< Mateyu 12 >
1 Pa nthawi imeneyo Yesu anadutsa pakati pa minda ya tirigu pa tsiku la Sabata. Ophunzira ake anamva njala nayamba kuthyola ngala za tirigu nʼkumadya.
En ce temps-là, — un jour de sabbat, — Jésus passa par les blés. Ses disciples avaient faim; ils se mirent à cueillir des épis et à manger.
2 Afarisi ataona zimenezi anati kwa Iye, “Taonani! Ophunzira anu akuchita zosaloledwa pa tsiku la Sabata.”
Les Pharisiens les virent. «Voilà tes disciples, dirent-ils à Jésus, qui font ce qu'il n'est pas permis de faire un jour de sabbat.»
3 Iye anayankha kuti, “Kodi simunawerenge zimene anachita Davide pamene iye ndi anzake anamva njala?
Il leur répondit: «N'avez-vous pas lu ce que fit David lorsqu'il eut faim, et ce que firent ses compagnons?
4 Analowa mʼNyumba ya Mulungu, ndipo iye ndi anzakewo anadya buledi wopatulika amene sikunali kololedwa kwa iwo kudya koma ansembe okha.
— comment il entra dans la maison de Dieu et mangea les pains de proposition, qu'il n'était permis de manger ni à lui, ni à ses compagnons, mais aux prêtres seuls?
5 Kodi simunawerenge mʼmalamulo kuti pa Sabata ansembe mʼNyumba ya Mulungu amaphwanya lamulo la Sabata komabe sawayesa olakwa?
N'avez-vous pas aussi lu dans la Loi que, le jour du sabbat, les prêtres violent dans le Temple le repos sabbatique et cependant sont innocents?
6 Ine ndikuwuzani kuti wamkulu kuposa Nyumba ya Mulunguyo ali pano.
Or, je vous le dis, il y a ici quelque chose de plus grand que le Temple.
7 Ngati mukanadziwa zomwe mawu awa atanthauza, ‘Ine ndifuna chifundo osati nsembe,’ inu simukanatsutsa osalakwa.
Si vous saviez ce que signifie: «Je veux miséricorde et non sacrifice» vous n'auriez pas condamné des innocents:
8 Pakuti Mwana wa Munthu ndiye Mbuye wa Sabata.”
le Fils de l'homme est maître du sabbat.»
9 Atachoka kumeneko anakalowa mʼsunagoge mwawo.
Il partit de là et se rendit dans leur synagogue.
10 Ndipo mʼmenemo munali munthu wolumala dzanja. Pofuna chifukwa chokamunenezera, iwo anamufunsa Yesu kuti, “Kodi nʼkololedwa kuchiritsa munthu tsiku la Sabata?”
Il s'y trouvait un homme qui avait une main paralysée; pour avoir un prétexte à accusation, ils lui posèrent une question: «Est-il permis, dirent ils, de guérir les jours de sabbat?»
11 Iye anawawuza kuti, “Ngati wina wa inu ali ndi nkhosa nigwera mʼdzenje tsiku la Sabata, kodi simudzayigwira ndi kuyitulutsa kunja?
Il leur répondit: «Si l’un de vous n'a qu'une brebis et que, le jour du sabbat, cette brebis tombe dans une fosse, est-ce qu'il ne la prendra pas, est-ce qu'il ne la retirera pas?
12 Nanga munthu sali oposa nkhosa kwambiri! Chifukwa chake nʼkololedwa kuchita zabwino pa Sabata.”
De quel prix cependant n'est pas un être humain en comparaison d'une brebis? Donc, il est permis les jours de sabbat d'être bienfaisant.»
13 Pamenepo Yesu anati kwa munthuyo, “Wongola dzanja lako.” Iye analiwongola ndipo linakhala monga linalili kale.
Là-dessus, il dit à l'homme: «Étends ta main. Il l’étendit et elle redevint aussi saine que l’autre.
14 Koma Afarisi anatuluka kunja ndi kukonza njira yoti amuphere.
Quant aux Pharisiens, ils sortirent et allèrent se concerter entre eux sur les moyens de le perdre.
15 Podziwa zimenezi, Yesu anachoka kumalo amenewo. Ambiri anamutsata Iye ndipo anachiritsira odwala awo onse
Jésus l'apprit et partit de là. Beaucoup le suivirent; il les guérit tous
16 nawachenjeza kuti asamuwulule kuti yani.
et, par des menaces, il leur interdit de le faire connaître.
17 Uku kunali kukwaniritsa zimene zinayankhulidwa kudzera mwa mneneri Yesaya kuti,
(C'était pour que fût accompli ce qu'avait dit le prophète Ésaïe:
18 “Taonani mnyamata wanga amene ndinamusankha, Wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye. Pa Iye ndidzayika Mzimu wanga, ndipo Iye adzalalikira chiweruzo kwa akunja.
