< Levitiko 23 >
1 Yehova anawuza Mose kuti,
And the LORD spoke unto Moses, saying:
2 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Awa ndi masiku anga osankhika a chikondwerero, masiku osankhika olemekeza Yehova amene uyenera kulengeza kuti akhale masiku opatulika a misonkhano.
Speak unto the children of Israel, and say unto them: The appointed seasons of the LORD, which ye shall proclaim to be holy convocations, even these are My appointed seasons.
3 “‘Pa masiku asanu ndi limodzi muzigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata lopuma, tsiku la msonkhano wopatulika. Kulikonse kumene inu mukukhala musamagwire ntchito iliyonse tsiku limeneli popeza ndi tsiku la Sabata la Yehova.
Six days shall work be done; but on the seventh day is a sabbath of solemn rest, a holy convocation; ye shall do no manner of work; it is a sabbath unto the LORD in all your dwellings.
4 “‘Awa ndiwo masiku osankhidwa a zikondwerero za Yehova, masiku woyera a misonkhano amene muti mudzalengeze pa nthawi yake:
These are the appointed seasons of the LORD, even holy convocations, which ye shall proclaim in their appointed season.
5 Chikondwerero cha Paska chiziyamba madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba.
In the first month, on the fourteenth day of the month at dusk, is the LORD'S passover.
6 Tsiku la 15 la mwezi womwewo ndi tsiku lolemekeza Yehova ndipo muziyamba Chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti. Muzidya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri.
And on the fifteenth day of the same month is the feast of unleavened bread unto the LORD; seven days ye shall eat unleavened bread.
7 Pa tsiku loyamba muzichita msonkhano wopatulika. Musamagwire ntchito iliyonse.
In the first day ye shall have a holy convocation; ye shall do no manner of servile work.
8 Pa masiku asanu ndi awiri muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri muzikhala ndi msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito yolemetsa.’”
And ye shall bring an offering made by fire unto the LORD seven days; in the seventh day is a holy convocation; ye shall do no manner of servile work.
9 Yehova anawuza Mose kuti,
And the LORD spoke unto Moses saying:
10 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukupatsanilo ndi kukolola za mʼminda mwanu, mudzabwere kwa wansembe ndi mtolo wa tirigu woyambirira kucha wa mʼminda mwanu.
Speak unto the children of Israel, and say unto them: When ye are come into the land which I give unto you, and shall reap the harvest thereof, then ye shall bring the sheaf of the first-fruits of your harvest unto the priest.
11 Wansembeyo auweyule mtolowo pamaso pa Yehova kotero mtolowo udzalandiridwa mʼmalo mwanu. Wansembe auweyule tsiku lotsatana ndi la Sabata.
And he shall wave the sheaf before the LORD, to be accepted for you; on the morrow after the sabbath the priest shall wave it.
12 Pa tsiku limene muweyula mtolowo, muperekenso mwana wankhosa wa mwamuna wa chaka chimodzi, wopanda chilema kuti akhale nsembe yopsereza ya kwa Yehova.
And in the day when ye wave the sheaf, ye shall offer a he-lamb without blemish of the first year for a burnt-offering unto the LORD.
13 Chopereka chachakudya chake chikhale cha makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta kuti chikhale nsembe yopsereza yopereka kwa Yehova, ya fungo lokoma. Ndipo chopereka cha chakumwa chake chikhale vinyo wa malita anayi ndi theka.
And the meal-offering thereof shall be two tenth parts of an ephah of fine flour mingled with oil, an offering made by fire unto the LORD for a sweet savour; and the drink-offering thereof shall be of wine, the fourth part of a hin.
14 Musadye buledi aliyense kapena tirigu wokazinga, kapena wamuwisi mpaka tsiku limene mwabwera ndi chopereka ichi kwa Mulungu wanu. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse, kulikonse kumene mukakhale.
And ye shall eat neither bread, nor parched corn, nor fresh ears, until this selfsame day, until ye have brought the offering of your God; it is a statute for ever throughout your generations in all your dwellings.
15 “‘Kuyambira tsiku lotsatana ndi la Sabata lija, tsiku limene munabwera ndi mtolo wa nsembe yoweyula, muziwerenga masabata asanu ndi awiri athunthu.
And ye shall count unto you from the morrow after the day of rest, from the day that ye brought the sheaf of the waving; seven weeks shall there be complete;
16 Ndiye kuti muwerenge masiku makumi asanu kuchokera pa tsiku lotsatana ndi Sabata la chisanu ndi chiwiri, ndipo kenaka mupereke nsembe ya tirigu watsopano kwa Yehova.
even unto the morrow after the seventh week shall ye number fifty days; and ye shall present a new meal-offering unto the LORD.
