< Marko 9 >
1 Ndipo anawawuza kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti ena amene ayimirira pano sadzafa asanaone ufumu wa Mulungu ukubwera mwa mphamvu.”
He said to them, "Truly I tell you, there are some standing here who will in no way taste death until they see the Kingdom of God come with power."
2 Patatha masiku asanu ndi limodzi Yesu anatenga Petro, Yakobo ndi Yohane nawatsogolera kupita ku phiri lalitali, kumene anali okhaokha. Kumeneko maonekedwe ake anasinthika pamaso pawo.
After six days Jesus took with him Peter, James, and John, and brought them up onto a high mountain privately by themselves, and he was changed into another form in front of them.
3 Zovala zake zinawala monyezimira kwambiri, kotero kuti palibe sopo wina aliyense amene angaziyeretse monyezimira chotere pa dziko la pansi.
His clothing became glistening, exceedingly white, such as no launderer on earth can whiten them.
4 Ndipo anaonekera Eliya ndi Mose pamaso pawo, amene ankayankhulana ndi Yesu.
Elijah and Moses appeared to them, and they were talking with Jesus.
5 Petro anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, ndi kwabwino kuti ife tili pano. Tiyeni timange misasa itatu; umodzi wanu, wina wa Mose ndi wina wa Eliya.”
Peter said to Jesus, "Rabbi, it is good for us to be here. Let us make three tents: one for you, one for Moses, and one for Elijah."
6 (Iye sanadziwe choti anene, anali ndi mantha akulu).
For he did not know what to answer, for they became very afraid.
7 Pamenepo mtambo unaoneka ndi kuwaphimba, ndipo mawu anamveka kuchokera mu mtambo kuti, “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa. Mvereni Iye!”
A cloud came, overshadowing them, and a voice came out of the cloud, "This is my beloved Son. Listen to him."
8 Mwadzidzidzi, atayangʼanayangʼana, sanaonenso wina aliyense ali ndi iwo kupatula Yesu.
Suddenly looking around, they saw no one with them anymore, except Jesus alone.
9 Pamene ankatsika kuchokera ku phiri, Yesu anawalamulira kuti asawuze aliyense zimene anaona mpaka Mwana wa Munthu atauka kwa akufa.
As they were coming down from the mountain, he commanded them that they should tell no one what things they had seen, until after the Son of Man had risen from the dead.
10 Iwo anayisunga nkhaniyo nakambirana za tanthauzo lake la “Kuuka kwa akufa.”
They kept this saying to themselves, questioning what the "rising from the dead" meant.
11 Ndipo anamufunsa Iye kuti, “Nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amati Eliya ayenera kuyamba wabwera?”
They asked him, saying, "Why do the scribes say that Elijah must come first?"
12 Yesu anayankha kuti, “Kunena motsimikiza, Eliya ayeneradi kuyamba kubwera kudzakonzanso zinthu zonse. Nʼchifukwa chiyani tsono zinalembedwa, kuti Mwana wa Munthu ayenera kuvutika kwambiri ndi kukanidwa?
And he said to them, "Elijah indeed comes first, and restores all things. And why is it written of the Son of Man that he should suffer many things and be rejected?
13 Koma ndikuwuzani, kuti Eliya wabweradi, ndipo amuchitira iye zonse zimene iwo anafuna, monga momwe zalembedwera za iye.”
But I tell you that Elijah has come, and they have also done to him whatever they wanted to, even as it is written about him."
14 Atafika kwa ophunzira ena aja, anaona gulu lalikulu la anthu litawazungulira ndi aphunzitsi amalamulo akutsutsana nawo.
And when they came to the disciples, they saw a large crowd around them, and scribes questioning them.
15 Nthawi yomweyo anthu onse atamuona, anadabwa kwambiri ndipo anathamanga kukamulonjera.
Immediately all the crowd, when they saw him, were greatly amazed, and running to him greeted him.
16 Iye anafunsa kuti, “Mukukangana nawo chiyani iwowa?”
He asked them, "What are you arguing about with them?"
17 Munthu wina mʼgululo anayankha kuti, “Aphunzitsi, ndinakubweretserani mwana wanga wamwamuna, amene ndi ogwidwa ndi mzimu umene umamulepheretsa kuyankhula.
