< Marko 5 >
1 Ndipo anawoloka nyanja napita ku dera la Gerasa.
2 Yesu atatuluka mʼbwato, munthu amene anali ndi mzimu woyipa anachoka ku manda ndi kukumana naye.
3 Munthuyu amakhala ku manda, ndipo panalibe amene akanatha kumumanganso ngakhale ndi unyolo.
4 Pakuti nthawi zambiri akamumanga manja ndi miyendo amadula maunyolo ndi kudula zitsulo zimene zinali mʼmapazi ake. Panalibe amene anali ndi mphamvu yoti ndi kumugonjetsa.
5 Usana ndi usiku ankakhala ku manda ndi kumapiri, akulira ndi kudzicheka ndi miyala.
6 Ataona Yesu ali patali, anathamanga nagwa pa mawondo ake pamaso pake.
7 Iye anafuwula kwambiri nati, “Mukufuna muchite nane chiyani, Yesu Mwana wa Mulungu Wammwambamwamba? Lumbirani kwa Mulungu kuti simundizunza!”
8 Pakuti Yesu anati kwa iye, “Tuluka mwa munthuyu, iwe mzimu woyipa!”
9 Ndipo Yesu anamufunsa iye, “Dzina lako ndani?” Iye anayankha kuti, “Dzina langa ndine Legiyo, pakuti tilipo ambiri.”
10 Ndipo anamupempha Yesu mobwerezabwereza kuti asazitulutse mʼderalo.
11 Gulu lalikulu la nkhumba limadya mʼmbali mwa phiri limene linali pafupi.
12 Ziwandazo zinapempha Yesu kuti, “Titumizeni pakati pa nkhumbazo; ndipo mutilole tilowe mwa izo.”
13 Iye anazipatsa chilolezo, ndipo mizimu yoyipayo inatuluka ndi kukalowa mu nkhumbazo. Gulu la nkhumba, zokwana pafupifupi 2,000 zinathamanga kutsetserekera ku nyanja ndipo zinamira.
14 Omwe amaweta nkhumbazo anathawa ndi kukawuza anthu za izi mu mzinda ndi ku madera a ku midzi, ndipo anthu anapita kukaona zomwe zinachitika.
15 Atafika kwa Yesu, anaona munthu amene anagwidwa ndi ziwanda zambiri uja atakhala pansi pomwepo, atavala, ndipo ali bwinobwino. Iwo anachita mantha.
16 Amene anaona zimenezi anawuza anthu zomwe zinachitika kwa munthu wogwidwa ndi ziwandayo ndipo anawawuzanso za nkhumbazo.
17 Ndipo anthu anayamba kumupempha Yesu kuti achoke mʼdera lawo.
18 Yesu akulowa mʼbwato, munthu amene anagwidwa ndi ziwanda uja anamupempha kuti apite nawo.
19 Yesu sanamulole, koma anati, “Pita kwanu ku banja lako ndipo ukawawuze zimene Ambuye wakuchitira, ndi chifundo chimene wakuchitira.”
20 Pomwepo munthuyo anapita nayamba kuwuza anthu a ku Dekapoli zinthu zimene Yesu anamuchitira. Ndipo anthu onse anadabwa.
21 Yesu atawolokeranso pa bwato kupita mbali ina ya nyanja, gulu lalikulu la anthu linasonkhana momuzungulira. Ali mʼmbali mwa nyanja,
22 mmodzi wa akulu a mʼsunagoge, dzina lake Yairo anafika pamenepo. Ataona Yesu, anagwa pa mapazi ake,
23 ndi kumudandaulira kwambiri nati, “Mwana wanga wamkazi wamngʼono ali pafupi kufa. Chonde tiyeni kuti mukamusanjike manja kuti akachiritsidwe nakhala ndi moyo.”
24 Ndipo Yesu anapita naye. Gulu lalikulu la anthu linamutsata ndi kumamupanikiza Iye.
25 Pomwepo panali mayi amene amadwala nthenda yotaya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri.
26 Iye anavutika kwambiri pamene asingʼanga ambiri ankamusamalira ndipo anagwiritsa ntchito zonse anali nazo, koma mʼmalo mochira, nthenda yake inkakulakulabe.
27 Atamva za Yesu, anabwera kumbuyo kwake mʼgulu la anthu ndipo anakhudza mkanjo wake,
28 chifukwa anaganiza kuti, “Ngati nditangokhudza mkanjo wake, ndidzachiritsidwa.”
29 Nthawi yomweyo magazi ake analeka kutuluka ndipo anamva mʼthupi mwake kuti wamasulidwa ku vuto lake.
30 Pomwepo Yesu anazindikira kuti mphamvu inachoka mʼthupi mwake. Anatembenuka mʼgulu la anthu ndipo anafunsa kuti, “Ndani wakhudza zovala zanga?”
31 Ophunzira ake anayankha kuti, “Mukuona kuti anthu akukupanikizani, ndipo Inu mukufunsa kuti, ‘Ndani wandikhudza?’”
32 Koma Yesu anapitirizabe kuyangʼana kuti aone amene anachita zimenezi.
33 Kenaka mayi uja pozindikira chimene chinamuchitikira, anabwera ndi kugwa pa mapazi ake, ndipo akunjenjemera ndi mantha, anamuwuza zoona zokhazokha.
34 Anati kwa iye, “Mwana wamkazi, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere ndipo khala womasulidwa ku mavuto ako.”
35 Pamene Yesu ankayankhulabe, amuna ena anafika kuchokera ku nyumba ya Yairo, mkulu wa sunagoge. Iwo anati, “Mwana wanu wamkazi wamwalira, muvutitsiranjinso aphunzitsiwa?”
36 Posasamala zomwe ananena, Yesu anamuwuza mkulu wa sunagoge uja kuti, “Usachite mantha; ingokhulupirira.”
37 Iye sanalole munthu wina aliyense kuti amutsatire koma Petro, Yakobo ndi Yohane mʼbale wa Yakobo.
38 Atafika ku nyumba ya mkulu wa sunagoge, Yesu anaona chipiringu cha anthu akulira ndi kufuwula kwambiri.
39 Analowa nati kwa iwo, “Mukuchita phokoso ndi kulira chifukwa chiyani? Mwanayu sanamwalire koma ali mtulo.”
40 Koma anamuseka Iye. Atawatulutsa onse panja, Iye anatenga abambo ndi amayi ake a mwanayo ndi ophunzira omwe anali naye, ndipo analowa mʼmene munali mwanayo.
41 Anagwira dzanja lake nanena kwa iye, “Talita Kumi!” (Kutanthauza kuti, “Mtsikana, ndikunena ndi iwe, imirira!”)
42 Nthawi yomweyo anayimirira nayenda mozungulira (anali wa zaka khumi ndi ziwiri). Pa ichi onse anadabwa kwambiri.
43 Anawalamulira kwambiri kuti asawuze wina aliyense za ichi, ndipo anawawuza kuti amupatse kanthu koti adye.