< Mateyu 13 >
1 Tsiku lomwelo Yesu anatuluka mʼnyumba ndipo anakhala mʼmbali mwa nyanja.
Téhož dne vyšel Ježíš z domu a usedl na břehu jezera.
2 Magulu a anthu anasonkhana mozungulira ndipo Iye analowa mʼbwato nakhala pansi ndipo anthu onse anayimirira ku mtunda.
Zanedlouho se kolem něho shromáždilo tolik lidí, že musel vstoupit do loďky, aby je mohl všechny oslovit.
3 Pamenepo Iye anawawuza zinthu zambiri mʼmafanizo ndi kuti, “Mlimi anapita kukafesa mbewu zake.
Rád vyjadřoval duchovní pravdy obrazně. Tentokrát začal vyprávět:
4 Akufesa, zina zinagwera mʼmbali mwa njira ndipo mbalame zinabwera ndi kuzidya.
„Rolník zaséval na poli obilí. Některá zrna padla na okraj cesty. Slétli se ptáci a sezobali je.
5 Zina zinagwa pamalo a miyala pamene panalibe dothi lambiri. Zinamera mofulumira chifukwa panalibe dothi lambiri.
Jiná zrna dopadla na skalnatou zem, kde bylo málo ornice. Obilí rychle vyhnalo do výšky,
6 Koma dzuwa litakwera, mbewu zinapserera ndipo zinawuma chifukwa zinalibe mizu.
ale když začalo pálit slunce, uschlo, protože kořínky nešly do hloubky.
7 Mbewu zina zinagwa pa minga ndipo mingayo inayanga ndi kuzirepheretsa kukula.
Další část zrna zapadla mezi bodláky. Když vyrostlo bodláčí, udusilo klásky.
8 Koma mbewu zina zinagwa pa nthaka yabwino ndipo zinabala zipatso 100, zina 60 ndipo zinanso makumi atatu mwa zimene zinafesedwa.
Ostatní zrna padla do dobré ornice. Vyrostlo obilí a přineslo úrodu. Některý klas měl sto zrnek, jiný šedesát a jiný třicet.
9 Amene ali ndi makutu amve.”
Víte, co tím myslím?“
10 Ophunzira anabwera kwa Iye ndikumufunsa kuti, “Chifukwa chiyani Inu mukuyankhula kwa anthu mʼmafanizo?”
Učedníci se ho zeptali: „Proč mluvíš v obrazech?“
11 Iye anayankha kuti, “Nzeru zakudziwa zinsinsi za ufumu wakumwamba zapatsidwa kwa inu koma osati kwa iwo.
Vysvětlil jim to: „Vám už Bůh odkrývá svoje záměry se světem. Ostatním je to zatím skryto.
12 Aliyense amene ali nazo adzapatsidwa zowonjezera ndipo iye adzakhala nazo zambiri. Aliyense amene alibe, ngakhale zimene ali nazo adzamulanda.
Kdo přijímá ochotně, bude mít stále víc. Kdo je spokojen s tím, co má, přijde nakonec o všechno.
13 Ichi ndi chifukwa chake ndimayankhula kwa iwo mʼmafanizo: “Ngakhale akupenya koma saona, ngakhale akumva koma samvetsetsa kapena kuzindikira.
Používám obrazy, lidé slyší i vidí, a přece nechápou.
14 Mwa iwo zimene ananenera Yesaya zikwaniritsidwa: “‘Kumva mudzamva koma osamvetsetsa. Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu.
Tak se na nich plní Izajášovo proroctví: ‚Budete poslouchat, ale neporozumíte, budete se dívat, ale neuvidíte.
15 Pakuti mtima wa anthu awa ndi wokanika, mʼmakutu mwawo ndi mogontha, ndipo atsinzina kuti asaone kanthu. Mwina angapenye ndi maso awo, angamve ndi makutu awo, angamvetse ndi nzeru zawo ndi kutembenuka, Ineyo nʼkuwachiritsa.’
Protože srdce tohoto lidu otupělo, jsou hluší a zavřeli oči, aby neviděli, neslyšeli a neporozuměli, aby se neobrátili k Bohu, kde by mohli být uzdraveni.‘
16 Koma maso anu ndi odala chifukwa amapenya ndi makutu anu chifukwa amamva.
Jak je dobře, že vaše oči vidí a uši slyší.
