< Marko 11 >

1 Atayandikira ku Yerusalemu, anafika ku Betifage ndi Betaniya ku phiri la Olivi. Yesu anatuma awiri a ophunzira ake
When they had almost reached Jerusalem, as far as Bethphage and Bethany, near the Mount of Olives, Jesus sent on two of his disciples.
2 nati kwa iwo, “Pitani ku mudzi uli patsogolo panu, ndipo mukamakalowa, mukapeza mwana wabulu atamangiriridwa pamenepo, amene wina aliyense sanakwerepo. Kamumasuleni ndi kubwera naye kuno.
“Go to the village facing you,” he said; “and, as soon as you get there, you will find a foal tethered, which no one has ever ridden; untie it, and bring it.
3 Ngati wina aliyense akakufunsani kuti, ‘Mukuchita zimenezi chifukwa chiyani?’ Kamuwuzeni kuti, ‘Ambuye akumufuna ndipo akamutumiza kuno msanga.’”
And, if any one says to you ‘Why are you doing that?’, say ‘The Master wants it, and will be sure to send it back here at once.’”
4 Anapita ndipo anakapeza mwana wabulu ali kunja mu msewu waukulu atamumangirira pa chipata. Pamene anamumasula,
The two disciples went, and, finding a foal tethered outside a door in the street, they untied it.
5 anthu ena amene anayima pomwepo anafunsa kuti, “Mukuchita chiyani, kumasula mwana wabuluyo?”
Some of the by-standers said to them: “What are you doing, untying the foal?”
6 Iwo anayankha monga mmene Yesu anawawuzira, ndipo anthu aja anawalola kuti apite.
And the two disciples answered as Jesus had told them; and they allowed them to go.
7 Atafika naye mwana wabulu kwa Yesu, nayika mikanjo yawo pa buluyo, Iye anakwerapo.
Then they brought the foal to Jesus, and, when they had laid their cloaks on it, he seated himself upon it.
8 Anthu ambiri anayala mikanjo yawo pa msewu, pamene ena anayala nthambi zomwe anadula mʼminda.
Many of the people spread their cloaks on the road, while some strewed boughs which they had cut from the fields;
9 Amene anatsogola ndi iwo amene ankatsatira ankafuwula kuti, “Hosana! “Odala Iye amene akudza mʼdzina la Ambuye!”
and those who led the way, as well as those who followed, kept shouting: “‘God save him! Blessed is He who comes in the name of the Lord!’
10 “Odala ndi ufumu umene ukubwera wa abambo athu Davide!” “Hosana Mmwambamwamba!”
Blessed is the coming Kingdom of our father David! ‘God save him from on high!’”
11 Yesu analowa mu Yerusalemu napita ku Nyumba ya Mulungu. Anayangʼana zonse, koma popeza kuti nthawi inali itapita, anatuluka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwo.
Jesus entered Jerusalem, and went into the Temple Courts; and, after looking round at everything, as it was already late, he went out to Bethany with the Twelve.
12 Mmawa mwake pamene amachoka ku Betaniya, Yesu anamva njala.
The next day, after they had left Bethany, Jesus became hungry;
13 Ataonera patali mtengo wamkuyu uli ndi masamba, anapita kuti akaone ngati unali ndi chipatso chilichonse. Atafika, sanapezemo kanthu koma masamba, chifukwa sinali nthawi ya nkhuyu.
and, noticing a fig-tree at a distance in leaf, he went to it to see if by any chance he could find something on it; but, on coming up to it, he found nothing but leaves, for it was not the season for figs.
14 Ndipo Iye anati kwa mtengo, “Palibe amene adzadyenso chipatso kuchokera kwa iwe.” Ndipo ophunzira ake anamva Iye akunena izi. (aiōn g165)
So, addressing the tree, he exclaimed: “May no man ever again eat of your fruit!” And his disciples heard what he said. (aiōn g165)
15 Atafika ku Yerusalemu, Yesu analowa mʼbwalo lakunja la Nyumba ya Mulungu ndipo anayamba kupirikitsa anthu amene amagula ndi kugulitsa mʼmenemo. Anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda,
They came to Jerusalem. Jesus went into the Temple Courts, and began to drive out those who were buying and selling there. He overturned the tables of the money-changers, and the seats of the pigeon-dealers,
16 ndipo Iye sanalole aliyense kugulitsa malonda mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu.
and would not allow any one to carry anything across the Temple Courts.