17 Kuchokera kulikonse kumene mukukhala, mubwere pamaso pa Yehova ndi buledi muwiri wa ufa wosalala wa makilogalamu awiri, ophikidwa ndi yisiti kuti akhale nsembe yoweyula ya zakudya zoyamba kucha.
Ye shall bring out of your dwellings two wave-loaves of two tenth parts of an ephah; they shall be of fine flour, they shall be baked with leaven, for first-fruits unto the LORD.
18 Pamodzi ndi bulediyu muperekenso ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri, aliyense akhale wa chaka chimodzi ndi wopanda chilema. Pakhalenso ngʼombe yayingʼono yayimuna ndi nkhosa zazimuna ziwiri. Zimenezi zidzakhala nsembe zopsereza zopereka kwa Yehova pamodzi ndi nsembe za zakudya ndi nsembe za zakumwa. Zonsezi zikhale nsembe zopsereza za fungo lokomera Yehova.
And ye shall present with the bread seven lambs without blemish of the first year, and one young bullock, and two rams; they shall be a burnt-offering unto the LORD, with their meal-offering, and their drink-offerings, even an offering made by fire, of a sweet savour unto the LORD.
19 Kenaka mupereke mbuzi imodzi yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ndiponso ana ankhosa awiri, aliyense wa chaka chimodzi kuti akhale nsembe yachiyanjano.
And ye shall offer one he-goat for a sin-offering, and two he-lambs of the first year for a sacrifice of peace-offerings.
20 Wansembe aweyule ana ankhosa awiriwo pamaso pa Yehova monga nsembe yoweyula, pamodzi ndi buledi wa tirigu woyambirira kucha. Zimenezi ndi zopereka zopatulika za Yehova zopatsidwa kwa ansembe.
And the priest shall wave them with the bread of the first-fruits for a wave-offering before the LORD, with the two lambs; they shall be holy to the LORD for the priest.
21 Pa tsiku lomwelo mulengeze za msonkhano wopatulika ndipo musagwire ntchito zolemetsa. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse, kulikonse kumene mukakhale.
And ye shall make proclamation on the selfsame day; there shall be a holy convocation unto you; ye shall do no manner of servile work; it is a statute for ever in all your dwellings throughout your generations.
22 “‘Pamene mukukolola zinthu mʼmunda mwanu, musakolole munda wanu mpaka mʼmalire mwenimweni, ndipo musatole khunkha lake. Zimenezo musiyire anthu osauka ndi alendo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”
And when ye reap the harvest of your land, thou shalt not wholly reap the corner of thy field, neither shalt thou gather the gleaning of thy harvest; thou shalt leave them for the poor, and for the stranger: I am the LORD your God.
23 Yehova anawuza Mose kuti,
And the LORD spoke unto Moses, saying:
24 “Uza Aisraeli kuti, ‘Tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri, likhale tsiku lopumula, la msonkhano wopatulika, mulilengeze poyimba lipenga.
Speak unto the children of Israel, saying: In the seventh month, in the first day of the month, shall be a solemn rest unto you, a memorial proclaimed with the blast of horns, a holy convocation.
25 Musagwire ntchito zolemetsa koma mupereke nsembe yopsereza kwa Yehova.’”
Ye shall do no manner of servile work; and ye shall bring an offering made by fire unto the LORD.
26 Yehova anawuza Mose kuti,
And the LORD spoke unto Moses, saying:
27 “Tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri ndi tsiku lochita Mwambo Wopepesera Machimo. Muzichita msonkhano wopatulika. Muzidzichepetsa pamaso pa Yehova ndi kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova.
Howbeit on the tenth day of this seventh month is the day of atonement; there shall be a holy convocation unto you, and ye shall afflict your souls; and ye shall bring an offering made by fire unto the LORD.
28 Tsiku limeneli musamagwire ntchito chifukwa ndi tsiku la Mwambo Wopepesera Machimo, kupepesera machimo anu pamaso pa Yehova Mulungu wanu.
And ye shall do no manner of work in that same day; for it is a day of atonement, to make atonement for you before the LORD your God.
29 Munthu aliyense amene sasala zakudya pa tsiku limeneli ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu a mtundu wake.
For whatsoever soul it be that shall not be afflicted in that same day, he shall be cut off from his people.
30 Aliyense wogwira ntchito tsiku limeneli ndidzamuwononga pakati pa anthu a mtundu wake.
And whatsoever soul it be that doeth any manner of work in that same day, that soul will I destroy from among his people.
