< Mateyu 16 >
1 Afarisi ndi Asaduki anabwera kwa Yesu ndi kumuyesa pomufunsa kuti awaonetse chizindikiro chochokera kumwamba.
2 Iye anayankha kuti, “Kunja kukamada, inu mumati, kudzakhala nyengo yabwino popeza thambo ndi lofiira.
3 Ndipo mmawa mumati, ‘Lero kudzakhala mvula yamphepo popeza thambo ndi lofiira ndi mitambo ya mvula.’ Inu mumadziwa kutanthauzira maonekedwe a thambo koma simungathe kutanthauzira zizindikiro za nthawi.
4 Mʼbado woyipa ndi wachigololo umafuna chizindikiro chodabwitsa koma palibe ngakhale chimodzi chidzapatsidwa kupatula chizindikiro cha Yona.” Pamenepo Yesu anawasiya nachoka.
5 Koma atawoloka nyanja, ophunzira anayiwala kutenga buledi.
6 Yesu anawawuza kuti, “Chenjerani, khalani tcheru ndi yisiti wa Afarisi ndi Asaduki.”
7 Iwo anakambirana pakati pawo za izi ndipo anati, “Ichi nʼchifukwa chakuti sitinatenge buledi aliyense.”
8 Yesu atadziwa zokambirana zawo, anawafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukukambirana zakuti, ‘mulibe buledi?’ Inu achikhulupiriro chochepa.
9 Kodi inu simukumvetsetsabe? Kodi simukukumbukira za buledi musanu amene anadya anthu 5,000 ndi madengu amene munadzaza?
10 Kapena buledi musanu ndi muwiri amene anadya anthu 4,000, nanga ndi madengu angati amene munadzaza?
11 Zitheka bwanji kuti inu simukumvetsetsa kuti Ine sindinkayankhula nanu za buledi? Koma inu chenjerani ndi yisiti wa Afarisi ndi Asaduki.”
12 Kenaka iwo anazindikira kuti Iye samawawuza kuti achenjere ndi yisiti wa buledi koma ndi chiphunzitso cha Afarisi ndi Asaduki.
13 Yesu atafika ku chigawo cha Kaisareya Filipo, Iye anafunsa ophunzira ake kuti, “Kodi anthu amati Mwana wa Munthu ndi ndani?”
14 Iwo anayankha kuti, “Ena amati ndi Yohane Mʼbatizi; ena amati ndi Eliya; komanso ena amati Yeremiya kapena mmodzi wa aneneri.”
15 Iye anafunsa kuti, “Nanga inuyo mumati ndine yani?”
16 Simoni Petro anayankha kuti, “Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.”
17 Yesu anati kwa iye, “Ndiwe wodala Simoni mwana wa Yona, popeza si munthu amene anakuwululira izi koma Atate anga akumwamba.
18 Ndipo Ine ndikuwuza iwe kuti ndiwe Petro ndipo pa thanthwe ili Ine ndidzamangapo mpingo wanga ndipo makomo a ku gehena sadzawugonjetsa. (Hadēs )
19 Ine ndidzakupatsa makiyi a Ufumu wakumwamba, ndipo chilichonse chimene iwe udzachimanga pansi pano chidzamangidwanso kumwamba.”
20 Pamenepo Iye anachenjeza ophunzira ake kuti asawuze wina aliyense kuti ndi Khristu.
21 Kuyambira nthawi imeneyo Yesu anayamba kuwafotokozera ophunzira ake kuti Iye ayenera kupita ku Yerusalemu ndi kukazunzidwa kwambiri mʼmanja mwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo kuti ayenera kuphedwa, ndi kuti tsiku lachitatu adzaukitsidwa.
22 Petro anamutengera Iye pambali nayamba kumudzudzula kuti, “Dzichitireni chifundo Ambuye, sizingachitike kwa Inu ayi.”
23 Yesu anatembenuka nati kwa Petro, “Choka pamaso panga Satana! Iwe ndi chokhumudwitsa kwa Ine; iwe suganizira zinthu za Mulungu koma zinthu za anthu.”
24 Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Ngati wina aliyense abwera pambuyo panga ayenera kudzikana ndi kutenga mtanda wake ndi kunditsata Ine.
25 Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupeza.
26 Kodi munthu adzapindula chiyani ngati atapeza zonse za dziko lapansi nataya moyo wake? Kapena munthu angapereke chiyani chosinthana ndi moyo wake?
27 Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate ake ndi angelo ake ndipo pamenepo Iye adzapereka mphotho kwa munthu mofanana ndi zimene anachita.
28 “Ine ndikuwuzani inu choonadi, ena amene akuyimirira pano sadzalawa imfa asanaone Mwana wa Munthu akudza mu ufumu.”