< Luka 9 >
1 Yesu atawayitana khumi ndi awiriwo pamodzi, Iye anawapatsa mphamvu ndi ulamuliro wotulutsa ziwanda zonse ndi kuchiritsa matenda.
He called the twelve together, and gave them power and authority over all demons and to cure diseases.
2 Ndipo Iye anawatumiza kukalalikira za ufumu wa Mulungu ndi kukachiritsa odwala.
He sent them forth to proclaim the Kingdom of God, and to heal the sick.
3 Iye anawawuza kuti, “Musatenge kanthu paulendo. Musatenge ndodo, thumba, buledi, ndalama, ndi malaya apadera.
And he said to them, "Take nothing for your journey—neither staff, nor pack, nor bread, nor money; neither have two tunics.
4 Nyumba iliyonse imene mulowa, mukhale momwemo kufikira mutachoka mu mzindawo.
Into whatever house you enter, stay there, and depart from there.
5 Ngati anthu sakulandirani, sasani fumbi la kumapazi anu pomwe mukuchoka mu mzinda wawo ngati umboni owatsutsa.”
As many as do not receive you, when you depart from that city, shake off even the dust from your feet for a testimony against them."
6 Ndipo iwo ananyamuka napita, mudzi ndi mudzi, kulalikira Uthenga Wabwino ndi kuchiritsa anthu paliponse.
They departed, and went throughout the villages, preaching the gospel, and healing everywhere.
7 Tsopano Herode olamulirayo anamva zonse zimachitikazi. Ndipo iye anavutika kwambiri chifukwa ena amati Yohane waukitsidwa kwa akufa,
Now Herod the tetrarch heard of all that was done; and he was very perplexed, because it was said by some that John had risen from the dead,
8 ena amati Eliya waonekera, ndipo ena anatinso mmodzi wa aneneri akalekale waukanso.
and by some that Elijah had appeared, and by others that one of the old prophets had risen again.
9 Koma Herode anati, “Ine ndinamudula mutu Yohane. Nanga uyu ndani amene ndikumva zinthu zotere za Iye?” Ndipo iye anayesetsa kuti amuone Iye.
Herod said, "John I beheaded, but who is this, about whom I hear such things?" He sought to see him.
10 Atumwi atabwerera, anamuwuza Yesu zimene anachita. Kenaka Iye anawatenga napita kwa okha ku mudzi wa Betisaida.
The apostles, when they had returned, told him what things they had done. He took them, and withdrew apart to a city called Bethsaida.
11 Koma gulu la anthu linadziwa ndipo anamutsatira. Iye anawalandira ndi kuyankhula nawo za ufumu wa Mulungu, ndi kuchiritsa amene amafuna machiritso.
But the crowds, perceiving it, followed him. He welcomed them, and spoke to them of the Kingdom of God, and he cured those who needed healing.
12 Chakumadzulo dzuwa litapita, khumi ndi awiriwo anabwera kwa Iye ndipo anati, “Uzani gulu la anthuli lichoke kuti apite ku midzi yotizungulira ndi madera a ku mudzi kuti akapeze chakudya ndi pogona, chifukwa kuno ndi kuthengo.”
The day began to wear away; and the twelve came, and said to him, "Send the crowd away, that they may go into the surrounding villages and farms, and lodge, and get food, for we are here in a deserted place."
13 Iye anayankha kuti, “Apatseni chakudya kuti adye.” Iwo anayankha kuti, “Ife tili ndi malofu a buledi asanu okha ndi nsomba ziwiri, pokhapokha titapita kukagula chakudya cha gulu la anthu onsewa.”
But he said to them, "You give them something to eat." They said, "We have no more than five loaves and two fish, unless we should go and buy food for all these people."
14 (Pamenepo panali amuna pafupifupi 5,000). Koma Iye anati kwa ophunzira ake, “Akhazikeni pansi mʼmagulu a anthu pafupifupi makumi asanu.”
For they were about five thousand men. He said to his disciples, "Make them sit down in groups of about fifty each."
15 Ophunzira ake anachita zomwezo ndipo aliyense anakhala pansi.
They did so, and made them all sit down.
