< Marko 2 >
1 Patapita masiku pangʼono, Yesu atalowanso mu Kaperenawo, zinamveka kuti wabwera ali mʼnyumba.
After many days, he returned to Capernaum; and when it was known that he was in the house,
2 Choncho anthu ambiri anasonkhana kotero kuti panalibenso malo, ngakhale ndi pa khomo pomwe, ndipo Iye anawalalikira mawu.
such a multitude flocked thither, that there was no room for them, not even near the door, and he taught them the word.
3 Amuna anayi anabwera, atanyamula munthu wofa ziwalo.
A paralytic was then brought, carried by four men,
4 Popeza sakanatha kufika naye kwa Yesu chifukwa cha gulu la anthu, anasasula denga chapamwamba pamene panali Yesu, ndipo atabowoleza, anatsitsa mphasa yomwe munthu wofa ziwaloyo anagonapo.
who, not being able to come nigh him for the crowd, uncovered the place where Jesus was; and, through the opening, let down the conch, on which the paralytic lay.
5 Yesu ataona chikhulupiriro chawo, anati kwa wofa ziwaloyo, “Mwana, machimo ako akhululukidwa.”
Jesus perceiving their faith, said to the paralytic, Son, your sins are forgiven you.
6 Ndipo ena mwa aphunzitsi amalamulo anakhala pansi pomwepo, namaganiza mʼmitima mwawo kuti,
But certain scribes who were present, reasoned thus within themselves:
7 “Nʼchifukwa chiyani munthuyu ayankhula chotere? Iye akuchitira mwano Mulungu! Ndani angakhululukire munthu machimo kupatula Mulungu yekha?”
How does this man speak such blasphemies? Who can forgive sins but God?
8 Nthawi yomweyo Yesu anadziwa mu mzimu wake kuti izi ndi zimene ankaganiza mʼmitima yawo, ndipo anawawuza kuti, “Chifukwa chiyani mukuganiza zinthu izi?
Jesus, immediately knowing in himself that they made these reflections, said to them, Why do you reason thus within yourselves?
9 Chapafupi nʼchiyani; kunena kwa wofa ziwaloyu kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kuti, ‘Imirira, tenga mphasa yako ndipo yenda?’
Which is easier, to say to the paralytic, Your sins are forgiven, or to say, with effect, Arise, take up your couch and walk?
10 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko lapansi wokhululukira machimo.” Anati kwa wofa ziwaloyo,
But that you may know that the Son of Man has power upon the earth to forgive sins, rise, (he said to the paralytic, )
11 “Ndikuwuza iwe, imirira, tenga mphasa yako ndipo pita kwanu.”
I command you, take up your couch, and go home.
12 Anayimirira, nanyamula mphasa yake natuluka onse akumuona. Izi zinadabwitsa aliyense ndipo anayamika Mulungu nati, “Sitinaonepo zinthu ngati izi!”
Immediately he rose, took up the couch, and walked out before them all; insomuch that they were all amazed, and glorified God, saying, We never saw anything like this.
13 Yesu anatulukanso napita kumbali ya nyanja. Gulu lalikulu la anthu linabwera kwa Iye, ndipo anayamba kuliphunzitsa.
Again, he went out toward the sea, and all the multitude repaired to him, and he taught them.
14 Pamene ankayendabe, anaona Levi mwana wa Alufeyo atakhala mʼnyumba ya msonkho. Yesu anamuwuza kuti, “Tsate Ine.” Ndipo Levi anayimirira namutsata Iye.
Passing along, he saw Levi, son of Alpheus, sitting at the toll office, and said to him, Follow me. And he arose and followed him.
15 Yesu atakalandira chakudya ku nyumba kwa Levi, amisonkho ambiri ndi “ochimwa” ankadya naye pamodzi ndi ophunzira ake, pakuti anali ambiri amene anamutsatira.
Now when Jesus was eating in this man's house, several publicans and sinners placed themselves at table with him and his disciples: for many of these people followed him.
