< Mateyu 22 >
1 Yesu anayankhula nawonso mʼmafanizo, nati,
Again Jesus spoke to them in figurative language.
2 “Ufumu wakumwamba uli ngati mfumu imene inakonzera phwando mwana wake wamwamuna.
"The Kingdom of the Heavens," He said, "may be compared to a king who celebrated the marriage of his son,
3 Anatumiza antchito ake kwa amene anayitanidwa kuphwando koma anakana kubwera.
and sent his servants to call the invited guests to the wedding, but they were unwilling to come.
4 “Kenaka anatumiza antchito ena nati, ‘Awuzeni oyitanidwa kuti phwando lakonzedwa: ndapha ngʼombe yayimuna ndi nyama zina zonenepa ndipo zonse zakonzedwa. Bwerani ku phwando laukwati.’
"Again he sent other servants with a message to those who were invited. "'My breakfast is now ready," he said, 'my bullocks and fat cattle are killed, and every preparation is made: come to the wedding.'
5 “Koma iwo sanalabadire ndipo anachoka; wina anapita ku munda wake ndi wina ku malonda ake.
"They however gave no heed, but went, one to his home in the country, another to his business;
6 Ndipo otsalawo anagwira antchito ake, nawazunza ndi kuwapha.
and the rest seized the king's servants, maltreated them, and murdered them.
7 Mfumu inakwiya. Inatumiza asilikali ake ndipo anawononga opha anzawowo ndi kutentha mzinda wawo.
So the king's anger was stirred, and he sent his troops and destroyed those murderers and burnt their city.
8 “Pamenepo anati kwa antchito ake, ‘Phwando laukwati lakonzedwa, koma amene ndinawayitana sanali oyenera.
Then he said to his servants, "'The wedding banquet is ready, but those who were invited were unworthy of it.
9 Pitani ku mphambano za misewu ndipo kayitaneni aliyense amene mukamupeze kuti abwere ku phwando.’
Go out therefore to the crossroads, and everybody you meet invite to the wedding.'
10 Pamenepo antchitowo anapita ku misewu nakasonkhanitsa anthu onse amene anakawapeza, abwino ndi oyipa omwe, ndipo nyumba ya madyerero inadzaza ndi oyitanidwa.
"So they went out into the roads and gathered together all they could find, both bad and good, and the banqueting hall was filled with guests.
11 “Koma pamene mfumu inabwera kudzaona oyitanidwawo, inaona munthu amene sanavale zovala zaukwati.
"Now the king came in to see the guests; and among them he discovered one who was not wearing a wedding-robe.
12 Inamufunsa kuti, ‘Bwenzi walowa bwanji muno wopanda zovala zaukwati?’ Munthuyo anakhala chete.
"'My friend,' he said, 'how is it that you came in here without a wedding robe?'
13 “Pamenepo mfumuyo inawuza otumikira kuti, ‘Mʼmangeni manja ndi miyendo, ndipo muponyeni kunja, ku mdima kumene kudzakhale kulira ndi kukuta mano.’
"The man stood speechless. Then the king said to the servants, "'Bind him hand and foot and fling him into the darkness outside: there will be the weeping aloud and the gnashing of teeth.'
14 “Popeza oyitanidwa ndi ambiri koma osankhidwa ndi ochepa.”
"For there are many called, but few chosen."
15 Kenaka Afarisi anatuluka nakakonza njira zomupezera zifukwa Yesu mʼmawu ake.
Then the Pharisees went and consulted together how they might entrap Him in His conversation.
16 Anatumiza ophunzira awo kwa Iye pamodzi ndi Aherodia. Anati, “Aphunzitsi, tidziwa kuti ndinu wangwiro ndi kuti mumaphunzitsa mawu a Mulungu monga mwa choonadi. Simutekeseka ndi anthu, popeza simusamala kuti kodi ndi ndani?
So they sent to Him their disciples together with the Herodians; who said, "Teacher, we know that you are truthful and that you faithfully teach God's truth; and that no fear of man misleads you, for you are not biased by men's wealth or rank.
17 Tiwuzeni tsono maganizo anu ndi otani, kodi nʼkololedwa kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?”
Give us your judgement therefore: is it allowable for us to pay a poll-tax to Caesar, or not?"
18 Koma Yesu podziwa maganizo awo oyipa anati, “Inu achiphamaso, bwanji mufuna kundipezera chifukwa?
Perceiving their wickedness, Jesus replied, "Why are you hypocrites trying to ensnare me?
19 Onetseni ndalama imene mumapereka msonkho.” Iwo anabweretsa dinari,
Show me the tribute coin." And they brought Him a shilling.
20 ndipo anawafunsa kuti, “Kodi chithunzi ichi ndi malemba awa ndi za ndani?”
"Whose likeness and inscription," He asked, "is this?"
21 Iwo anayankha kuti, “Ndi za Kaisara.” Pamenepo anawawuza kuti, “Perekani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”
"Caesar's," they replied. "Pay therefore," He rejoined, "what is Caesar's to Caesar; and what is God's to God."