16 Atatenga malofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri zija anayangʼana kumwamba, nayamika ndipo anazigawa. Kenaka anazipereka kwa ophunzira ake kuti azipereke kwa anthu.
He took the five loaves and the two fish, and looking up to the sky, he blessed them, and broke them, and gave them to the disciples to set before the crowd.
17 Onse anadya nakhuta, ndipo ophunzira ake anatolera madengu khumi ndi awiri odzaza ndi nyenyeswa zomwe zinatsala.
They ate, and were all filled. They gathered up twelve baskets of broken pieces that were left over.
18 Nthawi ina pamene Yesu amapemphera malo a yekha ali ndi ophunzira ake, Iye anawafunsa kuti, “Kodi anthu amati Ine ndine yani?”
It happened, as he was praying alone, that the disciples were with him, and he asked them, "Who do the crowds say that I am?"
19 Iwo anayankha kuti, “Ena amati Yohane Mʼbatizi; ena amati Eliya; ndipo enanso amati mmodzi wa aneneri akalekale waukanso.”
They answered, "'John the Baptist,' but others say, 'Elijah,' and others, that one of the old prophets is risen again."
20 Iye anafunsa kuti, “Koma nanga inu mumati Ine ndine yani?” Petro anayankha kuti, “Mpulumutsi wolonjezedwa uja wa Mulungu.”
He said to them, "But who do you say that I am?" Peter answered, "The Messiah of God."
21 Yesu anawachenjeza kwambiri kuti asawuze wina aliyense za izi.
But he warned them, and commanded them to tell this to no one,
22 Ndipo Iye anati, “Mwana wa Munthu ayenera kuzunzika kwambiri ndi kukanidwa ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, Iye ayenera kuphedwa ndipo tsiku lachitatu adzauka kwa akufa.”
saying, "The Son of Man must suffer many things, and be rejected by the elders, chief priests, and scribes, and be killed, and the third day be raised up."
23 Ndipo Iye anawuza onse kuti, “Ngati wina aliyense akufuna kutsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kusenza mtanda wake tsiku ndi tsiku nʼkumanditsata Ine.
He said to all, "If anyone desires to come after me, let him deny himself, take up his cross daily, and follow me.
24 Popeza aliyense amene akufuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene adzataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupulumutsa.
For whoever desires to save his life will lose it, but whoever will lose his life for my sake, the same will save it.
25 Kodi chabwino ndi chiti kwa munthu, kupata zonse zapansi pano, koma ndi kutaya moyo wake kapena kudziwononga iye mwini?
For what does it profit a person if he gains the whole world, and loses or forfeits his own self?
26 Ngati wina aliyense achita nane manyazi ndi ndiponso mawu anga, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wake ndi mu ulemerero wa Atate ndi angelo oyera.
For whoever will be ashamed of me and of my words, of him will the Son of Man be ashamed, when he comes in his glory, and the glory of the Father, and of the holy angels.
27 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ena mwa inu amene mwayima pano simudzalawa imfa musanaone ufumu wa Mulungu.”
But I tell you the truth: There are some of those who stand here, who will in no way taste of death, until they see the Kingdom of God."
28 Patatha pafupifupi masiku asanu ndi atatu Yesu atanena izi, Iye anatenga Petro, Yohane ndi Yakobo ndi kukwera ku phiri kukapemphera.
It happened about eight days after these sayings, that he took with him Peter, John, and James, and went up onto the mountain to pray.
29 Pamene Iye ankapemphera, maonekedwe a nkhope yake, ndi zovala zake zinawala monyezimira kwambiri.
As he was praying, the appearance of his face was altered, and his clothing became white and dazzling.
30 Anthu awiri, Mose ndi Eliya,
And look, two men were talking with him, who were Moses and Elijah,
31 anaonekera mu ulemerero opambana akuyankhulana ndi Yesu. Iwo amayankhulana za kuchoka kwake, kumene Iye anali pafupi kukakwaniritsa ku Yerusalemu.
who appeared in glory, and spoke of his departure, which he was about to accomplish at Jerusalem.
32 Petro ndi anzake anali ndi tulo tambiri, koma atadzuka, iwo anaona ulemerero wake ndi anthu awiri atayima pamodzi ndi Iye.
