< Mateyu 20 >

1 “Ufumu wakumwamba uli ngati mwini munda amene anapita mmawa kukalemba anthu aganyu kuti akagwire ntchito mʼmunda wake wa mpesa.
「因為天國好像家主清早去雇人進他的葡萄園做工,
2 Anagwirizana kuwalipira dinari monga malipiro a tsiku limodzi ndipo anawatumiza mʼmunda wake wamphesa.
和工人講定一天一錢銀子,就打發他們進葡萄園去。
3 “Nthawi 9 koloko mmawa, anatulukanso naona ena atayimirira pa msika akungokhala.
約在巳初出去,看見市上還有閒站的人,
4 Anawawuza kuti, ‘Inunso pitani mukagwire ntchito mʼmunda wanga wa mpesa, ndipo ndidzakulipirani malipiro oyenera.’
就對他們說:『你們也進葡萄園去,所當給的,我必給你們。』他們也進去了。
5 Ndipo anapita. “Anatulukanso nthawi ya 12 koloko masana, ndi nthawi ya 3 koloko masananso nachita chimodzimodzi.
約在午正和申初又出去,也是這樣行。
6 Nthawi ya 5 koloko madzulo anatulukanso ndipo anapeza enanso atangoyimirira. Anawafunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mukungoyimirira pano tsiku lonse osagwira ntchito?’
約在酉初出去,看見還有人站在那裏,就問他們說:『你們為甚麼整天在這裏閒站呢?』
7 “Iwo anayankha kuti, ‘Chifukwa palibe munthu amene watilemba ganyu.’ “Iye anawawuza kuti, ‘Inunso pitani mukagwire ntchito mʼmunda wanga wa mpesa.’
他們說:『因為沒有人雇我們。』他說:『你們也進葡萄園去。』
8 “Ndipo pofika madzulo, mwini munda wamphesa anayitana kapitawo wake nati, ‘Itana antchito ndipo uwapatse malipiro awo, kuyambira omalizira aja mpaka oyamba.’
到了晚上,園主對管事的說:『叫工人都來,給他們工錢,從後來的起,到先來的為止。』
9 “Antchito amene anawalemba ganyu pa 5 koloko masana anafika ndipo aliyense analandira dinari.
約在酉初雇的人來了,各人得了一錢銀子。
10 Ndipo atabwera kwa amene analembedwa poyamba anayembekezera kuti alandira zambiri. Koma aliyense wa iwo analandira dinari.
及至那先雇的來了,他們以為必要多得;誰知也是各得一錢。
11 Atalandira, anayamba kuderera kwa mwini mundayo.
他們得了,就埋怨家主說:
12 Iwo anati, ‘Anthu amene munawalemba pomalizira agwira ntchito ora limodzi, ndipo mwawafananitsa ndi ife amene tathyoka nayo ntchito ndi kutentha kwa dzuwa tsiku lonse.’
『我們整天勞苦受熱,那後來的只做了一小時,你竟叫他們和我們一樣嗎?』
13 “Koma iye anamuyankha mmodzi wa iwo nati, ‘Bwenzi, ine sikuti sindinachite chilungamo. Kodi sunavomereze kuti ugwira ntchito ndi kulandira dinari?
家主回答其中的一人說:『朋友,我不虧負你,你與我講定的不是一錢銀子嗎?
14 Tenga malipiro ako pita. Ndikufuna kumupatsa munthu amene ndinamulemba pomaliza mofanana ndi mmene ndakupatsira iwe.
拿你的走吧!我給那後來的和給你一樣,這是我願意的。
15 Kodi ndilibe ufulu wochita zimene ndikufuna ndi ndalama zanga? Kapena ukuyipidwa chifukwa ndine wopereka mowolowamanja?’
我的東西難道不可隨我的意思用嗎?因為我作好人,你就紅了眼嗎?』
16 “Momwemo omalizira adzakhala oyamba ndipo oyamba adzakhala omalizira.”