«Voici mon serviteur, celui que j'ai élu, Mon bien-aimé, celui en qui mon âme s'est complu; Je mettrai m on Esprit sur lui Et il annoncera le jugement aux nations;
19 Sadzalimbana, sadzafuwula, ngakhale mmodzi sadzamva mawu ake mʼmakwalala.
Il ne disputera pas; il ne criera pas; On n'entendra pas sa voix dans les places publiques;
20 Bango lophwanyika sadzalithyola, ndi nyale yofuka sadzayizimitsa, kufikira Iye adzatumiza chiweruziro chikagonjetse.
Il ne brisera pas le roseau froissé Et il n'éteindra pas la mèche encore fumante, Jusqu'à ce qu'il ait fait triompher sa cause
21 Ndipo akunja adzakhulupirira dzina lake.”
Et les nations espéreront en son nom.»)
22 Pomwepo anthu anabwera naye kwa Yesu munthu wogwidwa ndi chiwanda amene anali wosaona ndi wosamva ndipo Yesu anamuchiritsa kotero kuti atatha anayamba kumva ndi kuona.
On lui présenta alors un démoniaque aveugle et muet; il le guérit de sorte que le muet parlait et voyait.
23 Anthu onse anadabwa ndipo anati, “Kodi uyu ndi kukhala mwana wa Davide?”
Et la multitude était toute transportée et disait: «Celui-là n'est-il point le Fils de David?
24 Koma Afarisi atamva zimenezi, anati, “Uyu amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu mkulu wa ziwandazo.”
Les Pharisiens, l'entendant, dirent: «Celui-là ne chasse les démons que par le prince des démons, Beelzéboul.»
25 Yesu anadziwa maganizo awo ndipo anawawuza kuti, “Ufumu uliwonse ukagawanika mwa iwo udzawonongeka ndi mzinda uliwonse kapena banja likagawanika, mwa izo zokha sizidzayima.
Mais Jésus, connaissant leurs pensées, leur dit: «Tout Royaume divisé contre lui-même tombe en ruines; nulle ville, nulle maison divisée contre elle-même ne subsistera.
26 Ngati Satana atulutsa Satana, iye adzigawa yekha. Nanga ufumu wake ungayime bwanji?
Or, si Satan chasse Satan, il est divisé contre lui-même, comment alors son Royaume subsistera-t-il?
27 Ndipo ngati Ine nditulutsa ziwanda ndi Belezebule, anthu anu amatulutsa ziwandazo ndi chiyani? Potero tsono adzakhala oweruza anu.
Et si, moi, je chasse les démons par Beelzéboul, par qui vos fils les chassent-ils? C'est pourquoi ils seront eux-mêmes vos juges!
28 Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi Mzimu wa Mulungu, pamenepo ufumu wa Mulungu wafika pa inu.
Mais si c'est par l'Esprit de Dieu que je chasse les démons, le Royaume de Dieu est donc venu jusqu'à vous.»
29 “Kapenanso wina aliyense angathe bwanji kulowa mʼnyumba ya munthu wamphamvu ndi kunyamulamo zinthu zake, sipokhapo atayamba wamanga munthu wa mphamvuyo? Pamenepo iye akhoza kuba mʼnyumbamo.
«Comment quelqu'un peut-il entrer dans la maison du guerrier et lui ravir ce qu'il possède s'il n'a tout d'abord chargé de liens le guerrier. Ce n'est qu'alors qu'il pourra piller sa maison.»
30 “Iye amene sali ndi Ine atsutsana nane ndipo iye amene sasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amamwaza.
«Qui n'est point avec moi est contre moi, et qui n'amasse point, avec moi, disperse.
31 Ndipo potero Ine ndikuwuzani inu, tchimo lililonse ndi cha mwano chilichonse zidzakhululukidwa kwa anthu koma chamwano cha pa Mzimu Woyera, sichidzakhululukidwa.
C'est pourquoi je vous dis ceci: tout péché, tout blasphème sera pardonné aux hommes, mais le blasphème contre l'Esprit ne sera point pardonné.
32 Aliyense amene anena mawu otsutsana ndi Mwana wa Munthu adzakhululukidwa koma aliyense wonena motsutsana ndi Mzimu Woyera sadzakhululukidwa mu mʼbado uno kapena umene ukubwerawo. (aiōn )
Si quelqu'un prononce un mot contre le Fils de l'homme, il lui sera pardonné; mais si quelqu'un parle contre l'Esprit saint, il ne lui sera pardonné ni dans ce siècle, ni dans l'autre.». (aiōn )
33 “Mtengo wabwino umabala zipatso zabwino ndipo mtengo woyipa umabalanso zipatso zoyipa, pajatu mtengo umadziwika ndi zipatso zake.
«Dites l'arbre bon et son fruit bon, ou dites l'arbre mauvais et son fruit mauvais, car au fruit on connaît l'arbre.»
34 Ana anjoka inu, woyipa inu, mungathe bwanji kuyankhula kanthu kalikonse kabwino? Pakuti pakamwa pamayankhula zosefuka kuchokera mu mtima.
«Engeance de vipères! Comment, étant méchants, pourriez-vous dire de bonnes choses; c'est de l'abondance du coeur que la bouche parle.
35 Munthu wabwino amatulutsa zinthu zabwino zomwe zili mumtima mwake ndipo munthu woyipa amatulutsanso zinthu zoyipa zomwe zili mwa iye.
