< Malaki 3 >
1 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndidzatuma mthenga wanga amene adzakonza njira pamaso panga. Kenaka mwadzidzidzi Ambuye amene mukumufunafuna adzafika ku Nyumba yake. Mthenga wapangano amene mukumuyembekezera adzabwera.”
2 Koma ndani adzatha kupirira pa tsiku la kubwera kwake? Ndani adzatha kuyima pamene Iye wafika? Pakuti adzakhala ngati moto wa mmisiri wa pa ngʼanjo, kapenanso ngati sopo wa munthu wochapa.
3 Iye adzachita kukhalira pansi ngati mmisiri woyenga ndi woyeretsa siliva. Iye adzayeretsa Alevi ndi kuwayenga ngati golide ndi siliva. Pamenepo Yehova adzakhala ndi anthu amene azidzabweretsa zopereka mwachilungamo,
4 ndipo Yehova adzalandira zopereka za Yuda ndi Yerusalemu, ngati masiku akale, masiku amakedzana.
5 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Tsono ndidzakuyandikirani kuti ndikuweruzeni. Mosataya nthawi ndidzanena mawu otsutsa mfiti, achigololo, a umboni wonama, amene salipira bwino antchito awo, amene amazunza akazi ndi ana amasiye, amene saweruza alendo mwachilungamo, komanso amene sandiopa Ine.”
6 “Ine ndine Yehova, ndipo sindisintha. Choncho inu zidzukulu za Yakobo, simunawonongedwe.
7 Kuyambira nthawi ya makolo anu mwakhala mukuphwanya malamulo anga ndipo simunawatsatire. Bwererani kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Koma inu mukufunsa kuti, ‘Tibwerere motani kwa Yehova?’
8 “Kodi munthu angathe kuba za Mulungu? Komatu inu mumandibera. “Koma inu mukufunsa kuti, ‘Kodi timakuberani motani?’ “Pa zakhumi ndi pa zopereka.
9 Mtundu wanu wonse ndinu otembereredwa, chifukwa mukundibera.
10 Bweretsani chakhumi chathunthu ku nyumba yosungira, kuti mukhale chakudya mʼnyumba mwanga.” Akutero Yehova Wamphamvuzonse, “Tandiyesani, ndipo muone ngati sindidzatsekula zipata zakumwamba, ndi kukugwetserani madalitso ochuluka amene mudzasowe malo owayikamo.
11 Ndidzaletsa tizirombo kuti tisawononge mbewu zanu, ndipo mpesa wa mʼminda mwanu zipatso zake sizidzayoyoka,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
12 “Motero anthu amitundu yonse adzakutchulani odala, pakuti dziko lanu lidzakhala lokondweretsa,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
13 Yehova akuti, “Mwayankhula mawu owawa onena za Ine. “Komabe inu mukufunsa kuti, ‘Kodi tanena chiyani chotsutsana nanu?’
14 “Mwanena kuti, ‘Kutumikira Mulungu nʼkosapindulitsa. Kodi timapindulanji pochita zofuna zake, ndi kumayenda ngati anamfedwa pamaso pa Yehova Wamphamvuzonse?
15 Koma tsono ife timati anthu odzikuza ndiye odalitsika. Kunena zoona anthu oyipa ndiye amapeza bwino, ngakhale amene amanyoza Mulungu amapulumuka.’”
16 Ndipo woopa Yehova anayamba kukambirana, ndipo Yehova anamvetsera. Buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, lonena za amene amaopa Yehova ndi kulemekeza dzina lake.
17 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Anthu amenewo adzakhala anga, tsiku limene Ine ndidzachita izi, adzakhala angaanga. Ndidzawaleka osawalanga monga mmene munthu amachitira chifundo mwana wake amene amamutumikira.
18 Pamenepo mudzaonanso kusiyana pakati pa anthu olungama ndi oyipa, pakati pa amene amatumikira Mulungu ndi amene satumikira Mulungu.”