17 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti aneneri ambiri ndi anthu olungama anafuna kuona zimene inu mukupenya koma sanazione ndi kumva zimene inu mukumva koma sanazimve.
Mnoho proroků toužilo vidět to, co vy vidíte, a slyšet to, co vy slyšíte, ale nebylo jim to dopřáno.
18 “Tamverani tsono zimene fanizo la wofesa litanthauza:
A teď k tomu příběhu o rozsévači.
19 Pamene aliyense akumva uthenga wa ufumu koma sawuzindikira, woyipayo amabwera ndi kuchotsa zimene zafesedwa mu mtima mwake. Iyi ndi mbewu yofesedwa mʼmbali mwa njira.
Cesta, kam padla některá zrna, představuje srdce lidí, kteří slyší o Božím království a nezajímá je to. Přichází satan a sebere, co bylo zaseto.
20 Zimene zinafesedwa pa malo amiyala ndi munthu amene amamva mawu ndi kuwalandira msanga ndi chimwemwe.
Skalnatá země představuje srdce člověka, který slyší Boží poselství a přijímá je sice s velkou radostí, ale povrchně a ono v něm nezapustí kořeny. Když pak přijdou těžkosti nebo pronásledování pro víru, jeho nadšení ochabne a to, co bylo zaseto, zmizí.
21 Koma popeza alibe muzu, iwo amakhala nthawi yochepa. Pamene vuto kapena zunzo libwera chifukwa cha mawu, iye amagwa mofulumira.
22 Zimene zinafesedwa pakati pa minga, ndi munthu amene amamva mawu koma nkhawa za moyo uno ndi chinyengo cha chuma zimalepheretsa mawuwo kuti abale chipatso. (aiōn )
Země porostlá bodláčím představuje člověka, který slyší poselství, ale v jehož srdci záležitosti každodenního života a touha po lepším hmotném zajištění slovo udusí. (aiōn )
23 Koma zimene zinafesedwa pa nthaka yabwino, ndi munthu amene amamva mawu ndipo amawazindikira. Iye amabala zipatso zokwanira 100, zina 60 ndipo zinanso makumi atatu mwa zimene zinafesedwa.”
Dobrá ornice představuje srdce člověka, který slyší Boží poselství, rozumí mu a nechává působit jeho životodárný vliv. Užitek z toho je mnohonásobný, u někoho větší, u jiného menší.“
24 Yesu anawawuza fanizo lina kuti: “Ufumu wakumwamba ufanana ndi munthu amene anafesa mbewu zabwino mʼmunda mwake.
Potom použil dalšího přirovnání. „Bůh je jako dobrý hospodář, který zasel na své pole dobré semeno.
25 Koma aliyense akugona usiku mdani wake anabwera ndi kufesa namsongole pakati pa tirigu ndipo anachoka.
V noci, když lidé spali, hospodářův nepřítel rozhodil mezi pšenici semeno plevele.
26 Pamene tirigu anamera ndi kutulutsa ngala, namsongole anaonekanso.
Když vyrostlo obilí a s ním i plevel, přišli služebníci za hospodářem a řekli mu: ‚Vždyť jsi zasel dobré semeno, kde se tedy vzal plevel?‘
27 “Antchito ake anabwera kwa iye ndi kuti, ‘Bwana, kodi simunafese mbewu zabwino mʼmunda mwanu? Nanga namsongole wachokera kuti?’
28 “Iye anayankha kuti, ‘Ndi mdani amene anachita izi.’ “Antchito anamufunsa iye kuti, ‘Kodi mufuna kuti tipite tikamuzule?’
‚To udělal nepřítel!‘odpověděl. ‚My půjdeme a vyplejeme to pole, ‘nabídli se.
29 “Iye anakana nati, ‘Ayi. Chifukwa pamene mukuzula namsongoleyo mwina inu mungazulire pamodzi ndi tirigu.
Ten jim na to řekl: ‚Ne, to nedělejte. Spolu s plevelem byste mohli snadno vytrhnout i pšenici.