De son bon trésor l'homme bon tire de bonnes choses; de son mauvais trésor l'homme mauvais tire de mauvaises choses.»
36 Ine ndikukuwuzani kuti pa tsiku la chiweruziro munthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mawu aliwonse wopanda pake amene anayankhula.
Je vous le déclare, au jour du Jugement les hommes rendront compte de toute parole oiseuse qu'ils auront dite.
37 Pakuti ndi mawu anu mudzapezeka osalakwa ndiponso ndi mawu anu mudzapezeka olakwa.”
Par tes paroles, en effet, tu seras justifié et par tes paroles condamné.»
38 Pamenepo ena mwa Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo anati kwa Iye, “Aphunzitsi, tikufuna tione chizindikiro chodabwitsa kuchokera kwa Inu.”
«Alors quelques-uns des Scribes et des Pharisiens vinrent lui dire: «Maître, nous voulons voir un signe de toi.»
39 Iye anayankha kuti, “Mʼbado woyipa ndi wachigololo ufunsa za chizindikiro chodabwitsa! Koma ndi chimodzi chomwe sichidzapatsidwa kwa inu kupatula chizindikiro cha mneneri Yona.
Il répondit par ces paroles: «Mauvaise et adultère génération! elle demande un signe! et nul signe ne lui sera donné, sinon celui du prophète Jonas.
40 Pakuti monga Yona anali mʼmimba mwa nsomba yayikulu masiku atatu, usana ndi usiku, momwemonso Mwana wa Munthu adzakhala masiku atatu, usana ndi usiku, mʼkati mwa nthaka.
De même, en effet, que Jonas fut trois jours et trois nuits dans le ventre de la baleine, de même le Fils de l'homme sera trois jours et trois nuits dans le sein de la terre.»
41 Anthu a ku Ninive adzayimirira pachiweruzo ndi mʼbado uwu ndi kuwutsutsa pakuti iwo analapa Yona atalalikira ndipo tsopano wamkulu kuposa Yona ali pano.
Lors du jugement, les hommes de Ninive se lèveront avec cette génération et la condamneront, car, eux, ils se repentirent à la prédication de Jonas. Et voici, sous vos yeux, plus que Jonas!
42 Mfumu yayikazi yakummwera idzayimirira pa tsiku lachiweruzo ndi mʼbado uwu ndipo idzawutsutsa pakuti inachokera kumathero a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomoni, ndipo pano pali woposa Solomoni.
Lors du jugement, la reine du Midi se lèvera avec cette génération et la condamnera, car cette reine vint des extrémités de la terre pour écouter la sagesse de Salomon. Et voici, sous vos yeux, plus que Salomon!»
43 “Pamene mzimu woyipa utuluka mwa munthu, umadutsa malo wopanda madzi kufunafuna malo opumulira ndipo suwapeza.
Lorsque l'Esprit impur est sorti d'un homme, il erre par des lieux arides, cherchant du repos, et il n'en trouve pas.
44 Pamenepo umati, ‘Ndidzabwerera ku nyumba yanga komwe ndinatuluka.’ Pamene ufika, upeza mopanda kanthu, mosesedwa ndi mokonzedwa bwino.
Il dit alors: «Je retournerai dans ma maison, d'où je suis parti»; il y revient et la trouve vide, nettoyée et parée.
45 Kenaka umapita kukatenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoyipa kwambiri kuposa uwowo ndipo imapita ndi kukakhala mʼmenemo. Choncho khalidwe lotsiriza la munthu uyu limakhala loyipa kwambiri kuposa loyambalo. Umo ndi mmene zidzakhalire ndi mʼbado oyipawu.”
Là-dessus, il va s'associer sept autres Esprits plus méchants que lui-même; ils y pénètrent et y demeurent; et le dernier état de cet homme devient pire que le premier. Ainsi en sera-t-il de cette génération mauvaise!»
46 Pamene Yesu anali kuyankhulabe ndi gulu la anthu, amayi ndi abale ake anayimirira kunja, akufuna kuyankhulana naye.
Comme il parlait encore à la foule, sa mère et ses frères, qui se tenaient dehors, demandèrent à l'entretenir.
47 Wina anamuwuza Iye kuti, “Amayi ndi abale anu ayima kunjaku akufuna kuyankhulana nanu.”
(Quelqu'un lui dit: voilà ta mère et tes frères, qui se tiennent dehors et demandent à te parler.)
48 Iye anayankha kuti, “Amayi anga ndani ndipo abale anga ndi ndani?”
Il répondit à celui qui le lui disait: «Qui est ma mère et qui sont mes frères?»
49 Ndipo akuloza ophunzira ake, Iye anati, “Awa ndiwo amayi anga ndi abale anga.
Puis, étendant la main sur ses disciples, il ajouta:
50 Pakuti aliyense amene achita chifuniro cha Atate anga akumwamba ndiye mʼbale wanga, mlongo wanga ndi amayi anga.”
«Voici ma mère et mes frères! Car faire la volonté de mon Père, qui est dans les cieux, c'est être mon frère, c'est être ma soeur, c'est être ma mère!»