< Marko 15 >
1 Mmamawa, akulu a ansembe pamodzi ndi akuluakulu, aphunzitsi amalamulo ndi olamulira onse anamanga fundo. Anamumanga Yesu, namutenga ndi kukamupereka kwa Pilato.
Odmah izjutra glavari svećenički zajedno sa starješinama i pismoznancima - cijelo Vijeće - upriličili su vijećanje pa Isusa svezali, odveli i predali Pilatu.
2 Pilato anafunsa kuti, “Kodi Iwe ndi Mfumu ya Ayuda?” Yesu anayankha kuti, “Mwatero ndinu.”
I upita ga Pilat: “Ti li si kralj židovski?” On mu odgovori: “Ti kažeš.”
3 Akulu a ansembe anamunenera zinthu zambiri.
I glavari ga svećenički teško optuživahu.
4 Ndipo Pilato anamufunsanso Iye kuti, “Kodi Iwe suyankhapo kanthu? Tamva zinthu zambiri akukunenerazi.”
Pilat ga opet upita: “Ništa ne odgovaraš? Gle, koliko te optužuju.”
5 Koma Yesu sanayankhebe, ndipo Pilato anadabwa.
A Isus ništa više ne odgovori te se Pilat čudio.
6 Pa nthawi ya Phwando, panali chizolowezi chomasula munthu wamʼndende amene anthu amupempha.
O Blagdanu bi im pustio uznika koga bi zaiskali.
7 Munthu wotchedwa Baraba anali mʼndende pamodzi ndi anthu owukira amene anapha anthu pa nthawi ya chipolowe.
A zajedno s pobunjenicima koji u pobuni počiniše umorstvo bijaše u okove bačen čovjek zvani Baraba.
8 Gulu la anthu linabwera kwa Pilato ndi kumufunsa kuti awachitire zimene amachita nthawi zonse.
I uziđe svjetina te poče od Pilata iskati ono što im običavaše činiti.
9 “Kodi mukufuna kuti ndikumasulireni mfumu ya Ayuda?” Pilato anafunsa,
A on im odgovori: “Hoćete li da vam pustim kralja židovskoga?”
10 podziwa kuti akulu a ansembe anamupereka Yesu kwa iye chifukwa cha nsanje.
Znao je doista da ga glavari svećenički bijahu predali iz zavisti.
11 Koma akulu a ansembe anasonkhezera anthu kuti Pilato amasule Baraba mʼmalo mwa Yesu.
Ali glavari svećenički podjare svjetinu da traži neka im radije pusti Barabu.
12 Pilato anawafunsa kuti, “Kodi nanga ndichite chiyani ndi uyu amene mukumutcha mfumu ya Ayuda?”
Pilat ih opet upita: “Što dakle da učinim s ovim kojega zovete kraljem židovskim?”
13 Anafuwula kuti, “Mpachikeni!”
A oni opet povikaše: “Raspni ga!”
14 Pilato anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani? Wapalamula mlandu wotani?” Koma anafuwula kwambiri, “Mpachikeni!”
Reče im Pilat: “Ta što je zla učinio?” Povikaše još jače: “Raspni ga!”
15 Pilato pofuna kuwakondweretsa anthuwo, anawamasulira Baraba. Analamula kuti Yesu akwapulidwe mwankhanza, ndipo anamupereka kuti akapachikidwe.
Hoteći ugoditi svjetini, Pilat im pusti Barabu, a Isusa izbičeva i preda da se razapne.
16 Asilikali anamutenga Yesu ndi kupita naye mʼkati mwa nyumba yaufumu (dera lokhalako asilikali a mfumu) ndipo anasonkhanitsa gulu lonse la asilikali.
Vojnici ga odvedu u unutarnjost dvora, to jest u pretorij, pa sazovu cijelu četu
17 Anamuveka Iye mwinjiro wofiira, kenaka analuka chipewa cha minga ndi kuyika pa mutu pake.
i zaogrnu ga grimizom; spletu trnov vijenac i stave mu na glavu
18 Ndipo anayamba kunena kwa lye kuti, “Ulemu kwa inu Mfumu ya Ayuda!”
te ga stanu pozdravljati: “Zdravo, kralju židovski!”
