< Levitiko 3 >

1 “‘Ngati munthu apereka nsembe ya chiyanjano kwa Yehova, ndipo choperekacho nʼkukhala ngʼombe yayimuna kapena yayikazi, ikhale yopanda chilema.
若有人奉獻和平祭,如所獻的是牛,應在上主面前獻一頭無瑕的公牛或母牛,
2 Munthuyo asanjike dzanja lake pamutu pa ngʼombeyo, ndipo ayiphere pa khomo la tenti ya msonkhano. Ndipo ansembe, ana a Aaroni, awaze magazi mbali zonse za guwalo.
先按手在犧牲頭上,後在會幕門口宰了;亞郎的兒子司祭們,將血灑在祭壇四週。
3 Pa nsembe yachiyanjanopo, ayenera kupatula zamʼkati mwa nyamayo ndi mafuta onse amene amakuta zamʼkati kupereka nsembe ya chakudya kwa Yehova.
由和平犧牲中,應取出獻與上主做火祭的是:遮蓋內臟的脂肪,和貼在內臟上所有的脂肪,
4 Apatulenso impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta ake omwe ndiponso mafuta okuta chiwindi amene achotsedwa pamodzi ndi impsyo zija.
左右兩腎和兩腎靠腰部的脂肪,以及兩腎一起取出的肝葉。
5 Ndipo ana a Aaroni atenthe zimenezi pa guwa, pamwamba pa chopereka chopsereza chimene chili pa nkhuni zoyakazo. Imeneyi ndi nsembe yotentha pa moto, ya fungo lokomera Yehova.
亞郎的兒子們應將這一切放在祭壇上的柴火上,同全燔祭犧牲一起焚燒,作為中悅上主的馨香火祭。
6 “‘Ngati munthu apereka nsembe ya chiyanjano kwa Yehova, choperekacho chikhale nkhosa yayimuna kapena yayikazi yopanda chilema.
若有人給上主奉獻一隻羊作和平祭犧牲,應奉獻一隻無瑕的公羊或母羊。
7 Ngati apereka nsembe ya mwana wankhosa, abwere naye pamaso pa Yehova.
如果奉獻一隻棉羊作犧牲,應將他牽到上主面前,
8 Asanjike dzanja lake pamutu pa nkhosayo ndipo ayiphere pa khomo la tenti ya msonkhano. Ndipo ana a Aaroni awaze magaziwo mbali zonse za guwalo.
先按手在犧牲頭上,後會在會幕前宰了;亞郎的兒子將血灑在祭壇四週。
9 Pa nsembe yachiyanjanopo ayenera kuchotsa ndi kubweretsa: mafuta a nkhosayo, mchira wake wonse wonona atawudulira mʼtsinde pafupi ndi fupa la msana, zamʼkati zonse ndi mafuta onse amene akuta ziwalo zamʼkatimo,
那人由和平祭犧牲中應取出脂肪作獻與上主的火祭:即靠脊骨割下的整個肥尾,遮蓋內臟的脂肪,貼在內臟上所有的脂肪,
10 impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta amene akuta impsyozo, msonga ya chiwindi imene idzachotsedwere limodzi ndi impsyozo.
左右兩腎和兩腎靠腰部的脂肪,以及兩腎一起取出的肝葉。
11 Wansembe awotche zonsezi pa guwa. Ichi ndi chakudya chotentha pa moto choperekedwa kwa Yehova.
司祭應將這一切放在祭壇上焚燒,有如食物,作為獻與上主的火祭。
12 “‘Ngati munthuyo apereka mbuzi ngati nsembe, abwere nayo kwa Yehova.
如果奉獻的祭品是一隻山羊,應將他牽到上主前,
13 Asanjike dzanja lake pamutu pa mbuziyo ndipo ayiphere pa khomo la tenti ya msonkhano. Ndipo ana a Aaroni awaze magazi ake mbali zonse za guwa.
先按手在犧牲頭上,後會在會幕前宰了;亞郎的兒子將血灑在祭壇四週。
14 Tsono pa nsembe yoti iwotchedwe kukhala nsembe chakudya ya Yehova, achotse ndi kubweretsa: mafuta onse amene amaphimba zamʼkati kapena mafuta onse a mʼkatimo,
那人由犧牲中應取出獻與上主作火祭的是:遮蓋內臟的脂肪,貼在內臟上所有的脂肪,
15 impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta onse omwe akuta impsyozo ndi msonga ya chiwindi imene adzachotsera pamodzi ndi impsyo zija.
左右兩腎和兩腎靠腰部的脂肪,以及兩腎一起取出的肝葉。
16 Wansembe awotche zonsezi pa guwa. Ichi ndi chakudya cha Yehova, chowotcha pa moto ndiponso cha fungo lokomera Yehova. Mafuta onse ndi a Yehova.
司祭應將這一切放在祭壇上焚燒,有如食物,作為中悅上主的馨香火祭。
17 “‘Limeneli likhale lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse kuti musadzadye mafuta kapena magazi kulikonse kumene mudzakhale.’”
一切脂肪應歸於上主。凡是脂肪和血,你們都不可吃:這為你們世世代代,在你們任何所居之地,是一條永久的法令。

< Levitiko 3 >