16 Pamene aphunzitsi amalamulo a Afarisi anamuona akudya ndi “ochimwa” ndi amisonkho, anafunsa ophunzira ake kuti, “Chifukwa chiyani amadya ndi olandira msonkho ndi ochimwa?”
The Scribes and the Pharisees, seeing him eat with publicans and sinners, said to his disciples, Wherefore does he eat and drink with publicans and sinners?
17 Yesu atamva zimenezi, anawawuza kuti, “Anthu amene ali bwino safuna singʼanga koma odwala. Ine sindinabwere kudzayitana olungama, koma ochimwa.”
Jesus, hearing this, replied, The whole need not a physician, but the sick. I came not to call the righteous, but sinners.
18 Ndipo ophunzira a Yohane ndi a Afarisi amasala kudya. Anthu ena anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Zitheka bwanji kuti ophunzira a Yohane ndi ophunzira a Afarisi amasala kudya, koma anu satero?”
The disciples of John, and those of the Pharisees, accustomed to fasting, came to him and said, John's disciples, and those of the Pharisees, fast; why do not your disciples fast?
19 Yesu anayankha nati, “Kodi alendo a mkwati angasale kudya bwanji pamene iye ali nawo pamodzi? Iwo sangatero, pamene iye ali nawo pamodzi.
Jesus answered, Do the bridemen fast while the bridegroom is with them? While the bridegroom is with them they do not fast.
20 Koma nthawi idzafika pamene mkwati adzachotsedwa pakati pawo, ndipo pa tsiku limenelo adzasala kudya.
But the days will come when the bridegroom shall be take from them; and in those days they will fast.
21 “Palibe amene amasokerera chigamba chatsopano pa chovala chakale. Ngati atatero, chigamba chatsopanocho chidzazomola chovala chakalecho, kukulitsa chibowocho.
No person sews a piece of undressed cloth on an old garment; otherwise the new patch tears the old cloth, and makes a worse rent.
22 Ndipo palibe amene amathira vinyo watsopano mʼmatumba akale a vinyo. Ngati atatero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa matumba a vinyo ndipo vinyoyo pamodzi ndi matumbawo zidzawonongeka. Ayi, satero, amathira vinyo watsopano mʼmatumba atsopanonso.”
No person puts new wine into old leather bottles; else the new wine bursts the bottle; and thus both the wine is split, and the bottles are rendered useless; but new wine must be put into new bottles.
23 Tsiku lina la Sabata, Yesu amadutsa pakati pa minda ya tirigu, ndipo ophunzira ake amayenda naye limodzi, nayamba kubudula ngala za tiriguyo.
Once, when he was going through the corn on the Sabbath, his disciples began to pluck the ears of corn as they went.
24 Afarisi anati kwa Iye, “Taonani, chifukwa chiyani akuchita chosaloledwa ndi lamulo pa Sabata?”
The Pharisees said to him, Why do they that which on the Sabbath, it is unlawful to do?
25 Iye anayankha kuti, “Kodi simunawerenge zimene Davide anachita pamene iye ndi anzake anali osowa ndi anamva njala?
He answered, Did you never read what David and his attendants did, in a strait, when they were hungry,
26 Pa nthawi ya Abiatara mkulu wa ansembe, iye analowa mʼnyumba ya Mulungu ndi kudya buledi wopatulika amene amaloledwa kuti adye ndi ansembe okha. Ndipo anapereka wina kwa anzake.”
how he entered the tabernacle of God, in the days of Abiathar the high priest, and eat the loaves of the presence, which none but the priests could lawfully eat, and gave of them also to his attendants?
27 Pamenepo anawawuza kuti, “Sabata linapangidwira munthu, osati munthu kupangidwira Sabata.
He added, The Sabbath was made for man, and not man for the Sabbath.
28 Choncho Mwana wa Munthu ali Ambuye ngakhale wa Sabata.”
Therefore the Son of Man is master even of the Sabbath.