Now Peter and those who were with him were heavy with sleep, but when they were fully awake, they saw his glory, and the two men who stood with him.
33 Pamene anthuwo ankamusiya Yesu, Petro anati kwa Iye, “Ambuye, ndi chabwino kwa ife kuti tikhale pano. Tiloleni kuti timange misasa itatu, umodzi wanu, umodzi wa Mose ndi umodzi wa Eliya.” (Iye sanadziwe chimene amayankhula).
It happened, as they were parting from him, that Peter said to Jesus, "Master, it is good for us to be here. Let us make three tents: one for you, and one for Moses, and one for Elijah," not knowing what he said.
34 Pamene Iye ankayankhula, mtambo unaonekera ndi kuwaphimba iwo, ndipo anachita mantha pamene mtambowo unawakuta.
While he said these things, a cloud came and overshadowed them, and they were afraid as they entered into the cloud.
35 Mawu anachokera mu mtambomo nati, “Uyu ndi Mwana wanga amene ndamusankha; mumvereni Iye.”
A voice came out of the cloud, saying, "This is my Son, my Chosen One. Listen to him."
36 Atamveka mawuwa, anaona kuti Yesu anali yekha. Ophunzirawo anazisunga izi mwa iwo okha ndipo sanawuze wina aliyense pa nthawiyi za zomwe iwo anaziona.
When the voice came, Jesus was found alone. They were silent, and told no one in those days any of the things which they had seen.
37 Mmawa mwake, akutsika ku phiri, anthu ambiri anakumana naye.
It happened on the next day, when they had come down from the mountain, that a large crowd met him.
38 Munthu wina mʼgulu la anthulo anayitana kuti, “Aphunzitsi, ndikupemphani kuti muone mwana wangayu, pakuti ndi mmodzi yekhayu.
And look, a man from the crowd called out, saying, "Teacher, I beg you to look at my son, for he is my only child.
39 Chiwanda chikamugwira amafuwula mwadzidzidzi; chimamugwedeza kolimba mpaka kutuluka thovu kukamwa. Sichimusiya ndipo chikumuwononga.
And look, a spirit seizes him, and all at once he cries out, and it convulses him so that he foams, and it hardly departs from him, bruising him severely.
40 Ine ndinapempha ophunzira anu kuti achitulutse, koma alephera.”
I begged your disciples to cast it out, and they could not."
41 Yesu anayankha kuti, “Haa! Anthu osakhulupirira ndi mʼbado wokhota. Kodi Ine ndidzakhala nanu nthawi yayitali yotani ndi kukupirirani? Bweretsa mwana wako kuno.”
Jesus answered, "Faithless and perverse generation, how long must I be with you and put up with you? Bring your son here."
42 Ngakhale pamene mnyamata amabwera kwa Yesu, chiwandacho chinamugwetsa pansi ndi kumugwedeza. Koma Yesu anadzudzula mzimu woyipawo nachiritsa mwa mnyamatayo ndi kumuperekanso kwa abambo ake.
While he was still coming, the demon threw him down and convulsed him violently. But Jesus rebuked the unclean spirit, and healed the boy, and gave him back to his father.
43 Ndipo iwo onse anadabwa ndi ukulu wa Mulungu. Aliyense akudabwa ndi zimene Yesu anachita, Iyeyo anati kwa ophunzira ake,
They were all astonished at the majesty of God. But while all were marveling at all the things which Jesus did, he said to his disciples,
44 “Tamvetsetsani zimene ndikufuna kukuwuzani: Mwana wa Munthu akupita kukaperekedwa mʼmanja mwa anthu.”
"Let these words sink into your ears, for the Son of Man will be delivered up into the hands of men."
45 Koma iwo sanazindikire zimene amatanthauza. Izi zinawadabwitsa kotero sanathe kuzimvetsa ndipo anaopa kumufunsa.
But they did not understand this saying. It was concealed from them, that they should not perceive it, and they were afraid to ask him about this saying.
46 Mkangano unayambika pakati pa ophunzira wa kuti wamkulu koposa akanakhala ndani mwa iwo.
There arose an argument among them about which of them was the greatest.
