< Mateyu 17 >

1 Patapita masiku asanu ndi limodzi Yesu anatenga Petro, Yakobo, ndi Yohane mʼbale wa Yakobo pa okha ndipo anakwera nawo pa phiri lalitali.
Καὶ μεθ᾽ ἡμέρας ἓξ παραλαμβάνει ὁ Ἰησοῦς τὸν Πέτρον καὶ Ἰάκωβον καὶ Ἰωάννην τὸν ἀδελφὸν αὐτοῦ, καὶ ἀναφέρει αὐτοὺς εἰς ὄρος ὑψηλὸν κατ᾽ ἰδίαν.
2 Pamenepo Iye anasinthika maonekedwe ake pamaso pawo. Nkhope yake inawala ngati dzuwa ndipo zovala zake zinayera kuti mbuu.
Καὶ μετεμορφώθη ἔμπροσθεν αὐτῶν, καὶ ἔλαμψε τὸ πρόσωπον αὐτοῦ ὡς ὁ ἥλιος, τὰ δὲ ἱμάτια αὐτοῦ ἐγένοντο λευκὰ ὡς τὸ φῶς.
3 Nthawi yomweyo Mose ndi Eliya anaonekera kwa iwo akuyankhulana ndi Yesu.
Καὶ ἰδού, ὤφθησαν αὐτοῖς Μωσῆς καὶ Ἠλίας, μετ᾽ αὐτοῦ συλλαλοῦντες.
4 Petro anati kwa Yesu, “Ambuye ndi bwino kuti ife tikhale pano. Ngati mufuna ndidzamanga misasa itatu umodzi wanu, wina wa Mose ndi wina wa Eliya.”
Ἀποκριθεὶς δὲ ὁ Πέτρος εἶπε τῷ Ἰησοῦ, Κύριε, καλόν ἐστιν ἡμᾶς ὧδε εἶναι· εἰ θέλεις, ποιήσωμεν ὧδε τρεῖς σκηνάς, σοὶ μίαν, καὶ Μωσῇ μίαν, καὶ μίαν Ἠλίᾳ.
5 Iye akuyankhulabe, mtambo owala unawaphimba, ndipo mawu ochokera mu mtambo anati, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimukonda ndipo ndikondwera naye kwambiri. Mumumvere Iye!”
Ἔτι αὐτοῦ λαλοῦντος, ἰδού, νεφέλη φωτεινὴ ἐπεσκίασεν αὐτούς· καὶ ἰδού, φωνὴ ἐκ τῆς νεφέλης, λέγουσα, Οὗτός ἐστιν ὁ υἱός μου ὁ ἀγαπητός, ἐν ᾧ εὐδόκησα· αὐτοῦ ἀκούετε.
6 Ophunzira atamva zimenezi, anachita mantha nagwa pansi chafufumimba.
Καὶ ἀκούσαντες οἱ μαθηταὶ ἔπεσον ἐπὶ πρόσωπον αὐτῶν, καὶ ἐφοβήθησαν σφόδρα.
7 Ndipo Yesu anabwera nawakhudza nati, “Dzukani, musaope.”
Καὶ προσελθὼν ὁ Ἰησοῦς ἥψατο αὐτῶν καὶ εἶπεν, Ἐγέρθητε καὶ μὴ φοβεῖσθε.
8 Atayangʼana, sanaone wina aliyense kupatula Yesu yekha.
Ἐπάραντες δὲ τοὺς ὀφθαλμοὺς αὐτῶν, οὐδένα εἶδον, εἰ μὴ τὸν Ἰησοῦν μόνον.
9 Akutsika ku phiriko, Yesu anawalamula kuti, “Musawuze wina aliyense zimene mwaona, mpaka Mwana wa Munthu ataukitsidwa kwa akufa.”
Καὶ καταβαινόντων αὐτῶν ἐκ τοῦ ὄρους, ἐνετείλατο αὐτοῖς ὁ Ἰησοῦς, λέγων, Μηδενὶ εἴπητε τὸ ὅραμα, ἕως οὗ ὁ υἱὸς τοῦ ἀνθρώπου ἐκ νεκρῶν ἀναστῇ.
10 Ophunzira anamufunsa Iye kuti, “Nanga nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amati Eliya ayenera kukhala woyamba kubwera?”