22 Atamva izi, anadabwa, ndipo anamusiya Iye, nachoka.
They heard this, and were astonished; then left Him, and went their way.
23 Tsiku lomwelo Asaduki amene amati kulibe za kuukanso, anabwera kwa Iye ndi funso.
On the same day a party of Sadducees came to Him, contending that there is no resurrection. And they put this case to Him.
24 Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatiwuza kuti munthu akamwalira wosasiya ana, mʼbale wake akuyenera kukwatira mkazi wamasiyeyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo.
"Teacher," they said, "Moses enjoined, 'If a man die childless, his brother shall marry his widow, and raise up a family for him.'
25 Tsopano panali abale asanu ndi awiri pakati pathu. Woyambayo anakwatira ndipo anamwalira, ndipo popeza analibe ana, mʼbale wake analowa chokolo.
Now we had among us seven brothers. The eldest of them married, but died childless, leaving his wife to his brother.
26 Izi zinachitikiranso mʼbale wa chiwiri ndi wachitatu mpaka wachisanu ndi chiwiri.
So also did the second and the third, down to the seventh,
27 Pa mapeto pake mkaziyo anamwaliranso.
till the woman also died, after surviving them all.
28 Tsopano, kodi akadzaukitsidwa adzakhala mkazi wa ndani mwa asanu ndi awiriwa popeza aliyense anamukwatirapo?”
At the Resurrection, therefore, whose wife of the seven will she be? for they all married her."
29 Yesu anayankha kuti, “Inu mukulakwitsa chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu ya Mulungu.
The reply of Jesus was, "You are in error, through ignorance of the Scriptures and of the power of God.
30 Anthu akadzaukitsidwa, sadzakwatira kapena kukwatiwa; adzakhala ngati angelo kumwamba.
For in the Resurrection, men neither marry nor are women given in marriage, but they are like angels in Heaven.
31 Koma za kuukitsidwa kwa akufa, kodi simunawerenge zimene Mulungu ananena kwa inu kuti,
But as to the Resurrection of the dead, have you never read what God says to you,
32 ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo?’ Iyeyo si Mulungu wa akufa koma wa amoyo.”
'I am the God of Abraham, the God of Isaac, and the God of Jacob'? He is not the God of dead, but of living men."
33 Magulu a anthu atamva zimenezi, anazizwa ndi chiphunzitso chake.
All the crowd heard this, and were filled with amazement at His teaching.
34 Pakumva kuti Yesu anawakhalitsa chete Asaduki, Afarisi anasonkhana pamodzi.
Now the Pharisees came up when they heard that He had silenced the Sadducees,
35 Mmodzi wa iwo, katswiri wa malamulo anamuyesa Iye ndi funso ndipo anati,
and one of them, an expounder of the Law, asked Him as a test question,
36 “Aphunzitsi, kodi lamulo lalikulu koposa mu malamulo ndi liti?”
"Teacher, which is the greatest Commandment in the Law?"
37 Yesu anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse.
"'Thou shalt love the Lord thy God,'" He answered, "'with thy whole heart, thy whole soul, thy whole mind.'
38 Ili ndi lamulo loyamba ndi loposa onse.
This is the greatest and foremost Commandment.
39 Ndipo lachiwiri ndi lofanana nalo: ‘Konda mnansi wako monga iwe mwini.’
And the second is similar to it: 'Thou shalt love thy fellow man as much as thyself.'
40 Malamulo onse ndi aneneri zakhazikika pa malamulo awiriwa.”
The whole of the Law and the Prophets is summed up in these two Commandments."
41 Afarisi atasonkhana pamodzi, Yesu anawafunsa kuti,
While the Pharisees were still assembled there, Jesus put a question to them.
42 “Kodi mukuganiza bwanji za Khristu? Ndi Mwana wa ndani?” Iwo anayankha kuti, “Mwana wa Davide.”
"What think you about the Christ," He said, "whose son is He?" "David's," they replied.
43 Iye anawawuza kuti, “Nanga zikutheka bwanji kuti Davide poyankhula mwa Mzimu Woyera amatchula Iye ‘Ambuye?’ Pakuti akuti,
"How then," He asked, "does David, taught by the Spirit, call Him Lord, when he says,
44 “Ambuye anati kwa Ambuye wanga: ‘Khala pa dzanja langa lamanja mpaka ndiyike adani ako pansi pa mapazi ako.’
"'The Lord said to my Lord, sit at My right hand until I have put thy foes beneath thy feet'?
45 Ngati tsono Davide amamutchula ‘Ambuye,’ zingatheke bwanji kukhala mwana wake?”
"If therefore David calls Him Lord, how can He be his son?"
46 Panalibe wina anatha kuyankha, ndipo kuchokera pamenepo, panalibe wina anayerekeza kumufunsa funso.
No one could say a word in reply, nor from that day did any one venture again to put a question to Him.