19 Ndipo anamugogoda pa mutu mobwerezabwereza ndi ndodo ndi kumulavulira. Anamugwadira ndi kumulambira Iye.
I udarahu ga trskom po glavi, pljuvahu po njemu i klanjahu mu se prigibajući koljena.
20 Ndipo anamuchita chipongwe, anamuvula mwinjiro wofiira uja ndi kumuveka zovala zake. Kenaka anamutenga kuti akamupachike.
A pošto ga izrugaše, svukoše mu grimiz i obukoše mu njegove haljine. I izvedu ga da ga razapnu.
21 Munthu wina ochokera ku Kurene, Simoni, abambo a Alekisanda ndi Rufasi amadutsa kuchokera ku dziko la kwawo, ndipo anamuwumiriza kuti anyamule mtanda.
I prisile nekog prolaznika koji je dolazio s polja, Šimuna Cirenca, oca Aleksandrova i Rufova, da mu ponese križ.
22 Anafika naye Yesu pa malo otchedwa Gologota (kutanthauza kuti, malo a bade)
I dovuku ga na mjesto Golgotu, što znači Lubanjsko mjesto.
23 Kenaka anamupatsa Iye vinyo wosakaniza ndi mure, koma Iye sanamwe.
I nuđahu mu piti namirisana vina, ali on ne uze.
24 Ndipo anamupachika Iye. Anachita maere ogawana zovala zake kuti aone chimene aliyense angatenge.
Kad ga razapeše, razdijele među se haljine njegove bacivši za njih kocku - što će tko uzeti.
25 Linali ora lachitatu mmawa pamene anamupachika Yesu.
A bijaše treća ura kad ga razapeše.
26 Chikwangwani cholembedwapo mlandu wake chinali choti: mfumu ya ayuda.
Bijaše napisan i natpis o njegovoj krivici: “Kralj židovski.”
27 Achifwamba awiri anapachikidwanso pamodzi ndi Iye, wina kumanja kwake ndi wina kumanzere kwake.
A zajedno s njime razapnu i dva razbojnika, jednoga njemu zdesna, drugoga slijeva.
28 (Ndipo malemba anakwaniritsidwa amene amati, “Iye anayikidwa mʼgulu la anthu oyipa).”
29 Amene amadutsa pafupi anamunenera mawu amwano, akupukusa mitu yawo ndi kuti, “Haa! Iwe amene udzawononga Nyumba ya Mulungu ndi kuyimanganso masiku atatu,
Prolaznici su ga pogrđivali mašući glavama: “Ej, ti, koji razvaljuješ Hram i sagradiš ga za tri dana,
30 tsika kuchoka pa mtandapo ndipo udzipulumutse wekha!”
spasi sam sebe, siđi s križa!”
31 Chimodzimodzinso akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo anamunyoza Iye pakati pawo. Iwo anati, “Anapulumutsa ena, koma sangathe kudzipulumutsa yekha!
Slično i glavari svećenički s pismoznancima rugajući se govorahu jedni drugima: “Druge je spasio, sebe ne može spasiti!
32 Musiyeni Khristu, Mfumu ya Aisraeli, atsike tsopano kuchoka pa mtanda, kuti ife tione ndi kukhulupirira.” Iwonso amene anapachikidwa naye pamodzi anamulalatira.
Krist, kralj Izraelov! Neka sad siđe s križa da vidimo i povjerujemo!” Vrijeđahu ga i oni koji bijahu s njim raspeti.
33 Pa ora lachisanu ndi chimodzi masana mdima unabwera pa dziko lonse mpaka pa ora lachisanu ndi chinayi masana.
A o šestoj uri tama nasta po svoj zemlji - sve do ure devete.