Καὶ ἐπηρώτησαν αὐτὸν οἱ μαθηταὶ αὐτοῦ λέγοντες, Τί οὖν οἱ γραμματεῖς λέγουσιν ὅτι Ἠλίαν δεῖ ἐλθεῖν πρῶτον;
11 Yesu anayankha kuti, “Kunena zoona, Eliya adzayenera kubwera ndipo adzakonza zinthu zonse.
Ὁ δὲ Ἰησοῦς ἀποκριθεὶς εἶπεν αὐτοῖς, Ἠλίας μὲν ἔρχεται πρῶτον, καὶ ἀποκαταστήσει πάντα·
12 Koma Ine ndikuwuzani inu kuti Eliya anabwera kale koma iwo sanamuzindikire ndipo anachita naye chilichonse chimene anafuna. Momwemonso iwo adzazunza Mwana wa Munthu.”
λέγω δὲ ὑμῖν ὅτι Ἠλίας ἤδη ἦλθε, καὶ οὐκ ἐπέγνωσαν αὐτόν, ἀλλὰ ἐποίησαν ἐν αὐτῷ ὅσα ἠθέλησαν· οὕτω καὶ ὁ υἱὸς τοῦ ἀνθρώπου μέλλει πάσχειν ὑπ᾽ αὐτῶν.
13 Pamenepo ophunzira anazindikira kuti amawawuza za Yohane Mʼbatizi.
Τότε συνῆκαν οἱ μαθηταὶ ὅτι περὶ Ἰωάννου τοῦ βαπτιστοῦ εἶπεν αὐτοῖς.
14 Atafika ku gulu la anthu, munthu wina anamuyandikira Yesu ndi kugwada pamaso pake.
Καὶ ἐλθόντων αὐτῶν πρὸς τὸν ὄχλον, προσῆλθεν αὐτῷ ἄνθρωπος γονυπετῶν αὐτὸν
15 Iye anati, “Ambuye, muchitireni chifundo mwana wanga akudwala matenda akugwa ndipo akuvutika kwambiri. Kawirikawiri iye amagwa pa moto kapena mʼmadzi.
καὶ λέγων, Κύριε, ἐλέησόν μου τὸν υἱόν, ὅτι σεληνιάζεται καὶ κακῶς πάσχει· πολλάκις γὰρ πίπτει εἰς τὸ πῦρ, καὶ πολλάκις εἰς τὸ ὕδωρ.
16 Ine ndinabwera naye kwa ophunzira anu koma alephera kumuchiritsa.”
Καὶ προσήνεγκα αὐτὸν τοῖς μαθηταῖς σου, καὶ οὐκ ἠδυνήθησαν αὐτὸν θεραπεῦσαι.
17 Yesu anayankha nati, “Haa, mʼbado wosakhulupirira ndi wokhota maganizo! Kodi ndidzakhala nanu mpaka liti? Ndidzapirira nanu mpaka liti? Bwera nayeni kwa Ine mnyamatayo.”
Ἀποκριθεὶς δὲ ὁ Ἰησοῦς εἶπεν, Ὦ γενεὰ ἄπιστος καὶ διεστραμμένη, ἕως πότε ἔσομαι μεθ᾽ ὑμῶν; Ἕως πότε ἀνέξομαι ὑμῶν; Φέρετέ μοι αὐτὸν ὧδε.
18 Yesu anadzudzula chiwandacho ndipo chinatuluka mwa mnyamatayo ndipo anachira nthawi yomweyo.
Καὶ ἐπετίμησεν αὐτῷ ὁ Ἰησοῦς, καὶ ἐξῆλθεν ἀπ᾽ αὐτοῦ τὸ δαιμόνιον, καὶ ἐθεραπεύθη ὁ παῖς ἀπὸ τῆς ὥρας ἐκείνης.
19 Pamenepo ophunzira anabwera kwa Yesu mwamseri ndi kumufunsa kuti, “Chifukwa chiyani ife tinalephera kutulutsa chiwandacho?”
Τότε προσελθόντες οἱ μαθηταὶ τῷ Ἰησοῦ κατ᾽ ἰδίαν εἶπον, Διὰ τί ἡμεῖς οὐκ ἠδυνήθημεν ἐκβαλεῖν αὐτό;
20 Iye anayankha kuti, “Chifukwa inu muli ndi chikhulupiriro chachingʼono. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro monga kambewu ka mpiru, mukhoza kunena ndi phiri ili kuti, ‘Choka apa nupite apo,’ ndipo lidzachoka. Palibe kanthu kamene kadzakukanikani.
