< Levitiko 4 >

1 Yehova anayankhula ndi Mose kuti,
Yahvé parla à Moïse et dit:
2 “Awuze Aisraeli kuti, ‘Munthu akachimwa mosadziwa ndi kuchita chilichonse chimene Yehova walamula kuti asachite, azichita izi:
Parle aux enfants d'Israël et dis-leur: Si quelqu'un commet un péché involontaire en faisant l'une des choses que Yahvé a ordonné de ne pas faire, et qu'il la commette,
3 “‘Ngati wansembe wodzozedwa achimwa, ndi kuchimwitsa anthu onse, iyeyu ayenera kupereka mwana wangʼombe wamphongo wopanda chilema chifukwa cha tchimo limene wachitalo. Imeneyi ndi nsembe ya Yehova yopepesera tchimo lake.
si le prêtre oint a péché au point de rendre le peuple coupable, qu'il offre à Yahvé, en sacrifice pour le péché qu'il a commis, un jeune taureau sans défaut.
4 Wansembeyo abwere nayo ngʼombeyo pa khomo la tenti ya msonkhano pamaso pa Yehova. Asanjike dzanja lake pamutu pa ngʼombeyo ndipo ayiphe pamaso pa Yehova.
Il amènera le taureau à l'entrée de la Tente d'assignation, devant l'Éternel; il posera sa main sur la tête du taureau et l'égorgera devant l'Éternel.
5 Kenaka wansembe wodzozedwa atengeko magazi a ngʼombeyo ndi kulowa nawo mu tenti ya msonkhano.
Le prêtre oint prendra du sang du taureau et l'apportera dans la tente de la Rencontre.
6 Iye aviyike chala chake mʼmagazi, ndipo awawaze kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova, patsogolo pa katani yotchinga malo wopatulika.
Le prêtre trempera son doigt dans le sang et fera sept fois l'aspersion du sang devant l'Éternel, devant le voile du sanctuaire.
7 Kenaka wansembe apake magaziwo pa nyanga za guwa lofukizira lubani limene lili pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano. Magazi ena otsalawo awathire pa tsinde pa guwa lansembe zopsereza, limene lili pa khomo la tenti ya msonkhano.
Le prêtre mettra une partie du sang sur les cornes de l'autel des parfums doux, devant l'Éternel, qui est dans la tente de la Rencontre; il versera le reste du sang du taureau au pied de l'autel des holocaustes, qui est à l'entrée de la tente de la Rencontre.
8 Pambuyo pake achotse mafuta onse a ngʼombe yayimuna yopepesera machimoyo: mafuta okuta zamʼkati kapena mafuta onse amʼkatimo.
Il enlèvera toute la graisse du taureau du sacrifice pour le péché: la graisse qui couvre les entrailles et toute la graisse qui est sur les entrailles,
9 Achotsenso ndi kubwera ndi impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta onse ndiponso mafuta onse amene aphimba chiwindi ndi impsyo
les deux rognons et la graisse qui est sur eux, qui est près des reins, et la couverture du foie, avec les rognons, il les enlèvera,
10 monga momwe amachotsera mafuta a ngʼombe yoperekedwa kuti ikhale chopereka chachiyanjano. Tsono wansembe atenthe zimenezi pa guwa lansembe zopsereza.
comme on les enlève du taureau du sacrifice d'actions de grâces. Le prêtre les brûlera sur l'autel des holocaustes.
11 Koma chikopa cha ngʼombe yayimunayo ndi mnofu wake wonse, pamodzi ndi mutu ndi miyendo, zamʼkati ndi matumbo,
Il portera la peau du taureau, toute sa viande, avec sa tête et ses pattes, ses entrailles et ses excréments
12 kapena kuti ngʼombe yonse yotsalayo apite nayo kunja kwa msasa ku malo woyeretsedwa, kumene amatayako phulusa ndi kuyitentha pa nkhuni, pa phulusapo.
-tout le reste du taureau- hors du camp, dans un lieu propre où l'on répand les cendres, et il le brûlera au feu sur du bois. On le brûlera à l'endroit où l'on a répandu les cendres.