30 Zisiyeni zonse zikulire pamodzi mpaka nthawi yokolola. Pa nthawi imeneyo ndidzawuza okolola kuti: Poyamba sonkhanitsani namsongole ndi kumumanga mʼmitolo kuti atenthedwe, kenaka sonkhanitsani tirigu ndi kumuyika mʼnkhokwe yanga.’”
Necháme obojí vyrůst a při žních řeknu žencům, aby vybrali plevel a spálili ho a pšenici dali do mé stodoly.‘“
31 Iye anawawuza fanizo lina kuti, “Ufumu wakumwamba uli ngati mbewu ya mpiru, imene munthu anatenga ndi kudzala mʼmunda mwake.
Předložil jim jiný obraz: „S Božím dílem je to jako s hořčičným seménkem, které člověk zasel na poli.
32 Ngakhale mbewuyi ndi yayingʼono mwa mbewu zanu zonse za mʼmunda, imakula ndi kukhala mtengo kotero kuti mbalame zamlengalenga zimabwera ndi kupumula mʼnthambi zake.”
Je sice drobné, ale vyroste z něho tak mohutná bylina, že i ptáci na ní stavějí hnízda.“
33 Iye anawawuzanso fanizo lina nati: “Ufumu wakumwamba ufanana ndi yisiti amene mayi anatenga ndi kusakaniza mu ufa wambiri mpaka wonse unafufuma.”
Dále užil tohoto obrazu: „Boží vliv působí jako kvas. Malé množství prokvasí i velkou dávku těsta.“
34 Yesu anayankhula zinthu zonsezi kwa gulu la anthu mʼmafanizo ndipo Iye sananene kalikonse kwa iwo osagwiritsa ntchito fanizo.
V tomto kázání Ježíš používal výhradně podobenství.
35 Kotero zinakwaniritsidwa zimene zinayankhulidwa ndi mneneri kuti, “Ndidzatsekula pakamwa panga ndi mafanizo, ndidzawulula zinthu zobisika chiyambire kukhazikidwa kwa dziko lapansi.”
Tak se naplnilo staré proroctví: „Budu mluvit v obrazech a vypovím, co bylo skryto od stvoření světa.“
36 Kenaka Iye anasiya gulu la anthu ndi kukalowa mʼnyumba. Ophunzira ake anapita kwa Iye nati, “Timasulireni fanizo la namsongole mʼmunda.”
Ježíš pak opustil shromážděné posluchače a šel domů. Obklopili ho jeho učedníci a žádali, aby jim vyložil obraz plevele na poli.
37 Iye anayankha nati, “Munthu amene anafesa mbewu yabwino ndi Mwana wa Munthu.
„Dobře, “řekl, „já jsem ten hospodář, který seje dobré zrní.
38 Munda ndi dziko lapansi ndipo mbewu yabwino ndi ana a ufumu. Namsongole ndi ana a woyipayo.
Pole představuje svět a zrna, to jsou lidé, kteří patří Bohu. Plevel, to jsou lidé propadlí zlému.
39 Ndipo amene anafesa namsongole ndi Satana. Kukolola ndiko kutha kwa dzikoli ndipo otuta ndi angelo. (aiōn )
Nepřítel, který ho zasel, je ďábel. Žně představují konec světa a ženci jsou andělé. (aiōn )
40 “Monga momwe namsongole azulidwa ndi kutenthedwa ndi moto, momwemonso kudzakhala pakutha kwa dziko. (aiōn )
Tak jako v tomto příběhu je plevel oddělen a spálen, tak bude na konci světa. (aiōn )
41 Mwana wa Munthu adzatumiza angelo ake ndipo iwo adzachotsa mu ufumu wake chilichonse chochimwitsa ndi onse amene amachita zoyipa.
Pošlu své anděly a ti vyženou z Boží blízkosti všechny, kteří stáli v cestě Boží věci a páchali zlo.
42 Adzawaponya mʼngʼanjo yamoto kumene kudzakhala kulira ndi kukuta mano.
Jejich konec bude hrozný. Zbyde jim pláč a zoufalství.
