< Luka 22 >
1 Phwando la buledi wopanda yisiti lotchedwa Paska litayandikira,
Men de usyrede Brøds Højtid, som kaldes Paaske, nærmede sig.
2 akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo amafunafuna mpata woti amuphere Yesu, pakuti ankachita mantha ndi anthu.
Og Ypperstepræsterne og de skriftkloge søgte, hvorledes de kunde slaa ham ihjel; thi de frygtede for Folket.
3 Kenaka Satana analowa mwa Yudasi, wotchedwa Isikarioti, mmodzi wa khumi ndi a iwiriwo.
Men Satan gik ind i Judas, som kaldes Iskariot og var en af de tolv.
4 Ndipo Yudasi anapita kwa akulu a ansembe ndi akulu oyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndi kukambirana nawo za mmene iye angaperekere Yesu.
Og han gik hen og talte med Ypperstepræsterne og Høvedsmændene om, hvorledes han vilde forraade ham til dem.
5 Iwo anakondwa ndipo anagwirizana zomupatsa ndalama.
Og de bleve glade og lovede at give ham Penge.
6 Iye anavomera, ndipo anayamba kufunafuna mpata wabwino wakuti amupereke Yesu kwa iwo pamene panalibe gulu la anthu pafupi.
Og han tilsagde det; og han søgte Lejlighed til at forraade ham til dem uden Opløb.
7 Kenaka linafika tsiku la buledi wopanda yisiti pamene mwana wankhosa wa Paska amaperekedwa nsembe.
Men de usyrede Brøds Dag kom, paa hvilken man skulde slagte Paaskelammet.
8 Yesu anatuma Petro ndi Yohane nati, “Pitani kukatikonzera Paska kuti tikadye.”
Og han udsendte Peter og Johannes og sagde: „Gaar hen og bereder os Paaskelammet, at vi kunne spise det.”
9 Iwo anafunsa kuti, “Kodi mukufuna tikakonzere kuti?”
Men de sagde til ham: „Hvor vil du, at vi skulle berede det?”
10 Iye anayankha kuti, “Taonani, mukamalowa mu mzinda, mudzakumana ndi mwamuna atanyamula mtsuko wamadzi. Mulondoleni ku nyumba imene akalowe,
Men han sagde til dem: „Se, naar I ere komne ind i Staden, skal der møde eder en Mand, som bærer en Vandkrukke; følger ham til Huset, hvor han gaar ind,
11 ndipo mukamuwuze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi kufunsa kuti, chili kuti chipinda cha alendo, kumene Ine ndi ophunzira anga tikadyere Paska?’
og I skulle sige til Husbonden i Huset: Mesteren siger: Hvor er det Herberge, hvor jeg kan spise Paaskelammet med mine Disciple?
12 Iyeyo adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokhala ndi zonse. Kachiteni zokonzekera mʼmenemo.”
Og han skal vise eder en stor Sal opdækket; der skulle I berede det.”
13 Iwo anapita nakapeza zinthu monga mmene Yesu anawawuzira. Tsono anakonza Paska.
Og de gik hen og fandt det saaledes, som han havde sagt dem; og de beredte Paaskelammet.
14 Ora litakwana, Yesu ndi ophunzira ake anakhala pa tebulo.
Og da Timen kom, satte han sig til Bords, og Apostlene med ham.
15 Ndipo Iye anawawuza kuti, “Ine ndakhala ndikuyembekezera kudya Paska uyu ndi inu ndisanamve zowawa.
Og han sagde til dem: „Jeg har hjerteligt længtes efter at spise dette Paaskelam med eder, førend jeg lider.
16 Pakuti Ine ndikukuwuzani kuti sindidzadyanso Paska wina mpaka Paskayi itakwaniritsidwa mu ufumu wa Mulungu.”
Thi jeg siger eder, at jeg skal ingen Sinde mere spise det, førend det bliver fuldkommet i Guds Rige.”
17 Atanyamula chikho, Iye anayamika ndipo anati, “Tengani ndipo patsiranani pakati panu.
Og han tog en Kalk, takkede og sagde: „Tager dette, og deler det imellem eder!
18 Pakuti ndikukuwuzani kuti, Ine sindidzamwanso zochokera ku chipatso cha mphesa mpaka ufumu wa Mulungu utabwera.”
Thi jeg siger eder, at fra nu af skal jeg ikke drikke af Vintræets Frugt, førend Guds Rige kommer.”
19 Ndipo Iye anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema, nagawira iwo nati, “Ili ndi thupi langa lomwe laperekedwa kwa inu; muzichita zimenezi pokumbukira Ine.”
Og han tog Brød, takkede og brød det og gav dem det og sagde: „Dette er mit Legeme, det, som gives for eder; gører dette til min Ihukommelse!”