13 “‘Ngati gulu lonse la Aisraeli lichimwa mosadziwa, nachita chomwe ndi choletsedwa ndi Yehova, ngakhale kuti gulu lonselo silikudziwa kuti lachimwa, anthuwo ndi olakwa ndithu.
"'Si toute l'assemblée d'Israël a péché, si la chose est cachée aux yeux de l'assemblée, si elle a fait l'une des choses que l'Éternel a ordonné de ne pas faire et si elle s'est rendue coupable,
14 Akazindikira tchimo limene achita, gulu lonse lipereke mwana wangʼombe wamphongo kuti akhale chopereka chopepesera tchimo ndipo abwere naye pa khomo la tenti ya msonkhano.
si le péché qu'elle a commis est connu, l'assemblée offrira un jeune taureau en sacrifice pour le péché et l'amènera devant la tente d'assignation.
15 Akuluakulu a anthuwo asanjike manja awo pa mutu pa ngʼombe pamaso pa Yehova, ndipo ayiphe pomwepo pamaso pa Yehova.
Les anciens de l'assemblée poseront leurs mains sur la tête du taureau devant l'Éternel, et le taureau sera égorgé devant l'Éternel.
16 Tsono wansembe wodzozedwa atengeko magazi a ngʼombeyo ndi kulowa nawo mu tenti ya msonkhano.
Le prêtre oint apportera une partie du sang du taureau dans la tente de la Rencontre.
17 Aviyike chala chake mʼmagaziwo ndi kuwawaza pamaso pa Yehova kasanu ndi kawiri patsogolo pa nsalu yotchinga.
Le prêtre trempera son doigt dans le sang et en fera sept fois l'aspersion devant l'Éternel, en face du voile.
18 Pambuyo pake iye apake magaziwo pa nyanga za guwa limene lili pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano. Magazi ena otsalawo awathire pa tsinde pa guwa lansembe zopsereza limene lili pa khomo la tenti ya msonkhano.
Il mettra une partie du sang sur les cornes de l'autel qui est devant l'Éternel, dans la tente de la Rencontre, et il versera le reste du sang au pied de l'autel des holocaustes, à l'entrée de la tente de la Rencontre.
19 Kenaka achotse mafuta onse a ngʼombeyo ndi kuwatentha pa guwa,
Il en prélèvera toute la graisse et la brûlera sur l'autel.
20 ndipo achite ndi ngʼombe yayimunayi monga anachitira ndi ngʼombe yayimuna yopepesera machimo. Potero, wansembe adzapereka nsembe yopepesera anthu, ndipo machimo awo adzakhululukidwa.
Il fera cela avec le taureau; comme il a fait avec le taureau du sacrifice pour le péché, il fera de même avec celui-ci; le prêtre fera l'expiation pour eux, et ils seront pardonnés.
21 Kenaka atulutse ngʼombeyo kunja kwa msasa ndi kuyitentha monga anatenthera ngʼombe yoyamba ija. Imeneyi ndiyo nsembe yopepesera machimo a gulu lonse.
Il portera le taureau hors du camp, et il le brûlera comme il a brûlé le premier taureau. C'est le sacrifice pour le péché de l'assemblée.
22 “‘Ngati mtsogoleri achimwa mosadziwa nachita zimene ndi zoletsedwa ndi Yehova Mulungu wake, ndiye kuti wapalamula.
"'Lorsqu'un chef péchera et fera involontairement l'une de toutes les choses que l'Éternel, son Dieu, a ordonné de ne pas faire, et qu'il en sera coupable,
23 Ndipo ngati wauzidwa za tchimo limene wachita, iye abwere ndi mbuzi yayimuna yopanda chilema kuti ikhale chopereka chake.
si le péché qu'il a commis lui est connu, il apportera en offrande un bouc, un mâle sans défaut.
24 Asanjike dzanja lake pa mutu wa mbuziyo ndi kuyiphera pamalo pamene amaphera zopereka zopsereza pamaso pa Yehova. Ichi ndi chopereka chopepesera tchimo.
Il posera sa main sur la tête du bouc, et il l'égorgera dans le lieu où l'on égorge l'holocauste devant l'Éternel. C'est un sacrifice pour le péché.
25 Pambuyo pake wansembe atengeko magazi a chopereka chopepesera tchimocho ndi chala chake, ndipo awapake pa nyanga za guwa lansembe zopsereza. Athire magazi otsalawo pa tsinde la guwalo.
