< Luka 5 >

1 Tsiku lina Yesu anayima mʼmbali mwa nyanja ya Genesareti, gulu la anthu litamuzungulira likumvetsera mawu a Mulungu.
و هنگامی که گروهی بر وی ازدحام می نمودند تا کلام خدا را بشنوند، او به کناردریاچه جنیسارت ایستاده بود.۱
2 Iye anaona mabwato awiri ali mʼmphepete mwa nyanja, asodzi amene ankachapa makhoka awo atawasiya pamenepo.
و دو زورق رادر کنار دریاچه ایستاده دید که صیادان از آنهابیرون آمده، دامهای خود را شست و شومی نمودند.۲
3 Iye analowa mʼbwato limodzi limene linali la Simoni, ndi kumupempha kuti alikankhire mʼkati mwa nyanja pangʼono. Kenaka Iye anakhala pansi nayamba kuphunzitsa anthu ali mʼbwatomo.
پس به یکی از آن دو زورق که مال شمعون بود سوار شده، از او درخواست نمود که از خشکی اندکی دور ببرد. پس در زورق نشسته، مردم را تعلیم می‌داد.۳
4 Atatha kuyankhula anati kwa Simoni, “Kankhirani kwa kuya ndipo muponye makhoka kuti mugwire nsomba.”
و چون از سخن‌گفتن فارغ شد، به شمعون گفت: «به میانه دریاچه بران و دامهای خود رابرای شکار بیندازید.»۴
5 Simoni anayankha kuti, “Ambuye, tagwira ntchito molimbika usiku wonse, koma sitinagwire kanthu. Koma pakuti mwatero, ndiponya makhoka.”
شمعون در جواب وی گفت: «ای استاد، تمام شب را رنج برده چیزی نگرفتیم، لیکن به حکم تو، دام را خواهیم انداخت.»۵
6 Atachita izi, anagwira nsomba zambiri kotero kuti makhoka awo anayamba kungʼambika.
و چون چنین کردند، مقداری کثیر ازماهی صید کردند، چنانکه نزدیک بود دام ایشان گسسته شود.۶
7 Choncho anakodola anzawo a bwato linalo kuti abwere ndi kuwathandiza, ndipo anabwera nadzaza mabwato onse awiri mpaka kuyamba kumira.
و به رفقای خود که در زورق دیگربودند اشاره کردند که آمده ایشان را امداد کنند. پس آمده هر دو زورق را پر کردند بقسمی که نزدیک بود غرق شوند.۷
8 Simoni Petro ataona izi, anagwa pa mawondo a Yesu nati, “Chokani kwa ine Ambuye: Ine ndine munthu wochimwa!”
شمعون پطرس چون این را بدید، بر پایهای عیسی افتاده، گفت: «ای خداوند از من دور شو زیرا مردی گناهکارم.»۸
9 Iye ndi anzake onse anadabwa ndi nsomba zimene anagwira,
چونکه به‌سبب صیدماهی که کرده بودند، دهشت بر او و همه رفقای وی مستولی شده بود.۹
10 chimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, anzake a Simoniyo. Kenaka Yesu anati kwa Simoni, “Musachite mantha; kuyambira tsopano ndidzakusandutsani asodzi a anthu.”
و هم چنین نیز بریعقوب و یوحنا پسران زبدی که شریک شمعون بودند. عیسی به شمعون گفت: «مترس. پس از این مردم را صید خواهی کرد.»۱۰
11 Kenaka anakokera mabwato awo ku mtunda, nasiya zonse namutsata Iye.
پس چون زورقهارا به کنار آوردند همه را ترک کرده، از عقب اوروانه شدند.۱۱
12 Yesu ali ku mudzi wina, munthu amene anali ndi khate thupi lonse anabwera kwa Iye. Munthuyo ataona Yesu, anagwa chafufumimba ndipo anamupempha Iye kuti, “Ambuye, ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”
و چون او در شهری از شهرها بود ناگاه مردی پر از برص آمده، چون عیسی را بدید، به روی در‌افتاد و از او درخواست کرده، گفت: «خداوندا، اگر خواهی می‌توانی مرا طاهرسازی.»۱۲
13 Yesu anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo. Iye anati, “Ine ndikufuna, yeretsedwa!” Ndipo nthawi yomweyo khate lake linachoka.
پس او دست آورده، وی را لمس نمود و گفت: «می‌خواهم. طاهر شو.» که فور برص از او زایل شد.۱۳
14 Kenaka Yesu anamulamula kuti, “Usawuze wina aliyense, koma pita, kadzionetse kwa wansembe ndi kukapereka nsembe zimene Mose anakulamulirani za kuyeretsedwa kwanu monga umboni kwa iwo.”
