< Levitiko 21 >

1 Yehova anawuza Mose kuti, “Yankhula ndi ansembe, ana a Aaroni, ndipo uwawuze kuti, ‘Wansembe asadzidetse pokhudza munthu wakufa pakati pa abale ake.
Yahvé dit à Moïse: « Parle aux prêtres, les fils d'Aaron, et dis-leur: « Le prêtre ne se souillera pas pour les morts de son peuple,
2 Koma akhoza kukhudza thupi lakufa la amayi ake, abambo ake, mwana wake wamwamuna, mwana wake wamkazi, mchimwene wake,
sauf pour ses proches: pour sa mère, pour son père, pour son fils, pour sa fille, pour son frère,
3 kapena mlongo wake wosakwatiwa amene amadalira iye chifukwa sanakwatiwe. Iye akhoza kudzidetsa pokhudza thupi lakufa la mchemwali wake wosakwatiwa yekha.
et pour sa sœur vierge qui est près de lui et qui n'a pas eu de mari; pour elle, il pourra se souiller.
4 Koma wansembe asadzidetse chifukwa cha anthu amene ali nawo pa ubale obwera chifukwa cha ukwati.
Il ne se souillera pas, étant le chef de son peuple, pour se profaner.
5 “‘Ansembe asamete tsitsi kumutu kwawo kapena mʼmphepete mwa ndevu zawo, kapenanso kudzichekacheka pa thupi lawo.
"'Ils ne se raseront pas la tête, ne raseront pas les coins de leur barbe et ne feront aucune incision dans leur chair.
6 Ayenera kukhala oyera pamaso pa Mulungu wawo ndipo asachititse manyazi dzina la Mulungu wawo. Popeza amapereka nsembe zotentha pa moto kwa Yehova, chakudya cha Mulungu wawo, iwo azikhala woyera.
Ils seront saints pour leur Dieu et ne profaneront pas le nom de leur Dieu, car ils offrent les sacrifices de l'Éternel faits par le feu, le pain de leur Dieu. C'est pourquoi ils seront saints.
7 “‘Asakwatire akazi amene adzidetsa ndi chiwerewere kapena akazi amene amuna awo awasudzula, chifukwa ansembe ndi oyera pamaso pa Mulungu wawo.
"'Ils n'épouseront pas une femme qui se prostitue ou qui est profane. Le prêtre n'épousera pas une femme divorcée de son mari, car il est saint pour son Dieu.
8 Iwo akhale oyera chifukwa amapereka nsembe kwa Mulungu wanu. Muziwaona kuti ndi oyera, popeza Ine Yehova amene ndimawayeretsa ndine woyera, nawonso akhale oyera.
Vous le sanctifierez donc, car il offre le pain de votre Dieu. Il sera saint pour toi, car moi, Yahvé, qui te sanctifie, je suis saint.
9 “‘Ngati mwana wamkazi wa wansembe adziyipitsa pochita zachiwerewere, ndiye kuti iye akuchititsa manyazi abambo ake; mwanayo atenthedwe pa moto.
"'La fille d'un prêtre, si elle se profane en se prostituant, elle profane son père. Elle sera brûlée au feu.
10 “‘Munthu amene ali mkulu wa ansembe pakati pa abale ake, amene anamudzoza pomutsanulira mafuta pamutu pake, ndiponso amene anapatulidwa pomuveka zovala zaunsembe, asalekerere tsitsi lake kapena kungʼamba zovala zake kusonyeza kuti ali pa chisoni.
"'Celui qui est le grand prêtre parmi ses frères, sur la tête duquel on verse l'huile d'onction, et qui est consacré pour revêtir les vêtements, ne laissera pas pendre les cheveux de sa tête et ne déchirera pas ses vêtements.
11 Asalowe mʼnyumba mmene muli munthu wakufa ngakhale womwalirayo ndi amayi ake kapena abambo ake.
Il n'entrera pas auprès d'un cadavre, et ne se souillera pas pour son père ou pour sa mère.
