< Marko 16 >
1 Litapita tsiku la Sabata, Mariya Magadalena, ndi amayi ake a Yakobo, ndi Salome anagula zonunkhiritsa ndi cholinga chakuti apite akadzoze thupi la Yesu.
When the Sabbath was past, Miriam Magdalene, and Miriam the mother of Jacob, and Shalom bought spices, that they might come and anoint him.
2 Mmamawa, tsiku loyamba la Sabata, dzuwa litangotuluka kumene, anali pa ulendo wopita ku manda
Very early on the first day of the week, they came to the tomb when the sun had risen.
3 ndipo anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi akatikugudubuzira mwala pa khomo la manda ndani?”
They were saying among themselves, “Who will roll away the stone from the door of the tomb for us?”
4 Koma atakweza maso awo, anaona kuti mwala umene unali waukulu kwambiri wagubuduzidwa kale.
for it was very big. Looking up, they saw that the stone was rolled back.
5 Atalowa mʼmanda, anaona mnyamata atavala mwinjiro woyera atakhala ku mbali ya kumanja, ndipo iwo anachita mantha.
Entering into the tomb, they saw a young man sitting on the right side, dressed in a white robe; and they were amazed.
6 Iye anati, “Musaope. Kodi mukufuna Yesu wa ku Nazareti, amene anapachikidwa? Wauka! Sali muno. Onani malo amene anamugonekapo.
He said to them, “Don’t be amazed. You seek Yeshua, the Nazarene, who has been crucified. He has risen! He is not here. See the place where they laid him!
7 Koma pitani, kawuzeni ophunzira ake ndi Petro kuti, ‘Iye watsogola kupita ku Galileya. Kumeneko mukamuona Iye monga momwe anakuwuzirani.’”
But go, tell his disciples and Peter, ‘He goes before you into Galilee. There you will see him, as he said to you.’”
8 Akunjenjemera ndi kudabwa, amayiwo anatuluka ndipo anathawa ku mandako. Sananene china chilichonse kwa aliyense, chifukwa anachita mantha.
They went out, and fled from the tomb, for trembling and astonishment had come on them. They said nothing to anyone; for they were afraid.
9 (note: The most reliable and earliest manuscripts do not include Mark 16:9-20.) Yesu atauka kwa akufa mmawa pa tsiku loyamba la Sabata, anayamba kuonekera kwa Mariya Magadalena, amene anatulutsa mwa iye ziwanda zisanu ndi ziwiri.
(note: The most reliable and earliest manuscripts do not include Mark 16:9-20.) Now when he had risen early on the first day of the week, he appeared first to Miriam Magdalene, from whom he had cast out seven demons.
10 Iye anapita ndi kukawawuza amene anali ndi Yesu, amene ankakhuza maliro ndi kulira.
She went and told those who had been with him, as they mourned and wept.
11 Atamva kuti Yesu ali moyo ndikuti amuona, iwo sanakhulupirire.
When they heard that he was alive and had been seen by her, they disbelieved.
12 Zitatha izi Yesu anaonekera mʼmaonekedwe ena kwa awiri a iwo amene anali ku dera la ku mudzi.
After these things he was revealed in another form to two of them as they walked, on their way into the country.
13 Iwo anabwerera ndi kudzawawuza enawo; koma iwo sanakhulupirirebe.
They went away and told it to the rest. They didn’t believe them, either.
14 Pambuyo pake Yesu anaonekera kwa khumi ndi mmodziwo pamene ankadya; anawadzudzula chifukwa chopanda chikhulupiriro ndi kukanitsitsa kwawo kuti akhulupirire amene anamuona Iye atauka.
Afterward he was revealed to the Eleven themselves as they sat at the table; and he rebuked them for their unbelief and hardness of heart, because they didn’t believe those who had seen him after he had risen.
15 Anati kwa iwo, “Pitani mʼdziko lonse lapansi ndipo mukalalikire Uthenga Wabwino kwa zolengedwa zonse.
He said to them, “Go into all the world and proclaim the Good News to the whole creation.
16 Aliyense amene akakhulupirire nabatizidwa adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira adzalangidwa.
He who believes and is immersed will be saved; but he who disbelieves will be condemned.
17 Tsono zizindikiro izi zidzawatsata amene adzakhulupirira: Mʼdzina langa adzatulutsa ziwanda; adzayankhula malilime atsopano;
These signs will accompany those who believe: in my name they will cast out demons; they will speak with new languages;
18 adzanyamula njoka ndi manja awo; ndipo pamene adzamwa mankhwala akupha, sadzawapweteka nʼpangʼonongʼono pomwe; adzasanjika manja awo pa anthu odwala ndipo odwalawo adzachira.”
they will take up serpents; and if they drink any deadly thing, it will in no way hurt them; they will lay hands on the sick, and they will recover.”
19 Ambuye Yesu atatha kuyankhulana nawo, anatengedwa kupita kumwamba ndipo anakhala kudzanja lamanja la Mulungu.
So then the Lord, after he had spoken to them, was received up into heaven and sat down at the right hand of God.
20 Pamenepo ophunzira aja anapita ndi kukalalikira ponseponse, ndipo Ambuye anagwira nawo ntchito pamodzi, ndipo anatsimikizira mawuwo ndi zizindikiro zimene ankachita.
They went out and preached everywhere, the Lord working with them and confirming the word by the signs that followed. Amen.