و او را قدغن کرد که «هیچ‌کس را خبر مده، بلکه رفته خود را به کاهن بنما و هدیه‌ای بجهت طهارت خود، بطوری که موسی فرموده است، بگذران تا بجهت ایشان شهادتی شود.»۱۴
15 Koma mbiri yake inafalikirabe kwambiri kotero kuti magulu a anthu anabwera kudzamvetsera ndi kuti achiritsidwe ku matenda awo.
لیکن خبر او بیشتر شهرت یافت و گروهی بسیار جمع شدند تا کلام او رابشنوند و از مرضهای خود شفا یابند،۱۵
16 Koma Yesu nthawi zambiri ankachoka kupita ku malo a yekha kukapemphera.
و او به ویرانه‌ها عزلت جسته، به عبادت مشغول شد.۱۶
17 Tsiku lina pamene ankaphunzitsa, Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo, amene anachokera ku midzi yonse ya Galileya ndi ku Yudeya ndi Yerusalemu, anakhala pansi pomwepo. Ndipo mphamvu ya Ambuye inalipo yakuti Iye achiritse odwala.
روزی از روزها واقع شد که او تعلیم می‌دادو فریسیان و فقها که از همه بلدان جلیل و یهودیه و اورشلیم آمده، نشسته بودند وقوت خداوندبرای شفای ایشان صادر می‌شد،۱۷
18 Amuna ena anabwera atanyamula munthu wofa ziwalo pa mphasa ndipo anayesa kumulowetsa mʼnyumba kuti amugoneke pamaso pa Yesu.
که ناگاه چندنفر شخصی مفلوج را بر بستری آوردند ومی خواستند او را داخل کنند تا پیش روی وی بگذارند.۱۸
19 Atalephera kupeza njira yochitira zimenezi chifukwa cha gulu la anthu, anakwera naye pa denga ali pa mphasa pomwepo ndi kumutsitsira mʼkati pakati pa gulu la anthu, patsogolo penipeni pa Yesu.
و چون به‌سبب انبوهی مردم راهی نیافتند که او را به خانه درآورند بر پشت بام رفته، او را با تختش از میان سفالها در وسط پیش عیسی گذاردند.۱۹
20 Yesu ataona chikhulupiriro chawo, anati, “Mnzanga, machimo ako akhululukidwa.”
چون او ایمان ایشان را دید، به وی گفت: «ای مرد، گناهان تو آمرزیده شد.»۲۰
21 Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo anayamba kuganiza mwa iwo okha kuti, “Kodi munthu uyu ndi ndani amene ayankhula zamwano? Kodi ndani amene angakhululukire machimo kupatula Mulungu?”
آنگاه کاتبان و فریسیان در خاطر خود تفکرنموده، گفتن گرفتند: «این کیست که کفر می‌گوید. جز خدا و بس کیست که بتواند گناهان رابیامرزد؟»۲۱
22 Yesu anadziwa zomwe iwo amaganiza ndipo anafunsa kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani mukuganiza zimenezi mʼmitima mwanu?
عیسی افکار ایشان را درک نموده، در جواب ایشان گفت: «چرا در خاطر خود تفکرمی کنید؟۲۲
23 Kodi chapafupi ndi chiti: kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Nyamuka ndipo yenda?’”
کدام سهلتر است، گفتن اینکه گناهان تو آمرزیده شد، یا گفتن اینکه برخیز و بخرام؟۲۳
24 Koma kuti inu mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko lapansi wokhululukira machimo, Iye anati kwa munthu wofa ziwaloyo, “Ine ndikuwuza iwe kuti, ‘Imirira, nyamula mphasa ndipo uzipita kwanu.’”
لیکن تا بدانید که پسر انسان را استطاعت آمرزیدن گناهان بر روی زمین هست، مفلوج راگفت، تو را می‌گویم برخیز و بستر خود رابرداشته، به خانه خود برو.»۲۴
25 Nthawi yomweyo anayimirira patsogolo pawo, nanyamula mphasa yake ndipo anapita kwawo akuyamika Mulungu.
در ساعت برخاسته، پیش ایشان آنچه بر آن خوابیده بودبرداشت و به خانه خود خدا را حمدکنان روانه شد.۲۵
26 Aliyense anadabwa ndi kuchita mantha ndipo anayamika Mulungu. Iwo anadabwa kwambiri ndipo anati, “Lero taona zinthu zosayiwalika.”
