< Levitiko 9 >

1 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu Mose anayitana Aaroni, ana ake ndi akuluakulu a Aisraeli.
Und am achten Tage rief Mose Aaron und seine Söhne und die Ältesten in Israel
2 Ndipo anawuza Aaroni kuti, “Tenga mwana wangʼombe wamwamuna kuti akhale nsembe yako yopepesera machimo ndi nkhosa yayimuna kuti ikhale nsembe yopsereza. Zonsezi zikhale zopanda chilema ndipo uzipereke pamaso pa Yehova.
und sprach zu Aaron: Nimm zu dir ein junges Kalb zum Sündopfer und einen Widder zum Brandopfer, beide ohne Fehl, und bringe sie vor den Herrn.
3 Kenaka uwawuze Aisraeli kuti, ‘Tengani mbuzi yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. Mutengenso mwana wangʼombe ndi mwana wankhosa. Zonsezi zikhale za chaka chimodzi ndi zopanda chilema kuti zikhale nsembe yopsereza.
Und rede mit den Kindern Israel und sprich: Nehmt einen Ziegenbock zum Sündopfer und ein Kalb und ein Schaf, beide ein Jahr alt und ohne Fehl, zum Brandopfer
4 Mutengenso ngʼombe yayimuna ndi nkhosa yayimuna kuti zikhale nsembe yachiyanjano zoti ziperekedwe pamaso pa Yehova. Pamodzi ndi izi mubwerenso ndi nsembe yachakudya yosakaniza ndi mafuta pakuti lero Yehova akuonekerani.’”
und einen Ochsen und einen Widder zum Dankopfer, daß wir dem HERRN opfern, und ein Speisopfer, mit Öl gemengt. Denn heute wird euch der HERR erscheinen.
5 Anthu anatenga zonse zimene Mose analamula nabwera nazo pa khomo la tenti ya msonkhano. Gululo linasendera pafupi ndi kuyima pamaso pa Yehova.
Und sie nahmen, was Mose geboten hatte, vor der Tür der Hütte des Stifts; und es trat herzu die ganze Gemeinde und stand vor dem HERRN.
6 Tsono Mose anati, “Izi ndi zimene Yehova walamula kuti muchite kuti ulemerero wa Yehova ukuonekereni.”
Da sprach Mose: Das ist's, was der HERR geboten hat, daß ihr es tun sollt, so wird euch des HERRN Herrlichkeit erscheinen.
7 Pambuyo pake Mose anawuza Aaroni kuti, “Sendera pafupi ndi guwa ndipo upereka nsembe yako yopepesera machimo ndi nsembe yako yopsereza ndikuchita mwambo wopepesera machimo ako ndi machimo a anthu. Anthuwa apereke nsembe zawo zopepesera machimo monga momwe Yehova walamulira.”
Und Mose sprach zu Aaron: Tritt zum Altar und mache dein Sündopfer und dein Brandopfer und versöhne dich und das Volk; darnach mache des Volkes Opfer und versöhne sie auch, wie der HERR geboten hat.
8 Choncho Aaroni anasendera pafupi ndi guwa, napha mwana wangʼombe uja kukhala nsembe yake yopepesera machimo.
Und Aaron trat zum Altar und schlachtete das Kalb zu seinem Sündopfer.
9 Ana a Aaroni anabwera ndi magazi kwa Aaroni ndipo iye anaviyika chala chake mʼmagaziwo, nawapaka pa nyanga za guwa. Magazi wotsalawo anawathira pa tsinde la guwalo.
Und seine Söhne brachten das Blut zu ihm, und er tauchte mit seinem Finger ins Blut und tat's auf die Hörner des Altars und goß das Blut an des Altars Boden.
10 Kenaka anatentha paguwapo, mafuta, impsyo pamodzi ndi mafuta amene amakuta chiwindi ngati nsembe yopepesera machimoyo, monga momwe Yehova analamulira Mose.
Aber das Fett und die Nieren und das Netz von der Leber am Sündopfer zündete er an auf dem Altar, wie der HERR dem Mose geboten hatte.
11 Koma nyama ndi chikopa anazitenthera kunja kwa msasa.
Und das Fleisch und das Fell verbrannte er mit Feuer draußen vor dem Lager.
