< Levitiko 8 >

1 Yehova anawuza Mose kuti,
여호와께서 모세에게 일러 가라사대
2 “Tenga Aaroni ndi ana ake, zovala zawo, mafuta wodzozera, ngʼombe yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo, nkhosa ziwiri zazimuna ndi dengu la buledi wopanda yisiti,
너는 아론과, 그 아들들과, 그 의복과, 관유와, 속죄제의 수송아지와 수양 둘과 무교병 한 광주리를 이끌고
3 ndipo usonkhanitse gulu la anthu pa khomo la tenti ya msonkhano.”
온 회중을 회막 문에 모으라
4 Mose anachita zomwe Yehova anamulamula ndipo gulu la anthu linasonkhana pa khomo la tenti ya msonkhano.
모세가 여호와꼐서 자기에게 명하신 대로 하매 회중이 회막 문에 모인지라
5 Mose anawuza gulu la anthuwo kuti, “Izi ndi zimene Yehova walamulira kuti zichitike.”
모세가 회중에게 이르되 '여호와께서 행하라고 명하신 것이 이러하니라' 하고
6 Pamenepo Mose anabwera ndi Aaroni ndi ana ake nawasambitsa ndi madzi.
아론과 그 아들들을 데려다가 물로 그들을 씻기고
7 Anamuveka Aaroni mwinjiro, ndi kumumanga lamba mʼchiwuno. Anamuvekanso mkanjo wa efodi ndi efodiyo. Anamangira lamba efodiyo amene analukidwa mwaluso uja, motero efodiyo analimba mʼchiwunomo.
아론에게 속옷을 입히며 띠를 띠우고 겉옷을 입히며 에봇을 더하고 에봇의 기묘하게 짠 띠를 띠워서 에봇을 몸에 매고
8 Anamuvekanso chovala chapachifuwa ndipo mʼchovalacho anayikamo Urimu ndi Tumimu.
흉패를 붙이고 흉패에 우림과 둠밈을 넣고
9 Kenaka anamuveka Aaroniyo nduwira kumutu ndipo patsogolo pa nduwirayo anayikapo duwa lagolide, chizindikiro chopatulika monga momwe Yehova analamulira Mose.
그 머리에 관을 씌우고 그 관 위 전면에 금패를 붙이니 곧 거룩한 관이라 여호와께서 모세에게 명하심과 같았더라
10 Pamenepo Mose anatenga mafuta wodzozera nadzoza tenti ya msonkhano pamodzi ndi zonse zimene zinali mʼmenemo, ndipo potero anazipatula.
모세가 관유를 취하여 장막과 그 안에 있는 모든 것에 발라 거룩하게 하고
11 Anawaza mafuta ena pa guwa kasanu ndi kawiri, nalidzoza guwalo pamodzi ndi ziwiya zake zonse. Anadzozanso beseni ndi tsinde lake, nazipatula.
또 단에 일곱번 뿌리고 또 그 단과 그 모든 기구와 물두멍과 그 받침에 발라 거룩하게 하고
12 Anathira mafuta wodzozera ena pamutu pa Aaroni ndipo anamudzoza ndi kumupatula.
또 관유로 아론의 머리에 부어 발라 거룩하게 하고
13 Kenaka anabwera ndi ana a Aaroni. Anawaveka minjiro, ndi kuwamanga malamba mʼchiwuno ndi kuwaveka nduwira kumutu monga momwe Yehova analamulira Mose.
모세가 또 아론의 아들들을 데려다가 그들에게 속옷을 입히고 띠를 띠우며 관을 씌웠으니 여호와께서 모세에게 명하심과 같았더라
14 Kenaka Mose anabwera ndi ngʼombe yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, ndipo Aaroni ndi ana ake anasanjika manja awo pamutu pa ngʼombeyo.
모세가 또 속죄제의 수송아지를 끌어오니 아론과 그 아들들이 그 속죄제 수송아지 머리에 안수하매
15 Mose anapha ngʼombeyo, ndi kutenga magazi ena angʼombeyo ndi kupaka ndi chala chake pa nyanga zaguwa lansembe, naliyeretsa. Magazi otsalawo anawakhuthulira pa tsinde laguwalo. Motero anachita mwambo wopepesera machimo.
