilibe nazo kanthu izo ndi zako.”
”חטאתי“, הכריז יהודה.”בגדתי באדם חף מפשע.“”לא אכפת לנו“, השיבו.”זאת הבעיה שלך.“
5 Pamenepo Yudasi anaponya ndalamazo mʼNyumba ya Mulungu nachoka. Kenaka anapita nakadzimangirira.
יהודה זרק את הכסף על הרצפה במקדש, והלך לתלות את עצמו.
6 Akulu a ansembe anatola ndalamazo nati, “Sikololedwa ndi lamulo kuti ndalamazi tiziyike mosungira chuma cha Mulungu, popeza ndi ndalama za magazi.”
ראשי הכוהנים אספו את הכסף מהרצפה ואמרו:”איננו יכולים להכניס את הכסף לאוצר, כי התורה אוסרת קבלת כסף דמים.“
7 Choncho anagwirizana kuti ndalamazo azigwiritse ntchito pogulira munda wa wowumba mbiya kuti ukhale manda alendo.
הם התייעצו ביניהם, ולבסוף החליטו לקנות בכסף זה את שדה היוצר בירושלים, שהשתמשו בו לקבורת גויים.
8 Ndi chifukwa chake umatchedwa munda wamagazi mpaka lero lino.
משום כך נקרא השדה ההוא עד היום הזה:”שדה הדם“.
9 Pamenepo zimene anayankhula mneneri Yeremiya zinakwaniritsidwa kuti, “Anatenga ndalama zamasiliva makumi atatu mtengo umene anamuyikira Iye anthu a Israeli.
בזאת התקיימה נבואת זכריה:”הם לקחו את שלושים שקלי הכסף – המחיר שבו העריכו אותו בני ישראל – וקנו שדה מאת הקדר, כפי שהדריך אותי ה׳.“
10 Ndipo anazigwiritsa ntchito kugula munda wa wowumba mbiya monga mmene Ambuye anandilamulira ine.”
11 Pa nthawi yomweyo Yesu anayimirira pamaso pa bwanamkubwa ndipo bwanamkubwayo anamufunsa Iye kuti, “Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Koma Yesu anayankha kuti, “Mwanena ndinu.”
ישוע עמד לפני פילטוס, המושל הרומאי, וזה שאל אותו:”האם אתה מלך היהודים?“”אתה אומר“, השיב ישוע.
12 Pamene akulu a ansembe ndi akuluakulu ankamuneneza, sanayankhe kanthu.
אולם כאשר ראשי הכוהנים והזקנים האשימו אותו, ישוע לא אמר דבר.
13 Kenaka Pilato anamufunsa Iye kuti, “Kodi sukumva zinthu zimene akukunenerazi?”
”האם אינך שומע את מה שהם אומרים?“שאל פילטוס.
14 Koma Yesu sanayankhe ngakhale mawu amodzi mpaka bwanamkubwa anadabwa kwambiri.
אך להפתעתו הרבה של המושל לא אמר ישוע דבר.
15 Pa nthawiyi chinali chizolowezi cha bwanamkubwa kuti pachikondwerero cha Paska amamasula wamʼndende wosankhidwa ndi anthu.
כל שנה, לכבוד חג הפסח, נהג המושל לשחרר אסיר יהודי אחד לפי בחירת העם.
16 Pa nthawiyo anali ndi wamʼndende woyipa kwambiri dzina lake Baraba.
באותה שנה היה בכלא אסיר ידוע לשמצה בשם ישוע בר־אבא.
17 Gulu la anthu litasonkhana, Pilato anawafunsa kuti, “Ndi ndani amene mufuna kuti ndikumasulireni; Baraba kapena Yesu wotchedwa Khristu?”
כאשר התאסף באותו בוקר המון רב לפני ביתו של פילטוס, הוא שאל:”את מי אשחרר לכם, את ישוע בר־אבא, או את ישוע הנקרא משיח?“
18 Pakuti anadziwa kuti anamupereka Yesu chifukwa cha kaduka.
כי פילטוס ידע היטב שמסרו את ישוע מתוך קנאה.
19 Pamene Pilato anakhala pa mpando woweruza, mkazi wake anamutumizira uthenga uwu, “Musachite kanthu ndi munthuyo, ndi wosalakwa pakuti ndavutika kwambiri lero mʼmaloto chifukwa cha munthuyo.”
