< Luka 16 >

1 Yesu anawuza ophunzira ake kuti, “Panali munthu wina wachuma amene kapitawo wake anzake anamuneneza kuti amawononga chuma chakecho.
And he said also to the disciples, There was a certain rich man, who had a steward; and the same was accused to him as wasting his goods.
2 Choncho anamuyitana ndi kumufunsa kuti, ‘Kodi nʼchiyani chimene ndikumva za iwe? Pereka tsatanetsatane wa ntchito yako, pakuti supitirizanso kukhala kapitawo wanga.’
And he called him, and said to him, What is this that I hear of thee? Give an account of thy stewardship; for thou canst be no longer steward.
3 “Kapitawoyo analingalira kuti, ‘Kodi tsopano ndidzachita chiyani? Bwana wanga andichotsa ntchito. Ine ndilibe mphamvu zokwanira zolimira, komanso ine ndimachita manyazi kupempha.
Then the steward said within himself, What shall I do, now that my lord taketh away from me the stewardship? I cannot dig, I am ashamed to beg.
4 Ine ndikudziwa chimene ndidzachita kotero kuti, pamene ntchito yanga yatha pano, anthu adzandilandire mʼnyumba zawo.’
I am resolved what to do, that, when I am put out of the stewardship, I may be received into their houses.
5 “Choncho iye anayitana aliyense amene anali ndi ngongole kwa bwana wake. Iye anafunsa woyamba, ‘Kodi uli ndi ngongole yotani kwa bwana wanga?’
So he called to him every one of his lord's debtors, and said to the first, How much dost thou owe my lord?
6 “Iye anayankha kuti, ‘Migolo yamafuta a olivi 800.’ “Kapitawo uja anamuwuza iye, ‘Tenga pamene unalemba ngongole yakoyo, khala pansi msanga ndipo lemba kuti ndi migolo 400.’
And he said, A hundred measures of oil. And he said to him, Take thy bond, and sit down quickly, and write fifty.
7 “Kenaka iye anafunsa wachiwiri kuti, ‘Nanga iwe uli ndi ngongole yotani?’ “Iye ayankha kuti madengu a tirigu 1,000. “Iye anati, ‘Tenga pamene unalemba ngongole yakoyo ndipo ulembepo 800.’
Then he said to another, And how much owest thou? And he said, A hundred measures of wheat. He saith to him, Take thy bond, and write eighty.
8 “Bwana anayamikira kapitawo wosakhulupirikayo popeza anachita mochenjera. Pakuti anthu a dziko lino lapansi ndi ochenjera kwambiri akamachita zinthu ndi anthu ofanana nawo kuposa anthu a kuwunika. (aiōn g165)
And the lord commended the unjust steward for having done wisely; for the sons of this world are wiser toward their generation than the sons of light. (aiōn g165)
9 Ine ndikukuwuzani inu, gwiritsani ntchito chuma cha dziko lapansi kuti mudzipezere nokha abwenzi, kuti pamene chatha mudzalandiridwe mʼmalo okhala amuyaya. (aiōnios g166)
And I say to you, Make to yourselves friends with the unrighteous mammon; that, when it faileth, ye may be received into everlasting habitations. (aiōnios g166)
10 “Amene akhulupirika pa zinthu zochepa akhoza kukhulupirikanso pa zinthu zambiri, ndipo amene sakhulupirika pa zinthu zochepa adzakhala wosakhulupirika pa zinthu zambiri.
He that is faithful in that which is least, is faithful also in much; and he that is unjust in the least, is unjust also in much.
11 Ndipo ngati simunakhale okhulupirika pogwiritsa ntchito chuma cha dziko lapansi, ndani amene adzakusungitsani chuma chenicheni?
If therefore ye have not been faithful in the unrighteous mammon, who will commit to your trust the true riches?
12 Ndipo ngati simunakhale okhulupirika ndi chuma cha mwini wake, ndani amene adzakupatsani katundu wanuwanu?
and if ye have not been faithful in that which is another's, who will give you that which is your own?
13 “Palibe wantchito amene angatumikire mabwana awiri. Mwina iye adzadana ndi wina ndi kukonda winayo, kapena adzakhala wodzipereka kwa wina ndi kumunyoza winayo. Inu simungathe kutumikira Mulungu komanso ndalama nthawi imodzi.”
No servant can serve two masters; for either he will hate one, and love the other; or he will cleave to one, and despise the other. Ye cannot serve God and mammon.
14 Afarisi amene ankakonda ndalama atamva zimenezi anamuseka Yesu.
And the Pharisees, who were covetous, heard all this, and they derided him.
15 Yesu anawawuza kuti, “Inu ndi amene mumadzilungamitsa nokha pamaso pa anthu, koma Mulungu amadziwa mitima yanu. Zinthu zimene anthu amaziyesa zopambana, ndi zonyansa pamaso pa Mulungu.
And he said to them, Ye are they who justify yourselves before men; but God knoweth your hearts; for that which is highly exalted among men is an abomination before God.