47 Yesu podziwa maganizo awo, anatenga kamwana nakayimika pambali pake.
Jesus, knowing the reasoning of their hearts, took a little child, and set him by his side,
48 Ndipo Iye anawawuza kuti, “Aliyense wolandira bwino kamwana aka mʼdzina langa, ndiye kuti akulandiranso bwino Ine; ndipo aliyense wolandira bwino Ine, ndiye kuti akulandiranso bwino amene anandituma Ine. Pakuti amene ndi wamngʼono pakati panu, ndiye amene ali wamkulu koposa.”
and said to them, "Whoever receives this little child in my name receives me. Whoever receives me receives him who sent me. For whoever is least among you all, this one is great."
49 Yohane anati, “Ambuye, ife tinaona munthu akutulutsa ziwanda mʼdzina lanu ndipo tinayesa kumuletsa, chifukwa iyeyo si mmodzi wa ife.”
John answered, "Master, we saw someone casting out demons in your name, and we forbade him, because he does not follow with us."
50 Yesu anati, “Wosamuletsa, pakuti amene satsutsana nanu ali mbali yanu.”
Jesus said to him, "Do not forbid him, for he who is not against you is for you."
51 Nthawi itayandikira yoti Iye atengedwe kupita kumwamba, Yesu anatsimikiza zopita ku Yerusalemu,
It came to pass, when the days were near that he should be taken up, he intently set his face to go to Jerusalem,
52 ndipo anatuma nthumwi kuti zitsogole. Iwo anapita mʼmudzi wa Asamariya kuti akonzekere kumulandira,
and sent messengers before his face. They went, and entered into a village of the Samaritans, so as to prepare for him.
53 koma anthu kumeneko sanamulandire chifukwa Iye ankapita ku Yerusalemu.
But they did not receive him, because he was traveling with his face set towards Jerusalem.
54 Ophunzira awa, Yohane ndi Yakobo ataona zimenezi, anafunsa kuti, “Ambuye, kodi mukufuna ife tiyitane moto kuchokera kumwamba kuti uwawononge?”
When his disciples, James and John, saw this, they said, "Lord, do you want us to command fire to come down from the sky, and consume them?"
55 Koma Yesu anatembenuka ndi kuwadzudzula,
And he turned and rebuked them, and said, "You do not realize what kind of Spirit you belong to.
56 ndipo iwo anapita ku mudzi wina.
For the Son of Man did not come to destroy people's lives, but to save them." And they went to another village.
57 Pamene iwo ankayenda mu msewu, munthu wina anati kwa Iye, “Inu ndikutsatirani kulikonse kumene mudzapita.”
As they went on the way, a certain man said to him, "I want to follow you wherever you go."
58 Yesu anayankha kuti, “Nkhandwe zili ndi mapanga ake, mbalame zili ndi zisa zake, koma Mwana wa Munthu alibe malo wogonekapo mutu wake.”
And Jesus said to him, "The foxes have holes, and the birds of the sky have nests, but the Son of Man has no place to lay his head."
59 Iye anati kwa wina, “Nditsate Ine.” Koma munthuyo anayankha kuti, “Ambuye, choyamba loleni ndipite kuti ndikayike maliro a abambo anga.”
He said to another, "Follow me." But he said, "Lord, allow me first to go and bury my father."
60 Yesu anati kwa iye, “Aleke akufa ayikane akufa okhaokha, koma iwe pita ukalalikire ufumu wa Mulungu.”
But Jesus said to him, "Leave the dead to bury their own dead, but you go and announce the Kingdom of God."
61 Koma winanso anati, “Ine ndidzakutsatani Ambuye; koma choyamba ndiloleni ndibwerere kuti ndikatsanzikane nalo banja langa.”
Another also said, "I want to follow you, Lord, but first allow me to bid farewell to those who are at my house."
62 Yesu anayankha kuti, “Munthu amene akulima ndi khasu lokokedwa nʼkumayangʼana mʼmbuyo, si woyenera kugwira ntchito mu ufumu wa Mulungu.”
But Jesus said to him, "No one, having put his hand to the plow, and looking back, is fit for the Kingdom of God."