< Levitiko 19 >

1 Yehova anawuza Mose kuti,
וידבר יהוה אל משה לאמר
2 “Uza gulu lonse la Aisraeli kuti, ‘Khalani oyera mtima chifukwa Ine, Yehova Mulungu wanu, ndine Woyera.
דבר אל כל עדת בני ישראל ואמרת אלהם--קדשים תהיו כי קדוש אני יהוה אלהיכם
3 “‘Aliyense mwa inu azilemekeza abambo ake ndi amayi ake. Ndipo muzisunga masabata anga. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
איש אמו ואביו תיראו ואת שבתתי תשמרו אני יהוה אלהיכם
4 “‘Musatembenukire ku mafano kapena kudzipangira nokha milungu ya zitsulo zosungunula. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
אל תפנו אל האלילם ואלהי מסכה לא תעשו לכם אני יהוה אלהיכם
5 “‘Pamene mukupereka nsembe yachiyanjano kwa Yehova, muyipereke mwanjira yoti ilandiridwe.
וכי תזבחו זבח שלמים ליהוה--לרצנכם תזבחהו
6 Nsembe izidyedwa tsiku lomwe mwayiperekalo kapena mmawa mwake. Chilichonse chotsala mpaka tsiku lachitatu chiyenera kutenthedwa.
ביום זבחכם יאכל וממחרת והנותר עד יום השלישי באש ישרף
7 Ngati mudya choperekacho tsiku lachitatu, ndiye kuti mwachita chonyansa ndipo chakudyacho sichidzalandiridwa.
ואם האכל יאכל ביום השלישי--פגול הוא לא ירצה
8 Munthu aliyense amene adya chakudyacho adzasenza machimo ake chifukwa wayipitsa chinthu chimene ndi choyera kwa Yehova. Munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake.
ואכליו עונו ישא כי את קדש יהוה חלל ונכרתה הנפש ההוא מעמיה
9 “‘Pamene mukolola zinthu mʼmunda mwanu musakolole mpaka mʼmphepete mwa munda, ndipo musatole khunkha lake.
ובקצרכם את קציר ארצכם לא תכלה פאת שדך לקצר ולקט קצירך לא תלקט
10 Musakolole mphesa zonse mʼmunda wanu wa mpesa kapena kutola mphesa zakugwa mʼmundamo. Zimenezi muzisiyire anthu osauka ndi alendo. Ine ndine Yehova Mulungu wako.
וכרמך לא תעולל ופרט כרמך לא תלקט לעני ולגר תעזב אתם אני יהוה אלהיכם
11 “‘Musabe. “‘Musamanamizane. “‘Musachitirane zinthu mwachinyengo.
לא תגנבו ולא תכחשו ולא תשקרו איש בעמיתו
12 “‘Musalumbire mʼdzina langa monyenga popeza kutero ndi kuyipitsa dzina la Mulungu wanu. Ine ndine Yehova.
ולא תשבעו בשמי לשקר וחללת את שם אלהיך אני יהוה
13 “‘Musapsinje mnzanu kapena kumulanda zinthu zake. “‘Musasunge malipiro a munthu wantchito usiku wonse mpaka mmawa.
לא תעשק את רעך ולא תגזל לא תלין פעלת שכיר אתך--עד בקר
14 “‘Musatemberere wosamva kapena kuyikira munthu wosaona chinthu choti apunthwe nacho patsogolo pake, koma muziopa Mulungu wanu. Ine ndine Yehova.
לא תקלל חרש--ולפני עור לא תתן מכשל ויראת מאלהיך אני יהוה
15 “‘Musamaweruze mopanda chilungamo. Musachite tsankho pakati pa osauka ndi olemera, koma muweruze mlandu wa mnzanu mwachilungamo.
לא תעשו עול במשפט--לא תשא פני דל ולא תהדר פני גדול בצדק תשפט עמיתך
16 “‘Musamapite uku ndi uku kunena bodza pakati pa anthu anu. “‘Musachite kanthu kalikonse kamene kangadzetse imfa kwa mnzanu. Ine ndine Yehova.
לא תלך רכיל בעמיך לא תעמד על דם רעך אני יהוה
17 “‘Musamude mʼbale wanu mu mtima mwanu. Koma mudzudzuleni mnzanu moona mtima kuti musakhale wolakwa.
לא תשנא את אחיך בלבבך הוכח תוכיח את עמיתך ולא תשא עליו חטא
18 “‘Musamubwezere mnzanu choyipa kapena kumusungira kanthu kunkhosi, koma konda mnansi wako monga iwe mwini. Ine ndine Yehova.
לא תקם ולא תטר את בני עמך ואהבת לרעך כמוך אני יהוה
19 “‘Muzisunga malangizo anga. “‘Tsono musamalole kuti ngʼombe zanu zikwerane ndi chiweto cha mtundu wina. “‘Ndiponso musamadzale mbewu za mitundu iwiri mʼmunda umodzi. “‘Musavale chovala chopangidwa ndi nsalu za mitundu iwiri.