And one out of the crowd answered him, "Teacher, I brought to you my son, who has a mute spirit;
18 Nthawi iliyonse ukamugwira umamugwetsa pansi. Amatuluka thovu kukamwa, amakukuta mano ake ndipo amawuma. Ndinapempha ophunzira anu kuti awutulutse mzimuwo, koma sanathe.”
and wherever it seizes him, it throws him down, and he foams at the mouth, and grinds his teeth, and wastes away. I asked your disciples to cast it out, and they weren't able."
19 Yesu anayankha kuti, “Haa! Mʼbado osakhulupirira, kodi ndidzakhala nanu mpaka liti? Mubweretseni kwa Ine mnyamatayo.”
And answering, he said to them, "You unbelieving generation, how long must I be with you? How long must I put up with you? Bring him to me."
20 Ndipo anamubweretsa kwa Iye. Mzimu woyipawo utaona Yesu, nthawi yomweyo unamukomola mnyamatayo. Anagwa pansi ndi kumagubuduka, ndi kuchita thovu kukamwa.
They brought him to him, and when he saw him, immediately the spirit convulsed him, and he fell on the ground, wallowing and foaming at the mouth.
21 Yesu anafunsa abambo a mnyamatayo kuti, “Kodi wakhala chotere nthawi yayitali bwanji?” Iye anayankha kuti, “Kuyambira ali wamngʼono,
He asked his father, "How long has it been since this has come to him?" He said, "From childhood.
22 wakhala ukumuponya pa moto kapena mʼmadzi kuti umuphe. Koma ngati mungathe kuchita kanthu, tichitireni chifundo ndipo mutithandize.”
And it has often cast him both into fire and into water, to destroy him. But if you can do anything, have compassion on us, and help us."
23 Yesu anati, “‘Ngati mungathe!’ Zinthu zonse ndi zotheka kwa iye amene akhulupirira.”
Jesus said to him, "'If you can?' All things are possible to him who believes."
24 Nthawi yomweyo abambo a mwanayo anafuwula kuti, “Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga!”
Immediately the father of the child cried out and said, "I believe. Help my unbelief."
25 Yesu ataona kuti gulu la anthu likuthamangira kumalowo, anadzudzula mzimu woyipawo kuti, “Iwe mzimu wolepheretsa kuyankhula ndi kumva, ndikulamulira tuluka mwa iye ndipo usadzalowenso.”
When Jesus saw that a crowd came running together, he rebuked the unclean spirit, saying to him, "You deaf and mute spirit, I command you, come out of him, and never enter him again."
26 Mzimuwo unafuwula ndi kumugubuduza kwambiri ndipo unatuluka. Mnyamatayo anaoneka ngati mtembo ndipo ambiri anati, “Wafa.”
Having screamed, and convulsed greatly, it came out of him. The boy became like one dead; so much that most of them said, "He is dead."
27 Koma Yesu anamugwira dzanja ndipo anamuyimiritsa, ndipo anayimirira.
But Jesus took him by the hand, and raised him up; and he arose.
28 Yesu atalowa mʼnyumba, ophunzira ake anamufunsa ali pa okha kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani ife sitinathe kutulutsa chiwandacho?”
And when he had come into the house, his disciples asked him privately, "Why could we not cast it out?"
29 Iye anayankha kuti, “Mtundu uwu umatuluka pokhapokha mwapemphera ndi kusala kudya.”
And he said to them, "This kind cannot come out by anything but prayer and fasting."
30 Anachoka malo amenewo nadutsa ku Galileya. Yesu sanafune kuti wina aliyense adziwe kumene anali,
They went out from there, and passed through Galilee. He did not want anyone to know it.
31 chifukwa amaphunzitsa ophunzira ake. Anati kwa iwo, “Mwana wa Munthu adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu. Adzamupha, ndipo patatha masiku atatu adzauka.”
For he was teaching his disciples, and said to them, "The Son of Man is being handed over to the hands of men, and they will kill him; and when he is killed, after three days he will rise again."
32 Koma sanazindikire chimene amatanthauza, ndipo anachita mantha kuti amufunse.
But they did not understand the saying, and were afraid to ask him.
