< Luka 14 >

1 Pa tsiku lina la Sabata, Yesu atapita kukadya ku nyumba ya Mfarisi wodziwika, Afarisi anamulonda mosamalitsa.
One Sabbath, Jesus went to eat in the home of a leading Pharisee, and those in attendance were watching Him closely.
2 Poteropo, patsogolo pake panali munthu amene anadwala matenda otupa mimba ndi miyendo.
Right there before Him was a man with dropsy.
3 Yesu anafunsa Afarisi ndi akatswiri amalamulo kuti, “Kodi ndi zololedwa kuchiritsa pa tsiku la Sabata kapena ayi?”
So Jesus asked the experts in the law and the Pharisees, “Is it lawful to heal on the Sabbath or not?”
4 Koma iwo sanayankhe. Tsono atamutenga munthuyo, Iye anamuchiritsa ndipo anamuwuza kuti azipita.
But they remained silent. Then Jesus took hold of the man, healed him, and sent him on his way.
5 Kenaka Iye anawafunsa kuti, “Kodi ngati mmodzi mwa inu ali ndi mwana wamwamuna kapena ngʼombe imene yagwera mʼchitsime tsiku la Sabata, kodi simungamuvuwulemo tsiku lomwelo?”
And He asked them, “Which of you whose son or ox falls into a pit on the Sabbath day will not immediately pull him out?”
6 Ndipo iwo analibe choyankha.
And they were unable to answer these questions.
7 Iye ataona momwe alendo amasankhira malo aulemu pa tebulo, Iye anawawuza fanizo ili:
When Jesus noticed how the guests chose the places of honor, He told them a parable:
8 “Pamene wina wakuyitanani ku phwando la ukwati, musakhale pa malo aulemu ayi, chifukwa mwina anayitananso munthu wina wolemekezeka kuposa inu.
“When you are invited to a wedding banquet, do not sit in the place of honor, in case someone more distinguished than you has been invited.
9 Ngati zitatero, ndiye kuti munthu uja amene anakuyitani inu nonse awiri adzakuwuzani kuti, ‘Mupatseni munthu uyu malo anu.’ Pamenepo inu mudzachita manyazi, pokakhala malo wotsika.
Then the host who invited both of you will come and tell you, ‘Give this man your seat.’ And in humiliation, you will have to take the last place.
10 Koma akakuyitanani, khalani pa malo otsika, kuti amene anakuyitanani uja adzakuwuzeni kuti, ‘Bwenzi, bwera udzakhale pa malo aulemu pano.’ Pamenepo inu mudzalandira ulemu pamaso pa alendo anzanu onse.
But when you are invited, go and sit in the last place, so that your host will come and tell you, ‘Friend, move up to a better place.’ Then you will be honored in front of everyone at the table with you.
11 Pakuti aliyense wodzikuza adzamuchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamukweza.”
For everyone who exalts himself will be humbled, and the one who humbles himself will be exalted.”
12 Kenaka Yesu anati kwa mwini malo uja, “Ukakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usamayitane abwenzi ako, abale ako, anthu afuko lako kapena anzako achuma; ngati iwe utero, iwo adzakuyitananso, choncho udzalandiriratu mphotho yako.
Then Jesus said to the man who had invited Him, “When you host a dinner or a banquet, do not invite your friends or brothers or relatives or rich neighbors. Otherwise, they may invite you in return, and you will be repaid.
13 Koma ukakonza phwando, itana anthu osauka, ofa ziwalo, olumala ndi osaona.
But when you host a banquet, invite the poor, the crippled, the lame, and the blind,
14 Pamenepo udzakhala wodala, chifukwa iwo sangakubwezere kanthu, koma Mulungu ndiye adzakubwezera pa chiukitso cha olungama.”
and you will be blessed. Since they cannot repay you, you will be repaid at the resurrection of the righteous.”
15 Mmodzi mwa amene amadya naye atamva izi, anati kwa Yesu, “Ndi wodala munthu amene adzadye nawo mu ufumu wa Mulungu.”
When one of those reclining with Him heard this, he said to Jesus, “Blessed is everyone who will eat at the feast in the kingdom of God.”
16 Yesu anayankha kuti, “Munthu wina ankakonza phwando lalikulu ndipo anayitana alendo ambiri.
But Jesus replied, “A certain man prepared a great banquet and invited many guests.
17 Nthawi yaphwando itakwana anatuma wantchito wake kuti akawuze onse amene anayitanidwa kuti, ‘Bwerani, pakuti zonse zakonzeka.’
When it was time for the banquet, he sent his servant to tell those who had been invited, ‘Come, for everything is now ready.’