20 Chimodzimodzinso, utatha mgonero, anatenga chikho nati, “Chikho ichi ndi pangano latsopano la magazi anga, amene akhetsedwa chifukwa cha inu.
Ligesaa tog han ogsaa Kalken efter Aftensmaaltidet og sagde: „Denne Kalk er den nye Pagt i mit Blod, det, som udgydes for eder.
21 Koma dzanja la amene akundipereka Ine lili pamodzi ndi langa pa chakudya pano.
Men se, hans Haand, som forraader mig, er her paa Bordet hos mig.
22 Mwana wa Munthu apita monga mmene zinalembedwera, koma tsoka kwa munthu amene amupereka Iye.”
Thi Menneskesønnen gaar bort, som det er beskikket; dog ve det Menneske, ved hvem han bliver forraadt!”
23 Iwo anayamba kufunsana pakati pawo kuti ndi ndani wa iwo amene akanachita ichi.
Og de begyndte at spørge hverandre indbyrdes om, hvem af dem det dog kunde være, som skulde gøre dette.
24 Komanso mkangano unabuka pakati pawo kuti ndani mwa iwo amene amaganiziridwa kukhala wamkulu.
Men der opstod ogsaa en Trætte iblandt dem om, hvem af dem der maatte synes at være den største.
25 Yesu anawawuza kuti, “Mafumu a anthu a mitundu ina amaonetsa mphamvu za ufumu wawo pa anthuwo; ndipo amene ali ndi ulamuliro, amapatsidwa dzina la kuti ‘Opindula.’
Men han sagde til dem: „Folkenes Konger herske over dem, og de, som bruge Myndighed over dem, kaldes deres Velgørere.
26 Koma inu simuyenera kukhala choncho. Mʼmalo mwake, wamkulu pakati panu akhale ngati wamngʼono pa onse, ndipo iye amene alamulira akhale ngati wotumikira.
I derimod ikke saaledes; men den ældste iblandt eder blive som den yngste, og Føreren som den, der tjener.
27 Pakuti wamkulu ndani, iye amene ali pa tebulo kapena iye amene akutumikira? Kodi si iye amene ali pa tebulo? Koma ndili pakati panu ngati mmodzi wokutumikirani.
Thi hvem er størst: den, som sidder til Bords? eller den, som tjener? Mon ikke den, som sidder til Bords? Men jeg er iblandt eder som den, der tjener.
28 Inu ndinu amene mwayima nane mʼmayesero.
Men I ere de, som have holdt ud med mig i mine Fristelser.
29 Ndipo Ine ndikupatsani inu ufumu, monga momwe Atate anga anandipatsiranso Ine,
Og ligesom min Fader har tildelt mig Kongedømme, tildeler jeg eder
30 kuti inu muthe kudya ndi kumwa pa tebulo langa mu ufumu wanga ndi kukhala pa mipando yaufumu kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israeli.”
at skulle spise og drikke ved mit Bord i mit Rige og sidde paa Troner og dømme Israels tolv Stammer.”
31 “Simoni, Simoni, Satana wapempha kuti akupete ngati tirigu.
Men Herren sagde: „Simon, Simon! se, Satan begærede eder for at sigte eder som Hvede.
32 Koma Ine ndakupempherera Simoni, kuti chikhulupiriro chako chisafowoke ndipo pamene udzabwerera kwa Ine, udzalimbikitse abale ako.”
Men jeg bad for dig, at din Tro ikke skal svigte; og naar du engang omvender dig, da styrk dine Brødre!”
33 Koma iye anayankha kuti, “Ambuye, ndine wokonzeka kupita nanu ku ndende ndi kufa komwe.”
Men han sagde til ham: „Herre! jeg er rede til at gaa med dig baade i Fængsel og i Døden.”
34 Yesu anayankha kuti, “Ine ndikukuwuza Petro, tambala asanalire lero lino, udzandikana katatu kuti sukundidziwa Ine.”
Men han sagde: „Peter! jeg siger dig: Hanen skal ikke gale i Dag, førend du tre Gange har nægtet, at du kender mig.”
35 Kenaka Yesu anawafunsa iwo kuti, “Ine nditakutumizani wopanda chikwama cha ndalama, thumba kapena nsapato, kodi inu munasowa kanthu?” Iwo anayankha kuti, “Palibe chimene tinasowa.”
Og han sagde til dem: „Da jeg udsendte eder uden Pung og Taske og Sko, manglede I da noget?” Og de sagde: „Intet.”
36 Iye anawawuza kuti, “Koma tsopano ngati muli ndi chikwama cha ndalama, chitengeni, ndiponso thumba. Ndipo ngati mulibe lupanga, gulitsani mkanjo wanu ndi kugula.