12 Kenaka anapha nsembe yopsereza. Ana a Aaroni atabwera ndi magazi kwa iye, Aaroniyo anawawaza mbali zonse za guwa.
Darnach schlachtete er das Brandopfer; und Aarons Söhne brachten das Blut zu ihm, und er sprengte es auf den Altar umher.
13 Ana akewo anamupatsa nyama yoduladula ya nsembe yopsereza ija pamodzi ndi mutu ndipo anazitentha pa guwa.
Und sie brachten das Brandopfer zu ihm zerstückt und den Kopf; und er zündete es an auf dem Altar.
14 Aaroni anatsuka matumbo ndi miyendo nazitentha pa guwa pamodzi ndi nsembe yopsereza ija.
Und er wusch das Eingeweide und die Schenkel und zündete es an oben auf dem Brandopfer auf dem Altar.
15 Kenaka Aaroni anapereka zopereka za anthuwo. Anatenga mbuzi yopepesera machimo a anthuwo, yopereka chifukwa cha tchimo, nayipha ndi kuyipereka kuti ikhale yopepesera machimo monga anachitira ndi nsembe yoyamba ija.
Darnach brachte er herzu des Volks Opfer und nahm den Bock, das Sündopfer des Volks, und schlachtete ihn und machte ein Sündopfer daraus wie das vorige.
16 Anabwera ndi nsembe yopsereza, nayipereka potsata mwambo wake.
Und brachte das Brandopfer herzu und tat damit, wie es recht war.
17 Anabweranso ndi chopereka cha chakudya. Anatapa ufa dzanja limodzi ndi kutentha pa guwa, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya mmawa ija.
Und brachte herzu das Speisopfer und nahm seine Hand voll und zündete es an auf dem Altar, außer dem Morgenbrandopfer.
18 Tsono Aaroni anapha ngʼombe ndi nkhosa yayimuna monga nsembe yachiyanjano ya anthu. Ana ake anamupatsira magazi ndipo anawawaza mbali zonse za guwa.
Darnach schlachtete er den Ochsen und den Widder zum Dankopfer des Volks; und seine Söhne brachten ihm das Blut, das sprengte er auf dem Altar umher.
19 Anamupatsiranso mafuta a ngʼombeyo ndi nkhosa yayimunayo: mchira wamafuta, mafuta wokuta matumbo, impsyo ndi mafuta wokuta chiwindi.
Aber das Fett vom Ochsen und vom Widder, den Schwanz und das Fett am Eingeweide und die Nieren und das Netz über der Leber:
20 Ana a Aaroni anayika mafutawo pa zidale. Pambuyo pake Aaroni anatentha mafutawo pa guwa lansembe.
alles solches Fett legten sie auf die Brust; und er zündete das Fett an auf dem Altar.
21 Koma zidale ndi ntchafu ya kumanja Aaroni anaziweyula ngati chopereka choweyula pamaso pa Yehova.
Aber die Brust und die rechte Schulter webte Aaron zum Webopfer vor dem HERRN, wie der HERR dem Mose geboten hatte.
22 Kenaka Aaroni anakweza manja ake pa anthuwo nawadalitsa. Ndipo atatha kupereka nsembe yopepesera machimo, nsembe yopsereza ndi nsembe yachiyanjano, anatsika pa guwapo.
Und Aaron hob seine Hand auf zum Volk und segnete sie; und er stieg herab, da er das Sündopfer, Brandopfer und Dankopfer gemacht hatte.
23 Ndipo Mose pamodzi ndi Aaroni analowa mu tenti ya msonkhano. Atatulukamo anadalitsa anthuwo ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera kwa anthu onse.
Und Mose und Aaron gingen in die Hütte des Stifts; und da sie wieder herausgingen, segneten sie das Volk. Da erschien die Herrlichkeit des HERRN allem Volk.
24 Pomwepo moto unatuluka pamaso pa Yehova niwutentha nsembe zopsereza ndi mafuta zimene zinali pa guwa. Anthu onse ataona zimenezi anafuwula mwachimwemwe ndipo anaweramitsa nkhope zawo pansi.
Und ein Feuer ging aus von dem HERRN und verzehrte auf dem Altar das Brandopfer und das Fett. Da das alles Volk sah, frohlockten sie und fielen auf ihr Antlitz.

< Levitiko 9 >