< Mateyu 15 >

1 Pamenepo Afarisi ena ndi aphunzitsi amalamulo anabwera kwa Yesu kuchokera ku Yerusalemu ndipo anamufunsa kuti,
Tunc accesserunt ad eum ab Ierosolymis Scribae, et Pharisaei, dicentes:
2 “Chifukwa chiyani ophunzira anu amaphwanya mwambo wa akuluakulu? Iwo sasamba mʼmanja pakudya!”
Quare discipuli tui transgrediuntur traditiones seniorum? non enim lavant manus suas cum panem manducant.
3 Yesu anayankha kuti, “Nanga chifukwa chiyani inu mumaphwanya lamulo la Mulungu chifukwa cha mwambo wa makolo anu?
Ipse autem respondens ait illis: Quare et vos transgredimini mandatum Dei propter traditionem vestram? Nam Deus dixit:
4 Pakuti Mulungu anati, ‘Lemekeza abambo ako ndi amayi ako’ ndipo ‘aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.’
Honora patrem, et matrem. et: Qui maledixerit patri, vel matri, morte moriatur.
5 Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, ‘Thandizo lililonse mukalirandira kuchokera kwa ine ndi mphatso yoperekedwa kwa Mulungu,’
Vos autem dicitis: Quicumque dixerit patri, vel matri, Munus, quodcumque est ex me, tibi proderit:
6 iye sakulemekeza nayo abambo ake ndipo ndi khalidwe lotere inu mumapeputsa nalo Mawu a Mulungu chifukwa cha mwambo wanu.
et non honorificabit patrem suum, aut matrem suam: et irritum fecistis mandatum Dei propter traditionem vestram.
7 Inu anthu achiphamaso, Yesaya ananenera za inu kuti,
Hypocritae, bene prophetavit de vobis Isaias, dicens:
8 “‘Anthu awa amandilemekeza Ine ndi milomo yawo, koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.
Populus hic labiis me honorat: cor autem eorum longe est a me.
9 Amandilambira Ine kwachabe ndi kuphunzitsa malamulo ndi malangizo a anthu.’”
Sine causa autem colunt me, docentes doctrinas, et mandata hominum.
10 Yesu anayitana gulu la anthu nati, “Mverani ndipo zindikirani.
Et convocatis ad se turbis, dixit eis: Audite, et intelligite.
11 Chimene chimalowa mʼkamwa mwa munthu sichimuchititsa kukhala woyipa, koma chimene chimatuluka mʼkamwa mwake, icho ndi chimene chimamuchititsa kukhala woyipa.”
Non quod intrat in os, coinquinat hominem: sed quod procedit ex ore, hoc coinquinat hominem.
12 Pamenepo ophunzira anabwera kwa Iye ndipo anamufunsa kuti, “Kodi mukudziwa kuti Afarisi anakhumudwa pamene anamva mawu aja?”
Tunc accedentes discipuli eius, dixerunt ei: Scis quia Pharisaei audito verbo hoc, scandalizati sunt?
13 Iye anayankha kuti, “Mbewu iliyonse imene Atate anga akumwamba sanadzale idzazulidwa ndi mizu yomwe.
At ille respondens ait: Omnis plantatio, quam non plantavit Pater meus caelestis, eradicabitur.
14 Alekeni, ndi atsogoleri osaona. Ngati munthu wosaona atsogolera wosaona mnzake, onse awiri adzagwera mʼdzenje.”
Sinite illos: caeci sunt, et duces caecorum. caecus autem si caeco ducatum praestet, ambo in foveam cadunt.
15 Petro anati, “Timasulireni fanizoli.”
Respondens autem Petrus dixit ei: Edissere nobis parabolam istam.
16 Yesu anawafunsa kuti, “Kani ngakhale inunso simumvetsa?
At ille dixit: Adhuc et vos sine intellectu estis?
17 Kodi inu simudziwa kuti chilichonse cholowa mʼkamwa chimapita mʼmimba ndipo kenaka chimatuluka kunja kwa thupi?
Non intelligitis quia omne, quod in os intrat, in ventrem vadit, et in secessum emittitur?
18 Koma zinthu zimene zituluka mʼkamwa zimachokera mu mtima ndipo zimenezi zimamuchititsa munthu kukhala woyipa.
Quae autem procedunt de ore, de corde exeunt, et ea coinquinant hominem:
19 Pakuti mu mtima mumatuluka maganizo oyipa, zakupha, zachigololo, zadama, zakuba, zaumboni wonama ndi zachipongwe.
de corde enim exeunt cogitationes malae, homicidia, adulteria, fornicationes, furta, falsa testimonia, blasphemiae.
20 Izi ndi zimene zimachititsa munthu kukhala woyipa; koma kudya ndi mʼmanja mosasamba sikumuchititsa munthu kukhala woyipa.”
haec sunt, quae coinquinant hominem. Non lotis autem manibus manducare, non coinquinat hominem.
21 Yesu atachoka kumalo amenewo anapita kudera la ku Turo ndi ku Sidoni.
Et egressus inde Iesus secessit in partes Tyri, et Sidonis.