באותו זמן, כשישב פילטוס על כסאו בבית־הדין, שלחה אליו אשתו הודעה:”עזוב את האיש הטוב הזה לנפשו, כי בלילה האחרון חלמתי עליו חלום נורא.“
20 Koma akulu a ansembe ndi akuluakulu ananyengerera gulu la anthu kuti apemphe Baraba ndi kuti Yesu aphedwe.
בינתיים הספיקו ראשי הכוהנים והזקנים לשכנע את ההמון לדרוש את שחרורו של בר־אבא, ואת הוצאתו להורג של ישוע.
21 Bwanamkubwayo anafunsa kuti, “Ndi ndani mwa awiriwa amene mufuna ine ndikumasulireni?” Iwo anayankha kuti, “Baraba.”
וכך כשחזר המושל ושאל:”את מי מהשניים אשחרר לכם?“צעק הקהל:”את בר־אבא!“
22 Pilato anafunsa kuti, “Nanga ndichite chiyani ndi Yesu wotchedwa Khristu?” Onse anayankha kuti “Mpachikeni!”
”אם כך, מה אעשה עם ישוע הנקרא משיח?“שאל פילטוס.”צלוב אותו!“הם צעקו.
23 Pilato anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani? Wachita choyipa chotani?” Koma anachita phokoso nafuwula kwambiri kuti, “Mpachikeni!”
”מדוע? מה עשה?“שאל פילטוס. הם לא ענו, ורק הגבירו את צעקותיהם:”צלוב אותו!“
24 Pilato ataona kuti samaphulapo kanthu, koma mʼmalo mwake chiwawa chimayambika, anatenga madzi nasamba mʼmanja mwake pamaso pa gulu la anthu. Iye anati “Ine ndilibe chifukwa ndi magazi a munthu uyu, ndipo uwu ndi udindo wanu!”
כשראה פילטוס שאין טעם להמשיך ושעלולה לפרוץ מהומה, דרש שיביאו אליו קערת מים. הוא רחץ את ידיו לעיני הקהל ואמר:”הידיים שלי נקיות מדמו של האיש הצדיק הזה. האחריות מוטלת עליכם!“
25 Anthu onse anayankha nati, “Magazi ake akhale pa ife ndi pa ana athu!”
וההמון השיב בצעקה:”דמו עלינו ועל בנינו!“
26 Pamenepo anawamasulira Baraba koma analamula kuti Yesu akakwapulidwe, ndipo anamupereka kuti akapachikidwe.
אז שחרר להם פילטוס את בר־אבא, ולאחר שהלקה את ישוע בשוטים מסרו לידי החיילים הרומאים, כדי שיקחו אותו לצליבה.
27 Pamenepo asilikali abwanamkubwayo anamutenga nalowa naye ku bwalo la milandu ndipo anasonkhanitsa gulu lonse la asilikali namuzungulira Iye.
אולם לפני כן הם לקחו אותו אל ארמון המושל וקראו לכל חיילי המשמר.
28 Anamuvula malaya ake namuveka Iye malaya ofiira aufumu.
הם הפשיטוהו והלבישוהו גלימת ארגמן.
29 Ndipo kenaka analuka chipewa chaminga nachiyika pa mutu pake. Anamugwiritsa ndodo mʼdzanja lake lamanja nagwada pamaso pake namuchitira chipongwe nati, “Tikulonjereni Mfumu ya Ayuda.”
לאחר מכן שזרו זר מקוצים ארוכים והניחו על ראשו ככתר, בידו הימנית שמו מקל כשרביט, כרעו ברך לפניו בלגלוג והתגרו בו בקריאות לעג:”יחי מלך היהודים!“
30 Anamuthira malovu ndipo anatenga ndodo namumenya nayo pa mutu mobwerezabwereza.
הם ירקו בפניו, חטפו מידו את המקל והכוהו על ראשו.
31 Atamaliza kumuchitira chipongwe, anamuvula malaya aja namuveka malaya ake aja napita naye kokamupachika.
לאחר שסיימו החיילים להתלוצץ ולצחוק עליו, הפשיטו מעליו את הגלימה והלבישו אותו בבגדיו, והוציאו אותו החוצה לצליבה.
32 Pamene gululi linkatuluka ndi Yesu, anakumana ndi munthu wochokera ku Kurene dzina lake Simoni ndipo anamuwumiriza kunyamula mtanda.
בדרך למקום הצליבה הם פגשו את שמעון מקירניה ואילצו אותו לסחוב את הצלב של ישוע.
33 Anafika ku malo wotchedwa Gologota amene atanthauza kuti malo a bade la mutu.
הם המשיכו בדרכם עד שהגיעו למקום הנקרא”גלגלתא“, או”מקום הגולגולת“.