Le prêtre prendra avec son doigt une partie du sang du sacrifice pour le péché, et il en mettra sur les cornes de l'autel des holocaustes. Il versera le reste du sang au pied de l'autel des holocaustes.
26 Wansembeyo atenthe mafuta onse pa guwapo monga amatenthera chopereka chachiyanjano. Pochita zimenezi, wansembe adzapereka nsembe yopepesera tchimo la munthuyo, ndipo adzakhululukidwa.
Il brûlera toute sa graisse sur l'autel, comme la graisse du sacrifice d'actions de grâces; le prêtre fera pour lui l'expiation de son péché, et il lui sera pardonné.
27 “‘Ngati munthu wamba achimwa mosadziwa nachita zimene ndi zoletsedwa ndi Yehova, ndiye kuti wapalamula.
"'Si quelqu'un du peuple pèche involontairement en faisant l'une des choses que l'Éternel a ordonné de ne pas faire, et s'il est coupable,
28 Ndipo ngati wauzidwa za tchimo limene wachita, abweretse mbuzi yayikazi yopanda chilema kuti ikhale chopereka chopepesera tchimo.
si le péché qu'il a commis lui est connu, il apportera en offrande une chèvre, une femelle sans défaut, pour le péché qu'il a commis.
29 Asanjike dzanja lake pamutu pa mbuziyo ndipo ayiphe pamalo pamene amaphera chopereka chopsereza.
Il posera sa main sur la tête du sacrifice pour le péché, et il égorgera le sacrifice pour le péché dans le lieu de l'holocauste.
30 Ndipo wansembe atenge magazi ndi chala chake ndi kuwapaka pa nyanga za guwa lansembe zopsereza ndi kuthira magazi wotsalawo pa tsinde la guwalo.
Le sacrificateur prendra de son sang avec son doigt, et en mettra sur les cornes de l'autel des holocaustes; il versera le reste du sang au pied de l'autel.
31 Kenaka iye achotse mafuta onse monga momwe anachotsera mafuta a chopereka chachiyanjano, ndipo awatenthe pa guwa kuti akhale fungo lokomera Yehova. Potero, wansembe adzapereka nsembe yopepesera tchimo la munthuyo ndipo adzakhululukidwa.
Il enlèvera toute la graisse, comme on enlève la graisse du sacrifice d'actions de grâces, et le prêtre la brûlera sur l'autel comme une odeur agréable à Yahvé; le prêtre fera l'expiation pour lui, et il lui sera pardonné.
32 “‘Ngati munthu apereka mwana wankhosa ngati chopereka chopepesera tchimo lake, abwere ndi mwana wankhosa wamkazi wopanda chilema.
"'S'il apporte un agneau en sacrifice pour le péché, il apportera une femelle sans défaut.
33 Asanjike dzanja lake pa mutu wa mwana wankhosayo ndipo amuphe pamalo pamene amaphera chopereka chopsereza.
Il posera sa main sur la tête du sacrifice pour le péché et l'égorgera en sacrifice pour le péché dans le lieu où l'on égorge l'holocauste.
34 Kenaka wansembe atengeko ndi chala chake magazi a mwana wankhosa uja ndi kuwapaka pa nyanga za guwa lansembe zopsereza. Magazi otsalawo athire pa tsinde la guwalo.
Le prêtre prendra avec son doigt une partie du sang du sacrifice pour le péché, et il en mettra sur les cornes de l'autel des holocaustes; il versera tout le reste du sang au pied de l'autel.
35 Iye achotse mafuta onse, monga amachotsera mafuta a mwana wankhosa wa chopereka chachiyanjano, ndipo wansembe awatenthe pa guwa pamodzi ndi zopereka zina zopsereza za Yehova. Potero, wansembe adzapereka nsembe yopepesera tchimo limene munthuyo anachita ndipo adzakhululukidwa.
Il enlèvera toute la graisse, comme on enlève la graisse de l'agneau pour le sacrifice d'actions de grâces. Le prêtre les brûlera sur l'autel, sur les offrandes de Yahvé faites par le feu. Le prêtre fera pour lui l'expiation du péché qu'il a commis, et il lui sera pardonné.

< Levitiko 4 >