< Luka 6 >
1 Tsiku lina la Sabata Yesu ankadutsa mʼminda yatirigu, ndipo ophunzira ake anayamba kubudula ngala zatirigu, namazifikisa mʼmanja mwawo ndi kumadya.
有一個安息日,耶穌從麥地經過。他的門徒掐了麥穗,用手搓着吃。
2 Ena mwa Afarisi anafunsa kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani mukuchita zosaloledwa pa tsiku la Sabata?”
有幾個法利賽人說:「你們為甚麼做安息日不可做的事呢?」
3 Yesu anawayankha iwo kuti, “Kodi simunawerenge zimene Davide anachita pamene iye ndi anzake anali ndi njala?
耶穌對他們說:「經上記着大衛和跟從他的人飢餓之時所做的事,連這個你們也沒有念過嗎?
4 Iye analowa mʼnyumba ya Mulungu ndipo atatenga buledi wopatulika anadya amene ndi ololedwa kudya ansembe okha. Ndipo anaperekanso wina kwa anzake.”
他怎麼進了上帝的殿,拿陳設餅吃,又給跟從的人吃?這餅除了祭司以外,別人都不可吃。」
5 Kenaka Yesu anawawuza kuti, “Mwana wa Munthu ndi Ambuye wa Sabata.”
又對他們說:「人子是安息日的主。」
6 La Sabata lina Iye analowa mʼsunagoge kukaphunzitsa ndipo mʼmenemo anapeza munthu wadzanja lolumala.
又有一個安息日,耶穌進了會堂教訓人,在那裏有一個人右手枯乾了。
7 Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo ankamuyangʼana kuti apeze chifukwa Yesu, choncho anamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati Iye akanamuchiritsa pa Sabata.
文士和法利賽人窺探耶穌,在安息日治病不治病,要得把柄去告他。
8 Koma Yesu anadziwa zimene ankaganiza ndipo anati kwa munthu wadzanja lolumalayo, “Tanyamuka ndipo uyime patsogolo pa onsewa.” Choncho iye ananyamuka nayima pamenepo.
耶穌卻知道他們的意念,就對那枯乾一隻手的人說:「起來!站在當中。」那人就起來,站着。
9 Kenaka Yesu anawawuza kuti, “Ndikufunseni, kodi chololedwa pa Sabata ndi chiti: kuchita chabwino kapena kuchita choyipa, kupulumutsa moyo kapena kuwononga?”
耶穌對他們說:「我問你們,在安息日行善行惡,救命害命,哪樣是可以的呢?」
10 Iye atawayangʼana onsewo, anati kwa munthuyo, “Wongola dzanja lako.” Iye anaterodi, ndipo dzanja lake linachiritsidwa.
他就周圍看着他們眾人,對那人說:「伸出手來!」他把手一伸,手就復了原。
11 Koma iwo anapsa mtima nayamba kukambirana wina ndi mnzake chomwe akanamuchitira Yesu.
他們就滿心大怒,彼此商議怎樣處治耶穌。
12 Tsiku lina, masiku amenewo, Yesu anapita ku phiri kukapemphera ndipo anakhala usiku wonse akupemphera kwa Mulungu.
那時,耶穌出去,上山禱告,整夜禱告上帝;
13 Kutacha, anayitana ophunzira ake ndipo anasankha khumi ndi awiri a iwo amene anawayika kukhala atumwi:
到了天亮,叫他的門徒來,就從他們中間挑選十二個人,稱他們為使徒。
14 Simoni (amene anamutcha Petro), mʼbale wake wa Andreya, Yakobo, Yohane, Filipo, Bartumeyu,
這十二個人有西門(耶穌又給他起名叫彼得),還有他兄弟安得烈,又有雅各和約翰,腓力和巴多羅買,
15 Mateyu, Tomasi, Yakobo mwana wa Alufeyo, Simoni amene amatchedwa Zaleti,
馬太和多馬,亞勒腓的兒子雅各和奮銳黨的西門,
16 Yudasi mwana wa Yakobo ndi Yudasi Isikarioti amene anamupereka.
雅各的兒子猶大,和賣主的加略人猶大。
17 Iye anatsika pamodzi ndi atumwiwo ndipo anayima pamalo athyathyathya. Gulu lalikulu la ophunzira ake, gulu lalikulu la anthu ochokera ku Yudeya konse, ku Yerusalemu ndi ochokera mʼmphepete mwa nyanja ya Turo ndi Sidoni anali pomwepo.