Men han sagde til dem: „Men nu, den, som har en Pung, tage den med, ligesaa ogsaa en Taske; og den, som ikke har noget Sværd, sælge sin Kappe og købe et!
37 Zalembedwa kuti, ‘Ndipo Iye anawerengedwa pamodzi ndi anthu ochimwa,’ ndipo Ine ndikuwuzani kuti izi ziyenera kukwaniritsidwa mwa Ine. Inde, zimene zinalembedwa za Ine, zikukwaniritsidwa.”
Thi jeg siger eder: Det, som er skrevet, bør opfyldes paa mig, dette: „Og han blev regnet iblandt Overtrædere;” thi ogsaa med mig har det en Ende.”
38 Ophunzira anati, “Taonani Ambuye, awa malupanga awiri.” Iye anayankha kuti, “Amenewa akwanira.”
Men de sagde: „Herre! se, her ere to Sværd.” Men han sagde til dem: „Det er nok.”
39 Yesu anapitanso monga mwa masiku onse ku Phiri la Olivi, ndipo ophunzira ake anamutsatira Iye.
Og han gik ud og gik efter sin Sædvane til Oliebjerget; men ogsaa Disciplene fulgte ham.
40 Atafika pamalopo, Iye anawawuza kuti, “Pempherani kuti musagwe mʼmayesero.”
Men da han kom til Stedet, sagde han til dem: „Beder om ikke at falde i Fristelse.”
41 Iye anapita patsogolo pangʼono patali ngati kuponya mwala, anagwada napephera kuti,
Og han rev sig løs fra dem, saa meget som et Stenkast, og faldt paa Knæ, bad og sagde:
42 “Atate ngati mukufuna chotsereni chikho ichi. Komatu muchite zimene mukufuna osati zimene ndikufuna ine.”
„Fader, vilde du dog tage denne Kalk fra mig! dog ske ikke min Villie, men din!”
43 Mngelo wochokera kumwamba anafika namulimbikitsa.
Men en Engel fra Himmelen viste sig for ham og styrkede ham.
44 Ndipo mopsinjika mtima, anapemphera moona mtima, ndipo thukuta lake linali ngati madontho a magazi akugwera pansi.
Og da han var i Dødsangest, bad han heftigere; men hans Sved blev som Blodsdraaber, der faldt ned paa Jorden.
45 Iye atamaliza kupemphera, ndi kubwerera kwa ophunzira ake, anawapeza atagona atafowoka ndi chisoni.
Og da han stod op fra Bønnen og kom til Disciplene, fandt han dem sovende af Bedrøvelse.
46 Iye anafunsa kuti, Nʼchifukwa chiyani mukugona? “Dzukani ndipo pempherani kuti inu musagwe mʼmayesero.”
Og han sagde til dem: „Hvorfor sove I? Staar op og beder, for at I ikke skulle falde i Fristelse.”
47 Pamene Iye ankayankhulabe, gulu la anthu linabwera, ndipo munthu wotchedwa Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo analitsogolera. Iye anamuyandikira Yesu kuti amupsompsone.
Medens han endnu talte, se, da kom der en Skare; og han, som hed Judas, en af de tolv, gik foran dem og nærmede sig til Jesus for at kysse ham.
48 Koma Yesu anamufunsa kuti, “Yudasi, kodi ukupereka Mwana wa Munthu ndi mpsopsono?”
Men Jesus sagde til ham: „Judas! forraader du Menneskesønnen med et Kys?”
49 Otsatira Yesu ataona zimene zimati zichitike, anati, “Ambuye, kodi timenyane ndi malupanga athu?”
Men da de, som vare omkring ham, saa, hvad der vilde ske, sagde de: „Herre! skulle vi slaa til med Sværd?”
50 Ndipo mmodzi wa iwo anatema wantchito wamkulu wa ansembe, nadula khutu lake lamanja.
Og en af dem slog Ypperstepræstens Tjener og afhuggede hans højre Øre.
51 Koma Yesu anayankha kuti, “Zisachitikenso zimenezi!” Ndipo Iye anakhudza khutu la munthuyo ndi kumuchiritsa.
Men Jesus tog til Orde og sagde: „Lad dem gøre ogsaa dette!” Og han rørte ved hans Øre og lægte ham.
52 Kenaka Yesu anafunsa akulu a ansembe, akuluakulu oyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndi akuluakulu ena amene anabwerawo kuti, “Kodi Ine ndikutsogolera gulu lowukira kuti mubwere ndi malupanga ndi zibonga?
Men Jesus sagde til Ypperstepræsterne og Høvedsmændene for Helligdommen og de Ældste, som vare komne til ham: „I ere gaaede ud som imod en Røver med Sværd og Knipler.
53 Tsiku lililonse ndinali nanu mʼmabwalo a mʼNyumba ya Mulungu ndipo inu simunandigwire. Koma iyi ndi nthawi yanu pamene mdima ukulamulira.”
