< Levitiko 18 >

1 Yehova anawuza Mose kuti,
And Jehovah spoke to Moses, saying,
2 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Speak unto the children of Israel, and say unto them, I am Jehovah your God.
3 Musamachite zomwe amachita anthu a ku Igupto kumene munkakhala kuja, ndiponso musamachite zomwe amachita anthu a ku Kanaani kumene ndikukupititsani. Musatsatire miyambo yawo.
After the doings of the land of Egypt, wherein ye dwelt, shall ye not do; and after the doings of the land of Canaan, whither I bring you, shall ye not do; neither shall ye walk in their customs.
4 Inu muzimvera malamulo anga ndipo muzisamalitsa kutsatira malangizo anga. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Mine ordinances shall ye do and my statutes shall ye observe to walk therein: I am Jehovah your God.
5 Choncho sungani malangizo ndi malamulo anga, popeza munthu amene amvera zimenezi adzakhala ndi moyo. Ine ndine Yehova.
And ye shall observe my statutes and my judgments, by which the man that doeth them shall live: I am Jehovah.
6 “‘Munthu aliyense asagonane ndi wachibale wake. Ine ndine Yehova.
No one shall approach to any that is his near relation, to uncover his nakedness: I am Jehovah.
7 “‘Usachititse manyazi abambo ako pogonana ndi amayi ako. Iwo ndi amayi ako. Usagonane nawo.
The nakedness of thy father, and the nakedness of thy mother, shalt thou not uncover: she is thy mother: thou shalt not uncover her nakedness.
8 “‘Usagonane ndi mkazi wa abambo ako (osakhala amayi okubala). Ukatero ukuchititsa manyazi abambo ako.
The nakedness of thy father's wife shalt thou not uncover: it is thy father's nakedness.
9 “‘Usagonane ndi mlongo wako, mwana wamkazi wa abambo ako, kapena mwana wamkazi wa amayi ako, kaya anabadwira mʼnyumba mwanu kapena kwina.
The nakedness of thy sister, the daughter of thy father, or daughter of thy mother, born at home, or born abroad — their nakedness shalt thou not uncover.
10 “‘Usagonane ndi mdzukulu wako: mwana wa mwana wako wamwamuna kapena mwana wa mwana wako wamkazi. Kutero nʼkudzichotsa ulemu.
The nakedness of thy son's daughter, or of thy daughter's daughter — their nakedness shalt thou not uncover; for theirs is thy nakedness.
11 “‘Usagonane ndi mwana wamkazi wa mkazi wa abambo ako, amene abambo akowo anabereka; popeza ameneyo ndi mlongo wako.
The nakedness of thy father's wife's daughter, begotten of thy father: she is thy sister: thou shalt not uncover her nakedness.
12 “‘Usagonane ndi mlongo wa abambo ako; popeza ameneyo ndi thupi limodzi ndi abambo ako.
The nakedness of thy father's sister shalt thou not uncover: she is thy father's near relation.
13 “‘Usagonane ndi mchemwali wa amayi ako chifukwa ameneyo ndi thupi limodzi ndi amayi ako.
The nakedness of thy mother's sister shalt thou not uncover; for she is thy mother's near relation.
14 “‘Usachititse manyazi mchimwene wa abambo ako pogonana ndi mkazi wake popeza amenewo ndi azakhali ako.
The nakedness of thy father's brother shalt thou not uncover; thou shalt not approach his wife: she is thine aunt.
15 “‘Usagonane ndi mpongozi wako popeza ameneyo ndi mkazi wa mwana wako. Choncho usamuchititse manyazi.
The nakedness of thy daughter-in-law shalt thou not uncover: she is thy son's wife; thou shalt not uncover her nakedness.
16 “‘Usagonane ndi mkazi wa mchimwene wako popeza potero ukuchititsa manyazi mʼbale wakoyo.
The nakedness of thy brother's wife shalt thou not uncover: it is thy brother's nakedness.