34 Pa ora lachisanu ndi chinayi Yesu analira mofuwula kuti, “Eloi, Eloi, lama sabakitani?” Kutanthauza kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?”
O devetoj uri povika Isus iza glasa: “Eloi, Eloi lama sabahtani?” To znači: “Bože moj, Bože moj, zašto si me ostavio?”
35 Ena amene anali pafupi atamva izi anati, “Tamverani, akuyitana Eliya.”
Neki od nazočnih čuvši to govorahu: “Gle, Iliju zove.”
36 Munthu wina anathamanga, natenga chinkhupule atachiviyika mu vinyo wosasa, anachizika ku mtengo, ndi kumupatsa Yesu kuti amwe. Munthuyo anati, “Musiyeni yekha tsopano. Tiyeni tione ngati Eliya angabwere kudzamutsitsa.”
A jedan otrča, natopi spužvu octom, natakne na trsku i pruži mu piti govoreći: “Pustite da vidimo hoće li doći Ilija da ga skine.”
37 Ndi mawu ofuwula, Yesu anapuma komaliza.
A Isus zavapi jakim glasom i izdahnu.
38 Chinsalu chotchinga cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati kuyambira pamwamba mpaka pansi.
I zavjesa se hramska razdrije nadvoje, odozgor dodolje.
39 Ndipo Kenturiyo, amene anayima patsogolo pa Yesu, atamva kulira kwake ndi kuona mmene anafera anati, “Zoonadi, uyu anali Mwana wa Mulungu.”
A kad satnik koji stajaše njemu nasuprot vidje da tako izdahnu, reče: “Zaista, ovaj čovjek bijaše Sin Božji!”
40 Amayi ena anali patali kuonerera. Pakati pawo panali Mariya Magadalena, Mariya amayi a Yakobo wamngʼono ndi Yose ndi Salome.
Izdaleka promatrahu i neke žene: među njima Marija Magdalena i Marija, majka Jakova Mlađega i Josipa, i Saloma -
41 Amayi awa ankamutsatira Iye mu Galileya ndi kumutumikira Iye pa zosowa zake. Amayi enanso ambiri amene anabwera naye ku Yerusalemu analinso pomwepo.
te su ga pratile kad bijaše u Galileji i posluživale mu - i mnoge druge koje uziđoše s njim u Jeruzalem.
42 Linali Tsiku Lokonzekera (kunena kuti, tsiku lomwe limatsatizana ndi Sabata). Choncho madzulo atayandikira,
A uvečer, budući da je bila Priprava, to jest predvečerje subote,
43 Yosefe wa ku Arimateyu, mkulu wolamulira odziwika bwino, amene amadikirira ufumu wa Mulungu, anapita kwa Pilato molimba mtima ndi kukapempha mtembo wa Yesu.
dođe Josip iz Arimateje, ugledan vijećnik, koji također isčekivaše kraljevstvo Božje: odvaži se, uđe k Pilatu i zaiska tijelo Isusovo.
44 Pilato anadabwa pakumva kuti anali atamwalira kale. Anayitana Kenturiyo, namufunsa ngati Yesu anali atamwalira kale.
Pilat se začudi da je već umro pa dozva satnika i upita ga je li odavna umro.
45 Atawuzidwa ndi Kenturiyo kuti zinali motero, anapereka mtembowo kwa Yosefe.
Kad sazna od satnika, darova Josipu tijelo.
46 Choncho Yosefe anagula nsalu yabafuta, natsitsa thupi, ndipo analikulunga mʼnsalu, naliyika mʼmanda amene anawagoba pa mwala. Kenaka anagubuduza mwala umene anatseka nawo mandawo.
Josip kupi platno, skine tijelo i zavije ga u platno te položi u grob, koji bijaše izduben iz stijene. I dokotrlja kamen na grobna vrata.
47 Mariya Magadalena ndi Mariya amayi a Yose anaona kumene anamuyika Yesu.
A Marija Magdalena i Marija Josipova promatrahu kamo ga polažu.