< Malaki 2 >

1 “Tsono chenjezo ili ndi la inu, inu ansembe.”
Et nunc ad vos mandatum hoc, o sacerdotes.
2 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ngati simumvera, ndipo ngati simulemekeza dzina langa mʼmitima mwanu, ndidzakutembererani ndipo madalitso onse munawalandira ndidzawatemberera. Ndithu, ndawatemberera kale, chifukwa simunalemekeze Ine mʼmitima mwanu.”
Si nolueritis audire, et si nolueritis ponere super cor, ut detis gloriam nomini meo, ait Dominus exercituum, mittam in vos egestatem, et maledicam benedictionibus vestris, et maledicam illis, quoniam non posuistis super cor.
3 “Ine ndidzalanga zidzukulu zanu chifukwa cha inu; ndidzakupakani kumaso ndowe za nsembe zanu zachikondwerero, ndipo ndidzakutayani pamodzi ndi ndowezo.”
Ecce ego projiciam vobis brachium, et dispergam super vultum vestrum stercus solemnitatum vestrarum, et assumet vos secum.
4 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Apo mudzadziwa kuti Ine ndatumiza chenjezoli kuti pangano langa ndi Levi lipitirire.
Et scietis quia misi ad vos mandatum istud, ut esset pactum meum cum Levi, dicit Dominus exercituum.
5 Ine ndinali naye pa pangano, pangano lopatsa moyo ndi mtendere, ndipo ndinamupatsa zimenezi kuti azindiopa, ndipo anandiopadi ndi kulemekeza dzina langa.
Pactum meum fuit cum eo vitæ et pacis: et dedi ei timorem, et timuit me, et a facie nominis mei pavebat.
6 Pakamwa pake pankatuluka malangizo woona, ndipo pa milomo yake sipanapezeke chinyengo. Iye anayenda nane mwamtendere ndi molungama mtima, ndipo anabweza anthu ambiri mʼnjira zawo zauchimo.
Lex veritatis fuit in ore ejus, et iniquitas non est inventa in labiis ejus: in pace et in æquitate ambulavit mecum, et multos avertit ab iniquitate.
7 “Pakuti wansembe ayenera kukhala ndi chidziwitso, ndipo anthu ayenera kufunafuna malangizo kuchokera kwa iye, popeza iye ndi mthenga wa Yehova Wamphamvuzonse.
Labia enim sacerdotis custodient scientiam, et legem requirent ex ore ejus, quia angelus Domini exercituum est.
8 Koma inu mwasiya njira yanga ndipo mwapunthwitsa anthu ambiri ndi ziphunzitso zanu; mwayipitsa pangano langa ndi Levi,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
Vos autem recessistis de via, et scandalizastis plurimos in lege: irritum fecistis pactum Levi, dicit Dominus exercituum.
9 “Choncho Ine ndachititsa kuti munyozedwe ndi kuchititsidwa manyazi pamaso pa anthu onse, chifukwa simunatsate njira zanga koma mwakhala mukuonetsa kukondera pa nkhani za malamulo.”
Propter quod et ego dedi vos contemptibiles, et humiles omnibus populis, sicut non servastis vias meas, et accepistis faciem in lege.
10 Kodi sitili naye Atate mmodzi tonsefe? Kodi anatilenga si Mulungu mmodzi? Chifukwa chiyani tikudetsa pangano la makolo athu posamakhulupirirana wina ndi mnzake?
Numquid non pater unus omnium nostrum? numquid non Deus unus creavit nos? quare ergo despicit unusquisque nostrum fratrem suum, violans pactum patrum nostrorum?
11 Yuda waleka kukhulupirika. Chinthu chonyansa chachitika mu Israeli ndi mu Yerusalemu: Yuda wayipitsa malo opatulika amene Yehova amawakonda, pokwatira mkazi wopembedza mulungu wachilendo.
Transgressus est Juda, et abominatio facta est in Israël et in Jerusalem, quia contaminavit Juda sanctificationem Domini, quam dilexit, et habuit filiam dei alieni.
12 Ndipo wina aliyense wochita zimenezi, kaya munthuyo ndi wotani, Yehova amuchotse ku banja la Yakobo, ngakhale atabweretsa zopereka kwa Yehova Wamphamvuzonse.
Disperdet Dominus virum qui fecerit hoc, magistrum et discipulum, de tabernaculis Jacob, et offerentem munus Domino exercituum.
13 China chimene mumachita ndi ichi: Mumakhathamiritsa guwa lansembe la Yehova ndi misozi. Mumalira ndi kufuwula kwambiri chifukwa Iye amakana kuyangʼana nsembe zanu, kapena kulandira mokondwera nsembe za mʼmanja mwanu.
Et hoc rursum fecistis: operiebatis lacrimis altare Domini, fletu et mugitu, ita ut non respiciam ultra ad sacrificium, nec accipiam placabile quid de manu vestra.
14 Inu mukufunsa kuti, “Chifukwa chake nʼchiyani?” Chifukwa chake nʼchakuti Yehova ndi mboni ya pangano limene unachita ndi mkazi wa unyamata wako, chifukwa sunakhulupirike kwa iye, ngakhale kuti iyeyo ndiye mnzako, ndi mkazi wako mwapangano.
Et dixistis: Quam ob causam? Quia Dominus testificatus est inter te et uxorem pubertatis tuæ, quam tu despexisti: et hæc particeps tua, et uxor fœderis tui.
15 Kodi Yehova sanawalenge iwo ngati munthu mmodzi? Ndi ake mʼthupi ndi mu mzimu. Nʼchifukwa chiyani ali mmodzi? Chifukwa Iye amafuna ana opembedza Mulungu. Motero samala moyo wako wauzimu, ndipo usakhale wosakhulupirika kwa mkazi wa unyamata wako.
Nonne unus fecit, et residuum spiritus ejus est? et quid unus quærit, nisi semen Dei? custodite ergo spiritum vestrum, et uxorem adolescentiæ tuæ noli despicere.
16 Yehova Mulungu wa Israeli akuti, “Ndimadana ndi kulekana ukwati. Ndimadana ndi munthu wochita zankhanza zotere kwa mkazi wake,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. Choncho tetezani mzimu wanu, ndipo musakhale osakhulupirika.
Cum odio habueris, dimitte, dicit Dominus Deus Israël: operiet autem iniquitas vestimentum ejus, dicit Dominus exercituum. Custodite spiritum vestrum, et nolite despicere.
17 Mwamutopetsa Yehova ndi zoyankhula zanu. Inu mukufunsa kuti, “Kodi tamutopetsa bwanji?” Mwamutopetsa ponena kuti, “Aliyense amene amachita zoyipa ndi wabwino pamaso pa Yehova ndipo iye amakondwera naye” kapena pofunsa kuti, “Ali kuti Mulungu woweruza mwachilungamo?”
Laborare fecistis Dominum in sermonibus vestris, et dixistis: In quo eum fecimus laborare? In eo quod dicitis: Omnis qui facit malum bonus est in conspectu Domini, et tales ei placent: aut certe ubi est Deus judicii?

< Malaki 2 >