17 “‘Usagonane ndi mkazi ndiponso mwana wake wamkazi. Usagonane ndi mwana wamkazi wa mwana wake wamwamuna, kapena mwana wamkazi wa mwana wake wamkazi. Amenewo ndi thupi limodzi ndi mkaziyo. Kutero ndikuchita chinthu choyipa kwambiri.
The nakedness of a woman and her daughter shalt thou not uncover; thou shalt not take her son's daughter, nor her daughter's daughter, to uncover her nakedness: they are her near relations: it is wickedness.
18 “‘Usakwatire mchemwali wa mkazi wako ndi kumagonana naye mkazi wakoyo ali moyo ngati wopikisana naye.
And thou shalt not take a wife to her sister, to vex her, to uncover her nakedness beside her, during her life.
19 “‘Usamuyandikire mkazi kuti ugonane naye pa nthawi yake yosamba.
And thou shalt not approach a woman in the separation of her uncleanness to uncover her nakedness.
20 “‘Usagonane ndi mkazi wa mnzako ndi kudziyipitsa naye.
And thou shalt not lie carnally with thy neighbour's wife, to become unclean with her.
21 “‘Usapereke mwana wako aliyense kuti akhale nsembe yamoto kwa Moleki ndi kuyipitsa dzina la Yehova. Ine ndine Yehova.
And thou shalt not give of thy seed to let them pass through [the fire] to Molech, neither shalt thou profane the name of thy God: I am Jehovah.
22 “‘Usagonane ndi mwamuna ngati mkazi; chimenecho ndi chinthu chonyansa.
And thou shalt not lie with mankind as one lieth with a woman: it is an abomination.
23 “‘Usagonane ndi nyama ndi kudziyipitsa nayo. Mkazi asadzipereke kwa nyama kuti agonane nayo. Chimenecho ndi chisokonezo.
And thou shalt lie with no beast to become unclean therewith; and a woman shall not stand before a beast to lie down with it: it is confusion.
24 “‘Musadzidetse ndi zinthu zimenezi chifukwa umo ndi mmene mitundu ina imene ndikuyithamangitsa pamaso panu inadzidetsera.
Make not yourselves unclean in any of these things; for in all these have the nations which I am casting out before you made themselves unclean.
25 Choncho dziko linayipa ndipo ndinalilanga chifukwa cha tchimo lake. Motero dzikolo linasanza anthu ake okhalamo.
And the land hath become unclean; and I visit the iniquity thereof upon it, and the land vomiteth out its inhabitants.
26 Koma inu mukasunge malangizo ndi malamulo anga. Mbadwa ndiponso alendo amene akukhala pakati panu asakachite china chilichonse cha zinthu zonyansazi,
But ye shall observe my statutes and my judgments, and shall not commit any of all these abominations: the home-born, and the stranger that sojourneth among you;
27 pakuti zinthu zonsezi ndi zomwe ankachita anthu amene ankakhala mʼdzikomo inu musanafike, ndipo dziko linayipitsidwa.
(for all these abominations have the men of the land done, who were before you, and the land hath been made unclean);
28 Koma inu musachite zimenezi kuti dziko lingakusanzeni mutaliyipitsa monga linasanzira mitundu imene imakhalamo inu musanafike.
that the land vomit you not out, when ye make it unclean, as it vomited out the nation that was before you.
29 “‘Aliyense wochita zinthu zonyansa zimenezi achotsedwe pakati pa anthu anzake.
For whoever committeth any of these abominations, ...the souls that commit them shall be cut off from among their people.
30 Choncho mverani malangizo anga oletsa kuchita miyambo yonyansayi imene ankatsatira anthu amene analipo inu musanafike ndi kudziyipitsa nayo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”
And ye shall observe my charge, that ye commit not [any] of the abominable customs which were committed before you; and ye shall not make yourselves unclean therein: I am Jehovah your God.

< Levitiko 18 >