17 Ndipo pamene ankawaphunzitsa, Iye anati, “Kodi sikunalembedwe kuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero kwa anthu a mitundu yonse?’ Koma inu mwayisandutsa ‘phanga la achifwamba.’”
Then he began to teach. “Does not Scripture say,” he asked, “‘My House shall be called a House of Prayer for all the nations’? But you have made it a den of robbers.’”
18 Akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo anamva izi ndipo anayamba kufuna njira yoti amuphere Iye, pakuti amamuopa, chifukwa gulu lonse la anthu linazizwa ndi chiphunzitso chake.
Now the Chief Priests and the Teachers of the Law heard this and began to look for some way of putting Jesus to death; for they were afraid of him, since all the people were greatly impressed by his teaching.
19 Pofika madzulo, iwo anatuluka mu mzindamo.
As soon as evening fell, Jesus and his disciples went out of the city.
20 Mmamawa, pamene ankayenda, anaona mtengo wamkuyu uja utafota kuyambira ku mizu.
As they passed by early in the morning, they noticed that the fig-tree was withered up from the very roots.
21 Petro anakumbukira nati kwa Yesu, “Aphunzitsi, taonani! Mtengo wamkuyu munawutemberera uja wafota!”
Then Peter recollected what had occurred. “Look, Rabbi,” he exclaimed, “the fig-tree which you doomed is withered up!”
22 Yesu anayankha kuti, “Khalani ndi chikhulupiriro mwa Mulungu.
“Have faith in God!” replied Jesus.
23 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati wina aliyense angalamule phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye mʼnyanja,’ ndipo wosakayika mu mtima mwake koma kukhulupirira kuti chimene akunena chidzachitika, chidzachitikadi kwa iyeyo.
“I tell you that if any one should say to this hill ‘Be lifted up and hurled into the sea!’, without ever a doubt in his mind, but in the faith that what he says will be done, he would find that it would be.
24 Nʼchifukwa chake ndikukuwuzani kuti chilichonse chimene mupempha mʼpemphero, khulupirirani kuti mwalandira, ndipo chidzakhala chanu.
And therefore I say to you ‘Have faith that whatever you ask for in prayer is already granted you, and you will find that it will be.’
25 Pamene muyimirira kupemphera, ngati muli ndi chifukwa ndi wina, mukhululukireni, kuti Atate anu akumwamba akukhululukireni machimo anu.”
‘And, whenever you stand up to pray, forgive any grievance that you have against any one, that your Father who is in Heaven also may forgive you your offences.”
26 (Koma ngati simukhululukirana, ngakhale Atate anu akumwamba sadzakhululukira machimo anu).
27 Iwo anafikanso ku Yerusalemu, ndipo pamene Yesu amayenda mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo ndi akuluakulu anabwera kwa Iye.
They came to Jerusalem again. While Jesus was walking about in the Temple Courts, the Chief Priests, the Teachers of the Law, and the Councillors came up to him.
28 Iwo anafunsa kuti, “Mukuchita izi ndi ulamuliro wanji? Ndipo anakupatsani ulamuliro umenewu ndi ndani?”
“What authority have you to do these things?” they said. “Who gave you the authority to do them?”
29 Yesu anayankha kuti, “Ndikufunsani funso limodzi. Mundiyankhe, ndipo ndikuwuzani ndi ulamuliro wanji umene ndikuchitira izi.
“I will put one question to you,” said Jesus. “Answer me that, and then I will tell you what authority I have to act as I do.
30 Ubatizo wa Yohane, unali wochokera kumwamba, kapena kwa anthu? Ndiwuzeni.”
It is about John’s baptism. Was it of divine or human origin? Answer me that.”
31 Iwo anakambirana pakati pawo ndipo anati, “Tikati, ‘Wochokera kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga nʼchifukwa chiyani simunamukhulupirire?’
They began arguing together; “If we say ‘divine,’ he will say ‘Why then did not you believe him?’
32 Koma ife tikati, ‘Wochokera kwa anthu.’” (Amaopa anthu, pakuti aliyense amakhulupirira kuti Yohane analidi mneneri).
Yet can we say ‘human’?” — They were afraid of the people, for everyone regarded John as undoubtedly a Prophet.
33 Ndipo anamuyankha Yesu kuti, “Sitikudziwa.” Yesu anati, “Nanenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wanji ndichitira zimenezi.”
So their answer to Jesus was — “We do not know.” “Then I,” replied Jesus, “refuse to tell you what authority I have to do these things.”

< Marko 11 >