34 Pamenepo anamupatsa vinyo wosakaniza ndi ndulu kuti amwe; koma atalawa anakana kumwa.
החיילים נתנו לו יין מסומם, אולם לאחר שטעם ממנו סרב לשתות אותו.
35 Atamupachika Iye, anagawana zovala zake pochita maere.
לאחר הצליבה הפילו החיילים גורל, כדי לחלק ביניהם את בגדיו של ישוע.
36 Ndipo anakhala pansi namulonda Iye.
ואז התיישבו והביטו בישוע על הצלב.
37 Pamwamba pa mutu wake analembapo mawu osonyeza mlandu wake akuti, “uyu ndi yesu, mfumu ya ayuda.”
מעל ראשו הם תלו שלט:”זהו ישוע מלך היהודים.“
38 Achifwamba awiri anapachikidwa pamodzi ndi Iye, mmodzi kudzanja lamanja wina kudzanja lamanzere.
יחד עם ישוע נצלבו גם שני פושעים – אחד לימינו ואחד לשמאלו.
39 Ndipo amene amadutsa anamunenera mawu a chipongwe, akupukusa mitu yawo.
העוברים ושבים קללו אותו, לעגו לו וקראו:
40 Ndipo anati, “Iwe amene ungapasule Nyumba ya Mulungu ndi kuyimanga masiku atatu, dzipulumutse wekha! Tsika pa mtandapo ngati ndiwe Mwana wa Mulungu!”
”נו, אתה יכול להרוס את בית המקדש ולבנותו מחדש בשלושה ימים? אם אתה בן־אלוהים, מדוע אינך יורד מהצלב ומציל את עצמך?“
41 Chimodzimodzinso akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo ndi akuluakulu anamuchitira chipongwe.
גם ראשי הכוהנים, הסופרים והזקנים חרפו אותו ולעגו לו:
42 Iwo anati, “Anapulumutsa ena koma sangathe kudzipulumutsa yekha! Ndi mfumu ya Israeli! Mulekeni atsike pa mtanda ndipo tidzamukhulupirira Iye.
”הוא יכול להושיע את כולם חוץ מאשר את עצמו!“צחקו.”משיח שכמוהו!“קראו.”מלך ישראל, הבה נראה אותו יורד מהצלב, ואז נאמין בו!
43 Amadalira Mulungu, mulekeni Mulunguyo amupulumutse tsopano ngati akumufuna pakuti anati, ‘Ndine Mwana wa Mulungu.’”
הרי בטח באלוהים, נראה אם אלוהים באמת יציל אותו. הרי אמר שהוא בן־אלוהים!“
44 Momwemonso mbala zimene zinapachikidwa naye pamodzi zinamuneneranso zachipongwe.
גם הפושעים שנצלבו לידו העליבו אותו בצורה דומה.
45 Kuyambira 12 koloko masana mpaka 3 koloko, kunachita mdima pa dziko lonse.
בשעה שתים־עשרה בצהריים כיסה חושך את כל הארץ למשך שלוש שעות.
46 Ndipo nthawi ili ngati 3 koloko, Yesu analira mofuwula nati, “Eloi, Eloi, lama sabakitani!” Kutanthauza kuti, “Mulungu Wanga, Mulungu Wanga, mwandisiyiranji Ine?”
בשעה שלוש אחר־הצהריים זעק ישוע זעקת שבר:”אלי, אלי, למה שבקתני?“(כלומר:”אלי, אלי, למה עזבתני?“)
47 Ena a oyimirira pamalopo atamva izi anati, “Akuyitana Eliya.”
אחדים מהנוכחים חשבו שהוא קורא לאליהו הנביא.
48 Mmodzi wa iwo anathamanga natenga chinkhupule. Anachidzaza ndi vinyo wosasa, nachizika ku mtengo namupatsa Yesu kuti amwe.
אחד מהם רץ והביא ספוג טבול בחומץ, שם אותו בקצה מקל והושיטו לישוע כדי שישתה.
49 Koma ena onse anati, “Mulekeni tiyeni tione ngati Eliyayo abwere kudzamupulutsa.”
אך יתר האנשים אמרו:”עזוב אותו. הבה נראה אם אליהו באמת יבוא להציל אותו!“
50 Ndipo pamene Yesu analiranso mofuwula, anapereka mzimu wake.
אז זעק ישוע שנית ונפח את נשמתו.
51 Pa nthawi imeneyo chinsalu chotchinga cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati kuyambira pamwamba mpaka pansi. Dziko linagwedezeka ndipo miyala inangʼambika.
