< Levitiko 26 >

1 “‘Musadzipangire mafano ndipo musayimike chifanizo chosema kapena mwala woti mudzipembedza. Musayike mwala wosema mʼdziko mwanu kuti muziwugwadira. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Немојте градити себи идола ни ликова резаних, нити ступова подижите, ни камена са сликама мећите у својој земљи да му се клањате; јер сам ја Господ Бог ваш.
2 “‘Muzisunga Masabata anga ndipo muzilemekeza malo anga wopatulika. Ine ndine Yehova.
Држите суботе моје, и светињу моју поштујте; ја сам Господ.
3 “‘Mukamayenda motsata malangizo anga ndi kumvera mosamalitsa malamulo anga,
Ако узживите по мојим уредбама, и заповести моје уздржите и ушчините,
4 ndidzakupatsani mvula pa nyengo yake. Nthaka yanu idzabala zokolola zake, ndipo mitengo ya mʼmunda idzabala zipatso zake.
Даваћу вам дажд на време, и земља ће рађати род свој, и дрвета ће у пољу рађати род свој;
5 Mudzakhala mukupuntha tirigu mpaka nthawi yothyola mphesa, ndipo mudzakhala mukuthyola mphesa mpaka nthawi yodzala. Mudzadya chakudya chanu mpaka kukhuta ndipo mudzakhala mʼdziko lanu mwamtendere.
И вршидба ће вам стизати бербу виноградску, а берба ће виноградска стизати сејање, и јешћете хлеб свој до ситости, и живећете без страха у земљи својој.
6 “‘Ndidzabweretsa mtendere mʼdziko lanu, ndipo muzidzagona popanda wokuopsezani. Ndidzachotsa nyama zakuthengo zoopsa mʼdziko mwanu, ndipo mʼdzikomo simudzakhala nkhondo.
Јер ћу дати мир земљи, те ћете спавати а неће бити никога да вас плаши; учинићу, те ће нестати зле звери из земље, и мач неће пролазити преко ваше земље.
7 Mudzapirikitsa adani anu, ndipo mudzawagonjetsa ndi lupanga pamaso panu.
Него ћете терати непријатеље своје, и падаће пред вама од мача.
8 Anthu asanu mwa inu adzapirikitsa anthu 100, ndipo anthu 100 mwa inu adzathamangitsa anthu 10,000, ndipo adani anuwo mudzawagonjetsa ndi lupanga.
Вас ће петорица терати стотину, а вас стотина тераће десет хиљада, и падаће непријатељи ваши пред вама од мача.
9 “‘Ndidzakukumbukirani ndi kukupatsani ana ambiri ndi kukuchulukitsani. Ndidzasunga pangano langa ndi inu.
И обратићу се к вама, и учинићу вам да растете, и умножићу вас, и утврдићу завет свој с вама.
10 Mudzakhala mukudyabe chakudya chogonera ndipo mudzachotse chakudyacho mʼnkhokwe kuti mupezemo malo woyika chakudya china chatsopano.
И јешћете жито старо, од много година, и изасипаћете старо кад дође ново.
11 Ndidzakhala pakati panu, ndipo sindidzayipidwa nanu.
И наместићу стан свој међу вама, и душа моја неће мрзети на вас.
12 Ine ndidzayendayenda pakati panu ndipo ndidzakhala Mulungu wanu. Inu mudzakhala anthu anga.
И ходићу међу вама, и бићу вам Бог, и ви ћете бити мој народ.
13 Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti musakhalenso akapolo a Aigupto. Ndinadula mipiringidzo ya goli lanu ndi kukuthandizani kuti muziyenda momasuka.
Ја сам Господ Бог ваш, који вас изведох из земље мисирске да им не робујете, и поломих палице јарма вашег, и исправих вас да ходите право.
14 “‘Koma mukadzapanda kundimvera ndi kuphwanya malamulo anga onsewa,
Ако ли ме не узаслушате, и не учините све ове заповести,
15 ndipo ngati mudzanyoza malangizo anga ndi kunyansidwa ndi malamulo anga, ndi kulephera kumvera zonse zimene ndakulamulani, ndi kuswa pangano langa,
Ако повргнете уредбе моје и души вашој омрзну закони моји да не творите све заповести моје, и раскинете завет мој,
16 Ine ndidzakuchitirani izi: ndidzabweretsa zoopsa zadzidzidzi monga chifuwa chachikulu chowondetsa ndiponso malungo amene adzawononga maso ndi kufowoketsa moyo wanu. Mudzangovutika kudzala mbewu zanu chifukwa adani anu adzazidya.
И ја ћу вама учинити ово: Пустићу на вас страх, суву болест и врућицу, које ће вам очи искварити и душу уцвелити; и залуду ћете сејати семе своје, јер ће га јести непријатељи ваши.
17 Ndidzakufulatirani, kotero kuti adani anu adzakugonjetsani. Odana nanu adzakulamulirani ndipo inu muzidzagothawa popanda wokupirikitsani.