모세가 잡고 그 피를 취하여 손가락으로 그 피를 단의 네 귀퉁이 뿔에 발라 단을 깨끗하게 하고 그 피는 단 밑에 쏟아 단을 속하여 거룩하게 하고
16 Mose anatenganso mafuta onse okuta matumbo, mafuta ophimba chiwindi, ndiponso impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta ake, nazitentha pa guwapo.
또 내장에 덮인 모든 기름과, 간 꺼풀과, 두 콩팥과, 그 기름을 취하여 단 위에 불사르고
17 Koma nyama yangʼombeyo, chikopa chake ndi matumbo ake anaziwotcha kunja kwa msasa monga momwe Yehova analamulira Mose.
그 수송아지 곧 그 가죽과 고기와 똥은 진 밖에 불살랐으니 여호와께서 모세에게 명하심과 같았더라
18 Kenaka anabwera ndi nkhosa yayimuna ya nsembe yopsereza, ndipo Aaroni ndi ana ake aamuna anasanjika manja awo pamutu pake.
또 번제의 수양을 드릴새 아론과 그 아들들이 그 수양의 머리에 안수하매
19 Ndipo Mose anapha nkhosayo ndi kuwaza magazi ake mbali zonse zaguwalo.
모세가 잡아 그 피를 단 주위에 뿌리고
20 Anayidula nkhosayo nthulinthuli ndipo anatentha mutu wake, nthulizo ndi mafuta.
그 수양의 각을 뜨고 그 머리와 각뜬 것과 기름을 불사르고
21 Anatsuka matumbo ake ndi miyendo yake, ndi kutentha nkhosa yonseyo pa guwa lansembe kuti ikhale nsembe yopsereza, fungo lokoma, nsembe yachakudya yoperekedwa kwa Yehova monga Yehovayo analamulira Mose.
물로 내장과 정갱이들을 씻고 그 수양의 전부를 단 위에 불사르니 이는 향기로운 냄새를 위하여 드리는 번제로 여호와께 드리는 화제라 여호와께서 모세에게 명하심과 같았더라
22 Kenaka Mose anapereka nkhosa yayimuna ina pamwambo wodzoza ansembe, ndipo Aaroni ndi ana ake aamuna anasanjika manja awo pamutu pake.
또 다른 수양 곧 위임식의 수양을 드릴새 아론과 그 아들들이 그 수양의 머리에 안수하매
23 Mose anayipha nkhosayo ndipo anatenga magazi ake ena ndi kupaka ndewere za khutu la kudzanja lamanja la Aaroni, pa chala chake chachikulu cha kudzanja lamanja, ndi pa chala chake chachikulu cha phazi lakumanja.
모세가 잡고 그 피를 취하여 아론의 오른 귓부리와, 오른손 엄지 가락과, 오른발 엄지가락에 바르고
24 Pambuyo pake Mose anabwera ndi ana aamuna a Aaroni ndi kupaka magazi pa ndewere za makutu awo akumanja, pa zala zawo zazikulu za dzanja lamanja, ndiponso pa zala zawo zazikulu za kuphazi lakumanja. Kenaka iye anawaza magazi otsalawo mbali zonse za guwalo.
아론의 아들들을 데려다가 그 오른 귓부리와, 오른손 엄지가락과, 오른발 엄지가락에 그 피를 바르고 또 그 피를 단 주위에 뿌리고
25 Anatenganso mafuta ake, mafuta a ku mchira wake, mafuta okuta matumbo, mafuta okuta chiwindi, impsyo zonse ziwiri ndi mafuta ake ndiponso ntchafu yakumanja.
그가 또 그 기름과, 기름진 꼬리와, 내장에 덮인 모든 기름과, 간 꺼풀과, 두 콩팥과, 기름과, 우편 뒷다리를 취하고
26 Ndipo mʼdengu la buledi wopanda yisiti limene linali pamaso pa Yehova, anatengamo buledi mmodzi, buledi mmodzi wokhala ndi mafuta a olivi, ndi buledi wopyapyala mmodzi. Zonsezi anaziyika pa mafuta aja ndi pa ntchafu ya ku dzanja lamanja ija.