22 Mayi wa Chikanaani wochokera dera la komweko anabwera kwa Iye akulira, nati, “Ambuye, Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo! Mwana wanga wamkazi akuzunzika kwambiri ndi chiwanda.”
Et ecce mulier Chananaea a finibus illis egressa clamavit, dicens ei: Miserere mei Domine fili David: filia mea male a daemonio vexatur.
23 Yesu sanayankhe kanthu. Ndipo ophunzira ake anabwera namupempha Iye kuti, “Muwuzeni achoke chifukwa akulira mofuwula pambuyo pathu.”
Qui non respondit ei verbum. Et accedentes discipuli eius rogabant eum dicentes: Dimitte eam: quia clamat post nos.
24 Iye anayankha kuti, “Ine ndinatumidwa kwa nkhosa zotayika za Israeli zokha.”
Ipse autem respondens ait: Non sum missus nisi ad oves, quae perierunt domus Israel.
25 Mayiyo anabwera ndi kugwada pamaso pake, nati, “Ambuye ndithandizeni!”
At illa venit, et adoravit eum, dicens: Domine, adiuva me.
26 Iye anayankha kuti, “Sibwino kutenga chakudya cha ana ndi kuponyera agalu.”
Qui respondens ait: Non est bonum sumere panem filiorum, et mittere canibus.
27 Mayiyo anati, “Inde Ambuye. Komatu ngakhale agalu amadya nyenyeswa zimene zimagwa kuchokera pa tebulo la mbuye wawo.”
At illa dixit: Etiam Domine: nam et catelli edunt de micis, quae cadunt de mensa dominorum suorum.
28 Pomwepo Yesu anayankha kuti, “Mayi iwe uli ndi chikhulupiriro chachikulu! Pempho lako lamveka.” Ndipo mwana wake wamkazi anachira nthawi yomweyo.
Tunc respondens Iesus, ait illi: O mulier, magna est fides tua: fiat tibi sicut vis. Et sanata est filia eius ex illa hora.
29 Yesu anachoka kumeneko napita mʼmbali mwa nyanja ya Galileya. Ndipo anakwera ku phiri nakhala pansi.
Et cum transisset inde Iesus, venit secus Mare Galilaeae: et ascendens in montem, sedebat ibi.
30 Gulu lalikulu la anthu linabwera kwa Iye ndi anthu olumala, osaona, ofa ziwalo, osayankhula ndi ena ambiri nawagoneka pa mapazi ake ndipo Iye anawachiritsa.
Et accesserunt ad eum turbae multae, habentes secum mutos, caecos, claudos, debiles, et alios multos: et proiecerunt eos ad pedes eius, et curavit eos:
31 Anthu ataona osayankhula akuyankhula, ofa ziwalo akuchira, olumala miyendo akuyenda ndi osaona akuona anadabwa kwambiri. Ndipo analemekeza Mulungu wa Israeli.
ita ut turbae mirarentur videntes mutos loquentes, claudos ambulantes, caecos videntes: et magnificabant Deum Israel.
32 Yesu anayitana ophunzira ake nati, “Ndili ndi chifundo ndi anthu awa; akhala kale ndi Ine masiku atatu ndipo alibe chakudya. Ine sindifuna kuti apite kwawo ndi njala chifukwa angakomoke pa njira.”
Iesus autem, convocatis discipulis suis, dixit: Misereor turbae, quia triduo iam perseverant mecum, et non habent quod manducent: et dimittere eos ieiunos nolo, ne deficiant in via.
33 Ophunzira anayankha kuti, “Ndikuti kumene tingakapeze buledi mʼtchire muno okwanira kudyetsa gulu lotere?”
Et dicunt ei discipuli: Unde ergo nobis in deserto panes tantos, ut saturemus turbam tantam?
34 Yesu anawafunsa kuti, “Muli ndi malofu a buledi angati?” Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri ndi tinsomba pangʼono.”
Et ait illis Iesus: Quot habetis panes? At illi dixerunt: Septem, et paucos pisciculos.
35 Iye anawuza gululo kuti likhale pansi.
Et praecepit turbae, ut discumberent super terram.
36 Kenaka anatenga malofu asanu ndi awiri aja ndi tinsombato ndipo atayamika anagawa napatsa ophunzira ake ndipo iwo anagawira anthuwo.
Et accipiens septem panes, et pisces, et gratias agens, fregit, et dedit discipulis suis, et discipuli dederunt populo.
37 Onse anadya ndipo anakhuta. Pomaliza ophunzira anatolera zotsalira nadzaza madengu asanu ndi awiri.
Et comederunt omnes, et saturati sunt. Et quod superfuit de fragmentis, tulerunt septem sportas plenas.
38 Chiwerengero cha anthu amene anadya chinali 4,000 kupatula amayi ndi ana.
Erant autem qui manducaverunt, quattuor millia hominum, extra parvulos, et mulieres.
39 Yesu atatha kuwuza gululo kuti lipite kwawo, analowa mʼbwato ndipo anapita kudera la Magadala.
Et, dimissa turba, ascendit in naviculam: et venit in fines Magedan.

< Mateyu 15 >