43 Pamenepo olungama adzawala ngati dzuwa mu ufumu wa Atate awo. Amene ali ndi makutu amve.”
A tehdy ti, kteří plnili Boží vůli, budou v království nebeského Otce zářit jako slunce. Přemýšlejte o tom!
44 “Ufumu wakumwamba ufanana ndi chuma chobisika mʼmunda. Munthu atachipeza anachibisanso ndipo ndi chimwemwe anapita nakagulitsa zonse anali nazo, nakagula mundawo.
Nový život, k němuž vás Bůh volá, je jako poklad zakopaný v poli. Kdo ho najde, zatím o tom nemluví, ale má takovou radost, že prodá všechno, jen aby to pole získal.
45 “Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi wogulitsa malonda amene amafuna ngale zabwino.
Nebo: je jako drahocenná perla, kterou objeví obchodník s perlami. Vyprodá všechno, co má, a koupí ji.
46 Atapeza imodzi ya mtengowapatali, iye anapita nakagulitsa chilichonse anali nacho ndi kukayigula.”
47 “Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi khoka limene linaponyedwa mʼnyanja ndipo linakola mitundu yonse ya nsomba.
Boží království je jako síť spuštěná do moře, ve které uváznou nejrůznější tvorové.
48 Litadzaza, asodzi analikokera ku mtunda. Pomwepo anakhala pansi nasonkhanitsa nsomba zabwino mʼmadengu koma zoyipa anazitaya.
Když je síť plná, vytáhnou ji rybáři na břeh, do košů vyberou dobré ryby a ostatní vyhodí.
49 Umu ndi mmene kudzakhalira pakutha kwa dziko. Angelo adzabwera ndi kulekanitsa oyipa ndi olungama. (aiōn )
Tak to bude i na konci světa. Přijdou Boží andělé a oddělí zlé od bohabojných (aiōn )
50 Ndipo oyipa adzawaponya mʼngʼanjo ya moto kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”
a zlé hodí do ohně. Tam bude pláč a zoufalství.
51 Yesu anawafunsa kuti, “Kodi mwamvetsetsa zonsezi?” Iwo anayankha kuti, “Inde.”
Porozuměli jste všemu?“„Ano, “odpověděli.
52 Iye anawawuza kuti, “Chifukwa chake mphunzitsi aliyense wa malamulo amene walangizidwa za ufumu wakumwamba ali ngati mwini nyumba amene amatulutsa chuma chatsopano komanso chakale.”
Potom dodal: „Každý vykladač Písma, který pochopil, oč mi jde, je jako hospodář, který ze své zásobárny nabízí nové i staré.“
53 Yesu atatsiriza mafanizowa anachoka kumeneko.
Když Ježíš skončil svůj výklad v podobenstvích, vrátil se do svého domovského města. Učil v tamní synagoze. Všichni se divili: „Kde se v něm bere taková moudrost a moc?
54 Atafika ku mudzi kwawo anayamba kuphunzitsa mʼmasunagoge awo ndipo iwo anadabwa nati, “Munthu uyu anayitenga kuti nzeru iyi ndi mphamvu zodabwitsazi?
55 Kodi si mwana wa wopala matabwa? Kodi dzina la amayi ake si Mariya ndipo kodi abale ake si Yakobo, Yosefe, Simoni ndi Yudasi?
Vždyť to je tesařův syn, jeho matka je přece Marie, a Jakub, Josef, Šimon a Juda to jsou jeho bratři!
56 Kodi alongo ake onse sali ndi ife? Tsono ndi kuti kumene anazitenga zinthu izi?”
I jeho sestry žijí mezi námi. Odkud to ten člověk má?“
57 Ndipo iwo anakhumudwa chifukwa cha Iye. Koma Yesu anawawuza kuti, “Mneneri sapatsidwa ulemu ku mudzi kwawo ndi ku nyumba kwawo.”
Nemohli se s tím vyrovnat a pro jejich nedůvěru tam Ježíš nemohl vykonat mnoho zázraků. Vysvětlil to slovy: „Proroka si váží všude víc než v jeho rodném městě a v jeho domově!“
58 Ndipo Iye sanachite zodabwitsa zambiri kumeneko chifukwa cha kusowa kwa chikhulupiriro kwawo.