Ὁ δὲ Ἰησοῦς εἶπεν αὐτοῖς, Διὰ τὴν ἀπιστίαν ὑμῶν. Ἀμὴν γὰρ λέγω ὑμῖν, ἐὰν ἔχητε πίστιν ὡς κόκκον σινάπεως, ἐρεῖτε τῷ ὄρει τούτῳ, Μετάβηθι ἐντεῦθεν ἐκεῖ, καὶ μεταβήσεται· καὶ οὐδὲν ἀδυνατήσει ὑμῖν.
21 Chiwanda cha mtundu uwu sichingachoke chabe koma ndi pemphero ndi kusala kudya.”
Τοῦτο δὲ τὸ γένος οὐκ ἐκπορεύεται εἰ μὴ ἐν προσευχῇ καὶ νηστείᾳ.
22 Atasonkhana pamodzi ku Galileya, Iye anawawuza kuti, “Mwana wa Munthu akupita kukaperekedwa mʼmanja mwa anthu.
Ἀναστρεφομένων δὲ αὐτῶν ἐν τῇ Γαλιλαίᾳ, εἶπεν αὐτοῖς ὁ Ἰησοῦς, Μέλλει ὁ υἱὸς τοῦ ἀνθρώπου παραδίδοσθαι εἰς χεῖρας ἀνθρώπων,
23 Iwo adzamupha koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.” Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chisoni.
καὶ ἀποκτενοῦσιν αὐτόν, καὶ τῇ τρίτῃ ἡμέρᾳ ἐγερθήσεται. Καὶ ἐλυπήθησαν σφόδρα.
24 Yesu ndi ophunzira ake atafika ku Kaperenawo, wolandira msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu anabwera kwa Petro namufunsa kuti, “Kodi aphunzitsi anu sapereka msonkho wa Nyumba ya Mulungu?”
Ἐλθόντων δὲ αὐτῶν εἰς Καπερναούμ, προσῆλθον οἱ τὰ δίδραχμα λαμβάνοντες τῷ Πέτρῳ καὶ εἶπον, Ὁ διδάσκαλος ὑμῶν οὐ τελεῖ τὰ δίδραχμα;
25 Iye anayankha kuti, “Inde amapereka.” Petro atalowa mʼnyumba, Yesu ndiye anayamba kuyankhula. Ndipo anamufunsa kuti, “Ukuganiza bwanji Simoni, kodi mafumu a dziko lapansi amalandira msonkho kuchokera kwa ana awo kapena kwa ena?”
Λέγει, Ναί. Καὶ ὅτε εἰσῆλθεν εἰς τὴν οἰκίαν, προέφθασεν αὐτὸν ὁ Ἰησοῦς, λέγων, Τί σοι δοκεῖ, Σίμων; Οἱ βασιλεῖς τῆς γῆς ἀπὸ τίνων λαμβάνουσι τέλη ἢ κῆνσον; Ἀπὸ τῶν υἱῶν αὐτῶν, ἢ ἀπὸ τῶν ἀλλοτρίων;
26 Petro anayankha kuti, “Kuchokera kwa ena.” Yesu ananena kwa iye kuti, “Ndiye kuti ana sapereka.”
Λέγει αὐτῷ ὁ Πέτρος, Ἀπὸ τῶν ἀλλοτρίων. Ἔφη αὐτῷ ὁ Ἰησοῦς, Ἄρα γε ἐλεύθεροί εἰσιν οἱ υἱοί.
27 Koma kuti ife tisawakhumudwitse pita ku nyanja kaponye mbedza yako. Katenge nsomba imene ukayambe kuyikola; kayitsekule kukamwa ndipo ukapezamo ndalama. Katenge ndalamayo ndi kukapereka msonkho wanga ndi wanu.
Ἵνα δὲ μὴ σκανδαλίσωμεν αὐτούς, πορευθεὶς εἰς τὴν θάλασσαν βάλε ἄγκιστρον, καὶ τὸν ἀναβαίνοντα πρῶτον ἰχθὺν ἆρον· καὶ ἀνοίξας τὸ στόμα αὐτοῦ, εὑρήσεις στατῆρα· ἐκεῖνον λαβὼν δὸς αὐτοῖς ἀντὶ ἐμοῦ καὶ σοῦ.

< Mateyu 17 >