و حیرت همه را فرو گرفت و خدا راتمجید می‌نمودند و خوف بر ایشان مستولی شده، گفتند: «امروز چیزهای عجیب دیدیم.»۲۶
27 Zitatha izi, Yesu anachoka ndipo anaona wolandira msonkho dzina lake Levi atakhala mʼnyumba ya msonkho. Yesu anati kwa iye, “Nditsate Ine.”
از آن پس بیرون رفته، باجگیری را که لاوی نام داشت، بر باجگاه نشسته دید. او را گفت: «از عقب من بیا.»۲۷
28 Ndipo Levi anayimirira, nasiya zonse ndi kumutsata Iye.
در حال همه‌چیز را ترک کرده، برخاست و در عقب وی روانه شد.۲۸
29 Kenaka Levi anakonzera Yesu phwando lalikulu ku nyumba yake ndipo gulu lalikulu la amisonkho ndi ena ankadya naye pamodzi.
و لاوی ضیافتی بزرگ در خانه خود برای او کرد و جمعی بسیار از باجگیران و دیگران با ایشان نشستند.۲۹
30 Koma Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo amene anali a gulu lawo anadandaula kwa ophunzira ake, “Kodi ndi chifukwa chiyani mukudya ndi kumwa pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?”
اما کاتبان ایشان و فریسیان همهمه نموده، به شاگردان او گفتند: «برای چه با باجگیران وگناهکاران اکل و شرب می‌کنید؟»۳۰
31 Yesu anawayankha kuti, “Amene sakudwala safuna singʼanga, koma odwala.
عیسی درجواب ایشان گفت: «تندرستان احتیاج به طبیب ندارند بلکه مریضان.۳۱
32 Ine sindinabwere kudzayitana olungama, koma ochimwa kuti atembenuke mtima.”
و نیامده‌ام تا عادلان بلکه تا عاصیان را به توبه بخوانم.»۳۲
33 Iwo anati kwa Iye, “Ophunzira a Yohane amasala kudya ndi kupemphera kawirikawiri, monganso ophunzira a Afarisi, koma anu amangodya ndi kumwa.”
پس به وی گفتند: «از چه سبب شاگردان یحیی روزه بسیار می‌دارند و نماز می‌خوانند وهمچنین شاگردان فریسیان نیز، لیکن شاگردان تواکل و شرب می‌کنند.»۳۳
34 Yesu anawayankha kuti, “Kodi alendo a mkwati angasale kudya pamene mkwati ali pakati pawo?
بدیشان گفت: «آیامی توانید پسران خانه عروسی را مادامی که دامادبا ایشان است روزه‌دار سازید؟۳۴
35 Koma nthawi ikubwera pamene mkwati adzachotsedwa pakati pawo. Masiku amenewo adzasala kudya.”
بلکه ایامی می‌آید که داماد از ایشان گرفته شود، آنگاه در آن روزها روزه خواهند داشت.»۳۵
36 Iye anawawuza fanizo ili: “Palibe amene amangʼamba chigamba kuchokera pa chovala chatsopano ndi kuchisokerera pa chakale. Ngati atatero, ndiye kuti adzangʼamba chovala chatsopanocho, ndipo chigamba chochokera pa chovala chatsopano chija sichidzagwirizana ndi chakale.
و مثلی برای ایشان آورد که «هیچ‌کس پارچه‌ای از جامه نو را بر جامه کهنه وصله نمی کند والا آن نو را پاره کند و وصله‌ای که از نوگرفته شد نیز در خور آن کهنه نبود.۳۶
37 Ndipo palibe amene amakhuthulira vinyo watsopano mʼmatumba a vinyo akale. Ngati atatero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa zikopazo, vinyo adzatayika ndipo zikopa za vinyozo zidzawonongeka.
و هیچ‌کس شراب نو را در مشکهای کهنه نمی ریزد والاشراب نو، مشکها را پاره می‌کند و خودش ریخته و مشکها تباه می‌گردد.۳۷
38 Ayi, vinyo watsopano ayenera kuthiridwa mʼmatumba a vinyo azikopa zatsopano.
بلکه شراب نو را درمشکهای نو باید ریخت تا هر دو محفوظ بماند.۳۸
39 Ndipo palibe amene atamwa vinyo wakale amafuna watsopano, pakuti amati, ‘Wakale ndi okoma.’”
و کسی نیست که چون شراب کهنه را نوشیده فی الفور نو را طلب کند، زیرا می‌گوید کهنه بهتراست.»۳۹

< Luka 5 >