耶穌和他們下了山,站在一塊平地上;同站的有許多門徒,又有許多百姓,從猶太全地和耶路撒冷,並泰爾、西頓的海邊來,都要聽他講道,又指望醫治他們的病;
18 Iwo anabwera kudzamvetsera ndi kuchiritsidwa ku matenda awo. Osautsidwa ndi mizimu yoyipa anachiritsidwa,
還有被污鬼纏磨的,也得了醫治。
19 ndipo anthu ankayesetsa kuti amukhudze chifukwa mphamvu imatuluka mwa Iye ndi kuchiritsa onse.
眾人都想要摸他;因為有能力從他身上發出來,醫好了他們。
20 Akuyangʼana ophunzira ake, Iye anati, “Odala ndinu amene ndi osauka, chifukwa ufumu wa Mulungu ndi wanu.
耶穌舉目看着門徒,說: 你們貧窮的人有福了! 因為上帝的國是你們的。
21 Inu amene mukumva njala tsopano, ndinu odala chifukwa mudzakhutitsidwa. Inu amene mukulira tsopano, ndinu odala chifukwa mudzasekerera.
你們飢餓的人有福了! 因為你們將要飽足。 你們哀哭的人有福了! 因為你們將要喜笑。
22 Ndinu odala, anthu akamakudani, kukusalani ndi kukunyozani ndi kumayipitsa dzina lanu chifukwa cha Mwana wa Munthu.
「人為人子恨惡你們,拒絕你們,辱罵你們,棄掉你們的名,以為是惡,你們就有福了!
23 “Nthawi imeneyo sangalalani ndipo lumphani ndi chimwemwe chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu kumwamba. Pakuti ndi zomwezonso zimene makolo awo anachitira aneneri.
當那日,你們要歡喜跳躍,因為你們在天上的賞賜是大的。他們的祖宗待先知也是這樣。
24 “Ndinu atsoka, anthu olemera, popeza mwalandiriratu zokusangalatsani.
但你們富足的人有禍了! 因為你們受過你們的安慰。
25 Tsoka inu amene mukudya bwino tsopano, chifukwa mudzakhala ndi njala. Ndinu atsoka, amene mukusekerera tsopano, chifukwa mudzabuma ndi kulira.
你們飽足的人有禍了! 因為你們將要飢餓。 你們喜笑的人有禍了! 因為你們將要哀慟哭泣。
26 Ndinu atsoka, anthu akamakuyamikirani, popeza makolo anu anawachitira aneneri onama zomwezi.”
「人都說你們好的時候,你們就有禍了!因為他們的祖宗待假先知也是這樣。」
27 “Koma Ine ndikuwuza inu amene mukundimva: Kondani adani anu, chitirani zabwino amene amakudani.
「只是我告訴你們這聽道的人,你們的仇敵,要愛他!恨你們的,要待他好!
28 Dalitsani amene amakutembererani, apempherereni amene amakusautsani.
咒詛你們的,要為他祝福!凌辱你們的,要為他禱告!
29 Ngati wina akumenyani patsaya limodzi mupatseninso tsaya linalo. Ngati wina akulanda mwinjiro wako, umulole atenge ndi mkanjo omwe.
有人打你這邊的臉,連那邊的臉也由他打。有人奪你的外衣,連裏衣也由他拿去。
30 Mupatseni aliyense amene akupemphani kanthu ndipo ngati wina atenga chinthu chanu, musamulamule kuti akubwezereni.
凡求你的,就給他。有人奪你的東西去,不用再要回來。
31 Inu muwachitire anthu ena, zomwe mukanafuna kuti iwo akuchitireni.
你們願意人怎樣待你們,你們也要怎樣待人。
32 “Ngati mukonda okhawo amene amakukondani, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amakonda amene amawakondanso.
你們若單愛那愛你們的人,有甚麼可酬謝的呢?就是罪人也愛那愛他們的人。
33 Ndipo ngati muchita zabwino kwa amene ndi abwino kwa inu, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amachita izi.
你們若善待那善待你們的人,有甚麼可酬謝的呢?就是罪人也是這樣行。
34 Ndipo ngati mukongoza amene mukuyembekeza kuti abweza, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amabwereketsa kwa ochimwa anzawo, ndipo amayembekezera kubwezeredwa zonse.
你們若借給人,指望從他收回,有甚麼可酬謝的呢?就是罪人也借給罪人,要如數收回。
35 Koma kondani adani anu, achitireni zabwino, akongozeni koma osayembekezera kulandira kanthu. Pamenepo mphotho yanu idzakhala yayikulu ndipo inu mudzakhala ana a Wammwambamwamba, chifukwa ndi wokoma mtima kwa anthu osayamika ndi oyipa.