את חקתי תשמרו--בהמתך לא תרביע כלאים שדך לא תזרע כלאים ובגד כלאים שעטנז לא יעלה עליך
20 “‘Ngati munthu agonana ndi kapolo wamkazi amene wafunsidwa mbeta ndi munthu wina, koma sanawomboledwe kapenanso kulandira ufulu wake, alangidwe. Koma onsewa asaphedwe, chifukwa mkaziyo anali asanalandire ufulu wake.
ואיש כי ישכב את אשה שכבת זרע והוא שפחה נחרפת לאיש והפדה לא נפדתה או חפשה לא נתן לה--בקרת תהיה לא יומתו כי לא חפשה
21 Koma mwamunayo abwere ndi nsembe yopepesera kupalamula kwa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano. Nsembe yake ikhale nkhosa yayimuna
והביא את אשמו ליהוה אל פתח אהל מועד--איל אשם
22 ndipo wansembe achite nayo mwambo wopepesera chifukwa cha kupalamula kumene anachita pamaso pa Yehova. Akatero tchimo lake lidzakhululukidwa.
וכפר עליו הכהן באיל האשם לפני יהוה על חטאתו אשר חטא ונסלח לו מחטאתו אשר חטא
23 “‘Mukadzalowa mʼdzikomo ndi kudzala mtengo wa mtundu uliwonse wa zipatso, zipatso zakezo mudzaziyese ngati zodetsedwa. Ndiye kuti kwa zaka zitatu zidzakhale zoletsedwa kwa inu. Musadzazidye nthawi imeneyi.
וכי תבאו אל הארץ ונטעתם כל עץ מאכל--וערלתם ערלתו את פריו שלש שנים יהיה לכם ערלים--לא יאכל
24 Chaka chachinayi, zipatso zake zonse zidzakhala zopatulika, ndipo zidzakhala chopereka cha matamando kwa Yehova.
ובשנה הרביעת יהיה כל פריו--קדש הלולים ליהוה
25 Koma chaka chachisanu, mudzatha kudya zipatso zake kuti mitengoyo idzakubalireni zochuluka. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
ובשנה החמישת תאכלו את פריו להוסיף לכם תבואתו אני יהוה אלהיכם
26 “‘Musadye nyama ya magazi. “‘Musamawombeze kapena kuchita zamatsenga.
לא תאכלו על הדם לא תנחשו ולא תעוננו
27 “‘Musamamete mduliro kapena kumeta mʼmphepete mwa ndevu zanu.
לא תקפו פאת ראשכם ולא תשחית את פאת זקנך
28 “‘Musadzichekecheke pathupi panu chifukwa cha munthu wakufa kapena kudzitema mphini pa thupi lanu. Ine ndine Yehova.
ושרט לנפש לא תתנו בבשרכם וכתבת קעקע לא תתנו בכם אני יהוה
29 “‘Musamuyipitse mwana wanu wamkazi pomusandutsa mkazi wachiwerewere. Mukatero dziko lidzasanduka la anthu achiwerewere ndi lodzaza ndi zoyipa.
אל תחלל את בתך להזנותה ולא תזנה הארץ ומלאה הארץ זמה
30 “‘Muzisunga Masabata anga ndipo muzilemekeza malo anga opatulika. Ine ndine Yehova.
את שבתתי תשמרו ומקדשי תיראו אני יהוה
31 “‘Musamapite kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, kapena kwa owombeza. Musamawafunefune kuti angakuyipitseni. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
אל תפנו אל האבת ואל הידענים אל תבקשו לטמאה בהם אני יהוה אלהיכם
32 “‘Muzikhala mwa ulemu pamaso pa munthu wachikulire, ndipo muzichitira ulemu munthu wokalamba. Kumeneko ndiye kuopa Mulungu wanu. Ine ndine Yehova.
מפני שיבה תקום והדרת פני זקן ויראת מאלהיך אני יהוה
33 “‘Pamene mlendo akhala nanu mʼdziko mwanu, musamuzunze.
וכי יגור אתך גר בארצכם--לא תונו אתו
34 Mlendo amene akhala nanu akhale ngati mmodzi mwa mbadwa zanu. Mumukonde monga momwe mumadzikondera inu nomwe. Paja inu munali alendo mʼdziko la Igupto. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
כאזרח מכם יהיה לכם הגר הגר אתכם ואהבת לו כמוך--כי גרים הייתם בארץ מצרים אני יהוה אלהיכם
35 “‘Musamachite za chinyengo poweruza mlandu, kapena poyeza utali, kulemera ngakhalenso kuchuluka kwa zinthu.
לא תעשו עול במשפט במדה במשקל ובמשורה
36 Miyeso ya sikelo, miyeso yoyezera kulemera kwa zinthu, miyeso yotchedwa efa ndi miyeso yotchedwa hini zikhale zolungama. Ine ndine Yehova, Mulungu wanu amene ndinakutulutsani ku dziko la Igupto.
מאזני צדק אבני צדק איפת צדק והין צדק--יהיה לכם אני יהוה אלהיכם אשר הוצאתי אתכם מארץ מצרים
37 “‘Choncho muzisunga malangizo ndi malamulo angawa ndi kuwatsatira. Ine ndine Yehova.’”
ושמרתם את כל חקתי ואת כל משפטי ועשיתם אתם אני יהוה

< Levitiko 19 >