18 “Koma onse anayamba kupereka zifukwa mofanana. Woyamba anati, ‘Ine ndangogula kumene munda, ndipo ndikuyenera kupita kuti ndikawuone. Pepani mundikhululukire.’
But one after another they all began to make excuses. The first one said, ‘I have bought a field, and I need to go see it. Please excuse me.’
19 “Wina anati, ‘Ndangogula kumene ngʼombe khumi zokoka ngolo ndipo kupita kukaziyesa. Pepani mundikhululukire.’
Another said, ‘I have bought five yoke of oxen, and I am going to try them out. Please excuse me.’
20 “Wina anatinso, ‘Ine ndangokwatira kumene, choncho sinditha kubwera.’
Still another said, ‘I have married a wife, so I cannot come.’
21 “Wantchitoyo anabwera ndikudzamuwuza bwana wakeyo zimenezi. Pamenepo mphwandoyo anapsa mtima ndipo analamula wantchito wakeyo kuti, ‘Pita msangamsanga kunja mʼmisewu ndi mʼmakwalala a mu mzinda ndipo ukabweretse osauka, ofa ziwalo, osaona ndi olumala.’
The servant returned and reported all this to his master. Then the owner of the house became angry and said to his servant, ‘Go out quickly into the streets and alleys of the city, and bring in the poor, the crippled, the blind, and the lame.’
22 “Wantchitoyo anati, ‘Bwana, zimene munanena zachitika koma malo akanalipobe.’
‘Sir,’ the servant replied, ‘what you ordered has been done, and there is still room.’
23 “Ndipo mbuye uja anawuza wantchito wake kuti, ‘Pita kunja ku misewu ikuluikulu ndi kunja kwa mpanda ndipo ukawawuze kuti alowe, kuti nyumba yanga idzaze.
So the master told his servant, ‘Go out to the highways and hedges and compel them to come in, so that my house will be full.
24 Ine ndikukuwuzani inu kuti palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu amene anayitanidwa adzalawa phwandolo.’”
For I tell you, not one of those men who were invited will taste my banquet.’”
25 Gulu lalikulu la anthu linkayenda naye Yesu ndipo atatembenukira kwa iwo anati,
Large crowds were now traveling with Jesus, and He turned and said to them,
26 “Ngati wina aliyense abwera kwa Ine ndipo sadana ndi abambo ndi amayi ake, mkazi wake ndi ana, abale ake ndi alongo ake, inde ngakhale moyo wake omwe, iye sangakhale ophunzira wanga.
“If anyone comes to Me and does not hate his father and mother and wife and children and brothers and sisters—yes, even his own life—he cannot be My disciple.
27 Ndipo aliyense amene sasenza mtanda wake ndi kunditsata Ine sangakhale ophunzira wanga.
And whoever does not carry his cross and follow Me cannot be My disciple.
28 “Taganizani, ngati wina mwa inu akufuna kumanga nsanja, kodi iye sayamba wakhala pansi ndi kuganizira za mtengo wake kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kuti atsirizire?
Which of you, wishing to build a tower, does not first sit down and count the cost to see if he has the resources to complete it?
29 Pakuti ngati ayika maziko ndi kulephera kutsiriza, aliyense amene adzayiona adzamuseka,
Otherwise, if he lays the foundation and is unable to finish the work, everyone who sees it will ridicule him,
30 nanena kuti, ‘Munthu uyu anayamba kumanga koma sanathe kutsiriza.’
saying, ‘This man could not finish what he started to build.’
31 “Kapena mfumu imene ikupita ku nkhondo kukamenyana ndi mfumu ina, kodi siyamba yakhala pansi ndi kulingalira ngati ingathe ndi anthu 10,000 kulimbana ndi amene akubwera ndi 20,000?
Or what king on his way to war with another king will not first sit down and consider whether he can engage with ten thousand men the one coming against him with twenty thousand?
32 Ngati singathe, idzatuma nthumwi pomwe winayo ali kutali ndi kukapempha mgwirizano wamtendere.
And if he is unable, he will send a delegation while the other king is still far off, to ask for terms of peace.
33 Mʼnjira yomweyo, wina aliyense wa inu amene sasiya zonse ali nazo sangakhale ophunzira wanga.
In the same way, any one of you who does not give up everything he has cannot be My disciple.
34 “Mchere ndi wabwino, koma ngati usukuluka adzawukoleretsanso ndi chiyani?
Salt is good, but if the salt loses its savor, with what will it be seasoned?
35 Suyeneranso ngakhale mʼnthaka kapena kudzala la manyowa; umatayidwa kunja. “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”
It is fit neither for the soil nor for the manure pile, and it is thrown out. He who has ears to hear, let him hear.”

< Luka 14 >