你們倒要愛仇敵,也要善待他們,並要借給人不指望償還,你們的賞賜就必大了,你們也必作至高者的兒子,因為他恩待那忘恩的和作惡的。
36 Khalani achifundo, monga momwe Atate anu ali achifundo.”
你們要慈悲,像你們的父慈悲一樣。」
37 “Musaweruze, ndipo inu simudzaweruzidwa. Musatsutse ndipo inu simudzatsutsidwa. Khululukirani ena ndipo mudzakhululukidwa.
「你們不要論斷人,就不被論斷;你們不要定人的罪,就不被定罪;你們要饒恕人,就必蒙饒恕 ;
38 Perekani ndipo mudzapatsidwa. Adzakupatsani mʼthumba mwanu muyeso wabwino, wotsenderezeka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Pakuti muyeso umene mumagwiritsa ntchito, ndi omwewo adzakuyeserani.”
你們要給人,就必有給你們的,並且用十足的升斗,連搖帶按,上尖下流地倒在你們懷裏;因為你們用甚麼量器量給人,也必用甚麼量器量給你們。」
39 Iye anawawuzanso fanizo ili, “Kodi munthu wakhungu angatsogolere munthu wakhungu mnzake? Kodi onse sadzagwera mʼdzenje?
耶穌又用比喻對他們說:「瞎子豈能領瞎子,兩個人不是都要掉在坑裏嗎?
40 Wophunzira sangapose mphunzitsi wake, koma yense amene waphunzitsidwa bwinobwino adzakhala ngati mphunzitsi wake.
學生不能高過先生;凡學成了的不過和先生一樣。
41 “Kodi ndi chifukwa chiyani mumaona kachitsotso mʼdiso la mʼbale wanu ndi kusasamala mtengo uli mʼdiso mwanu?
為甚麼看見你弟兄眼中有刺,卻不想自己眼中有樑木呢?
42 Kodi munganene bwanji kwa mʼbale wanu kuti, ‘Mʼbale nʼtakuchotsa kachitsotso mʼdiso mwako,’ pamene inu eni ake mukulephera kuona mtengo uli mʼdiso mwanu? Inu achiphamaso, yambani mwachotsa mtengo uli mʼdiso mwanu, ndipo kenaka mudzaona bwinobwino ndi kuchotsa kachitsotso mʼdiso la mʼbale wanu.”
你不見自己眼中有樑木,怎能對你弟兄說:『容我去掉你眼中的刺』呢?你這假冒為善的人!先去掉自己眼中的樑木,然後才能看得清楚,去掉你弟兄眼中的刺。」
43 Palibe mtengo wabwino umene umabala chipatso choyipa, kapena mtengo oyipa umene umabala chipatso chabwino.
「因為,沒有好樹結壞果子,也沒有壞樹結好果子。
44 Mtengo uliwonse umadziwika ndi chipatso chake. Anthu sathyola nkhuyu pa mtengo waminga, kapena mphesa pa nthungwi.
凡樹木看果子,就可以認出它來。人不是從荊棘上摘無花果,也不是從蒺藜裏摘葡萄。
45 Munthu wabwino amatulutsa zinthu zabwino zosungidwa mu mtima mwake, koma munthu oyipa amatulutsa zinthu zoyipa zosungidwa mu mtima mwake. Pakamwa pake pamayankhula zimene zadzaza mu mtima mwake.
善人從他心裏所存的善就發出善來;惡人從他心裏所存的惡就發出惡來;因為心裏所充滿的,口裏就說出來。」
46 “Kodi nʼchifukwa chiyani munditchula kuti, ‘Ambuye, Ambuye’ koma simuchita zimene Ine ndinena?
「你們為甚麼稱呼我『主啊,主啊』卻不遵我的話行呢?
47 Ine ndidzakuonetsani mmene alili munthu amene amabwera kwa Ine ndi kumva mawu anga ndi kuwachita.
凡到我這裏來,聽見我的話就去行的,我要告訴你們他像甚麼人:
48 Iye ali ngati munthu womanga nyumba, amene anakumba mozama nayika maziko ake pa mwala. Madzi osefukira atabwera ndi mphamvu, nawomba nyumbayo koma sinagwedezeka, chifukwa anayimanga bwino.
他像一個人蓋房子,深深地挖地,把根基安在磐石上;到發大水的時候,水沖那房子,房子總不能搖動,因為根基立在磐石上 。
49 Koma amene amamva mawu anga koma osawachita, akufanana ndi munthu amene anamanga nyumba yake koma yopanda maziko. Nthawi yomwe madziwo anawomba nyumbayo, inagwa ndipo inawonongekeratu.”
惟有聽見不去行的,就像一個人在土地上蓋房子,沒有根基;水一沖,隨即倒塌了,並且那房子壞的很大。」