12 Asadzidetse potulukira kunja kwa malo opatulika popeza mafuta womupatula kukhala wansembe ali pamutu pake. Ine ndine Yehova.
Il ne sortira pas du sanctuaire et ne profanera pas le sanctuaire de son Dieu, car la couronne de l'huile d'onction de son Dieu est sur lui. Je suis Yahvé.
13 “‘Iye akwatire namwali wosadziwa mwamuna.
"'Il prendra sa femme dans sa virginité.
14 Asakwatire mkazi wamasiye, mkazi wosudzulidwa, kapena mkazi wachiwerewere, koma akwatire namwali wosadziwa mwamuna pakati pa anthu a mtundu wake,
Il n'épousera ni une veuve, ni une divorcée, ni une femme qui s'est souillée, ni une prostituée. Il prendra pour femme une vierge de son peuple.
15 kuti mtundu wake usakhale wodetsedwa pakati pa abale popeza ndine Yehova, amene ndimamuyeretsa.’”
Il ne profanera pas sa descendance parmi son peuple, car c'est moi, Yahvé, qui le sanctifie. »"
16 Yehova anawuza Mose kuti,
Yahvé parla à Moïse et dit:
17 “Muwuze Aaroni kuti, ‘Munthu aliyense mwa zidzukulu zake ku mibado yawo yonse ikubwera akakhala ndi chilema asabwere kudzapereka nsembe kwa Mulungu wake.
« Dis à Aaron: Aucun de tes descendants, de génération en génération, qui a un défaut ne pourra s'approcher pour offrir le pain de son Dieu.
18 Munthu aliyense wachilema motere: munthu wakhungu kapena wolumala miyendo, munthu wolumala nkhope kapena waziwalo zambiri,
Car quel que soit l'homme qui a un défaut, il ne s'approchera pas: un aveugle, ou un boiteux, ou celui qui a le nez aplati, ou toute autre difformité,
19 munthu wa phazi lolumala kapena dzanja lolumala,
ou un homme qui a un pied blessé, ou une main blessée,
20 kapena munthu wokhota msana kapena wamfupi kwambiri, kapena wolumala maso, munthu wa nthenda yonyerenyetsa, kapena wamphere, kapenanso wophwanyika mavalo, sayenera kusendera pafupi.
ou un bossu, ou un nain, ou celui qui a un défaut à l'œil, ou une maladie qui démange, ou des croûtes, ou qui a des testicules endommagés.
21 Mdzukulu aliyense wa Aaroni wansembe, amene ali ndi chilema asadzayandikire kukapereka nsembe zopsereza kwa Yehova. Popeza kuti ali ndi chilema, asayandikire kudzapereka nsembe ya chakudya kwa Mulungu wake.
Aucun homme de la descendance du prêtre Aaron qui a un défaut ne s'approchera pour offrir les offrandes consumées par le feu de Yahvé. Comme il a une tare, il ne s'approchera pas pour offrir le pain de son Dieu.
22 Koma iye angathe kudya chakudya chopatulika kwambiri chija, ngakhalenso chakudya chotsala pa nsembe zopatulika.
Il mangera le pain de son Dieu, celui qui est très saint et celui qui est saint.
23 Koma chifukwa cha kulumala kwake, sayenera kuyandikira katani kapena kufika pa guwa kuti angadetse malo anga wopatulika. Ine ndine Yehova, amene ndimawayeretsa.’”
Il ne s'approchera pas du voile, ni de l'autel, car il a un défaut, afin de ne pas profaner mes sanctuaires, car je suis l'Éternel qui les sanctifie.'"
24 Choncho Mose anawuza Aaroni ndi ana ake pamodzi ndi Aisraeli onse zimenezi.
Moïse parla à Aaron, à ses fils et à tous les enfants d'Israël.

< Levitiko 21 >