33 Anafika ku Kaperenawo. Pamene anali mʼnyumba, anawafunsa kuti, “Kodi mumatsutsana chiyani mʼnjira muja?”
He came to Capernaum, and when he was in the house he asked them, "What were you arguing on the way?"
34 Koma anakhala chete chifukwa ali mʼnjira amatsutsana za kuti wamkulu kuposa onse ndani.
But they were silent, for they had disputed one with another on the way about who was the greatest.
35 Atakhala pansi, Yesu anayitana khumi ndi awiriwo nati, “Ngati wina aliyense afuna kukhala woyamba, ayenera kukhala wotsiriza ndi wotumikira onse.”
And he sat down, and called the twelve; and he said to them, "If anyone wants to be first, he must be last of all, and servant of all."
36 Anatenga kamwana nakayimiritsa pakati pawo ndipo anawawuza kuti,
He took a little child, and set him in the midst of them. Taking him in his arms, he said to them,
37 “Aliyense wolandira mmodzi wa ana angʼono awa mʼdzina langa alandira Ine; ndipo aliyense wolandira Ine salandira Ine koma amene anandituma.”
"Whoever receives one such little child in my name, receives me, and whoever receives me, does not receive me, but him who sent me."
38 Yohane anati, “Aphunzitsi, tinaona munthu akutulutsa ziwanda mʼdzina lanu ndipo ife tinamuwuza kuti aleke, chifukwa sanali mmodzi wa ife.”
John said to him, "Teacher, we saw someone casting out demons in your name; and we forbade him, because he was not following us."
39 Yesu anati, “Musamuletse, palibe amene amachita chodabwitsa mʼdzina langa ndipo kenaka nanena zoyipa za Ine,
But Jesus said, "Do not forbid him, for there is no one who will do a mighty work in my name, and be able quickly to speak evil of me.
40 pakuti aliyense amene satsutsana nafe ali mbali yathu.
For whoever is not against us is for us.
41 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti aliyense amene akupatsani chikho cha madzi mʼdzina langa chifukwa ndinu ake a Khristu, sadzataya konse mphotho yake.”
For whoever will give you a cup of water to drink in my name, because you belong to the Christ, truly I tell you, he will in no way lose his reward.
42 “Ndipo ngati wina aliyense achimwitsa mmodzi wa ana angʼono awa amene akhulupirira Ine, kukanakhala bwino kwa iye kuti aponyedwe mʼnyanja atamangiriridwa mwala waukulu mʼkhosi mwake.
Whoever will cause one of these little ones who believe in me to stumble, it would be better for him if he was thrown into the sea with a millstone hung around his neck.
43 Ngati dzanja lako likuchimwitsa, lidule. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa mʼmoyo ndi dzanja limodzi kusiyana ndi kukhala ndi manja awiri ndi kupita ku gehena, kumene moto wake suzima. (Geenna )
If your hand causes you to stumble, cut it off. It is better for you to enter into life maimed, rather than having your two hands to go into hell, into the unquenchable fire, (Geenna )
44 (Kumene mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima).
45 Ndipo ngati phazi lako likuchimwitsa, lidule. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa mʼmoyo olumala kusiyana ndi kukhala ndi mapazi awiri ndi kuponyedwa mu gehena. (Geenna )
If your foot causes you to stumble, cut it off. It is better for you to enter into life lame, rather than having your two feet to be cast into hell. (Geenna )
46 (Kumene mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima).
47 Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi, kusiyana ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa mu gehena, (Geenna )
If your eye causes you to stumble, cast it out. It is better for you to enter into the Kingdom of God with one eye, rather than having two eyes to be cast into hell, (Geenna )
48 kumene “‘mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima.’
'where their worm does not die, and the fire is not quenched.'
49 Aliyense adzayesedwa ndi moto.
For everyone will be salted with fire, and every sacrifice will be salted with salt.
50 “Mchere ndi wabwino, koma ngati utasukuluka, mungawukoleretsenso bwanji? Mukhale nawo mchere mwa inu nokha, ndipo mukhale pa mtendere wina ndi mnzake.”
Salt is good, but if the salt has lost its saltiness, how can you make it salty? Have salt in yourselves, and be at peace with one another."