Da jeg var daglig hos eder i Helligdommen, udrakte I ikke Hænderne imod mig; men dette er eders Time og Mørkets Magt.”
54 Pamenepo anamugwira Iye, napita naye ndipo anamutengera ku nyumba ya mkulu wa ansembe. Petro anamutsatira patali.
Og de grebe ham og førte ham bort og bragte ham ind i Ypperstepræstens Hus; men Peter fulgte efter i Frastand.
55 Koma pamene anasonkha moto pakati pa bwalo la milandu, anakhala onse pansi ndipo Petro anakhalanso pansi.
Og de tændte en Ild midt i Gaarden og satte sig sammen, og Peter sad midt iblandt dem.
56 Mtsikana wantchito anamuona atakhala nawo pafupi ndi moto. Iye anamuyangʼanitsitsa ndipo anati, “Munthu uyu anali ndi Yesu.”
Men en Pige saa ham sidde i Lysskæret og stirrede paa ham og sagde: „Ogsaa denne var med ham.”
57 Koma Petro anakana nati, “Mtsikana, ine sindimudziwa ameneyu.”
Men han fornægtede ham og sagde: „Jeg kender ham ikke, Kvinde!”
58 Patatha kanthawi pangʼono, wina wake anamuona ndipo anati, “Iwenso ndiwe mmodzi mwa iwo.” Petro anayankha kuti, “Munthu iwe, ayi sindine.”
Og lidt derefter saa en anden ham og sagde: „Ogsaa du er en af dem.” Men Peter sagde: „Menneske! det er jeg ikke.”
59 Patatha pafupifupi ora limodzi, munthu winanso anati, “Zoonadi, munthu uyu anali ndi Iye, pakuti ndi mu Galileya.”
Og omtrent en Time derefter forsikrede en anden det og sagde: „I Sandhed, ogsaa denne var med ham; han er jo ogsaa en Galilæer.”
60 Petro anayankha kuti, “Munthu iwe, sindikudziwa zimene ukunena apa.” Pamene iye ankayankhula, tambala analira.
Men Peter sagde: „Menneske! jeg forstaar ikke, hvad du siger.” Og straks, medens han endnu talte, galede Hanen.
61 Ambuye anachewuka namuyangʼanitsitsa Petro. Pamenepo Petro anakumbukira mawu amene Ambuye anayankhula kwa iye kuti, “Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.”
Og Herren vendte sig og saa paa Peter; og Peter kom Herrens Ord i Hu, hvorledes han havde sagt til ham: „Førend Hanen galer i Dag, skal du fornægte mig tre Gange.”
62 Ndipo iye anapita panja nakalira kwambiri.
Og han gik udenfor og græd bitterligt.
63 Anthu amene ankalonda Yesu anayamba kumuchita chipongwe ndi kumumenya.
Og de Mænd, som holdt Jesus, spottede ham og sloge ham;
64 Anamumanga mʼmaso ndi kumufunsa kuti, “Tanenera! Wakumenya iwe ndi ndani?”
og de kastede et Klæde over ham og spurgte ham og sagde: „Profetér! hvem var det, som slog dig?”
65 Ndipo iwo anamunena zachipongwe zambiri.
Og mange andre Ting sagde de spottende til ham.
66 Kutacha, bungwe la akuluakulu, pamodzi ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, anakumana pamodzi, ndipo anamuyika Yesu patsogolo pawo.
Og da det blev Dag, samlede Folkets Ældste sig og Ypperstepræsterne og de skriftkloge, og de førte ham hen for deres Raad
67 Iwo anati, “Tiwuze, ngati ndiwe Khristu.” Yesu anayankha kuti, “Ine nditakuwuzani simungandikhulupirire.
og sagde: „Er du Kristus, da sig os det!” Men han sagde til dem: „Siger jeg eder det, tro I det ikke.
68 Ine nditakufunsani inu, simungandiyankhe.
Og om jeg spørger, svare I mig ikke, ej heller løslade I mig.
69 Koma kuyambira tsopano, Mwana wa Munthu adzakhala ku dzanja lamanja la Mulungu wamphamvu.”
Men fra nu af skal Menneskesønnen sidde ved Guds Krafts højre Haand.”
70 Onse anafunsa kuti, “Ndiye kuti ndiwe Mwana wa Mulungu?” Iye anayankha kuti, “Mwanena ndinu kuti Ndine.”
Men de sagde alle: „Er du da Guds Søn?” Og han sagde til dem: „I sige det; jeg er det.”
71 Pamenepo iwo anati, “Nanga tikufuniranjinso umboni wina? Ife tamva kuchokera pa milomo yake.”
Men de sagde: „Hvad have vi længere Vidnesbyrd nødig? vi have jo selv hørt det af hans Mund!”