16 “Malamulo ndi Aneneri zinagwira ntchito mpaka nthawi ya Yohane. Kuyambira nthawi imeneyo, Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ukulalikidwa, ndipo aliyense akuyesetsa mwamphamvu kuti alowemo.
The Law and the Prophets were till John; from that time the glad tidings of the kingdom of God have been published, and every one is forcing his way into it.
17 Nʼkwapafupi kuti kumwamba ndi dziko lapansi zichoke kulekana ndi kuti kalemba kakangʼono kachoke mʼMalamulo.
But it is easier for heaven and earth to pass away, than for one tittle of the law to fail.
18 “Aliyense amene asiya mkazi wake ndi kukakwatira mkazi wina akuchita chigololo, ndipo mwamuna amene akwatira mkazi wosiyidwayo akuchitanso chigololo.”
Whoever putteth away his wife, and marrieth another, committeth adultery; and he who marrieth a woman that hath been put away from her husband, committeth adultery.
19 “Panali munthu wachuma amene ankavala zovala zofiirira za mtengowapatali ndipo ankakhala moyo wachisangalalo tsiku lililonse.
There was a certain rich man, who was clothed in purple and fine linen, and feasted sumptuously every day.
20 Pa khomo la mpanda wake ankagonekapo munthu wopempha wotchedwa Lazaro, wazilonda thupi lonse
And a certain beggar named Lazarus was laid at his gate, full of sores,
21 ndipo ankafunitsitsa atadya zomwe zinkagwa pansi kuchokera pamene munthu wolemerayo amadyerapo. Agalu ankabweranso ndi kumanyambita zilonda zake.
and longing to be fed with what fell from the rich man's table. But even the dogs came and licked his sores.
22 “Nthawi inafika imene wopemphayo anamwalira ndipo angelo anamunyamula nakamuyika mʼmanja mwa Abrahamu. Munthu wolemerayo anamwaliranso ndipo anayikidwa mʼmanda.
And it came to pass, that the beggar died, and was carried by the angels to the bosom of Abraham. The rich man also died and was buried.
23 Ali mʼgehena kuzunzika, anakweza maso ake ndipo anaona Abrahamu ali ndi Lazaro pambali pake. (Hadēs g86)
And in the underworld he lifted up his eyes, being in torments, and seeth Abraham afar off, and Lazarus in his bosom. (Hadēs g86)
24 Ndipo anafuwula kwa iye kuti, ‘Abambo Abrahamu, mundimvere chisoni ine ndipo mutumeni Lazaroyo kuti aviyike msonga ya chala chake mʼmadzi kuti aziziritse lilime langa, chifukwa ndikumva ululu mʼmoto muno.’
And he called and said, Father Abraham, have pity on me, and send Lazarus to dip the tip of his finger in water, and cool my tongue; for I am tormented in this flame.
25 “Koma Abrahamu anayankha kuti, ‘Mwanawe kumbukira kuti nthawi yamoyo wako unalandira zinthu zako zabwino, pamene Lazaro analandira zinthu zoyipa, koma tsopano akusangalatsidwa kuno ndipo iwe uli mʼmazunzo.
But Abraham said, Son, remember that thou didst receive thy good things in thy lifetime, and Lazarus in like manner his evil things; but now he is comforted here, and thou art tormented.
26 Ndipo kuwonjezera pa zonsezi, pakati pa inu ndi ife pali chiphompho chachikulu chimene chinayikidwa, kotero kuti amene akufuna kubwera kumeneko sangathe, kapena palibe amene angawoloke kuchokera kumeneko kudzafika kuno.’
And besides all this, between us and you there is placed a great gulf, so that those who wish to cross from hence to you may not be able, and that those on that side cannot cross over to us.
27 “Iye anayankha kuti, ‘Ndipo ndikupemphani inu, abambo, mutumeni Lazaro ku nyumba ya abambo anga,
Then he said, I pray thee then, father, to send him to my father's house;
28 pakuti ine ndili ndi abale asanu. Lolani iye akawachenjeze kotero kuti asadzabwere kumalo ano amazunzo.’
for I have five brothers; that he may give earnest warning to them, that they too may not come into this place of torment.
29 “Abrahamu anayankha kuti, ‘Ali ndi Mose ndi Aneneri; aleke amvere iwo.’
But Abraham saith, They have Moses and the prophets; let them hear them.
30 “Iye anati, ‘Ayi, bambo Abrahamu, koma ngati wina ochokera kwa akufa adzapita kwa iwo, adzatembenuka mtima.’
But he said, Nay, father Abraham; but if one should go to them from the dead, they would repent.
31 “Anati kwa iye, ‘Ngati iwo samvera Mose ndi Aneneri, sadzakhulupirira ngakhale wina atauka kwa akufa.’”
But he said to him, If they hear not Moses and the prophets, they will not be persuaded, though one should rise from the dead.

< Luka 16 >