여호와 앞 무교병 광주리에서 무교병 한개와 기름 섞은 떡 한개와 전병 한개를 취하여 그 기름 위에와 우편 뒷다리 위에 놓아
27 Mose anapereka zonsezi mʼmanja mwa Aaroni ndi ana ake amene anazipereka kwa Yehova kuti zikhale nsembe yoweyula.
그 전부를 아론의 손과 그 아들들의 손에 두어 여호와 앞에 흔들어 요제를 삼게 하고
28 Kenaka Mose anazitenga mʼmanja mwawo ndipo anazipsereza pa guwa lansembe pamwamba penipeni pamodzi ndi nsembe yopsereza ija kuti ikhale nsembe yopereka pamwambo wodzoza ansembe, kuti ipereke fungo lokoma, chopereka chachakudya kwa Yehova.
모세가 그것을 그들의 손에서 취하여 단 윗 번제물 위에 불사르니 이는 향기로운 냄새를 위하여 드리는 위임식 제사로 여호와께 드리는 화제라
29 Mose anatenga chidale cha nkhosa yayimuna, chomwe ndi gawo lake pamwambo wodzoza ansembe, ndipo anachiweyula pamaso pa Yehova kuti chikhale nsembe yoweyula monga momwe Yehova analamulira Mose.
이에 모세가 그 가슴을 취하여 여호와 앞에 흔들어 요제를 삼았으니 이는 위임식 수양의 모세의 응식이라 여호와께서 모세에게 명하심과 같았더라
30 Kenaka Mose anatenga mafuta wodzozera ansembe ndi magazi amene anali pa guwa nawaza pa Aaroni ndi zovala zake ndiponso ana ake aja ndi zovala zawo. Motero Mose anapatula Aaroni ndi zovala zake, ndiponso ana ake ndi zovala zawo.
모세가 관유와 단 위의 피를 취하여 아론과 그 옷과 그 아들들과 그 아들들의 옷에 뿌려서 아론과 그 옷과 그 아들들과 그 아들들의 옷을 거룩하게 하고
31 Mose anawuza Aaroni ndi ana ake kuti, “Phikani nyamayo pa khomo la tenti ya msonkhano, ndipo mudyere pomwepo pamodzi ndi buledi amene ali mʼdengu la zopereka za pamwambo wodzoza ansembe monga Yehova analamulira kuti, ‘Aaroni ndi ana ake azidya zimenezi.’
아론과 그 아들들에게 이르되 `내게 이미 명하시기를 아론과 그 아들들은 먹으라 하셨은즉 너희는 회막 문에서 그 고기를 삶아 위임식 광주리 안의 떡과 아울러 그 곳에서 먹고
32 Ndipo nyama ndi buledi zotsalazo, muziwotche.
고기와 떡의 나머지는 불사를지며
33 Musatuluke kunja kwa tenti ya msonkhano kwa masiku asanu ndi awiri mpaka masiku amwambo wokudzozani unsembe atatha, pakuti mwambowu ndi wa masiku asanu ndi awiri.
위임식은 칠일 동안 행하나니 위임식이 마치는 날까지 칠일 동안은 회막 문에 나가지 말라
34 Zimene zachitika lerozi analamula ndi Yehova kuti zichitike ngati nsembe yopepesera machimo anu.
오늘날 행한 것은 여호와께서 너희를 위하여 속하게 하시려고 명하신 것이니
35 Muzikhala pa khomo la tenti ya msonkhano usana ndi usiku kwa masiku asanu ndi awiri. Ndipo muzichita zimene Yehova wakulamulani kuti musafe, pakuti zimenezi ndi zomwe Yehova wandilamulira.”
너희는 칠 주야를 회막 문에 거하여 여호와의 부탁을 지키라! 그리하면 사망을 면하리라 내가 이같이 명령을 받았느니라'
36 Choncho Aaroni ndi ana ake anachita zonse zimene Yehova analamula kudzera mwa Mose.
아론과 그 아들들이 여호와께서 모세로 명하신 모든 일을 준행하니라

< Levitiko 8 >