באותו רגע הפרוכת שלפני קודש הקודשים בבית־המקדש נקרעה לשניים – מלמעלה עד למטה. האדמה רעדה, סלעים נבקעו,
52 Manda anatsekuka ndipo mitembo yambiri ya anthu oyera mtima amene anafa inaukitsidwa.
קברים נפתחו, וצדיקים רבים קמו לתחייה.
53 Anatuluka mʼmanda mwawo, ndipo chitachitika chiukitso cha Yesu, anapita mu mzinda woyera naonekera kwa anthu ambiri.
לאחר תחייתו של ישוע, אלה עזבו את בית־הקברות, נכנסו לירושלים והופיעו לפני אנשים רבים.
54 Mkulu wa asilikali ndi amene ankalondera Yesu ataona chivomerezi ndi zonse zinachitika, anachita mantha, ndipo anati, “Zoonadi, uyu anali Mwana wa Mulungu!”
קצין רומאי והחיילים שהיו ליד הצלב, נבהלו מאוד מרעידת האדמה ומכל מה שקרה, וקראו:”איש זה באמת היה בן־אלוהים!“
55 Amayi ambirimbiri amene ankasamalira Yesu ankaonerera ali patali. Iwo anamutsatira Yesu kuchokera ku Galileya.
נשים רבות שבאו עם ישוע מהגליל, כדי לשרתו, עמדו מרחוק והתבוננו.
56 Pakati pawo panali Mariya wa ku Magadala, Mariya amayi ake Yakobo ndi Yosefe ndi amayi a ana a Zebedayo.
ביניהן היו מרים המגדלית, מרים אמם של יעקב ויוסף, ואמם של יעקב ויוחנן (בני זבדי).
57 Pamene kumada, kunabwera munthu wolemera wa ku Arimateyu dzina lake Yosefe amene anali wophunzira wa Yesu.
בערב ניגש אל פילטוס יוסף מן־הרמתיים, שהיה אדם עשיר ותלמיד של ישוע, וביקש את גופתו. פילטוס ציווה לשחרר את הגופה ולהעביר אותה ליוסף.
58 Anapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu, ndipo Pilato analamula kuti uperekedwe kwa iye.
59 Yosefe anatenga mtembowo, nawukulunga nsalu yabafuta.
יוסף לקח את הגופה, עטף אותה בסדין לבן,
60 Ndipo anawuyika mʼmanda ake atsopano amene anasema mu thanthwe, natsekapo ndi mwala waukulu pa khomo la mandawo nachokapo.
הניח אותה בתוך קבר חדש שחצב בשביל עצמו, סתם את הפתח באבן גדולה והלך לדרכו.
61 Mariya wa Magadala ndi Mariya wina anakhala pansi moyangʼanizana ndi mandawo.
מרים המגדלית ומרים השנייה ישבו במרחק והסתכלו.
62 Litapita tsiku lokonzekera Sabata, mmawa mwake, akulu a ansembe ndi Afarisi anapita kwa Pilato.
למחרת, בתום טקסי החג, באו ראשי הכוהנים והפרושים אל פילטוס
63 Iwo anati, “Bwana takumbukira kuti munthu wonyenga uja akanali ndi moyo anati, ‘Pakatha masiku atatu ndidzauka.’
ואמרו:”אדוננו, השקרן הזה אמר פעם שלאחר שלושה ימים ישוב ויקום לתחייה.
64 Choncho lamulirani kuti manda ake atetezedwe mpaka pa tsiku lachitatu. Chifukwa tikapanda kutero, ophunzira ake angabwere kudzaba mtembo wake ndipo angawuze anthu kuti waukitsidwa kwa akufa. Ndipo chinyengo chomalizachi chidzakhala choyipa kwambiri kusiyana ndi choyamba chija.”
משום כך אנחנו מבקשים ממך לחתום את הקבר עד לאחר היום השלישי, כדי שתלמידיו לא יגנבו את הגופה ויפיצו את השמועה שהוא קם מן המתים. אחרת תהיה התרמית גרועה מזו הראשונה.“
65 Pilato anayankha kuti, “Tengani mlonda kalondereni monga mudziwira.”
פילטוס אמר להם:”יש לכם משמר שלכם, אתם יודעים איך לטפל בזה כמו שצריך“.
66 Tsono anapita nakatseka manda kolimba ndi kuyikapo chizindikiro ndipo anayikapo mlonda.
וכך הם חתמו את הקבר והציבו שומרים.

< Mateyu 27 >