И окренућу лице своје насупрот вама, и сећи ће вас непријатељи ваши, и који мрзе на вас биће вам господари, и бежаћете кад вас нико не тера.
18 “‘Ngati simudzandimvera mutaona zonsezi, ndidzakulanganinso mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha kuchimwa kwanu.
Ако ме ни тада не станете слушати, караћу вас још седам пута више за грехе ваше.
19 Ndidzathyola mphamvu zanu zimene mukunyadirazo, ndipo ndidzasandutsa mitambo kuti ikhale yowuma ngati chitsulo, ndiponso nthaka yanu kuti ikhale ngati mkuwa.
Потрћу понос силе ваше, и учинићу да небо над вама буде као гвожђе, а земља ваша као бронза.
20 Mphamvu zanu zidzapita pachabe chifukwa nthaka yanu sidzabala kanthu, ngakhale mitengo yake sidzabala zipatso zake.
Снага ће се ваша трошити узалуд, јер земља ваша неће рађати рода свог, и дрвета по земљи неће рађати рода свог.
21 “‘Ngati mudzapitirira kutsutsana nane ndi kukana kundimvera, ndidzachulukitsa masautso anu kasanu ndi kawiri molingana ndi machimo anu.
Ако ми узидете насупрот и не будете хтели слушати ме, додаћу вам седам пута више мука према гресима вашим.
22 Ndidzabweretsa zirombo zolusa pakati panu, ndipo zidzakulandani ana anu ndi kuwononga ngʼombe zanu. Choncho zidzachepetsa chiwerengero chanu kotero kuti mʼnjira mwanu simudzapita anthu.
Пустићу на вас звери пољске, које ће вам децу изјести, и стоку потрти и вас умалити, и опустеће путеви ваши.
23 “‘Mukadzapanda kutembenukira kwa Ine ngakhale nditakulangani motere, ndi kumachitabe zotsutsana ndi Ine,
Ако се ни од тога не поправите, него ми још узидете насупрот,
24 Ine mwini ndidzalimbana nanu, ndipo ndidzakulangani mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha machimo anu.
И ја ћу вама ићи насупрот, и бићу вас још седам пута више за грехе ваше.
25 Ndipo ndidzabweretsa lupanga pa inu ndi kukulangani chifukwa chophwanya pangano langa. Mukadzasonkhana mʼmizinda yanu, ndidzatumiza miliri pakati panu ndipo ndidzakuperekani mʼmanja mwa adani anu.
Пустићу на вас мач, који ће осветити мој завет; а кад се слежете у градове своје, тада ћу пустити помор међу вас, и бићете предани у руке непријатељу.
26 Ndikadzachepetsa buledi wanu, akazi khumi adzaphika buledi wawo mu uvuni umodzi, ndipo adzakugawirani bulediyo pangʼonopangʼono. Choncho mudzadya koma wosakhuta.
И кад вам сломим потпору у хлебу, десет ће жена пећи хлеб ваш у једној пећи, и даваће вам хлеб ваш на меру, и јешћете а нећете се наситити.
27 “‘Mukadzapanda kundimvera ngakhale nditakulangani motere, ndi kumatsutsanabe ndi Ine,
Ако ме ни тако не станете слушати, него ми узидете насупрот,
28 pamenepo ndidzalimbana nanu mwaukali, ndipo Ine mwini ndidzakulangani mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha kuchimwa kwanu.
И ја ћу вама с гневом ићи насупрот, и седам пута већма караћу вас за грехе ваше.
29 Mudzadya ana anu aamuna ndiponso mudzadya ana anu aakazi.
И јешћете месо од синова својих, и месо од кћери својих јешћете.
30 Ine ndidzawononga malo anu opembedzera mafano a ku mapiri. Ndidzagwetsa maguwa anu ofukizira lubani, ndipo ndidzawunjika pamodzi mitembo ya mafano anu wopanda moyowo, ndipo ndidzanyansidwa nanu.
Развалићу висине ваше, и оборићу идоле ваше, и метнућу трупове ваше на трупове гадних богова ваших, и мрзиће душа моја на вас.
31 Ndidzasandutsa mizinda yanu kukhala mabwinja ndi kuwononga malo anu wopatulika. Sindidzakondweranso ndi fungo lokoma la zopereka zanu.
И обратићу градове ваше у пустош, и разорићу светиње ваше, и нећу више мирисати мириса вашег.
32 Ndidzawononga dziko kotero kuti adani anu mʼmenemo adzadabwa.
И опустећу земљу да ће јој се чудити непријатељи ваши, који ће живети у њој.
33 Ndidzakubalalitsani pakati pa mitundu ina ya anthu ndipo ndidzasolola lupanga langa ndi kukupirikitsani. Dziko lanu lidzawonongedwa, ndipo mizinda yanu idzasanduka mabwinja.
А вас ћу расејати по народима, и учинићу да вас гоне с голим мачем; и земља ће ваша бити пуста и градови ваши раскопани.