這樣,那在後的,將要在前;在前的,將要在後了。 」
17 Tsopano pamene Yesu ankapita ku Yerusalemu, anatengera pambali ophunzira ake khumi ndi awiriwo nati kwa iwo,
耶穌上耶路撒冷去的時候,在路上把十二個門徒帶到一邊,對他們說:
18 “Tikupita ku Yerusalemu, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo. Iwo adzamuweruza kuti aphedwe,
「看哪,我們上耶路撒冷去,人子要被交給祭司長和文士。他們要定他死罪,
19 ndipo adzamupereka kwa anthu a mitundu ina kuti amunyoze ndi kumukwapula ndi kumupachika. Pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa!”
又交給外邦人,將他戲弄,鞭打,釘在十字架上;第三日他要復活。」
20 Amayi a ana a Zebedayo anabwera ndi ana ake kwa Yesu, nagwada pansi namupempha Iye.
那時,西庇太兒子的母親同她兩個兒子上前來拜耶穌,求他一件事。
21 Yesu anawafunsa kuti, “Mukufuna chiyani?” Amayiwo anati, “Lolani kuti ana anga awiriwa adzakhale mmodzi ku dzanja lanu lamanja ndi wina ku dzanja lanu lamazere mu ufumu wanu.”
耶穌說:「你要甚麼呢?」她說:「願你叫我這兩個兒子在你國裏,一個坐在你右邊,一個坐在你左邊。」
22 Yesu anawawuza kuti, “Simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungathe kumwera chikho chimene ndidzamwera Ine?” Iwo anayankha nati, “Inde tingathe.”
耶穌回答說:「你們不知道所求的是甚麼;我將要喝的杯,你們能喝嗎?」他們說:「我們能。」
23 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi mudzamwera chikho changa, koma kuti mudzakhale ku dzanja langa lamanja kapena lamazere si kwa Ine kupereka. Malo awa ndi a iwo amene anakonzeredweratu ndi Atate anga.”
耶穌說:「我所喝的杯,你們必要喝;只是坐在我的左右,不是我可以賜的,乃是我父為誰預備的,就賜給誰。」
24 Ophunzira khumi aja, anawapsera mtima abale awiriwo.
那十個門徒聽見,就惱怒他們弟兄二人。
25 Yesu anawayitana onse pamodzi nati, “Mukudziwa kuti olamulira a mitundu ina ali ndi mphamvu pa iwo, ndipo akuluakulu awo amawalamulira.
耶穌叫了他們來,說:「你們知道外邦人有君王為主治理他們,有大臣操權管束他們。
26 Siziyenera kutero ndi inu. Mʼmalo mwake, aliyense amene akufuna kukhala wamkulu pakati panu akhale wotumikira wanu.
只是在你們中間,不可這樣;你們中間誰願為大,就必作你們的用人;
27 Ndipo aliyense amene akufuna kukhala woyamba akhale kapolo wanu.
誰願為首,就必作你們的僕人。
28 Momwenso Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kukhala dipo la anthu ambiri.”
正如人子來,不是要受人的服事,乃是要服事人,並且要捨命,作多人的贖價。」
29 Pamene Yesu ndi ophunzira ake ankachoka ku Yeriko, gulu lalikulu la anthu linawatsata.
他們出耶利哥的時候,有極多的人跟隨他。
30 Amuna awiri osaona anakhala mʼmbali mwa msewu, ndipo pamene anamva kuti Yesu akudutsa anafuwula kuti, “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!”
有兩個瞎子坐在路旁,聽說是耶穌經過,就喊着說:「主啊,大衛的子孫,可憐我們吧!」
31 Gulu la anthulo linawadzudzula iwo ndi kuwawuza kuti akhale chete, koma anafuwulitsabe kuti, “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!”
眾人責備他們,不許他們作聲;他們卻越發喊着說:「主啊,大衛的子孫,可憐我們吧!」
32 Yesu anayima ndi kuwayitana ndipo anawafunsa kuti, “Mukufuna ndikuchitireni chiyani?”
耶穌就站住,叫他們來,說:「要我為你們做甚麼?」
33 Anamuyankha nati, “Ambuye, tikufuna tione!”
他們說:「主啊,要我們的眼睛能看見!」
34 Yesu anamva nawo chifundo ndipo anakhudza maso awo. Nthawi yomweyo anaona namutsata Iye.
耶穌就動了慈心,把他們的眼睛一摸,他們立刻看見,就跟從了耶穌。

< Mateyu 20 >