31 Inu musadzagwire ntchito iliyonse. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse, kulikonse kumene mukakhale.
Ye shall do no manner of work; it is a statute for ever throughout your generations in all your dwellings.
32 Limeneli kwa inu ndi tsiku la Sabata lopumula, ndipo muyenera kusala zakudya. Kuyambira madzulo a tsiku lachisanu ndi chinayi la mwezi mpaka madzulo ena otsatirawo muzisunga tsikulo ngati Sabata lanu.”
It shall be unto you a sabbath of solemn rest, and ye shall afflict your souls; in the ninth day of the month at even, from even unto even, shall ye keep your sabbath.
33 Yehova anawuza Mose kuti,
And the LORD spoke unto Moses, saying:
34 “Uwawuze Aisraeli kuti pa masiku asanu ndi awiri kuyambira pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiwiri pazikhala Chikondwerero cha Misasa cholemekeza Yehova.
Speak unto the children of Israel, saying: On the fifteenth day of this seventh month is the feast of tabernacles for seven days unto the LORD.
35 Tsiku loyamba ndi la msonkhano wopatulika, musagwire ntchito zolemetsa.
On the first day shall be a holy convocation; ye shall do no manner of servile work.
36 Pa masiku asanu ndi awiri muzipereka nsembe zopsereza kwa Yehova. Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu muzikhala ndi msonkhano wopatulika ndipo muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Kumeneku ndi kutsekera kwa msonkhano waukulu. Musagwire ntchito zolemetsa.
Seven days ye shall bring an offering made by fire unto the LORD; on the eighth day shall be a holy convocation unto you; and ye shall bring an offering made by fire unto the LORD; it is a day of solemn assembly; ye shall do no manner of servile work.
37 (“‘Amenewa ndi masiku osankhika a chikondwerero cha Yehova, amene muziwalengeza kuti ndi nthawi ya msonkhano wopatulika. Masiku amenewa muzipereka nsembe zopsereza, nsembe za chakudya, nsembe zanyama ndi zopereka zachakumwa za tsiku ndi tsiku.
These are the appointed seasons of the LORD, which ye shall proclaim to be holy convocations, to bring an offering made by fire unto the LORD, a burnt-offering, and a meal-offering, a sacrifice, and drink-offerings, each on its own day;
38 Zopereka zimenezi ndi zowonjezera pa zopereka za Yehova za pa Sabata, zopereka zanu zolumbira ndiponso mphatso zanu zaufulu zopereka kwa Yehova.)
beside the sabbaths of the LORD, and beside your gifts, and beside all your vows, and beside all your freewill-offerings, which ye give unto the LORD.
39 “‘Choncho kuyambira pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, mutakolola zinthu mʼmunda mwanu, muchite chikondwerero cha Yehova kwa masiku asanu ndi awiri. Tsiku loyamba ndi tsiku lopumula, ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu ndi lopumulanso.
Howbeit on the fifteenth day of the seventh month, when ye have gathered in the fruits of the land, ye shall keep the feast of the LORD seven days; on the first day shall be a solemn rest, and on the eighth day shall be a solemn rest.
40 Pa tsiku loyamba muzitenga zipatso zabwino kwambiri zothyola mʼmitengo, nthambi za kanjedza, nthambi zazikulu za mitengo ya masamba ambiri, ndi za misondozi yakumtsinje, ndipo muzikondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu kwa masiku asanu ndi awiri.
And ye shall take you on the first day the fruit of goodly trees, branches of palm-trees, and boughs of thick trees, and willows of the brook, and ye shall rejoice before the LORD your God seven days.
41 Chaka chilichonse muzichita chikondwerero cha Yehova kwa masiku asanu ndi awiri. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse. Muzichita chikondwerero chimenechi mwezi wachisanu ndi chiwiri.
And ye shall keep it a feast unto the LORD seven days in the year; it is a statute for ever in your generations; ye shall keep it in the seventh month.
42 Muzikhala mʼmisasa masiku asanu ndi awiri. Onse amene ali mbadwa mʼdziko la Israeli azikhala mʼmisasa
Ye shall dwell in booths seven days; all that are home-born in Israel shall dwell in booths;
43 kuti zidzukulu zanu zidzadziwe kuti ndine amene ndinakhazika Aisraeli mʼmisasa nditawatulutsa ku Igupto. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”
that your generations may know that I made the children of Israel to dwell in booths, when I brought them out of the land of Egypt: I am the LORD your God.
44 Choncho Mose analengeza kwa Aisraeli masiku osankhika a zikondwerero za Yehova.
And Moses declared unto the children of Israel the appointed seasons of the LORD.