34 Nthawi imeneyo nthaka idzasangalalira kuyipumitsa kwake nthawi yonse imene idzakhala yosalimidwa, pamene inu mudzakhala muli mʼdziko la adani anu. Pa nthawi imeneyo dziko lidzapumula ndi kukondwerera kulipumuza kwake.
Тада ће земљи бити миле суботе њене за све време докле буде пуста; и кад будете у земљи својих непријатеља, земља ће почивати, и биће јој миле суботе њене.
35 Nthawi zonse pamene dzikolo lidzakhala lopanda anthu, nthaka idzapumula. Mpumulo umenewu udzakhala umene nthakayo sinapumulepo pa nthawi zimene inu munkapumula muli mʼdzikomo.
За све време докле буде пуста почиваће, јер није почивала у ваше суботе, кад сте у њој живели.
36 “‘Kunena za amene adzatsale, ndidzayika mantha mʼmitima mwawo mʼdziko la adani awo kotero kuti adzathawa ngakhale mtswatswa wa tsamba lowuluka ndi mphepo. Adzathawa ngati akuthawa lupanga, ndipo adzagwa pansi ngakhale padzakhale wopanda kuwapirikitsa.
А који вас остану, метнућу страх у срца њихова у земљама непријатеља њихових, те ће их гонити лист кад шушне заљуљавши се, и они ће бежати као испред мача, и падаће а нико их неће терати.
37 Iwo adzaphunthwitsana ngati akuthawa nkhondo, ngakhale padzakhale popanda wowapirikitsa. Choncho simudzatha kuyima pamaso pa adani anu.
И падаће један преко другог као од мача, а нико их неће терати; и нећете се моћи држати пред непријатељима својим.
38 Mudzatheratu pakati pa mitundu ya anthu. Dziko la adani anu lidzakudyani.
Него ћете изгинути међу народима, и прождреће вас земља непријатеља ваших.
39 Ngakhale iwo amene adzatsale adzatheratu mʼdziko la adani awo chifukwa cha machimo awo ndi machimo a makolo awo.
А који вас остану, чилеће за безакоње своје у земљи непријатеља својих, и за безакоње отаца својих чилеће.
40 “‘Tsono adzawulula machimo awo ndi machimo a makolo awo, kusakhulupirika kwawo ndi mayendedwe awo otsutsana nane,
Али ако признаду безакоње своје и безакоње отаца својих по гресима, којима ми грешише и којима ми идоше насупрот,
41 zomwe zinandipangitsa kuwafulatira ndi kuwapereka mʼmanja mwa adani awo. Ndipo mitima yawo yowumayo ikadzadzichepetsa ndi kuvomera kulangidwa chifukwa cha machimo awo,
Те и ја њима идох насупрот и одведох их у земљу непријатеља њихових; ако се тада понизи срце њихово необрезано, и буде им право што су покарани за безакоње своје,
42 Ine ndidzakumbukira pangano langa ndi Yakobo, pangano langa ndi Isake, pangano langa ndi Abrahamu. Ndidzakumbukiranso dzikolo.
Тада ћу се опоменути завета свог с Јаковом, и завета свог са Исаком, и завета свог са Аврамом опоменућу се, и земље ћу се опоменути.
43 Pakuti adzasiya dziko lawo lopanda anthu, nthaka idzakondwerera zaka zake zoyipumuza pamene iwo kudzakhala kulibe. Koma adzalangidwa chifukwa cha machimo awo popeza anakana malamulo anga ndipo mitima yawo inkayipidwa nawo malangizo anga.
Када се земља опрости њих и буду јој миле суботе њене кад опусти с њих, и њима буде право што су покарани за безакоње своје, јер судове моје повргоше и души њиховој омрзоше уредбе моје.
44 Komabe ngakhale adzachite zonsezi ali mʼdziko la adani awo, Ine sindidzawakana kapena kuyipidwa nawo kwakuti nʼkuwawononga kwathunthu ndi kuthetsa pangano langa ndi iwo. Ine ndine Yehova Mulungu wawo.
А зато ни онда кад буду у земљи непријатеља својих нећу их поврћи нити ћу тако омрзнути на њих да их потрем и раскинем завет свој са њима; јер сам ја Господ Бог њихов.
45 Koma powachitira chifundo, ndidzakumbukira pangano langa ndi makolo awo amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto mitundu ina ikuona kuti Ine ndikhale Mulungu wawo. Ine ndine Yehova.’”
Него ћу се њих ради опоменути завета са старима њиховим, које изведох из земље мисирске народима на видику да им будем Бог, ја Господ.
46 Amenewa ndi malamulo ndi malangizo amene Yehova anawayika pakati pa Iye mwini ndi Aisraeli pa Phiri la Sinai kudzera mwa Mose.
Ово су уредбе и судови и закони, које постави Господ између себе и синова Израиљевих на гори Синајској преко Мојсија.

< Levitiko 26 >